Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/15 tsamba 2
  • Kodi Tingawalalikire Bwanji Achibale Athu Omwe si Mboni?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Tingawalalikire Bwanji Achibale Athu Omwe si Mboni?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
km 9/15 tsamba 2

Kodi Tingawalalikire Bwanji Achibale Athu Omwe si Mboni?

1 Ambirife tili ndi achibale amene si Mboni. Kunena zoona timalakalaka achibale athuwa, makamaka amene timakhala nawo limodzi, atakhala a Mboni. Izi zingachititse kuti tiziyendera nawo limodzi panjira yopita ku moyo wosatha. Ngati tayesetsa kwa nthawi yaitali kuthandiza achibale athu kuti aphunzire choonadi, koma sizikutheka, tisataye mtima poganiza kuti sangakhale a Mboni.

2 Pamene Yesu ankalalikira, ‘abale ake sankamukhulupirira,’ moti pa nthawi ina ankamuganizira kuti wachita misala. (Yoh. 7:5; Maliko 3:21) Koma Yesu sanataye mtima n’kusiya kuwathandiza. Patapita nthawi abale akewo anaphunzira choonadi, ndipo Yakobo anakhala munthu wodalirika mumpingo wachikhristu. (Mac. 1:14; Agal. 1:18, 19; 2:9) Choncho ngati nanunso mukufuna kuti nthawi ina mudzasangalale kuona achibale anu ali a Mboni, musasiye kuwalalikira uthenga wabwino wa Ufumu.

3 Aziona Kuti Tikuwathandiza Osati Kuwatopetsa: Yesu akamalalikira anthu, anthuwo ankasangalala osati kuona kuti akuwatopetsa. (Mat. 11:28, 29) Yesu sankauza anthu zinthu zambirimbiri zomwe sakanatha kuzimvetsa. Nanunso mukamauza achibale anu choonadi, musamawauze zinthu zambirimbiri nthawi imodzi. Woyang’anira dera wina anati: “Zimakhala bwino kuwauza mfundo inayake pang’ono, n’kusiya kuti akhale ndi chidwi chofuna kudziwa zambiri.” Zimenezi zingachititse kuti achibale athu, ngakhale amene amatitsutsa, ayambe kufunsa mafunso ndipo kenako angakhale ndi ludzu la choonadi.—1 Pet. 2:2; yerekezerani ndi 1 Akorinto 3:1, 2.

4 Akhristu ena amalalikira kwa amuna kapena akazi awo omwe si Mboni posiya atatsegula patsamba la magazini kapena buku lomwe pali nkhani yomwe akuona kuti mnzawoyo angachite nayo chidwi. Mlongo wina amene ankakonda kuchita zimenezi ankachitanso phunziro ndi ana ake, mwamuna wake akumva ndipo paphunzirolo ankafotokozanso mfundo zomwe ankaona kuti zingathandize mwamuna wakeyo. Nthawi zina ankauza mwamuna wakeyo mfundo zimene wapeza pamene amaphunzira payekha, ndiyeno ankamufunsa kuti: “Mukuona kuti mfundo zimenezi n’zothandiza bwanji?” Patapita nthawi mwamuna wakeyo anayamba kuphunzira ndipo anakhala wa Mboni.

5 Muziwalemekeza Komanso Muzikhala Oleza Mtima: Wofalitsa wina ananena kuti: “Nawonso achibale athu ali ndi ufulu wokhulupirira zimene akufuna.” Choncho tiziwalola kufotokoza maganizo awo komanso ngati atiuza kuti tisamawalalikire, sitiyenera kuwakakamiza. Kuchita zimenezi kumasonyeza kuti timawalemekeza. (Mlal. 3:7; 1 Pet. 3:15) Tikamawamvetsera, kuchita zinthu mowaganizira komanso kuleza mtima, tikhoza kupeza mpata wowalalikira mosachita kuonetsera. Tikamachita zinthu moleza mtima ndi achibale athu omwe si Mboni zotsatira zake zimakhala zabwino. Zoterezi ndi zimene zinachitikira m’bale wina. Kwa zaka 20, mkazi wake ankamuchitira zinthu zankhanza. Koma kenako mkaziyo anayamba kusintha. M’baleyu anati: “Ndimathokoza kwambiri Yehova kuti anandithandiza kukhala woleza mtima. Zimenezi zathandiza kuti mkazi wanga asinthe ndipo tsopano akuyenda panjira yopita ku moyo wosatha.”

6 Nanunso achibale anu akhoza kusintha. Mukakhala ndi khalidwe labwino komanso mukamawapempherera angathe ‘kukopeka, osati ndi mawu, koma ndi khalidwe lanu.’—1 Pet. 3:1, 2.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena