-
Sitinalole Kusiya Zimene TimakhulupiriraBuku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016
-
-
INDONESIA
Sitinalole Kusiya Zimene Timakhulupirira
Daniel Lokollo
CHAKA CHOBADWA 1965
CHAKA CHOBATIZIDWA 1986
MBIRI YAKE Mpainiya wapadera amene anakhalabe wokhulupirika pa nthawi imene ankazunzidwa.
PA 14 April, 1989, akuluakulu a boma anandimanga pamodzi ndi anthu ena atatu. Pa nthawiyi ndinkachititsa msonkhano wa mpingo m’tauni ya Maumere pachilumba cha Flores.
Oyang’anira ndende ya m’derali anatikakamiza kuti tizichitira sailuti mbendera. Titakana, anatimenya n’kutikhazika panja kwa masiku 5, dzuwa likutentha kwambiri. Ndipo usiku, tinkazizidwa kwambiri chifukwa tinkagona pasimenti mundende zomwe zinali zazing’ono kwambiri komanso zauve. Nthawi zonse tinkakhala otopa komanso tinkamva kupweteka kwambiri chifukwa cha mabala. Woyang’anira ndendeyi ankatikakamiza kuti tingosiya zimene timakhulupirira koma tinamuuza kuti: “Tilolera kufa koma singachitire sailuti mbendera.” Ifenso tinaona kuti ndi mwayi wathu ‘kuvutika chifukwa cha chilungamo’ mofanana ndi Akhristu akale.—1 Pet. 3:14.
-
-
Tinapulumuka Chifukwa Chotsatira MalangizoBuku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016
-
-
INDONESIA
Tinapulumuka Chifukwa Chotsatira Malangizo
Blasius da Gomes
CHAKA CHOBADWA 1963
CHAKA CHOBATIZIDWA 1995
MBIRI YAKE Mkulu amene anasamalira nkhosa mwachikondi, pa nthawi imene panali mavuto a zachipembedzo mumzinda wa Ambon, womwe ndi mbali ya zilumba za Maluku.
PA 19 January 1999, Asilamu ndi Akhristu anayamba kumenyana koopsa chifukwa ankadana kwambiri. Maguluwa ankamenyana pa mtunda wa makilomita atatu kuchokera kumene ndinkakhala.a
Nditatsimikizira kuti banja langa ndi lotetezeka, ndinaimbira foni ofalitsa ena kuti ndidziwe mmene alili. Ndinawalimbikitsa kuti asachite mantha komanso kuti ayesetse kupewa kupita kumalo amene kunkachitika zachipolowezi. Kenako akulu anakalimbikitsa abale ndi alongo powauza mfundo za m’Malemba komanso anawalimbikitsa kuti azisonkhana m’timagulu.
A ku ofesi ya nthambi anatilimbikitsa kuti tiuze abale ndi alongo amene ankakhala m’madera omwe anthu ankamenyana kwambiri, kuti asamukeko. Tinauza mabanja angapo malangizo amenewa, koma m’bale wina amene sanamvere anaphedwa ndi gulu la anthu olusa. Aliyense amene anamvera malangizo ochokera ku ofesi ya nthambi anapulumuka.
a Kumenyanaku kunkachitika m’madera onse a ku Maluku ndipo kunatenga pafupifupi zaka ziwiri. Zipolowezi zinachititsa kuti anthu ambiri athawe m’nyumba zawo.
-