PHUNZIRO 45
Mafanizo ndi Zitsanzo Zophunzitsadi
MAFANIZO ndi zitsanzo, ndi zida zamphamvu zophunzitsira. Kaŵirikaŵiri zimakhudza mtima ndipo zimakopa chidwi kwambiri. Zimachititsa munthu kulingalira. Zimakhudza maganizo ndi kufika pamtima penipeni. Nthaŵi zina, tingagwiritse ntchito mafanizo pofuna kuwongolera maganizo olakwa. Amathandizanso kukumbukira zinthu. Kodi inu mumawagwiritsa ntchito pophunzitsa?
Mawu ophiphiritsa ndi mafanizo amene amakhala ndi mawu ochepa chabe; koma akhoza kupereka zithunzi za m’maganizo zooneka bwino. Mukawasankha bwino, amanena okha tanthauzo la zimene mukukamba. Koma mphunzitsi akhoza kuzamitsa tanthauzo lakelo mwa kuwonjezera mafotokozedwe achidule. Baibulo lili ndi zitsanzo zambirimbiri zimene mungatengepo phunziro.
Yambani ndi Mawu Oyerekeza Zinthu ndi Ofananitsa Zinthu. Mawu oyerekeza zinthu ndiwo osavuta pa mafanizo onse. Ngati mwangoyamba kumene kuphunzira kugwiritsa ntchito mafanizo, yambani ndi mawu oyerekeza zinthu. Kaŵirikaŵiri amayamba ndi mawu akuti “ngati” kapena “monga.” Poyerekeza zinthu ziŵiri zosiyana, mawu oyerekeza zinthu amaonetsa mbali yofanana mwa zinthu ziŵirizo. Baibulo lili ndi mawu ophiphiritsa ambirimbiri otengedwa ku zinthu zolengedwa—zomera, nyama, ndi zinthu za kumwamba—limodzinso ndi zochitika pa moyo wa munthu. Pa Salmo 1:3, amatiuza kuti munthu amene amaŵerenga Mawu a Mulungu nthaŵi zonse “akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi,” mtengo wobala zipatso ndipo wosafota. Munthu woipa akuti ali “monga mkango” umene umabisalira nyama. (Sal. 10:9) Yehova analonjeza Abrahamu kuti mbewu yake idzakhala “monga nyenyezi za kumwamba” kuchuluka kwake, ndi “monga mchenga wa m’mphepete mwa nyanja.” (Gen. 22:17) Ponena za chibale chenicheni chimene Yehova anali nacho ndi mtundu wa Israyeli, Mulungu anati: “Monga mpango uthina m’chuuno cha munthu,” Iyenso anachititsa Israyeli ndi Yuda kudziphatika kwa Iye.—Yer. 13:11.
Mawu ofananitsa zinthu nawonso amasonyeza kufanana kwa pakati pa zinthu zosiyana. Koma iwo amakhala otsimikiza kwambiri. Amaonetsa ngati kuti chinthu ichi ndicho chinacho, choncho amatenga makhalidwe a chinthu china n’kuika pa china. Yesu anati kwa ophunzira ake: “Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi.” (Mat. 5:14) Pofotokoza mmene mawu osasamala amavulazira, wophunzira Yakobo analemba kuti: “Lilime ndilo moto.” (Yak. 3:6) Davide anati kwa Yehova: “Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa.” (Sal. 31:3) Mawu ofananitsa zinthu osankhidwa bwino kaŵirikaŵiri salira kumasulira kwambiri, ndipo nthaŵi zina salira kumasulira kulikonse. Amagwira mtima chifukwa sapita m’mbali. Mawu ofananitsa zinthu angathandize omvera anu kukumbukira mfundo kwambiri kusiyana ndi mmene mawu chabe angachitire.
Mtundu winanso wa mafanizo othandiza kumveketsa mfundo ndi mawu okokomeza zinthu. Koma ndi ofunika kusamala nawo kuti asapereke ganizo lolakwika. Yesu anagwiritsa ntchito mawu okokomeza pofuna kupereka chithunzi chosaiŵalika pamene anafunsa kuti: “Upenya bwanji kachitsotso kali m’diso la mbale wako, koma mtanda [wa denga] uli m’diso la iwemwini suuganizira?” (Mat. 7:3) Musanayese kugwiritsa ntchito mawu okokomeza kapena mafanizo ena, dziŵani kaye kugwiritsa ntchito mawu oyerekeza zinthu ndi mawu ofananitsa zinthu.
Gwiritsaninso Ntchito Zitsanzo. M’malo mogwiritsa ntchito fanizo, mungaperekenso zitsanzo, kaya zopeka kapena zenizeni. Zitsanzonso n’zofunika kusamala nazo chifukwa kaŵirikaŵiri munthu amatha kupitirira nazo malire mosavuta. Zitsanzo zoterozo ziyenera kuperekedwa pomveketsa mfundo zofunika kwenikweni, ndipo ziperekedwe m’njira yoti mfundo yake ikakumbukike, osati anthu azikumbukira chitsanzo chokhacho.
Ngakhale si zitsanzo zonse zimene zingakhale zenizeni, zonse ziyenera kukhala zokhudza maganizo a anthu kapena zochitika zenizeni. N’chifukwa chake, Yesu pophunzitsa mmene tiyenera kuonera ochimwa olapa anapereka fanizo la munthu amene anakondwera atapeza nkhosa yake yosochera. (Luka 15:1-7) Poyankha munthu amene sanamvetse mfundo ya Chilamulo ya kukonda mnansi wako, Yesu anasimba nkhani ya Msamariya amene anathangata munthu wovulazidwa amene wansembe ndi Mlevi anamulambalala. (Luka 10:30-37) Ngati mukhala ndi chidwi choona mmene anthu amaganizira ndi mmene amachitira zinthu, mukhoza kuphunzitsa mwaluso pogwiritsa ntchito zitsanzo.
Mneneri Natani anasimba nkhani yongoyerekeza pamene anadzudzula Mfumu Davide. Nkhaniyo inam’gwira mtima Davide moti sanathe kupereka chodzikhululukira. Inali nkhani ya munthu wachuma amene anali ndi nkhosa zambiri, ndi munthu wina amene anali ndi kamwana ka nkhosa kakakazi kamodzi kokha kamene anali kukasamalira ndi mtima wake wonse. Davide anali mbusa, choncho anamvetsa mmene mwinikankhosako anakakondera. Davide anakwiya kwambiri ndi munthu wachuma amene analanda munthu wosaukayo kankhosa kamene anakakonda kwambiri. Ndiyeno Natani anauza Davide mosabisa mawu kuti: “Munthuyo ndi inu nomwe.” Nkhaniyo inam’lasa m’mtima Davide, ndipo analapa moonadi. (2 Sam. 12:1-14) Mwa kuyesetsa, mungadziŵe mmene mungasamalire bwino nkhani zimene zingakhale zokwiyitsa.
Zilipo zitsanzo zambiri zophunzitsa zimene tingapeze m’zochitika zolembedwa m’Malemba. Yesu anachita zimenezo m’mawu ochepa chabe pamene anati: “Kumbukirani mkazi wa Loti.” (Luka 17:32) Pofotokoza zizindikiro za kukhalapo kwake, Yesu anatchula “masiku a Nowa.” (Mat. 24:37-39) Pa Ahebri chaputala 11, mtumwi Paulo anatchula mayina a amuna ndi akazi 16 monga zitsanzo za chikhulupiriro. Mukalidziŵa kwambiri Baibulo, mudzatha kupereka zitsanzo zamphamvu kuchokera m’zochitika ndi anthu amene Malemba amanena.—Aroma 15:4; 1 Akor. 10:11.
Nthaŵi zina mungaone kuti mungamveketse mfundo mwa kufotokoza chochitika chenicheni m’moyo wamakono. Komabe, samalani pochita zimenezo kuti musanene nkhambakamwa chabe, komanso peŵani kunena zochitika zimene zingachititse manyazi aliyense mwa omvera anu kapena nkhani zimene anthu angatsutse koma zosakhudzana ndi nkhani yanuyo. Kumbukiraninso kuti cholinga chonenera chochitikacho ndi kuti chithandize kumveketsa mfundo yanu. Musafotokoze zinthu zosafunikira zimene zingachotse maganizo a omvera pa cholinga cha nkhani yanu.
Kodi Adzalimva? Fanizo lililonse kapena chitsanzo chimene mungagwiritse ntchito chiyenera kukwaniritsa cholinga chake. Kodi zingatheke ngati simusonyeza mfundo yake pankhani yanu?
Yesu atanena kuti ophunzira ake ndi “kuunika kwa dziko lapansi,” anawonjezera mawu ena mmene nyali amaigwiritsira ntchito ndi udindo umene anali nawo. (Mat. 5:15, 16) Atapereka fanizo lake la nkhosa yotayika, anafotokoza za chisangalalo chimene chimakhala kumwamba pamene wochimwa mmodzi alapa. (Luka 15:7) Ndiponso atasimba nkhani yake ya Msamariya wachifundo, Yesu anafunsa womvera wake funso lachindunji kenako n’kupereka uphungu wachindunjinso. (Luka 10:36, 37) Koma Yesu anafotokoza fanizo lake la nthaka ya mitundu yosiyanasiyana komanso lija la namsongole wa m’munda kwa odzichepetsa okha amene anatha kufunsa, osati kwa anthu aunyinji. (Mat. 13:1-30, 36-43) Kutatsala masiku atatu imfa yake isanachitike, Yesu anapereka fanizo la antchito olima munda wa mphesa aumbanda. Iye sanatanthauzire lililonse la mafanizowo; sanafunikire kutero. “Ansembe aakulu ndi Afarisi . . . anazindikira kuti alikunena za iwo.” (Mat. 21:33-45) Choncho, kuti mudziŵe ngati kutanthauzira fanizo n’kofunikira kapena ayi, ndiponso pamlingo wotani, zimadalira mtundu wa fanizolo, maganizo a omvera anu, ndi cholinga cha nkhani yanu.
Kuphunzira luso logwiritsa ntchito mafanizo ndi zitsanzo kumatenga nthaŵi, koma mpake chifukwa kumakhala ndi mapindu aakulu. Mafanizo osankhidwa bwino amakopa maganizo ndi kukhudza mtima. Zikatero, uthengawo umagwira mtima kusiyana ndi mmene mawu wamba angachitire.