Ntchito Yolalikira ndi Kuphunzitsa Padziko LonseMaine, U.S.A.: Abale athu ‘akusodza anthu,’ potengera chitsanzo cha Yesu
Maine, U.S.A.: Abale athu ‘akusodza anthu,’ potengera chitsanzo cha Yesu
PADZIKO LONSE
MAYIKO 239
OFALITSA 7,782,346
MAOLA ONSE AMENE TINATHERA MU UTUMIKI WAKUMUNDA 1,748,697,447
MAPHUNZIRO A BAIBULO 8,759,988
AFRICA
MAYIKO 58
CHIWERENGERO CHA ANTHU 968,989,710
OFALITSA 1,312,429
MAPHUNZIRO A BAIBULO 2,999,639
Anasintha Maganizo Ake Ofuna Kuchotsa Mimba
Mu mzinda wa Addis Ababa, womwe ndi likulu la dziko la Ethiopia, munkakhala mtsikana wina amene anali ndi shopu, dzina lake Saba. Tsiku lina, alongo awiri anamupeza n’kumupatsa magazini ya Galamukani! imene inali ndi nkhani yokhudza kuchotsa mimba. Saba analowetsa alongowo m’nyumba ndipo misozi ili m’maso anawauza kuti amaganiza zochotsa mimba. Pamene ankakambirana nkhaniyi, onse atatu anamva chisoni kwambiri moti anayamba kulira. Pa tsiku limenelo, Saba anaganiza zoti asachotse mimbayo ndipo anauza mwamuna wake chifukwa chake waganiza choncho. Patapita nthawi, anabereka mwana wamkazi wokongola zedi. Mtsikanayu anayambanso kuphunzira Baibulo n’kubatizidwa. Tikunena pano akusangalala ndi utumiki wa upainiya. Mwamuna wake nayenso anaphunzira Baibulo n’kubatizidwa, ndipo mu April 2012, ana awo awiri anabatizidwanso.
‘Kodi N’zotheka Kulankhula Nawo?’
Kaokoland, ku Namibia: Anthu a misinkhu yosiyanasiyana amachita chidwi ndi mabuku athu amene timagwiritsa ntchito pophunzitsa anthu Baibulo. Panopa kabuku kakuti Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha kakupezeka m’zinenero 452
M’dziko la Ethiopia, woyang’anira dera wina ankalalikira kunyumba ndi nyumba limodzi ndi m’bale wina. Atafika pakhomo lina, anapeza mtsikana wantchito ndipo anamuuza kuti akufuna kulankhula ndi bambo a m’nyumbamo. Wantchitoyo atayankha kuti n’zosatheka, iwo anam’funsa ngati angakonde kuti asiye magazini kuti bambowo awerenge. Wantchitoyo anapita kukafunsa kaye bambowo asanalandire. Atabwerako ananena kuti choyamba bambowo akufuna kuti akawaone kaye magaziniwo.
Choncho abalewo anam’patsa magaziniwo kuti akawaonetse. Patapita mphindi zowerengeka, iye anabwerera n’kudzauza abalewo kuti avomera kuwawerenga. Ndiyeno mmodzi mwa abalewo anafunsa kuti, “Ngati sangathe kutuluka, kodi n’zotheka kuti ifeyo tilowe tikalankhule nawo?” Apanso wantchitoyo anapita kukafunsa bambowo. Ulendo umenewu wantchitoyo anakhala nthawi yaitali kuposa ulendo woyamba uja moti abalewo anayamba kuganiza kuti mwina sabweranso. Kenako anabwera n’kuwauza kuti alowe. Zitatero abalewo anadziwa kuti bambowo, omwe dzina lawo ndi a Yirgu, anali okalamba kwambiri ndipo anakhala ali chigonere kwa zaka 10. Bambowo sankatha kudzuka pabedi kapena kukhala tsonga. Choncho wantchitoyo anachedwa kubwera chifukwa chakuti ankathandiza bambowo kuvala komanso ankakonza m’chipindamo kuti abalewo alowe.
Abalewo anayamba kufotokozera bambowo zokhudza uthenga wabwino. A Yirgu anasangalala kwambiri ndi zimene anamva choncho anavomera kuti aziphunzira Baibulo. Atayamba kuphunzira nawo, bambowo anayamba kupeza bwino. Patapita nthawi, anayamba kudzuka pabedi n’kumayendayenda panjinga ya olumala. Posakhalitsa anayamba kusonkhana ndipo anabatizidwa pa msonkhano wachigawo wapitawu.
Anapeza Tchalitchi Chomwe Chinapatsa Bambo Ake Mabuku
Calvin amene amakhala m’dziko la Zimbabwe, bambo ake anamwalira iye ali ndi zaka zinayi. Pamene bambo akewo ankamwalira, anangomusiyira thumba mmene munali Baibulo la Dziko Latsopano ndi buku la Ulosi wa Yesaya—Muuni wa Anthu Onse 1. Bambowo asanamwalire anauza Calvin kuti “Usadzachoke m’tchalitchi chimene chinandipatsa mabuku awa chifukwa zimene amaphunzitsa n’zoona.”
Nawonso mayi a Calvin atamwalira, iye anayamba kukhala ndi agogo ake aakazi. Kwa zaka 9 Calvin ankakana kupita kutchalitchi cha agogo akewo. Iye ankanena kuti tsiku lina adzapeza “tchalitchi” chimene chinapatsa bambo ake mabuku omwe bambo akewo anamusiyira.
Tsiku lina, agogo ake a Calvin anakumana ndi mlongo wina. Agogowo sanadziwe kuti mayiyo anali wa Mboni, choncho anayamba kumufotokozera kuti ali ndi mdzukulu wovuta kwabasi ndipo amakana kupita ku tchalitchi kwawo. M’malomwake, likafika Lamlungu amangokhalira kuwerenga buku linalake limene bambo ake anamusiyira. Mlongoyo anafunsa dzina la bukulo, ndipo agogowo anayankha kuti: “Liyenera kukhala limodzi mwa mabuku a Watchtower opanda pakewa.”
Ndiyeno mlongoyo anauza agogowo kuti akufuna kuonana naye mnyamatayo. Calvin atakumana ndi mlongoyo anasangalala kwambiri. Tsiku lomwelo, mlongoyo anayamba kuphunzira naye Baibulo pogwiritsa ntchito buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Ndipo nthawi yomweyo anayamba kusonkhana ngakhale kuti agogo akewo ankamutsutsa koopsa. Iye watsimikiza ndi mtima wonse kuti sadzasiya choonadi, ndipo akuyembekezera nthawi imene akufa adzauka kuti adzaonanenso ndi mayi komanso bambo ake. Calvin anabatizidwa mu August 2012.
“Mulungu Amene Ukumutumikira Ndi Wamphamvu Zedi”
Caro akukhala m’dziko la Uganda. Patangopita mwezi umodzi kuchokera pamene anayamba kuphunzira Baibulo, mwamuna wake Martin, amene ankachita zaufiti, anayamba kumutsutsa kwambiri. Martin ankanena kuti: “Mabuku akowa akuchititsa kuti mizimu ya makolo athu isalowenso m’nyumba muno.” Choncho ankamuzunza komanso kumuopseza kuti amupha akapanda kusiya kuphunzira Baibulo. Mwamunayo anasiyanso kusamalira banja lake. Koma Caro sanatekeseke mpang’ono pomwe, ndipo ankalima dimba kuti azipeza zosowa za banja lake kwinaku akupitiriza kuphunzira Baibulo. Patapita nthawi, zinthu zinafika poipa moti moyo wa Caro unali pangozi, choncho anathawa panyumbapo. Iye ankavutika kwambiri kupeza zinthu zofunika pa moyo wake. Komabe, atamva kuti ana ake akudwala, anatenga ndalama zochepa zimene anali nazo n’kuwagulira mankhwala.
Patapita nthawi, Caro analandira foni yochokera kwa mwamuna wake. Mwamunayo anati: “Ndikufuna kuti ubwere kuno. Ndaona kuti Mulungu amene ukumutumikirayo ndi wamphamvu zedi komanso wakhala akukuthandiza. Ndikufuna kuti uuze anthu amene akukuphunzitsawo kuti abwere kudzandiphunzitsanso nane. Ndikufunitsitsa kusintha moyo wanga.” Apa Martin anali atatsimikizadi mtima. Tikunena pano ali limodzi monga banja ndipo akukhala mosangalala. Martin ndi Caro anabatizidwa pa msonkhano wachigawo mu August 2012.
Ankalalikira Yekhayekha M’tauni Ina Yakutali
David yemwe amakhala m’dziko la Kenya, pa nthawi ina anachoka kwawo n’kumakakhala m’tawuni inayake yakutali. Ali kumeneko, iye anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Posakhalitsa, anabwerera kumudzi kwawo ku Lokichar, kumpoto cha kum’mwera kwa dzikolo. Kuchokera kwawo, mpingo wapafupi uli m’tauni ya Lodwar yomwe ili pa mtunda wa makilomita 165. Choncho kwa zaka zinayi, David sankakumana bwinobwino ndi Mboni za Yehova. Komabe iye ankalalikira kwa anthu oyandikana nawo nyumba ndiponso kwa achibale ake. Ankawafotokozera zinthu zimene anaziphunzira pa nthawi yochepa imene ankaphunzira Baibulo. Anthu ena ankamvetsera ndipo posakhalitsa David anayamba kuchititsa maphunziro a Baibulo ambirimbiri. Ndiyeno mu 2007, iye analankhulana ndi abale a ku Lodwar kuja ndipo anayambiranso kuphunzira Baibulo. Ankapitako kawiri pa mwezi ndipo kuti akafikeko ankakwera njinga yamoto, galimoto ndiponso minibasi.
Pamene David ankadziwa zinthu zambiri zokhudza Baibulo m’pamenenso ankachita khama kwambiri kulalikira. Iye anamanga “Nyumba ya Ufumu” yongoyembekezera pafupi ndi nyumba yake. Nyumbayi ndi yomata ndipo anafolera ndi udzu. Mmenemu ndi mmene ankachitiramo misonkhano ndi anthu omwe anali ndi mtima wofunitsitsa kuphunzira Baibulo. Komabe, si anthu onse m’mudzimo amene ankasangalala ndi ntchito yake yolalikira moti kwa zaka ziwiri anthu ankamunyoza ngakhalenso kumumenya kumene. Ulendo wina, anthu ena a m’mudzimo anamumenya mpaka kukomoka. Anthuwo ankanena kuti David akuyambitsa “chipembedzo cha Mdyerekezi” m’mudzimo. Komabe, David atakapempha kwa mkulu wa boma kuti amuthandize, anthu anasiya kumuchitira zankhanza ndipo anapitiriza kulalikira. Iye anati: “Choonadi ndi cha mtengo wapatali kwa ine, ndipo ngakhale atandizunza bwanji sindingachisiye.”
David anabatizidwa mu 2009 ndipo panopa ndi mtumiki wothandiza ndiponso mpainiya wokhazikika. M’dera lonse lakwawo, kuli Mboni ziwiri zokha, iyeyu ndi mwana wake wa zaka 15. Komabe mu April 2012, anthu ena a m’mudzimo okwana 60 anapezeka pa mwambo wokumbukira imfa ya Khristu womwe unachitikira m’Nyumba ya Ufumu yongoyembekezera ija, imene m’baleyu anamanga pafupi ndi nyumba yake.
“Ndiyetu Mutsegulireni Mavesi Osonyeza Kuti Akunenazo N’zabodza”
Janet yemwe ndi mpainiya wokhazikika ku Ghana, ankawerenga buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani m’basi pamene anali pa ulendo wautali. Ndiyeno m’basimo munakwera munthu wina amene ankalalikira. Munthuyo atamaliza kulalikira anapempha anthu kuti amupatse ndalama chifukwa cha ulaliki wakewo. Janet anamufunsa kuti: “Inu mwanena kuti Yesu ndi wofanana ndi Mulungu. Nanga ndi ndani amene analankhula kwa Yesu pa ubatizo wake?”
Wolalikirayo ananena kuti, “N’zovuta kuzimvetsa.”
Kenako Janet anatsegula mutu 4 m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, n’kusankha malemba angapo. Atatero anapempha anthu ena m’basimo kuti awerenge malembawo. Ndiyeno iye anafotokoza kusiyana kwa pakati pa Yesu ndi Yehova, Mulungu Wamphamvuyonse.
Pamenepo mlalikiyo ananena kuti, “Iwe ndiwe mfiti.”
Atanena zimenezi, anthu m’basimo anakhala kumbali ya Janet, ndipo anauza mlalikiyo kuti, “Ndiyetu mutsegulireni mavesi osonyeza kuti akunenazo n’zabodza, m’malo momunena kuti ndi mfiti.” Mlalikiyo anakwiya kwambiri ndipo anatsika pa siteji yotsatira. Mtsikana wina amene anakhala pafupi ndi Janet ananena kuti: “Ine ndinkaganiza kuti Yehova ndi dzina la matchalitchi a Mboni. Sindimadziwa kuti limeneli ndi dzina la Mulungu, moti ndadziwa pamene umakambirana ndi mlaliki uja.”
Janet anakambirana ndi mtsikanayo ndipo anatenga nambala yake ya foni n’kumulonjeza kuti amuimbira. Mtsikanayo atafika kunyumba, anafotokozera agogo ake zimene zinachitika m’basi zija. Agogo akewo anadabwanso kumva kuti dzina la Mulungu ndi Yehova. Ndiyeno Janet anapempha alongo ena kuti apitirize kuphunzira ndi mtsikana uja ndi agogo akewo. Panopa onse amafika pa misonkhano ya mpingo.
AMERICA
MAYIKO 57
CHIWERENGERO CHA ANTHU 946,087,916
OFALITSA 3,861,145
MAPHUNZIRO A BAIBULO 4,196,922
Anapeza Choonadi Kumalo Amene Sankayembekezera
Alonda a kundende m’dziko la Bolivia ankalimbana ndi mtsikana wina wa zaka 20, dzina lake Andrea, kuti alowe m’ndende. Apa n’kuti mtsikanayu akutukwana komanso kulankhula mawu oopseza. Popeza kuti anali wamphamvu ndiponso ankachita zachiwawa, anthu ankachita naye mantha. M’ndendemo munalinso Leidy, amene anali wa Mboni za Yehova, ndipo anamangidwa pa mlandu wongomunamizira. Leidy sankachita mantha ndi Andrea koma ankamumvera chisoni. M’mawa uliwonse Leidy ankakonda kuwerenga mokweza mawu a m’buku la nyimbo. Ndiyeno Andrea atamva mawu a m’nyimboyo, anafunsa kuti, “Kodi ndiwe wa Mboni za Yehova?”
Peru: Kulalikira kwa alimi m’mapiri a ku Utcubamba Valley
Leidy atavomera, Andrea anati: “Mayi anga ndi a Mboni za Yehova, ndipo tinkapitira limodzi ku misonkhano. Komanso ankandiphunzitsa Baibulo.” Atatero Andrea anayamba kulira. Kwa masiku angapo otsatira, Leidy anakhala akukambirana mfundo za m’Malemba ndi Andrea, ndipo tsiku loti Andrea akaonekere ku khoti litakwana, iwo anapempherera limodzi kuti Yehova amuthandize ndi kumutsogolera. Kenako Andrea anatulutsidwa m’ndende ndipo anapitiriza kuphunzira za Yehova. Posakhalitsa anavomerezedwa kukhala wofalitsa wosabatizidwa, ndipo panopa akukonzekera ubatizo.
Ngakhale kuti Leidy anamutsekera m’ndende asanalakwe chilichonse, iye anayambitsa maphunziro 21 m’ndendemo asanatulutsidwe. Panopa Leidy amapita kundendeko katatu pa mlungu kuti akalimbikitse anthu achidwi amene anawasiya kumeneko.
Anadziwa Choonadi Chifukwa cha Webusaiti ya www.pr2711.com
Lamlungu linalake m’chaka cha 2011, bambo wina ndi mkazi wake komanso ana awo awiri analowa m’Nyumba ya Ufumu ku Canada, atatchena bwino. Pa nthawiyi aliyense ankaganiza kuti ndi a Mboni za Yehova ndipo achokera mumzinda winawake. Nthawi yomweyo, bamboyo yemwe dzina lake ndi Marc-Andre, anadziwana ndi Dominic, amene ndi mtumiki wothandiza mumpingowo. Dominic ankaphunzira Baibulo ndi bamboyo zaka 17 m’mbuyomo. Kwa zaka ziwiri izi zisanachitike, Marc-André ndi mkazi wake Josée, ankakopera ndi kuwerenga magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! pa Webusaiti ya www.pr2711.com, ndipo anaona kuti ndi bwino kuti banja lonse lizipita ku Nyumba ya Ufumu. Nthawi yomweyo anayamba kuphunzira Baibulo komanso kupezeka ku misonkhano yonse. Atangophunzira Baibulo kwa miyezi iwiri yokha, banjali linayamba kuchita Kulambira kwa Pabanja mlungu uliwonse. Banjali likupita patsogolo mwauzimu ndipo Josée anakamba nkhani yake yoyamba mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu mu May 2012.
‘Anandipatsa Chakudya Chake Ndiponso Chipewa Chake’
Mnyamata wina wa zaka 10, dzina lake Marcelo, ali pa msonkhano wachigawo mu 2010 ku Chile, anaona kuti bambo wina wachikulire yemwe anakhala naye pafupi, analibe buku lililonse.
Marcelo ananong’oneza mayi ake kuti, “bambowa alibe Baibulo.”
Ndiyeno mayi akewo anamunong’onezanso kuti, “Muzionera limodzi Baibulo lakolo.” Choncho Marcelo anasunthira pafupi ndi bambowo n’kumaonera nawo limodzi Baibulo lake. Marcelo limodzi ndi bambowo, omwe dzina lawo anali a Victor, ankawerenga malemba onse amene atchulidwa. Nthawi yopuma itakwana, Marcelo anauzanso mayi akewo kuti, “Alibenso chakudya.” Mayi akewo anamuuza kuti adyere limodzi chakudya chakecho ndi bambowo. Choncho Marcelo anapatsa bambowo buledi ndi kapu ya tiyi. Pamene bambowo ankadya chakudyacho, Marcelo anawaonetsa malemba onse a m’Baibulo amene ankawakumbukira.
Masana, dzuwa linkatentha kwambiri. Ndiyeno Marcelo anauzanso mayi akewo kuti, “Bambowa alibensotu chipewa. “
Mayi akewo anamuyankha kuti, “Apatse chakocho.” Iye anawapatsadi. Msonkhanowo utatha, Marcelo ndi a Victor anatsanzikana.
Msonkhano wachigawo wotsatira, Marcelo anayamba kufufuzafufuza kuti aone ngati a Victor abwera ku msonkhanowo. Marcelo anasangalala kwambiri atawapeza ndipo pa nthawiyi anali atavala taye. Ndiyeno a Victor ataona Marcelo ananena kuti: “Ine ndili pano lero chifukwa cha mwana uyu. Chaka chatha, ndinaitanidwa ku msonkhano wachigawo ndipo ndinapitadi. Mwana uyu anandipatsa Baibulo lake kuti tiziwerengera limodzi. Anandipatsanso chakudya chake chamasana ndiponso chipewa chake. Tsopano ndikuphunzira Baibulo.” Panopa a Victor ndi wofalitsa wosabatizidwa.
Mtolankhani Wina Anayamikira Kwambiri
Mtolankhani wina wodziwika kwambiri ku Venezuela anafotokoza mu nyuzipepala, mmene anamuthandizira ku kampani ina ya mafoni atawaimbira kuti amuthandize. Iye anakhumudwa kwambiri chifukwa munthu amene anayankha foniyo anali wopanda ulemu komanso wolankhula mokhadzula. Koma ataimbanso, amene anayankha foniyo anali mnyamata wina amene anati dzina lake ndi “Misael” ndipo anamuthandiza bwino kwambiri komanso mwaulemu. Iye analemba kuti: “Ndinachita chidwi kwambiri ndi mmene mnyamatayu anandisonyezera kukoma mtima, ulemu ndiponso mtima wofunitsitsa kundithandiza. Nthawi yonse imene ndimakambirana naye, iye anali wofunitsitsa kuchita zimene ndinamupempha. Chifukwa cha thandizo lake, ndinaphunzira mmene ndingathetsere vuto limene ndinali nalo komanso zimene ndingachite mtsogolo ngati vutoli litachitikanso.”
Mayiyu atayamikira, Misael anafotokoza kuti monga wa Mboni za Yehova amayesetsa kuchita zinthu ndi anansi ake m’njira imene Yesu anaphunzitsa. Ndiyeno mtolankhaniyo anapempha kuti alankhule ndi abwana ake a Misael. Iye anayamikira kwambiri Misael pamaso pa abwanawo chifukwa cha ntchito yabwino imene akugwira. M’nkhani imene mtolankhaniyu analemba, ananena kuti Misael ndi nzika yachitsanzo chabwino ku Venezuela ndipo ndi wa Mboni za Yehova. Kumapeto kwa nkhaniyi, iye anati: “Anthu oterewa ndi amene akufunika pa ntchito zonse zokhudzana ndi kuthandiza anthu.”
“Khalani Omvera”
Mexico City, ku Mexico: Maphunziro a Baibulo ambiri pa maphunziro oposa 1 miliyoni amene anthu anachititsa m’dzikoli anawapeza pochita ulaliki wa mumsewu
Mtsikana wina wa zaka 15 yemwe anabadwa wogontha, dzina lake Gabriela amene amakhala m’dziko la Ecuador, anasangalala kwambiri atabatizidwa pa msonkhano wachigawo mu October 2011. Ndiyeno mlungu wotsatira atabwerera ku sukulu, anapempha aphunzitsi ake kuti ali ndi mawu achidule amene akufuna kuuza anzake m’kalasimo. Aphunzitsiwo anamulola kuchita zimenezi ndipo iye anapita kutsogolo n’kulankhula molimba mtima kwa anzake a m’kalasimo m’chinenero chamanja kuti: “Ndikufuna kukudziwitsani kuti mlungu watha Lachisanu, Loweruka ndi Lamlungu, ndinali ku msonkhano wachigawo kumene ndabatizidwa monga wa Mboni za Yehova. Ndikufuna kukuuzaninso kuti mapeto a nthawi ino ali pafupi kwambiri. Pangotsala nthawi yochepa kuti afike. Ndiye mukufunika kusintha mwamsanga moyo wanu. Choncho khalani omvera. Muziopa Mulungu.” Anzakewo anachita chidwi kwambiri.
Tsiku lomwelo pa nthawi yopuma, Katty anapita kwa Gabriela kuti akamufunse za msonkhanowo. Katty ndi wa Mboni amene anasiya kulalikira komanso ndi wogontha. Poyankha, Gabriela anamuuza mosapita m’mbali kuti: “Unali msonkhano wabwino kwambiri. Koma popeza kuti ndine Mboni yobatizidwa tsopano, ndikufuna kukhala wokhulupirika kwa Yehova. Choncho ndati ndikuuze kuti iweyo sukhalanso mnzanga chifukwa umachita zinthu zosayenera. Ndiye kuti ndikhale mnzako, ndiwononga ubwenzi wanga ndi Mulungu. Ukufunikira kusintha. Ungachite bwino kupemphera kwa Yehova ndiponso kukafotokozera akulu. Ndikudziwa kuti ukhoza kusintha n’kumachita zabwino.” Chifukwa cha malangizo achikondi komanso osapita m’mbali a Gabriela, Katty analankhula ndi akulu ndipo anathandizidwa mwauzimu moti anayambiranso kulalikira mwakhama.
Anagwiritsa Ntchito Kompyuta ya Aphunzitsi Ake
Mlongo wina wa zaka 16 ku United States anapanikizidwa ndi mafunso okhudza chipembedzo chake, ochokera kwa anzake a m’kalasi. Koma mlongoyu analibe buku lililonse, ngakhalenso Baibulo. Komabe iye ankafunitsitsa kuyankha mafunso a anzakewo pogwiritsa ntchito malemba. Choncho anabwereka kompyuta ya aphunzitsi ake n’kutsegula Webusaiti ya www.pr2711.com. Atatero anatha kuyankha mafunso awo onse komanso anawasonyeza mmene angagwiritsire ntchito Webusaiti yathu. Iye anawauza kuti akakhala ndi funso lililonse la m’Baibulo koma palibe wa Mboni woti awathandize, azingotsegula Webusaiti imeneyi ndipo adzapeza mayankho. Mkati mwa mlungu umenewo mlongoyu anaona kuti anzakewo sankamufunsanso mafunso ambiri ngati poyamba. Atawafunsa chifukwa chake, ena ankamuuza kuti nthawi zonse ankafufuza okha mayankho pa Webusaiti yathu pogwiritsa ntchito foni zawo za m’manja. Aphunzitsi akenso ankachita zomwezo.
KU ASIA NDI KU MIDDLE EAST
MAYIKO 48
CHIWERENGERO CHA ANTHU 4,222,869,785
OFALITSA 674,608
MAPHUNZIRO A BAIBULO 662,736
Kabuku Kanathandiza Kuti Pasachitike Ndewu
Tsiku lina abale ndi alongo m’dziko la Indonesia, ankapita kumaliro ndipo anadutsa m’mudzi wina waung’ono. Ndiye mpainiya wina anaona kagulu ka anyamata ali m’mbali mwa msewu. Iye anacheza nawo n’kuwapatsa kabuku kakuti, Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. Patapita nthawi, mlongo wina anadutsa njira yomweyo pobwerera kunyumba. Mlongoyu akuyenda, bambo wina anamuthamangira ali ndi kabukuko ndipo anamuthokoza chifukwa chopatsa ana ake kabukuko. Bamboyo anati: “Kabukuka kapulumutsa moyo wa ana anga.” Popeza kuti mlongoyo sankadziwa nkhani yonse anawapempha kuti amufotokozere zomwe zinachitika. Bamboyo anafotokoza kuti ana ake limodzi ndi anyamata ena anakonza zokachita ndewu m’mudzi winawake. Malinga ndi chikhalidwe chakumaloko, anyamatawo ankafuna kukabwezera anthu omwe anamenya mnzawo. Koma anyamatawo atawerenga kabukuko, anapeza mfundo yoti anthu andewu sadzalowa mu Paradaiso amene akubwera. Choncho anaganiza zoti asapitenso kokamenyanako ndipo anangobwerera kunyumba. Apatu uthenga wa m’Baibulo wa m’kabukuka unathandiza kuti ndewu yoopsa isachitike.
Mwamuna Wodziona Ngati Wamkazi Anasintha Moyo Wake
Shau Kei Wan, Hong Kong: Akulalikira mtsikana pamsika
Rek anakulira m’banja labwinobwino ku Cambodia. Koma kuyambira ali wamng’ono kwambiri, iye ndi m’bale wake amene anabadwa naye mapasa ankadziona kuti anali aakazi. Iwo ankasewera ndi zidole komanso ankakonda kuvala zovala zachitsikana. Amayi awo anathedwa nzeru ndipo ankachita manyazi moti sankadziwa choti achite kuti anyamatawa asiye zimenezi. Anyamatawa ankapita kusukulu atavala zovala zachimuna, koma akangofika kusukuluko ankasintha n’kuvala zovala zachikazi. Mapasawa atakwanitsa zaka 16, analowa mpikisano wa amuna okongola amene amadziona ngati akazi. Izi zinachititsa kuti atchuke kwambiri ndipo anayamba kuoneka m’mapulogalamu a pa TV komanso kuchita zisudzo. Posakhalitsa, Rek anayamba kugona ndi amuna anzake ndipo ankakonda kucheza ndi amuna amenenso amadziona ngati akazi.
Amayi ake a Rek analowa tchalitchi chinachake ndipo ankakakamiza Rek kuti azipita nawo. Amayi akewo anamukakamiza kuti azivala zovala zachimuna ndipo Rek anavomera. Komabe iye anakana kumeta tsitsi lake lomwe linali lalitali kwambiri. Kawirikawiri abusa akutchalitchiko ankamunyoza chifukwa cha zimene ankachitazo. Komabe, Rek ankaona kuti ndi bwino kuti azipitabe kutchalitchiko kuti abusawo azikam’phunzitsa Baibulo. Choncho mlungu woyamba, analawirira m’mawa kupita kutchalitchiko pa njinga, ngakhale kuti unali mtunda wa makilomita ambiri. Koma atafika kumeneko m’busa uja ananena kuti satha kumuphunzitsa. Mlungu wotsatira, m’busa uja analephera kufika kutchalitchiko ndipo zimenezi zinakhumudwitsanso Rek kwambiri.
Ndiyeno Rek atabwerera kunyumba, mchimwene wake uja anamuuza kuti kunabwera mayi wina ndipo wamupempha kuti aziphunzira naye Baibulo kwaulere. Mlongoyo anasiya buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Kenako iye limodzi ndi mwamuna wake anayamba kuphunzira Baibulo ndi mapasawo. Patapita miyezi 6, mchimwene wake wa Rek uja anaona kuti sangathe kusintha moyo wake ndipo anasiya kuphunzira. Koma Rek anakhudzidwa kwambiri ndi lemba la 1 Akorinto 6:9, 10 ndipo anaona kuti anafunika kusintha. Iye anasintha kwambiri moyo wake chifukwa chophunzira mwakhama, kuwerenga Baibulo, kupemphera ndiponso kusonkhana. Mayi akenso akuphunzira Baibulo ndipo akupita patsogolo mwauzimu. Rek atabatizidwa, mayi ake ananena misozi ili m’maso kuti, “Ndine wosangalala kwambiri kuti mwana wanga wabatizidwa monga mwamuna.” Panopa Rek ndi mpainiya wokhazikika.
Mayi Wochita za Mizimu Anasintha Moyo Wake
Or-Ya ankachita zamizimu, kuchiritsa, kupereka malangizo komanso kulosera za m’tsogolo. M’bale wina limodzi ndi mkazi wake, omwe akuchita upainiya wapadera ku Haifa m’dziko la Israel, anakumana ndi mayiyu pamene iwo ankalalikira nyumba ndi nyumba. Powalonjera, mayiyu anati: “Ngati mwabwerera za mawu a Mulungu, lowani.” M’nyumbamo munali modzaza zinthu zamizimu. Mayiyu ankanena kuti amalandira mauthenga ochokera kwa Mulungu ndipo ena ankadzera mwa “mzimu” wa mphunzitsi wina wachipembedzo chachiyuda yemwe anamwalira.
Mayiyu anasangalala kwambiri atamupempha kuti aziphunzira naye Baibulo kwaulere pogwiritsa ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Masiku awiri apainiyawa asanabwere panyumbayo, iye anali atapemphera kuti Mulungu amutumizire munthu woti azimuphunzitsa Baibulo n’kumatanthauzira popanda kugwiritsa ntchito zikhulupiriro za aphunzitsi achipembedzo chachiyuda. Pasanathe mwezi umodzi akuphunzira, mayiyu anafunsa kuti, “Kodi palinso anthu ena amene amakhulupirira zimenezi?” Choncho apainiya aja anamuitanira ku misonkhano ya mpingo ndipo anasangalala ndi mmene abale ndi alongo anamulandirira. Kuchokera pamenepo, Or-Ya wakhala akusonkhana nthawi zonse.
“Ndiyetu mwangotsala ndi miyezi iwiri yokha kuti mundithandize kukonzekera ubatizo”
Patadutsa miyezi iwiri akuphunzira, Or-Ya anafunsa za msonkhano wotsatira kuti: “Si paja kumsonkhano n’kumene kumakhala ubatizo? Ndiyetu mwangotsala ndi miyezi iwiri yokha kuti mundithandize kukonzekera ubatizo.” Posonyeza kuti wafunitsitsa kukabatizidwa, choyamba anataya zinthu zonse zodula zokhudzana ndi mizimu zomwe anali nazo. Kenako anasiya kuchita zamizimu ndipo anayamba kulalikira. Iye ankapereka buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani komanso magazini kwa anthu omwe kale ankawapatsa mankhwala. Or-Ya atadwala, anakana kugwiritsa ntchito njira zochiritsa zokhudzana ndi kukhulupirira mizimu. Chifukwa chosiya ntchito yake yokhudzana ndi zamizimu, anakhala wopanda ndalama kwa miyezi inayi. Komabe, pofufuza ntchito ankafuna ntchito yoti azigwira masiku 4 pa mlungu komanso maola 6 pa tsiku. Iye ankafuna ntchito yotere kuti azikhala ndi nthawi yophunzira payekha, kupita kumisonkhano komanso kupita kokalalikira. Patapita nthawi, anapezadi ntchito yabwino. Kenako anagulitsa nyumba yake yaikulu n’kumakachita lendi m’kanyumba kakang’ono.
Patapita nthawi, Or-Ya anakwanitsa zonse zofunika kuti akabatizidwe. Koma kutatsala mlungu umodzi kuti tsiku la msonkhano lifike, iye anathyoka mwendo. Ngakhale zinali choncho iye anabatizidwabe, koma mwendo wake uli m’chikhakha. Panopa Or-Ya ndi wofalitsa wakhama ndipo amalalikira kwa anthu amene kale ankawapatsa mankhwala komanso akuchititsa maphunziro a Baibulo.
Munthu wa Chipembedzo Chinachake Chachilendo Anaphunzira Choonadi
M’bale wina anayambitsa phunziro la Baibulo ndi anyamata awiri ogontha amapasa kudera lina lamapiri m’dziko la Philippines. Anyamatawa anali m’chipembedzo chinachake chimene anthu ake amakhulupirira kuti akavala zithumwa komanso masikafu, palibe chida chilichonse chimene chingawavulaze. Iwo anaphunzitsidwa mmene angagwiritsire ntchito mipeni, zikwanje komanso mfuti ndipo anamenya nkhondo zambiri polimbana ndi zigawenga m’mapiri. Akuluakulu achipembedzocho anauza anyamatawo kuti awalola kuphunzira Baibulo pokhapokha ngati a Mboniwo sawakakamiza kusiya chipembedzo chawocho.
Koma abale analimbikitsa anyamatawo kuti asankhe okha zochita malinga ndi zimene ankaphunzira m’Baibulo. Mnyamata mmodzi anaona kuti sangathe kusintha moyo wake kuti atumikire Mulungu m’njira yoyenera. Koma winayo anapitiriza kuphunzira. Pofuna kumulimbikitsa, m’bale amene ankaphunzira nayeyo anatsegula Baibulo n’kumufotokozera pogwiritsa ntchito chinenero chamanja kuti: “Dzina lako lakuti Samueli, lili m’Baibulo. Samueli wa m’Baibuloyu ankatumikira Yehova, Mulungu woona, mpaka atakalamba kwambiri. Iwenso ungathe kumvera Yehova ndi kukhala wokhulupirika kwa iye.” Mawu amenewa anamufika pa mtima Samueli. Iye anayamba kuganiza kuti: “Ngati dzina langa lili m’Baibulo, nanenso ndiyenera kukhala kumbali ya Yehova.” Kenako anauza akuluakulu a kuchipembedzo chakecho kuti akuchoka m’mapirimo. Atatero anawotcha zithumwa zake pamodzi ndi zinthu zonse zokhudzana ndi kukhulupirira mizimu, ndipo anapita patsogolo mwauzimu. Tikunena pano, anabatizidwa ndipo akutumikira Yehova mwakhama komanso akuthandiza anthu ena osamva kuti adziwe choonadi cha m’Baibulo.
Mnyamata Wamng’ono Anazunzidwa Chifukwa cha Chikhulupiriro Chake
Erdenet, ku Mongolia: M’bale ndi mlongo akuphunzira Baibulo ndi mayi yemwe amakhala kumidzi yakutali
Mnyamata wina dzina lake Rajiv amakhala m’mudzi wina kumpoto kwa dziko la India. Mnyamatayu ali ndi zaka 9 ndiponso ali mu sitandade 4, mphunzitsi wake, amene anali wa Mboni za Yehova ankaphunzitsa anawo kukhala ndi makhalidwe abwino pogwiritsa ntchito buku lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Rajiv anamvetsa mfundo za m’buku limeneli ndipo anayamba kuzigwiritsa ntchito. Iye anauza mphunzitsi wakeyo kuti wasiya kunena bodza komanso kumenyana ndi ana asukulu anzake. Rajiv ananenanso kuti tsopano akumagawana chakudya cha masana ndi anzake omwe alibe.
“Mwachita kundikakamiza kuti ndiweramire fanoli koma simungakakamize mtima wanga kusintha zimene ndimakhulupirira”
Iye anapitiriza kuphunzira za malonjezo okhudza Paradaiso ndipo anayamba kuuza anzake uthenga wabwinowu m’mudzi mwawo ndiponso kwa anthu amene ankakwera nawo sitima popita ndi pobwera kusukulu. Koma makolo ake ankadana nazo zimenezi ndiponso zinkawachititsa manyazi. Choncho anamuuza kuti asiye kulankhula za Yehova ndi Yesu. Koma iye anapitirizabe, chotero anayamba kumumenya. Akaweruka kusukulu, mayi ake ankamubisira zovala kuti asapite kukauza ena za chikhulupiriro chake chatsopanocho. Makolo akewo sankamulolanso kuti azigona pabedi lake ndipo ankamumana chakudya. Ataona kuti zonsezi zakanika, anaitana wansembe kuti adzathandize mnyamatayo kusintha maganizo ake.
Wansembeyo anakhala kunyumba kwawoko kwa masiku ambiri ndipo anayesetsa kukakamiza Rajiv kuti aweramire fano. Koma Rajiv ananena kuti fanolo ndi mwala chabe osati mulungu wamoyo. Atatero wansembeyo anayankha kuti ngati mnyamatayo akufuna kumvetsa bwino za fanolo, sakufunika kumangoganizira zimene akuonazo basi, koma aziganiziranso kuti kuseri kwa fanolo kuli mulungu. Pamenepo Rajiv anatenga pepala n’kulemba chiwerengero cha ndalama zokwana “100 rupee.” Kenako anapereka pepalalo kwa wansembe uja n’kumuuza kuti akamugulire chokoleti ndiponso akabweretse chenje. Wansembeyo anamuyankha kuti iye si wopusa, chifukwa imeneyo si ndalama, langokhala pepala lopanda ntchito. Ndiyeno Rajiv anauza wansembeyo kuti: “Musamangoganizira zimene mukuonazo basi, muziganiziranso kuti kuseri kwa pepalalo kuli ndalama.” Wansembeyo anapsa mtima ndipo anagwira mutu wa Rajiv n’kumuweramitsa pa fanolo. Pamenepo Rajiv anati: “Mwachita kundikakamiza kuti ndiweramire fanoli koma simungakakamize mtima wanga kusintha zimene ndimakhulupirira.” Pamapeto pake, wansembeyo anangotsazika n’kunena kuti n’zosathekanso kumusiyitsa mnyamatayo zimene amakhulupirira. Ndipo ananenanso kuti ngati atapitirizabe kukhala naye ndiye kuti wansembeyo ndi amene angasinthe chikhulupiriro chake. Zitatero makolo a Rajiv anamusamutsira ku sukulu ina. Koma iye sanasiye kuuza anthu ena za Yehova ndi lonjezo la Paradaiso. Panopa Rajiv ali ndi zaka 10 ndipo akupitiriza kudalira Yehova kuti amuthandize kukhalabe ndi chikhulupiriro cholimba.
Anapeza Baibulo Lomwe Ankalifuna
Pamene Larisa ankalalikira munthu wogulitsa m’sitolo yamabuku, ku Armenia, panabwera mayi wina kudzafunsa ngati m’sitoloyo muli Baibulo la “Dziko Latsopano.” Munthu wogulitsayo ananena kuti alibe Baibulo limenelo koma akhoza kumupatsa lina la Chiameniya. Mayiwo anamufunsa kuti: “Kodi ndi losavuta kumva?” Wogulitsayo anamuwerengera mavesi angapo n’kumuuza kuti: “Likuoneka ngati ndi losavuta kwenikweni.” Koma mayiwo sanakhutire ndipo ananena kuti amafunitsitsa Baibulo la “Dziko Latsopano.” Mwamsanga Larisa anakumbukira kuti anali ndi Baibulo la Chiameniya m’chikwama chake. Choncho anawasonyeza n’kuwauza kuti awerenge mutu wa Baibulolo. Mayiwo anawerenga kuti, “Baibulo la Dziko Latsopano,” chotero iwo anasangalala kwambiri kuti apeza Baibulo limene ankalifuna.
Mayiwo anafotokoza kuti mwana wawo wamkazi ndi mwamuna wake ali ku Greece ndipo anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Popeza kuti anali asanaphunzire Chigiriki iwo anapempha mayi awo kuti akamadzapitanso ulendo wotsatira adzawapititsire Baibulo la Dziko Latsopano la Chiameniya. Mlongo wathuyu anapereka Baibulolo kwa mayiwo n’kuwauza kuti, “Kawapatseni, ndipo mukawauze kuti ndi mphatso yochokera kwa Yehova.” Mayiwo anasangalala kwambiri Larisa atawapempha kuti aziphunzira nawo Baibulo. Choncho anapatsana manambala a foni kuti mayiwo akadzabwera kuchokera ku Greece, adzayambe kuphunzira nawo Baibulo.
EUROPE
MAYIKO 47
CHIWERENGERO CHA ANTHU 738,679,198
OFALITSA 1,595,888
MAPHUNZIRO A BAIBULO 841,260
Anabweza Kachikwama ka Ndalama
Mlongo wina yemwe ndi mpainiya wokhazikika ku Bosnia, dzina lake Nina, anayamba kuphunzira Baibulo ndi banja lina la anthu a mtundu wa Chiroma. Tsiku lina, mtsikana wa zaka 10 wa m’banjali akuyenda mumsewu anatola kachikwama ka ndalama, mmene munalinso makhadi akubanki ndi zinthu zina. M’mbuyomu asanaphunzire choonadi, akatola ndalama ankaona kuti wapatsidwa mphatso. Koma pa nthawiyi anaganiza zokambirana ndi amayi ake, ndipo anagwirizana zokapereka kachikwamako kwa apolisi. Kuchita zimenezi sikunali kophweka chifukwa banjali linali losauka ndipo linalibe ndalama yogulira chakudya. Apolisiwo anadabwa ndi zimene banjali linachita. Patapita maola awiri, analandira foni yowaitana kuti apite kupolisiko. Mwiniwake wa kachikwamako anali akuwadikirira kupolisiko kuti akawathokoze ndi kuwapatsa chionamaso. Iye anawapatsa ndalama zokwana madola 30 a ku United States, zomwe zinali zofanana ndi malipiro a ntchito ya masiku awiri.
Bambo Wina Anachita Chidwi ndi Mutu wa Nkhani ya M’magazini
Gjógv, ku Faroe Islands: Mu 2012, ku zilumba zimenezi kunali ofalitsa 118
Nihad wa ku Bosnia, atamaliza kulalikira n’kubwerera pamene anaimika galimoto lake, anapeza bambo wina ataima pafupi ndi galimoto lakelo. Atam’patsa moni, bamboyo ananena kuti: “Pepani, ndaona magazini inayake m’galimoto yanuyi, yomwe ili ndi nkhani yakuti ‘Kodi Mungatani Kuti Mukhale Bambo Wabwino?’ Ndikufuna mundigawireko. Ndakhala ndikukuyembekezerani pano kwa pafupifupi ola limodzi. Kodi mungandipatseko?” Nihad anasangalala kwambiri ndipo anam’patsa magaziniyo komanso anamulalikira.
Ogwira Ntchito M’sitima ya Pamadzi Analimbikitsidwa
Pamene m’bale wina ndi mkazi wake ankalalikira padoko la Rotterdam ku Netherlands, anakumana ndi anthu ogwira ntchito m’sitima yonyamula mafuta amene ankaoneka achisoni. Mkulu wa akatswiri okonza sitimayo anawauza misozi ili m’maso kuti akumana ndi zoopsa pa ulendo wawo moti sitimayo yawonongeka chifukwa inachita ngozi. Kenako anafunsa kuti, “Ndiye simutipempherera?” M’baleyo analonjeza anthuwo kuti mawa adzawakambira nkhani yolimbikitsa ya m’Baibulo. Ndiyeno tsiku lotsatira, 7 koloko madzulo, m’bale ndi mlongoyo limodzi ndi mabanja enanso awiri anafika padokopo ndipo anawalowetsa kutsogolo kwa sitimayo. Mmenemo anapeza muli anthu ogwira ntchito m’sitimayo okwana 15. Choncho atapereka pemphero, m’bale uja anakamba nkhani yakuti “Kodi Mulungu ndi Amene Amayambitsa Masoka?” Anthu ogwira ntchito m’sitimawo ankawerenga okha malemba chifukwa abalewo anabweretsa mabaibulo ena ndipo anathandiza anthuwo kuti azitsegula okha malemba. Atapereka pemphero lomaliza, anthuwo anakhalabe pansi n’kumakambirana ndi abalewo. Ogwira ntchito m’sitimawo analimbikitsidwa ndipo anathokoza kwambiri. Mmodzi wa iwo ananena kuti, “Ili ndi yankho la mapemphero athu.” Anthu ogwira ntchito m’sitimawo anatenga mabuku okwana 20 komanso mabaibulo ndi zinthu zina. Kenako woyendetsa sitimayo anapatsa abalewo envulopu mmene munali chopereka cha ndalama zokwana madola 200 a ku America.
Anapemphera Kuti Athandize Munthu Wina
Irene, amene amakhala ku Sweden, analemba kuti: “Panopa ndili ndi zaka 80, ndipo chifukwa cha kudwaladwala ndimalephera kupita mu utumiki. Ndinapemphera kwa Yehova kuti ndikufuna kuthandiza munthu aliyense amene ndinakumana naye m’mbuyomo ndipo panopa angakonde kuti ndipitirize kukambirana naye kapena kumuchezera.
“Tsiku lina ndinangomva foni ndipo amunanga anayankha. Mayi wina ndi amene anaimba foniyo ndipo anati: ‘Pepani, ndakumbukira inuyo pa anthu onse amene ndinacheza nawo, ndiye chifukwa chake ndakuimbirani. Kodi akazi anu angakonde kubwera kwathu kuti tidzakambirane Mawu a Mulungu? Ine ndinkaphunzira Baibulo zaka 15 kapena 20 zapitazo, koma malemu mwamuna wanga ankandikaniza, choncho ndinasiya kuphunzira.’
Irene anati: “Ndinakumbukira kuti tinapita kwa mayi ameneyu ndi mlongo wina amene ankaphunzira naye Baibulo. Ndinadabwa kuti mayiyo anandikumbukira. Koma ndinasangalala kwambiri, choncho ndinakonza zoti tikumane. Kuchokera nthawi imeneyo takhala tikuphunzira mlungu uliwonse moti anabwera ku Chikumbutso komanso ku nkhani yapadera. Panopa mayiyu anayamba kupezeka pa misonkhano ya mpingo. Ndimathokoza Yehova tsiku lililonse chifukwa choyankha pemphero langa.”
M’bokosi la Zopereka Sitingaponyemo Chokoleti
Mnyamata wina wa zaka 8 amene amakhala ku Italy, dzina lake Sergio, ankafuna kutsimikizira akulu kuti akufuna kukhala wofalitsa wosabatizidwa. Tsiku lina anapita ndi bambo ake kukakonza loko wa chitseko cha nyumba ya banja lina. Bambo ndi mayi a m’banjali ali ndi zaka za m’ma 70. Popita kumeneko, Sergio anatenga magazini. Iye anafotokoza kuti: “Pamene bambo ankakonza lokoyo, ine ndinkagawira magazini kwa abambo a m’nyumbamo. Abambowo anachita chidwi ndipo anaitana akazi awo n’kuwaonetsa magaziniwo. Kenako ndinalemba dzina lawo, adiresi yawo ndi nambala yawo ya foni kuti ndidzabwerenso. Akazi a bambowo ndi amene anandiuza zonse zimene ndinalembazo ndipo anandipatsanso chokoleti chachikulu.” Patapita masiku angapo, Sergio limodzi ndi mkulu wina wa mumpingo wawo anapitanso kukaonana ndi banjali. Atafika, Sergio anagogoda pakhomo ndipo mkazi wa bambo aja anayankha. Ndiyeno Sergio anawauza kuti akufuna kuwapatsa buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Mayiwo analandira bukulo mosangalala kwambiri ndipo anam’patsanso chokoleti china. Sergio ananena kuti: “Popeza kuti sindikanatha kuika chokoleticho m’bokosi la zopereka, ndinachidya.” Ndiyeno anawonjezera kuti, “Zitatero, akuluwo anamvetsa kuti ndikufunitsitsa kukhala wofalitsa wosabatizidwa.”
M’busa Ankafunitsitsa Kuphunzira Zambiri
Simeon anali m’busa wa tchalitchi china ku Gurkovo, m’dziko la Bulgaria, komwe kulibe Mboni za Yehova. Iye atayamba kuphunzira Baibulo, anadziwa kuti zimene Baibulo limaphunzitsa n’zosiyana ndi zimene ankaphunzira ku tchalitchi. Tsiku lina atakwera sitima, analandira magazini athu. Simeon anadabwa kwambiri ataphunzira kuti Yehova ndiye Mulungu woona komanso kuti chiphunzitso cha Utatu n’chabodza. Popeza kuti ankafunitsitsa kuphunzira zambiri, iye analembera kalata ku ofesi ya nthambi komanso ku matchalitchi onse amene ankawadziwa. Tchalitchi chimodzi chokha n’chimene chinamuyankha kuti asade nkhawa ndi “nkhani zopanda pakezo.” Mosiyana ndi zimenezi, ofesi ya nthambi inakonza zoti abale awiri apite kukamuchezera ndipo anafunika kuyenda mtunda wa makilomita pafupifupi 35 kuchokera ku Kazanlŭk. Abalewo anayamba kuphunzira naye Baibulo pamodzi ndi banja lake. Simeon ankasangalala kwambiri ndi zimene ankaphunzirazo ndipo anaitana anzake ndi anthu ena oyandikana nawo nyumba kuti azidzaphunzirira limodzi. Posapita nthawi, anthu 25 anayamba kukhala nawo pa phunzirolo mlungu uliwonse. Mayi wina wa zaka 75 atakhala nawo pa phunziroli kwa nthawi yoyamba, ananena misozi ili m’maso kuti, “Ndaphunzira zambiri pa ola limodzi lokha kuposa zimene ndaphunzira m’zaka 30 zomwe ndakhala ndikupita ku tchalitchi.” Anthu pafupifupi 60 amafika pa misonkhano imene abale ochokera ku Kazanlŭk amachita ku Gurkovo mwezi uliwonse, ndipo anthu 79 anafika kudzaonerera mwambo wa Chikumbutso.
“Ndaphunzira zambiri pa ola limodzi lokha kuposa zimene ndaphunzira m’zaka 30 zomwe ndakhala ndikupita ku tchalitchi”
“Chonde, pitiriza zabwino zimene ukuchitazi”
Mlongo wina wa zaka 15 wa ku Ukraine, dzina lake Valya, anaona kuti aphunzitsi ake ankabwera ku sukulu atavala zovala zamtundu wakuda ndipo nthawi zina ankalira. Kenako Valya anamva kuti amayi awo a aphunzitsi akewo anamwalira, choncho iye anaganiza zowalimbikitsa ndi malemba okhudza kuuka kwa akufa. Ndiyeno Valya anatenga Baibulo ndi kabuku kakuti What Happens to Us When We Die? komanso kakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira kuti akaweruka akakambirane ndi aphunzitsi akewo. Iye anati: “Pamene ndinkawadikirira pakhomo la ofesi yawo, ndinkachita mantha kwambiri, choncho ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize.”
Valya atalowa mu ofesi ya aphunzitsi akewo, aphunzitsiwo anamufunsa kuti, “Ukufuna chiyani?”
“Ndikufuna ndikulimbikitseni chifukwa ndaona kuti mukumva chisoni kwambiri. Inenso zaka zingapo zapitazo agogo anga anamwalira.”
Georgia: Akulalikira m’munda wa mpesa
Aphunzitsiwo anachita chidwi ndi zimene Valya anachitazo. Misozi ili m’maso aphunzitsiwo ananena kuti palibe wachibale kapena mnzawo aliyense amene anawasonyeza kuti akuwaganizira ngati mmene Valya anachitira. Kenako Valya anawerenga ndi kufotokoza lemba la Chivumbulutso 21:3, 4. Atatero aphunzitsiwo analandira timabukuto n’kunena kuti, “Ndiwe wosiyana kwambiri ndi ana ena.”
Valya ananena kuti, “Ndimayesetsa kuwerenga Baibulo ndiponso kuchita zimene ndimawerengazo komanso ndimamvera makolo anga.”
Patapita nthawi, aphunzitsiwo anamupempha kuti awabweretsere Baibulo ndi buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndipo Valya anachitadi zimenezo. Aphunzitsiwo anathokozanso kwambiri ndipo anauza Valya kuti: “Chipembedzo chako n’choona ndipo uli ndi makolo abwino kwambiri amene amakuphunzitsa zinthu zabwino. Chonde, pitiriza zabwino zimene ukuchitazi.”
Anaimba Nambala Yolakwika
Pa tsiku loyamba la msonkhano wachigawo wa 2011 umene unkachitikira ku Malakasa m’dziko la Greece, Natalie anaimbira foni bambo ake kuti akambirane nawo za basi imene akwere popita ku msonkhanowo. Koma mwangozi anaimba nambala yolakwika ndipo palibe amene anayankha. Patapita nthawi, mwiniwake wa foni ija anaona kuti munthu wina anamuimbira ndipo iyenso anamuimbira kuti adziwe amene anamuimbirayo. Popeza kuti pa nthawiyi msonkhanowo unali utayamba, Natalie anaganiza zongozimitsa foniyo. Koma m’malo modina batani lozimitsira anadina batani loyankhira. Choncho munthuyo anamvetsera mbali ina ya nkhani ya tcheyamani ndipo inam’chititsa chidwi kwambiri, koma Natalie sanadziwe zimenezi.
Kenako munthu uja anatumiza meseji yofunsa kuti: “Kodi ndiwe ndani? Ndiwe wansembe?” Chigawo cha m’mawa chitatha, Natalie anaona meseji ija ndipo anayankha kuti: “Si ine wansembe. Ndine wa Mboni za Yehova ndipo ndili pa msonkhano.”
Pittenweem, ku Scotland: Akulalikira padoko
Munthu uja anaimbanso Loweruka kuti adziwe ngati msonkhanowo ukupitirirabe. Choncho bambo ake a Natalie analankhula ndi munthuyo n’kumulalikira, ndipo munthuyo anafotokoza kuti, “Kwa mphindi zochepa chabe, nkhani imene ndinamvetsera pa foni inayankha mafunso ambiri amene ankandisowetsa mtendere.” Pambuyo pake zinadziwika kuti banja la munthuyo linkavutitsidwa kwambiri ndi ziwanda ndipo sankadziwa kuti ziwandazo n’chiyani komanso chifukwa chake zimenezo zinkawachitikira. Iye anafotokoza kuti: “M’mbuyo monsemu sindinkafuna kulankhula ndi a Mboni za Yehova, koma panopa ngati n’zotheka ndikufuna kulankhula ndi munthu amene anakamba nkhani uja.”
Izi zinathekadi chifukwa Lamlungu munthuyo anapita ku msonkhanowo ndipo anadabwa ndi zimene anaona. Anaona mabanja ovala bwino komanso anthu osangalala. Panalibe wotaya zinyalala paliponse, panalibe amene ankatukwana ndiponso kusuta fodya. Iye anati: “Sindinkadziwa kuti padzikoli palinso anthu ngati inu. Ndikungoona ngati ndili kudziko lina osati padziko lapansi pompano.” Kenako bambo ake a Natalie anatengana ndi munthuyu n’kupita naye ku ofesi ya tcheyamani kumene analankhula ndi tcheyamaniyo. Munthuyu anachita chidwi kwambiri ndi zimene anamva pa msonkhanowo komanso mayankho a mafunso amene anali nawo. Choncho analandira Baibulo, buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani komanso magazini, ndipo anapangana naye kuti adzacheze nayenso tsiku lina.
OCEANIA
MAYIKO 29
CHIWERENGERO CHA ANTHU 38,495,300
OFALITSA 94,924
MAPHUNZIRO A BAIBULO 59,431
“Sindinamvepo Nyimbo Yosangalatsa Ngati Imeneyi”
Pachilumba cha Savaii ku Samoa, ana asukulu asanayambe maphunziro awo amasonkhana pamodzi n’kuimba nyimbo yachipembedzo. Koma Celina wa zaka 5 ndi Levaai wa zaka 6 anauza mphunzitsi wamkulu pasukulupo mwaulemu kuti sadziimba nawo chifukwa ndi a Mboni za Yehova. Zimenezi zikanachititsa kuti anawa alandire chilango chowawa kwambiri. Koma zikuoneka kuti mphunzitsi wamkuluyo anaganiza zowachititsa manyazi anawo kuti aziimba nawo nyimbozo. Choncho anawauza kuti, “Chabwino, ngati simukufuna kuimba nawo nyimbo zathuzi, ndiye imbani yanu.” Atatero, Celina ndi Levaai anaimba nyimbo nambala 111, yakuti “Iye Adzaitana.” Iwo anali atangophunzira kumene nyimboyi pa Kulambira kwa Pabanja. Atamaliza kuimba, misozi inalengeza m’maso mwa mphunzitsiyo. Kenako iye anati, “Sindinamvepo nyimbo yosangalatsa ngati imeneyi. Chonde, taimbaninso kachiwiri.” Anawo anaimbadi. Pamenepo anawauza kuti, “Sindidzakukakamizaninso kuti muziimba nyimbo zathu, koma muziimba zanu.”
“Sindidzakukakamizaninso kuti muziimba nyimbo zathu, koma muziimba zanu”
Pa Moyo Wake Wonse Ankapemphera Kwa Yesu Basi
Timor-Leste: M’dzikoli, lomwe kale munkachitika nkhondo yoopsa, chiwerengero cha ofalitsa chawonjezeka ndi 9 peresenti
M’busa wa tchalitchi chinachake ku Fiji anaganiza zoti akhale nawo pa phunziro la Baibulo la munthu wina. Phunzirolo lili mkati, m’busayo anamva kuti Yesu si Mulungu. Zimenezi zinamuvutitsa maganizo kwabasi mpaka kusowa tulo. Mkazi wake ataona mmene m’busayo ankavutikira, ananena kuti, “Musadzapitenso kukamvetsera zimene anthu amenewa amaphunzitsa.” Komabe, m’busayo sanathe kuchotsa nkhani imeneyi m’maganizo mwake. Mlungu wotsatira, anapitanso kukakhala nawo pa phunziro la Baibulo lija. Patapita masiku owerengeka kuchokera pamene anakhala nawo kachiwiri pa phunzirolo, anapita ku tchalitchi chake kukanena kuti wasiya ntchito yaubusa. Iye anachita zimenezi ngakhale kuti panalibe munthu amene ankamuphunzitsa Baibulo. Zimenezi zinadabwitsa komanso kukhumudwitsa kwambiri achibale ake ndiponso anthu a m’tchalitchi chake. Izi zinali choncho chifukwa chakuti ankasiya tchalitchi chake komanso ntchito imene inkamupezetsa ndalama zambiri. Iye anaona mosavuta choonadi chokhudza Yesu kuchokera m’Baibulo, koma zinali zovuta kuti azipemphera kwa Yehova chifukwa chakuti pa moyo wake wonse ankapemphera kwa Yesu basi. Patadutsa miyezi yambiri anayamba kukwanitsa kupemphera kwa Yehova. Panopa iye amauza ena uthenga wabwino ndipo akuwathandiza kuti adziwe Yehova ndi kum’konda.
Anthu a Pachilumba China Chaching’ono Akuphunzira Choonadi
Pachilumba cha Makatea chomwe chili ku South Pacific pali anthu 62 okha. Mpingo wa Mboni za Yehova wa ku Tahiti ndi umene umathandiza anthu a pachilumbachi mwauzimu. Iwo amachititsa maphunziro a Baibulo pa foni ndi anthu 9 a pachilumbachi. Anthu pafupifupi 15 amakumana m’nyumba ya munthu wina amene akuphunzira Baibulo kuti amvetsere misonkhano imene ikuchitikira ku Tahiti. Mmodzi mwa anthu amene akuphunzira Baibulo panopa ndi mayi wina amene anali wodalirika kwambiri ku tchalitchi kwawo ndipo ankayembekezera kumusankha kuti akhale dikoni. Posachedwapa mayiyu anapita ku tchalitchi kwawoko kukawauza chifukwa chake anasiya kupita ku tchalitchiko. Pogwiritsa ntchito Baibulo iye anawafotokozera chifukwa chake mkazi sayenera kuphunzitsa mumpingo. Iye anafotokozanso udindo wa Yesu Khristu komanso tanthauzo la mwambo wa Mgonero wa Ambuye, umene uyenera kuchitika kamodzi pachaka osati Lamlungu lililonse. Mayiyu anafotokozanso kuti anthu 144,000 okha ndi amene adzakhale kumwamba ndi Khristu ndipo iwo okha ndi amene ayenera kudya zizindikiro za pa Chikumbutso. Mayi winanso analimbikitsidwa ndi chitsanzo chake ndipo nayenso anasiya kupita ku tchalitchiko moti pano akuphunzira Baibulo ndi Mboni.
Banja Lonse Linavomera Kupita ku Chikumbutso
Akulu awiri ku Solomon Islands ankayendera ofalitsa amene anasiya kulalikira kuti akawaitanire ku Chikumbutso cha imfa ya Khristu. Akuluwo anapita kwa Joshua, amene anasiya kusonkhana mu 1998. Choncho Joshua ndi achibale ake ena 20 anayenda kwa maola awiri kupita ku Chikumbutso. Abale anawalandira bwino kwambiri moti Joshua anagwetsa misozi. Ambiri mwa achibale akewo anapitanso kukamvetsera nkhani yapadera, ndipo kenako anauza akulu kuti akufuna aziphunzira Baibulo. Akuluwo anawathandiza moti anthu 15 anayamba kuphunzira Baibulo.
Ankadziwa Yankho Lake
Pa zilumba zoposa 1,000 zimene zili m’madera amene amayang’aniridwa ndi nthambi ya ku Guam, zilumba zoposa 100 n’zimene zili ndi anthu. Komabe, zilumba 13 zokha mwa zilumba zimenezi n’zomwe zili pafupi ndi mpingo. Popeza kuti a Mboni za Yehova sanafike m’zilumba zambiri mwa zilumba zimenezi, abale akupitiriza kufufuza njira yofikira m’zilumbazi. Mwachitsanzo, mu April 2012, gulu la ofalitsa linayenda paboti kupita ku chilumba cha Polowat, chomwe ndi chimodzi mwa zilumba zimene zili kutali ndi zilumba zina. Anthu a ku Polowat anazolowera kukhala moyo wakumudzi wosiyana kwambiri ndi wa anthu a m’tauni. Mwachitsanzo, amuna amangovala kathewera basi, amasema mabwato ndipo amadalira kwambiri ulimi kuti apeze zofuna zawo.
Wofalitsa wina amene anapita kumeneko, anafunsa mnyamata wina kuti, “Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?”
Mnyamatayo anayankha kuti: “Funso limenelo yankho lake ndikulidziwa.” Kenako anaimirira n’kukatenga buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Bukuli linali lachinenero cha Chichukese, ndipo anatsegula pa tsamba la Zamkatimu. Ndiyeno anatilozera mutu 8 wakuti, “Kodi Chimachitika N’chiyani pa Imfa?” Kenako anatifotokozera zimene anaphunzira m’bukuli.
Kingston, ku Norfolk Island: Akulalikira mumsewu waukulu wotchedwa Quality Row
Koma kodi bukuli analipeza bwanji? Mu 2009 ofalitsa ena a ku chilumba cha Chuuk ankalalikira padoko lina pofuna kulankhula ndi anthu amene ankapita ku zilumba zakutali, ndipo ankawapatsa mabuku a Mungathe. Munthu wina amene ankapita ku Polowat anavomera kutenga katoni imodzi ya mabukuwa kuti akagawire anthu a kwawo, ndipo mmodzi wa iwo anali mnyamata ameneyu.
Abalewo asanachoke ku Polowat, anapita kukacheza ndi mnyamatayu maulendo angapo kuti akamulimbikitse komanso kukamusonyeza mmene angaphunzirire zambiri. Anamuphunzitsanso mmene angapezere malemba komanso kulemba mfundo zofunika m’mbali mwa masamba a buku lakelo.
N’zosangalatsa kwambiri kudziwa kuti mabuku athu akuthandiza anthu kuphunzira choonadi m’chinenero chawo, ngakhale m’zilumba zakutali komwe kulibe TV, wailesi, nyuzipepala kapena Intaneti.
Zipolopolo Zitatu Komanso Zifukwa Zitatu
Pamene nkhondo yapachiweniweni inkafika pachimake ku Bougainville m’dziko la Papua New Guinea n’kuti Anna, amene pa nthawiyo anali ndi zaka za m’ma 20, ali wofalitsa wosabatizidwa. Mu 1991 iye anali m’gulu la Mboni zokwana 13, zochokera ku mpingo wa Arawa. Pa gululi panali akuluakulu 6 ndi ana 7 amene anakakamizika kuthawira kutchire ndi takatundu tochepa chabe. Kwa zaka ziwiri, iwo ankakhala m’nyumba zimene anthu ena anathawamo ndipo chakudya ankachipeza movutikira kwambiri. Iwo ankachita misonkhano pogwiritsa ntchito mabuku awiri okha omwe ndi Baibulo la Anna komanso buku lakuti Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona. Abalewa ankapempherera limodzi, ankaimba nyimbo za Ufumu komanso ankalalikira kwa anthu amene akumana nawo.
Kumene abalewa ankakhala kunafika asilikali oukira boma ndipo ankafuna kuti abale awiri alowe usilikali. Koma asilikaliwo anawasiya abalewo pofuna kulemekeza ufulu wawo wosafuna kulowerera ndale. Nthawi inayake msilikali anaonetsa Anna zipolopolo zitatu n’kumuuza kuti, “Ndikufuna ukhale mkazi wanga, ukakana ndikupha.” Anna anakana ndipo anam’patsa zifukwa zitatu zokanira mogwirizana ndi nambala ya zipolopolozo. Chifukwa chachikulu chinali chakuti Baibulo limanena kuti ayenera kukwatiwa “mwa Ambuye.” (1 Akor. 7:39) Atanena zimenezi, msilikaliyo anangotembenuka n’kumapita.
“Palibe chimene chingaimitse ntchito ya Yehova. Ngakhale nkhondo yapachiweniweni singaimitse ntchitoyi”
Mu 2012, Anna, amene panopa ndi mpainiya wokhazikika, anabwereranso ku Arawa kukakhazikitsa kagulu kakutali. Iye anachita zimenezi atamva kuti kuderali kukufunika ofalitsa Ufumu ambiri. Mlongoyu anafunsidwa ngati sanasangalale kubwerera kudera limene anaona zinthu zoopsa kwambiri pa nthawi ya nkhondo. Poyankha iye ananena kuti, “Ndikusangalala kuti ndabwereranso kuno. Palibe chimene chingaimitse ntchito ya Yehova. Ngakhale nkhondo yapachiweniweni singaimitse ntchitoyi.”