Kodi Mumayamikira Mabuku Athu?
1 Diamondi ndiponso miyala ina ndi yamtengo wapatali osati chifukwa chakuti ndi yokongola basi, komanso chifukwa chakuti imafuna ndalama zambiri kuti aipeze ndi kuikumba. Kudziwa Yehova ndi Yesu Khristu ndi kofunika kwambiri kuposa miyala imeneyi, ndipo mabuku athu ndi okhawo padziko lapansi amene amafotokoza chuma chauzimu chimenechi mozama ndiponso amafotokoza zinthu pogwiritsa ntchito nzeru za Mulungu. (Aroma 11:33; Afil. 3:8) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikiradi mabuku amenewa?
2 Anthu ndiponso mabanja ambiri amaika padera ndalama zokapereka ku Nyumba ya Ufumu m’mabokosi monga lakuti: “Zopereka za Ntchito ya Sosaite ya Padziko Lonse (Mateyo 24:14).” Anthu amaperekanso ndalama zina zothandiza pa ntchito ya padziko lonse akamatenga mabuku kapena magazini, komanso akamaponya m’bokosili ndalama zimene anthu awapatsa muutumiki.
3 Tingasonyezenso kuyamikira posankha anthu oyenera kuwagawira mabuku tikakhala muutumiki. Sitingapereke diamondi wokwera mtengo kwa mwana wamng’ono, amene sadziwa kufunika kwake. Sitiperekanso mabuku athu amtengo wapataliwa kwa anthu omwe sayamikira zinthu zauzimu. (Yerekezerani ndi Aheberi 12:16.) Kuti tifike podzipereka, tinachita zinthu mozindikira, choncho tiyeneranso kukhala ozindikira tikamapereka mabuku athu. Kodi mwininyumba akufunitsitsa kuti tilankhule naye? Kodi akumvetsera tikamalankhula, kuyankha tikamufunsa, ndiponso kuwerenga nawo Baibulo tikamawerenga? Ngati akusonyeza chidwi choterocho, tingathe kumusiyira buku kapena magazini oyenera. Tikamachititsa maphunziro pogwiritsa ntchito mabuku athu, anthu amaphunzira zimene Baibulo limanena ndipo amakhala ndi mwayi wokhala paubwenzi ndi Yehova. Mabuku athu amapindulitsa anthu kwambiri ngati agwiritsidwa ntchito bwino.
4 Ngati timangounjika mabuku ndi magazini pashelefu ku Nyumba ya Ufumu kapena kunyumba kwathu, ndiye kuti sakukwaniritsa cholinga chake ndiponso sitikudziwa kufunika kwake. Ngakhale zinthu zakale monga magazini, mabuku, timabuku ndi timapepala ziyenera kugwiritsidwa bwino ntchito. Kodi ndi liti pamene munapatula nthawi kuti muone magazini amene muli nawo pashelefu? Mungadabwe kupeza kuti muli ndi magazini ambirimbiri. Kodi mabuku ndi magazini amene tili nawo sanang’ambikeng’ambike ndiponso kuda? Ngati ndi choncho, tiyenera kuyesetsa kuwapatsa anthu mu utumiki? Mabuku ndi magazini amene awonongeka mungawasunge kuti muziwagwiritsa ntchito, kuwataya mosamala kapena kuwaotcha. Nthawi zina tingagawire magazini akale ngakhale ena akugawira magazini atsopano.
5 Musanatenge mabuku ndi magazini ogawira muutumiki, muziganizira kuti mufunika ochuluka bwanji. Ndi bwino kuchita zinthu mwanzeru. Ngakhale kuti kukhala ndi mabuku komanso magazini okwanira n’kofunika, makamaka ngati mukuchita upainiya, si bwino kutenga mabuku ndi magazini ambirimbiri. Zinthu zimenezi zimapezeka ku Nyumba ya Ufumu ndipo mungatenge misonkhano isanayambe kapena itatha. Muzikhala ndi mabuku komanso magazini ochepa ndipo mungatenge ena ngati atha.
6 Mabuku ndi magazini athu ndi othandiza kwambiri akaperekedwa kwa anthu amene amayamikira choonadi cha m’Mawu a Mulungu. Choncho, tonse tiziwagwiritsa ntchito mwanzeru, ndipo tikamachita zimenezi timasonyeza kuti tikuyamikira kwambiri mabuku athu.