MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Chikondi Chenicheni
Yehova poyambitsa ukwati, anafuna kuti mwamuna ndi mkazi akakwatirana azikhala limodzi kwa moyo wonse. (Gen. 2:22-24) Munthu angasankhe kuthetsa ukwati pokhapokha ngati wina wachita chigololo. (Mal. 2:16; Mat. 19:9) Popeza Yehova amafuna kuti anthu okwatirana azikhala mosangalala, anapereka malangizo othandiza Akhristu kuti azitha kusankha bwino munthu wokwatirana naye n’cholinga choti akhale ndi mabanja abwino.—Mlal. 5:4-6.
ONERANI VIDIYO YAKUTI CHIKONDI CHENICHENI KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
N’chifukwa chiyani malangizo omwe Liz analandira kwa bambo ndi mayi ake ali anzeru komanso othandiza?
N’chifukwa chiyani si nzeru kuganiza kuti mungathe kusintha khalidwe la munthu amene muli naye pa chibwenzi?
Kodi m’bale ndi mlongo Foster anapereka malangizo otani kwa Liz?
Kodi mavuto anayamba bwanji m’banja la Zack ndi Magi?
Kodi John ndi Liz anali ndi zolinga zauzimu ziti zomwe zinali zofanana?
N’chifukwa chiyani musanakwatirane mumafunika kudziwa “munthu wobisika wamumtima” wa munthu amene mukufuna kukwatirana naye? (1 Pet. 3:4)
Kodi chikondi chenicheni tingachidziwe bwanji? (1 Akor. 13:4-8)