Kalekale, ulendo wapansi unali wotopetsa kwambiri, anthu ankayenda nthawi yaitali asanafike kumene akupita ndipo n’kuthekanso kuti ulendo wake unkafuna ndalama zambiri kusiyana ndi ulendo wapanyanja. Komabe, panalibe njira ina yokafikira m’madera ambiri kuposa kuyenda wapansi.
Munthu amene ali paulendo, ankayenda makilomita pafupifupi 30 pa tsiku. Nthawi zina ankavutika chifukwa cha dzuwa, mvula, kutentha kapena kuzizira, komanso ankakumana ndi achifwamba amene ankalanda katundu. Mtumwi Paulo ananena kuti ‘ankayenda maulendo ambirimbiri, ankakumana ndi zoopsa m’mitsinje komanso ankakumana ndi achifwamba pamsewu.’—2 Akor. 11:26.
M’madera amene ankalamuliridwa ndi ufumu wa Roma munali misewu yambiri yokonzedwa bwino. M’mbali mwa misewu ikuluikulu munkapezeka nyumba zogona alendo ndipo kuti munthu apeze nyumba inanso yogona alendo, ankayenda tsiku lonse. Munthu asanapeze nyumba yotsatira yogona alendo, ankapeza mashopu amene ankatha kugula chakudya kapena zinthu zina zofunikira. Anthu olemba mabuku a pa nthawiyo anafotokoza kuti nyumba zogulitsiramo chakudya komanso zogona alendo zinkakhala zauve, munkadzaza anthu, munkakhala chinyezi komanso utitiri. Malo amenewa ankatchuka ndi mbiri yoipa chifukwa kunkapezeka anthu oipa. Kawirikawiri eniake a nyumba zogona alendo ankabera anthu apaulendo komanso ankasunga mahule kuti azigona ndi anthu apaulendowo.
N’zodziwikiratu kuti Akhristu ankayesetsa kupewa malo oterewa. Koma akamayenda m’dera limene kunalibe achibale kapena anzawo, ankakakamizika kukagona m’nyumba zoterezi.