Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr17 May tsamba 1-2
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya May 2017

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya May 2017
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu (2017)
  • Timitu
  • MAY 1-7
  • MAY 8-14
  • MAY 15-21
  • MAY 22-​28
  • MAY 29–JUNE 4
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu (2017)
mwbr17 May tsamba 1-2

Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya May 2017

MAY 1-7

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YEREMIYA 32-​34

it-1-E 105 ¶2

Anatoti

Yeremiya anali mneneri wochokera ku Anatoti koma sankalemekezedwa ndi anthu akwawo. Iwo ankamuopseza kuti amupha chifukwa choti ankalengeza uthenga wa Yehova. (Yer. 1:1; 11:21-23; 29:27) Choncho Yehova ananeneratu kuti awononga mzindawu ndipo zimenezi zinachitikadi pamene Ababulo anaulanda. (Yer. 11:21-23) Mzinda wa Yerusalemu usanawonongedwe, Yeremiya anatsatira malamulo pogula munda wa m’bale wake ku Anatoti ngati chizindikiro chosonyeza kuti Aisiraeli adzabwerera kwawo. (Yer. 32:7-9) Pakati pa anthu oyambirira kuchoka kuukapolo panali amuna okwana 128 a ku Anatoti omwe ankatsogoleredwa ndi Zerubabele. Malinga ndi zimene Yeremiya analosera, mzinda wa Anatoti ndi umodzi mwa mizinda imene inabwezeretsedwa.​—Ezara 2:23; Neh. 7:27; 11:32.

MAY 8-14

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YEREMIYA 35-​38

it-2-E 1228 ¶3

Zedekiya

Zimene Zedekiya anachita zimasonyeza kuti anali wolamulira wamantha. Akalonga atamupempha kuti Yeremiya aphedwe pomunamizira kuti ankapereka uthenga wofooketsa anthu, Zedekiya anati: “Taonani! Iye ali m’manja mwanu. Palibe chimene ine mfumu ndingachite motsutsana nanu.” Koma pambuyo pake Zedekiya anavomereza zimene Ebedi-meleki anapempha zoti akapulumutse Yeremiya ndipo analamula kuti atenge amuna 30 kuti akamuthandize. Kenako Zedekiya anakumana ndi Yeremiya mobisa ndipo anamutsimikizira kuti samupha kapenanso kumupereka kwa anthu omwe ankafuna kumuphawo. Zedekiya ankaopanso kuti azunzidwa ndi Ayuda omwe anali m’manja mwa Akasidi, n’chifukwa chake anakana kumvera malangizo a Yeremiya oti adzipereke kwa akalonga a ku Babulo. Iye anasonyezanso mantha pouza Yeremiya kuti asaulule kwa akalonga zimene ankakambirana.​—Yer. 38:1-28.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-2-E 759

Arekabu

Yehova anasangalala ndi mtima womvera umene Arekabu anali nawo. Iwo ankaona kuti kumvera kholo lawo inali nkhani yofunika kwambiri ndipo izi zinawachititsa kuti akhale osiyana ndi Ayuda omwe analephera kumvera Mlengi wawo. (Yer. 35:12-16) Mulungu analonjeza kuti adzadalitsa Arekabu powauza kuti: “Sipadzasowa munthu wa m’banja la Yonadabu mwana wa Rekabu woima pamaso panga kuti azinditumikira nthawi zonse.”​—Yer. 35:19.

MAY 15-21

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YEREMIYA 39-​43

it-2-E 1228 ¶4

Zedekiya

Kuwonongedwa kwa Yerusalemu. Mu 607 B.C.E., “m’chaka cha 11 cha mfumu Zedekiya, m’mwezi wachinayi, pa tsiku la 9,” Yerusalemu anawonongedwa. Usiku wa tsiku limeneli Zedekiya ndi amuna ake ankhondo anathawa. Kenako iye anagwidwa m’chipululu cha Yeriko ndipo anamutenga ndi kupita naye kwa Nebukadirezara ku Ribila. Zitatero, ana aamuna a Zedekiya anaphedwa iyeyo akuona. Popeza kuti pa nthawiyi iye anali ndi zaka 32, ndiye kuti ana akewa ayenera kuti anali ang’onoang’ono. Pambuyo pake, anam’chititsa khungu, n’kumumanga ndi maunyolo amkuwa ndipo anapita naye ku Babulo. Kumeneko anamuika m’ndende mpaka anafera momwemo.​—2 Maf. 25:2-7; Yer. 39:2-7; 44:30; 52:6-11; yerekezerani ndi Yer. 24:8-10; Ezek. 12:11-16; 21:25-27.

it-2-E 482

Nebuzaradani

Nebukadinezara analamula Nebuzaradani kuti amasule Yeremiya ndipo ankamuchitira zinthu mokoma mtima, anamupatsa mwayi wochita zimene akufuna, anamuuza kuti azimuyang’anira komanso anamupatsa chakudya ndi mphatso zina. Nebuzaradani ndi amenenso anatumidwa ndi mfumu ya ku Babulo kuti asankhe Gedaliya kukhala mtsogoleri woyang’anira anthu amene anatsala m’dzikolo. (2 Maf. 25:22; Yer. 39:11-14; 40:1-7; 41:10) Patatha zaka 5, m’chaka cha 602 B.C.E., Nebuzaradani anatenga Ayuda enanso, omwe anathawira m’madera ena kupita nawo ku ukapolo.​—Yer. 52:30.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-1-E 463 ¶4

Nthawi Imene Zinthu Zinachitika

Mzinda wa Yerusalemu unazunguliridwa ndi adani m’chaka cha 9 cha ufumu wa Zedekiya (mu 609 B.C.E.), ndipo unawonongedwa m’chaka cha 11 cha ufumuwu (mu 607 B.C.E.). Pa nthawiyi n’kuti Nebukadinezara atalamulira kwa zaka 19 (anayamba kulamulira m’chaka cha 625 B.C.E.). (2 Maf. 25:1-8) M’mwezi wa 5, mu 607 B.C.E., (wotchedwa Aba, womwe umapangidwa ndi hafu ya mwezi wa July ndi August) mzindawo unatenthedwa ndi moto, makoma ake anagumulidwa ndipo anthu ambiri anatengedwa kupita ku ukapolo. Koma “ena mwa anthu onyozeka a m’dzikolo” anawalola kuti atsale ndipo anakhalabe m’dzikolo mpaka pamene Gedaliya yemwe anasankhidwa ndi Nebukadinezara anaphedwa. Zitatero Ayuda otsalawo anathawira ku Iguputo ndipo izi zinachititsa kuti Yuda akhale bwinja. (2 Maf. 25:9-12, 22-26) Zimenezi zinachitika m’mwezi wa 7, womwe ndi wa Etanimu (kapena kuti Tishiri, womwe umapangidwa ndi hafu ya mwezi wa September ndi October). Choncho zaka 70 zimene Yerusalemu anakhala bwinja ziyenera kuti zinayambira cha m’ma October 1, 607 B.C.E., kudzathera mu 537 B.C.E. Pofika m’mwezi wa 7 m’chakachi, gulu loyamba la Ayuda omwe anali ku ukapolo linabwerera ku Yuda ndipo panali patatha zaka 70 dziko lawo lili bwinja.​—2 Mbiri 36:21-23; Ezara 3:1.

MAY 22-​28

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-1-E 430

Kemosi

Pamene mneneri Yeremiya ankaneneratu za tsoka limene lidzagwere Mowabu, ananena kuti mulungu wa Amowabu wotchedwa Kemosi limodzi ndi ansembe ake komanso akalonga adzatengedwa kupita ku ukapolo. Anati Amowabu adzachita manyazi ndi mulungu wawo chifukwa choti walephera kuwapulumutsa. Izi ndi zofanananso ndi zomwe zinachitikira Aisiraeli a mu ufumu wamafuko 10 omwe anachita manyazi ku Beteli pa nthawi imene analambira fano la mwana wa ng’ombe.​—Yer. 48:7, 13, 46.

it-2-E 422 ¶2

Mowabu

Maulosi onena za Mowabu anakwaniritsidwa ndipo kwa zaka zambiri tsopano, Amowabu sanakhalekonso monga mtundu wa anthu. (Yer. 48:42) Masiku ano mizinda yomwe inali ya Amowabu monga Nebo, Hesiboni, Aroweli, Beti-gamuli ndiponso Baala-meoni ndi mabwinja okhaokha. Palinso malo ena ambiri amene panopa sakudziwika.

MAY 29–JUNE 4

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YEREMIYA 49-​50

it-1-E 54

Mdani

Mulungu ankalola kuti anthu ake agonjetsedwe ndi adani awo, anthuwo akasiya kumumvera. (Sal. 89:42; Maliro 1:5, 7, 10, 17; 2:17; 4:12) Zikatero, adaniwo ankayamba kudzitama n’kumaona ngati apambana chifukwa cha mphamvu zawo ndiponso ankatamanda milungu yawo. Ankaonanso ngati Mulungu sangawaimbe mlandu pa nkhanza zimene ankachitira anthu ake. (Deut. 32:27; Yer. 50:7) Ndiyeno Yehova ankalanga adani a anthu ake onyada komanso odzikwezawo. (Yes. 1:24; 26:11; 59:18; Nah. 1:2) Iye ankachita izi chifukwa cha dzina lake loyera.​—Yes. 64:2; Ezek. 36:21-24.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

it-1-E 94 ¶6

Aamoni

Zikuoneka kuti Tigilati-pilesere III ndi mafumu ena a Asuri amene analamulira pambuyo pake, atagwira Aisiraeli a mu ufumu wakumpoto n’kuwachotsa m’dziko lawo, (2 Maf. 15:29; 17:6) Aamoni anayamba kukhala m’dera la fuko la Gadi. Kudera limeneli ndi komwe Yefita anagonjetsa Aamoniwa m’mbuyomo. (Yerekezerani ndi Sal. 83:4-8) Choncho, kudzera mwa Yeremiya, Yehova anadzudzula Aamoniwo chifukwa cholanda cholowa cha fuko la Gadi. Anawachenjezanso kuti awagwetsera tsoka pamodzi ndi mulungu wawo Malikamu (kapena kuti Milikomu). (Yer. 49:1-5) Aamoni ankatumizanso magulu a achifwamba kuti azikavutitsa Ayuda mu nthawi ya ulamuliro wa Mfumu Yehoyakimu, chakumapeto kwa maufumu a Yuda.​—2 Maf. 24:2, 3.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena