PHUNZIRO 18
Kugwiritsa Ntchito Baibulo Popereka Mayankho
PAMENE anthu atifunsa zimene timakhulupirira, za moyo wathu, za maganizo athu pankhani zomwe zikuchitika, kapena za chiyembekezo chathu cha zam’tsogolo, tiyenera kugwiritsa ntchito Baibulo poyankha. Chifukwa chiyani? Chifukwa ndi Mawu a Mulungu. Zimene timakhulupirira zimachokera m’Baibulo. Ndilo maziko a moyo wathu. Limatithandiza kumvetsa zochitika za padziko. Chiyembekezo chathu cha zam’tsogolo n’chozikika zolimba m’malonjezo ouziridwa a m’Baibulo.—2 Tim. 3:16, 17.
Timakhala ozindikira kwambiri za udindo wobwera ndi dzina lathu. Ndife Mboni za Yehova. (Yes. 43:12) Choncho, sitiyankha mafunso malinga ndi nzeru zaumunthu, koma malinga ndi zimene Yehova amanena m’Mawu ake ouziridwa. Zoona, aliyense payekhapayekha timakhala ndi malingaliro athuathu pankhani zina, koma timalola Mawu a Mulungu kutsogolera maganizo athu chifukwa tili otsimikiza ndi mtima wonse kuti ndiwo choonadi. Baibulo limatipatsadi ufulu wokhala ndi maganizo athuathu pankhani zambiri. Koma m’malo moumiriza malingaliro athu pa ena, tiyenera kuphunzitsa mfundo za makhalidwe abwino zoperekedwa m’Malemba, kotero kuti amene tikuwaphunzitsa akhalenso ndi ufulu wosankha zomwe akufuna ngati umene tili nawo. Mofanana ndi mtumwi Paulo, tikufuna kuti iwo “amvere [mwa] chikhulupiriro.”—Aroma 16:26.
Pa Chivumbulutso 3:14, Yesu Kristu akutchedwa “mboni yokhulupirika ndi yoona.” Kodi mafunso anawayankha motani, ndipo anatani ndi mikhalidwe imene anakunana nayo? Nthaŵi zina anagwiritsa ntchito mafanizo ochititsa anthu kuganiza. Nthaŵi zina anali kufunsa wofunsayo zimene anali kudziŵapo pa lembalo. Kaŵirikaŵiri, anali kugwira mawu malemba, kuwamasulira, kapena kutchula mfundo zake. (Mat. 4:3-10; 12:1-8; Luka 10:25-28; 17:32) M’zaka za 100 zoyambirira, kaŵirikaŵiri anthu anali kusunga mipukutu ya Malemba m’sunagoge. Palibe umboni woonetsa kuti Yesu anali ndi mipukutu yakeyake, koma Malemba anali kuwadziŵa bwino kwambiri ndipo anali kuwatchula kaŵirikaŵiri pophunzitsa. (Luka 24:27, 44-47) Ananenadi zoona kuti zomwe anali kuphunzitsa sizinali zochokera kwa iye mwini. Analankhula zimene anamva kwa Atate wake.—Yoh. 8:26.
Timafuna kutengera chitsanzo cha Yesu. Sikuti tinamvapo Mulungu akulankhula muja anachitira Yesu ayi. Koma Baibulo ndilo Mawu a Mulungu. Tikamaligwiritsa ntchito ngati gwero la mayankho athu, tidzapeŵa kudzitchukitsa tokha. Timasonyeza kuti m’malo mopereka malingaliro aumunthu, timaonetsetsa kuti choonadi chikhale chochokera kwa Mulungu.—Yoh. 7:18; Aroma 3:4.
Sikuti cholinga chathu ndi kungogwiritsa ntchito Baibulo chisawawa ayi, koma kuligwiritsa ntchito m’njira imene ingapindulitse kwathunthu womvera wathu. Timafuna kuti iye amvetsere moona mtima. Malinga ndi maganizo a munthuyo, mungayambe nkhani ya m’Baibulo mwa kufunsa kuti: “Ndikhulupirira inunso mukuvomereza kuti zimene Mulungu amanena n’zimene tiyenera kutsatira, si choncho nanga?” Kapena munganene kuti: “Kodi mukudziŵa kuti Baibulo limayankha funso limenelo?” Ngati mukambirana ndi munthu wosakhulupirira Baibulo, gwiritsani ntchito mawu osiyanako. Munganene kuti: “Ndikufuna ndikambirane nanu ulosi wakalewu.” Kapena munganene kuti: “Buku lofalitsidwa koposa mabuku onse m’mbiri ya anthu limanena kuti . . . ”
Nthaŵi zina mungangonena m’mawu anu mawu a palemba. Koma ngati n’kotheka, ndi bwino kutsegula Baibulo lenilenilo ndi kuŵerenga zimene limanena. Sonyezani munthuyo lembalo m’Baibulo lake ngati n’kotheka. Kugwiritsa ntchito Baibulo mwachindunji kotereku kaŵirikaŵiri kumakhudza kwambiri mitima ya anthu.—Aheb. 4:12.
Akulu achikristu ali ndi udindo wapadera wogwiritsa ntchito Baibulo poyankha mafunso. Chimodzi mwa ziyeneretso zakuti munthu akhale mkulu mumpingo ndicho ‘kugwira mawu okhulupirika monga mwa luso lake la kuphunzitsa.’ (Tito 1:9) Wina mumpingo angapange chosankha chachikulu pamoyo wake atalandira uphungu kwa mkulu. Ndiye chifukwa chake uphungu umenewo ukayenera kuzikika zolimba m’Malemba! Chitsanzo cha mkulu pochita zimenezo chingalimbikitse ambiri kuchita chimodzimodzi pophunzitsa ena.