-
Ndandanda ya Mlungu wa May 23Utumiki wa Ufumu—2011 | May
-
-
Ndandanda ya Mlungu wa May 23
MLUNGU WOYAMBIRA MAY 23
Nyimbo Na. 32 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 7 ndime 9-16 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Masalimo 19-25 (Mph. 10)
Na. 1: Salimo 23:1–24:10 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Ayuda Onse Adzatembenuzidwa Kuti Akhulupirire Khristu?—rs tsa. 44 ndime 1 ndi 2 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Lemba la Aroma 8:21 Lidzakwaniritsidwa Liti Ndiponso Motani? (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zilengezo. “Mmene Mungagwiritsire Ntchito Fomu Yakuti Kaonaneni Ndi Wachidwi Uyu (S-43).” Nkhani yokambirana.
Mph. 10: Mfundo Zitatu Zothandiza Kuti Mawu Oyamba Azikhala Ogwira Mtima. Nkhani yochokera m’buku la Kukambitsirana, tsamba 9 ndime 1. Mukamaliza kufotokoza mfundo za m’bukulo, chitani zitsanzo ziwiri zosonyeza mmene munganenere mawu oyamba pogawira buku logawira m’mwezi wa June.
Mph. 15: Kodi Mwayesapo? Nkhani yokambirana. Kambani nkhani yachidule yofotokoza mfundo za m’nkhani zaposachedwapa za mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Nkhani zake ndi izi: “Kagwiritseni Bwino Ntchito,” “Nkhani Zatsopano Zoyambitsira Maphunziro a Baibulo,” (km 12/10) ndi “Mphatso Yothandiza Kwa Mabanja” (km 1/11). Pemphani omvera kuti afotokoze zimene achita poyesa kugwiritsira ntchito malangizo a m’nkhanizi ndiponso phindu limene apeza.
Nyimbo Na. 6 ndi Pemphero
-
-
Ndandanda ya Mlungu wa May 30Utumiki wa Ufumu—2011 | May
-
-
Ndandanda ya Mlungu wa May 30
MLUNGU WOYAMBIRA MAY 30
Nyimbo Na. 33 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 7 ndime 17-21 ndi bokosi patsamba 75 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Masalimo 26-33 (Mph. 10)
Na. 1: Salimo 31:9-24 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Anthu Otchulidwa M’Baibulo Amene Anasonyeza Kudzichepetsa Kwenikweni (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Ayuda Ayenera Kukhulupirira Yesu Kuti Adzapulumuke?—rs tsa. 44 ndime 3 ndi 4 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zilengezo. Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chimene chili patsamba 4, chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo Loweruka loyamba m’mwezi wa June. Limbikitsani onse kuti ayesetse kuyambitsa maphunziro.
Mph. 15: Mmene Mungafufuzire. Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 33 mpaka 38. Chitani chitsanzo chachidule chosonyeza wofalitsa akulankhula yekha pofufuza m’mabuku athu yankho la funso limene wafunsidwa mu utumiki.
Mph. 10: Konzekerani Kugawira Magazini M’mwezi wa June. Nkhani yokambirana. Kwa mphindi imodzi kapena ziwiri, tchulani nkhani zina zimene zili m’magaziniwo. Kenako sankhani nkhani ziwiri kapena zitatu, ndipo funsani omvera kuti anene mafunso ndi malemba amene tingagwiritse ntchito pogawira magaziniwo. Chitani zitsanzo zosonyeza zimene tinganene pogawira magazini iliyonse.
Nyimbo Na. 37 ndi Pemphero
-
-
Mmene Mungagwiritsire Ntchito Fomu Yakuti Kaonaneni Ndi Wachidwi Uyu (S-43)Utumiki wa Ufumu—2011 | May
-
-
Mmene Mungagwiritsire Ntchito Fomu Yakuti Kaonaneni Ndi Wachidwi Uyu (S-43)
Muzilemba fomu imeneyi mukapeza munthu wachidwi amene sakhala m’gawo lanu kapena amene amalankhula chinenero china. M’mbuyomu tinkagwiritsa ntchito fomuyi tikakumana ndi munthu wolankhula chinenero china ngakhale amene sanachite chidwi ndi uthenga wathu. Koma tsopano tizilemba fomuyi munthuyo akachita chidwi basi. Komabe, tingalembe fomu ya S-43 tikakumana ndi munthu wogontha kaya wasonyeza chidwi kapena ayi.
Kodi fomuyi tizipita nayo kuti tikalembapo zonse zofunikira? Tiziipereka kwa mlembi wa mpingo wathu. Ngati mlembiyo akudziwa mpingo wakufupi ndi kumene munthuyo akukhala, angatumize fomuyo kwa akulu a mpingowo kuti akamuthandize. Koma ngati sakudziwa bwinobwino mpingo umene ungamuthandize, azitumiza fomuyo ku ofesi ya nthambi.
Ngati munthu wolankhula chinenero china amene wachita chidwi ndi uthenga wathuyo akukhala m’gawo lanu, muzimuyenderabe kuti mukulitse chidwi chake mpaka patapezeka wofalitsa wa mpingo wa chinenero chake amene angamuthandize.—Onani Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2009, tsamba 4.
-