Mmene Tingagwiritsire Ntchito Kapepala Kodziwitsa Anthu za Webusaiti Yathu
Kapepalaka kali ndi mutu wakuti, Kodi Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambiri Okhudza Moyo? Mafunso atatu ofunika kwambiri alembedwa patsamba lomaliza la kapepalaka. Mukakumana ndi munthu wachidwi, mupempheni kuti asankhe funso limene akufuna kudziwa yankho lake. Akasankha pitani naye pamene palembedwa kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO, kuti mupeze yankho lake. Pa webusaitiyi mungapezenso mayankho a mafunso monga akuti, Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani? komanso Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Chiyani?
Yesetsani kumatenga timapepalati kulikonse n’cholinga choti muthandize anthu kudziwa zimene Baibulo limanena pa zinthu zosangalatsa zimene Ufumu wa Mulungu udzachite ukadzayamba kulamulira dziko lapansi.