-
Mafuko a AnthuKukambitsirana za m’Malemba
-
-
Mwamsanga Ufumu wa Mulungu udzawononga dongosolo liripoli la zinthu lopanda umulungu, kuphatikizapo onse amene alibe chikondi chenicheni kwa onse aŵiri Yehova Mulungu ndi anthu anzawo. (Dan. 2:44; Luka 10:25-28) Mawu a Mulungu amalonjeza kuti opulumukawo adzakhala anthu “ochokera ku mitundu yonse ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” (Chiv. 7:9) Atagwirizanitsidwa pamodzi ndi kulambiridwa kwa Mulungu wowona mwa chikhulupiriro mwa Yesu Kristu, ndi mwa kukondana wina ndi mnzake, iwo adzapangadi banja laumuthu logwirizana.
-
-
MaholideKukambitsirana za m’Malemba
-
-
Maholide
Tanthauzo: Masiku amene kaŵirikaŵiri ali a mpumulo wakuthupi ndi sukulu kaamba ka kukumbukira chochitika. Masiku otero angakhalenso nthaŵi za kuchita mapwando abanja kapena achitaganya. Otenga mbali angawawone kukhala achipembedzo kapena kwakukulukulu a zochitika za anthu kapena zadziko.
Kodi Krisimasi iri phwando lochirikizidwa ndi Baibulo?
Deti la kuchita phwandolo
Cyclopædia ya M’Clintock ndi Strong imati: “Kusungidwa kwa Krisimasi sikuli kolamulidwa ndi Mulungu, ndiponso sikuli kochokera mu Chi[pangano] Cha[tsopano]. Tsiku la kubadwa kwa Kristu silingatsimikiziridwe kuchokera mu Chi[pangano] Cha[tsopano], kapenadi, kuchokera kumagwero ena alionse.”—(New York, 1871) Vol. II, p. 276.
Luka 2:8-11 imasonyeza kuti abusa anali kuthengo pausiku pa nthaŵi ya kubadwa kwa Yesu. Bukhu lotchedwa Daily Life in the Time of Jesus limafotokoza kuti: “Nkhosa . . . zinathera nthaŵi yadzinja m’makola; ndipo mwa ichi chokha kungawonedwe kuti deti lovomerezedwa ndi mwambo la Krisimasi, m’dzinja, silikuwonekera kukhala lolungama, popeza Uthenga Wabwino umanena kuti abusa anali kuthengo.”—(New York, 1962), Henri Daniel-Rops, p. 228.
The Encyclopedia Americana imatiuza kuti: “Chifukwa chokhazikitsira December 25 kukhala Krisimasi chiri chokaikiritsa pang’ono, koma kaŵirikaŵiri chimachitidwa patsiku limene linasankhidwa kuyenderana ndi mapwando achikunja amene
-