GAWO 2
“YEHOVA AMAKONDA CHILUNGAMO”
Masiku ano, padzikoli pakuchitika zinthu zopanda chilungamo zambiri ndipo anthu ambiri amanena kuti Mulungu ndi amene amachititsa zimenezi. Koma Baibulo limatiphunzitsa mfundo yolimbikitsa yakuti: “Yehova amakonda chilungamo.” (Salimo 37:28) M’chigawochi tiphunzira mmene iye wasonyezera kuti mawu amenewa ndi oona, zomwe zimapatsa anthu onse chiyembekezo.