Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya March 2018
MARCH 5-11
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 20-21
“Aliyense Wofuna Kukhala Wamkulu Pakati Panu Ayenera Kukhala Mtumiki Wanu”
nwtsty zithunzi ndi mavidiyo
Pamsika
Misika ina inkakhala m’mbali mwa msewu moti nthawi zina ogulitsa malonda ankatseka njira ndi malonda awo. Anthu ankapita kumsika kukagula katundu wa m’nyumba monga zipangizo zadothi, zagalasi zomwe zinkakhala zokwera mtengo komanso zinthu zakumunda ngati ndiwo zamasamba ndi zina zotere. Popeza pa nthawiyo kunalibe mafiriji, anthu ankapita kumsika tsiku lililonse kuti akagule zofunika pakhomo. Kumsikako, munthu ankatha kumva nkhani zosiyanasiyana kuchokera kwa odzagulitsa malonda kapena anthu ena odzagula. Ana ankasewera komanso anthu ofuna ntchito ankatha kukhala penapake n’kumadikira munthu woti awalembe ntchito. Yesu anachiritsanso odwala pamsika ndipo nayenso Paulo nthawi zina ankalalikira pamsika. (Mac. 17:17) Mosiyana ndi zimenezi, alembi ndi Afarisi onyada ankasangalala akamalemekezedwa komanso kupatsidwa ulemu m’malo ngati amenewa.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 20:20, 21
mkazi wa Zebedayo: Amenewa ndi mayi awo a mtumwi Yakobo ndi Yohane. Malinga ndi Uthenga Wabwino wa Maliko, Yakobo ndi Yonane ndi amene anapita kwa Yesu. Zikuoneka kuti atumwiwa ndi amene anatuma mayi awo a Salome kuti akawapemphere kwa Yesu. Salome anali mchemwali wake wa Mariya amayi ake a Yesu.—Mat. 27:55, 56; Maliko 15:40, 41; Yoh. 19:25.
mmodzi kudzanja lanu lamanja, wina kumanzere kwanu: Mbali zonsezi zikuimira udindo wapadera, koma munthu amene ankakhala kudzanja lamanja ndi amene ankakhala ndi udindo waukulu.—Sal. 110:1; Mac. 7:55, 56; Aroma 8:34.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 20:26
mtumiki: Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti di·aʹko·nos potanthauza munthu amene nthawi zonse amagwira ntchito modzichepetsa m’malo mwa anthu ena. Mawuwa amagwiritsidwanso ntchito ponena za Khristu (Aroma 15:8), atumiki a Khristu (1 Akor. 3:5-7; Akol. 1:23), atumiki othandiza (Afil. 1:1; 1 Tim. 3:8), antchito apakhomo (Yoh. 2:5, 9) komanso akuluakulu a boma (Aroma 13:4).
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 21:9
M’pulumutseni: Mawu ake enieni, “Hosana.” Mawu achigiriki amenewa amachokera ku mawu achiheberi omwe amatanthauza “m’pulumutseni” kapena “chonde m’pulumutseni.” Palembali, mawuwa anagwiritsidwa ntchito popempha mochonderera kwa Mulungu kuti apulumutse Mwana wa Davide. N’kupita kwa nthawi, anayamba kugwiritsidwa ntchito popemphera komanso potamanda Mulungu. Mawu achiheberiwa amapezeka pa Sal. 118:25, lomwe ndi mbali ya Masalimo omwe chaka ndi chaka ankaimbidwa m’nyengo ya Pasika. Choncho, nthawi zonse munthu akamachita mwambo wa Pasika ankakumbukira mawu amenewa. Njira ina imene Mulungu anayankhira pempheroli ndi pamene anaukitsa Yesu. Pa Mat. 21:42, Yesu anagwira mawu a Sal. 118:22, 23 ndipo ananena kuti ankanena za Mesiya.
Mwana wa Davide: Mawuwa akusonyeza kuti anthuwa ankadziwa bwino mzere wobadwira wa Yesu komanso udindo wake monga Mesiya wolonjezedwa.
MARCH 12-18
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 22-23
“Muzitsatira Malamulo Awiri Aakulu Kwambiri”
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 22:37
mtima: Mawuwa akagwiritsidwa ntchito mophiphiritsa, amatanthauza munthu wamkati. Koma akagwiritsidwa ntchito limodzi ndi “moyo” komanso “maganizo,” amakhala akutanthauza zimene munthu amalakalaka, kukonda komanso mmene amamvera. Mawu atatu omwe anagwiritsidwa ntchito palembali (mtima, moyo ndi maganizo) amasonyeza kuti tiyenera kukonda kwambiri Mulungu.
moyo: kapena kuti “munthu yense.”
maganizo: Mawuwa akutanthauza nzeru zonse. Munthu ayenera kugwiritsa ntchito nzeru zake zonse kuti adziwe bwino Mulungu komanso kumukonda. (Yoh. 17:3; Aroma 12:1) Mawuwa anachokera palemba la Deut. 6:5, ndipo palembali anagwiritsa ntchito mawu achiheberi omwe amatanthauza ‘mtima, moyo ndi mphamvu.’ Koma m’buku la Uthenga Wabwino wa Mateyu anagwiritsa ntchito mawu akuti “maganizo” m’malo mwa mawu akuti “mphamvu.” Pali zifukwa zingapo zomwe zinachititsa kuti agwiritsire ntchito mawu osiyanawa. Choyamba, ngakhale kuti m’Chiheberi mulibe mawu enieni otchulira “maganizo,” tanthauzo la mawu achiheberi akuti “mtima” limakhudzanso maganizo. Mawu akuti “mtima” akagwiritsidwa ntchito mophiphiritsa, amatanthauza munthu yense wamkati kuphatikizapo zimene munthu akuganiza, mmene akumvera, mmene amaonera zinthu komanso zolinga zake. (Deut. 29:4; Sal. 26:2; 64:6; onani mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 22:37 pankhani ya mtima.) Pa chifukwa chimenechi, pamene m’Chiheberi agwiritsa ntchito mawu akuti “mtima,” Baibulo lachigiriki la Septuagint limagwiritsa ntchito mawu ofanana nawo akuti “maganizo.” (Gen. 8:21; 17:17; Miy. 2:10; Yes. 14:13) Chifukwa chinanso chimene Mateyu anagwiritsira ntchito mawu achigiriki akuti “maganizo” m’malo mwa “mphamvu” pamene ankagwira mawu a pa Deut. 6:5 n’choti mawu achiheberi omwe anamasuliridwa kuti “mphamvu” angatanthauze mphamvu zenizeni, kaganizidwe kapena nzeru za munthu. Kaya anachita zimenezi chifukwa chiyani, kufanana matanthauzo kwa mawu achigiriki ndi achiheberi kungatithandize kumvetsa chifukwa chake anthu amene analemba mabuku a Uthenga Wabwino sanagwiritse ntchito ndendende mawu omwe ali m’buku la Deuteronomo.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 22:39
Lachiwiri: Pa Mat. 22:37, pali mawu amene Yesu ananena poyankha funso limene Mfarisi wina anafunsa. Koma m’malo mongoyankha funsolo, Yesu anafotokozanso zokhudza lamulo lachiwiri lomwe limapezeka pa Lev. 19:18. Iye anaphunzitsa kuti malamulo awiriwa amagwirizana kwambiri komanso kuti Chilamulo komanso zolemba zonse za aneneri zagona pa malamulo awiri amenewa.—Mat. 22:40.
mnzako: Mawu achigiriki omwe anamasuliridwa kuti “mnzako” (omwe mawu ake enieni ndi, “amene umakhala naye pafupi”) samangotanthauza anthu oyandikana nawo. Angatanthauzenso anthu ena onse amene umalankhula nawo.—Luka 10:29-37; Aroma 13:8-10.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 22:40
Chilamulo . . . Zolemba za Aneneri: Mawu akuti “Chilamulo” amatanthauza mabuku a m’Baibulo kuyambira Genesis mpaka Deuteronomo. Pomwe “Zolemba za Aneneri” ndi mabuku aulosi omwe amapezeka m’Malemba Achiheberi. Koma mawuwa akagwiritsidwa ntchito pamodzi, amatanthauza malemba onse achiheberi.—Mat. 7:12; 22:40; Luka 16:16.
chagona: Mawu achigiriki omwe anamasuliridwa kuti “chagona” amagwiritsidwa ntchito mophiphiritsa ndipo amatanthauza “chimadalira kapena chachokera.” Pamenepa Yesu ankatanthauza kuti malemba onse achiheberi, osati Chilamulo chokha, zagona pa chikondi.—Aroma 13:9.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 22:21
zinthu za Kaisara kwa Kaisara: Ndi mawu okhawa opezeka m’Baibulo omwe Yesu anatchula ponena za mfumu ya Roma. Mawuwa amapezekanso pa Maliko 12:17 komanso Luka 20:25. “Zinthu za Kaisara” zikuphatikizapo kupereka ndalama zamisonkho komanso kulemekeza ndi kugonjera olamulira a boma.—Aroma 13:1-7.
za Mulungu: Zinthu zimenezi zikuphatikizapo zimene timachita pa moyo wathu, kumulambira, kumukonda komanso kumumvera.—Mat. 4:10; 22:37, 38; Mac. 5:29; Aroma 14:8.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 23:24
amene mumasefa zakumwa zanu kuti muchotsemo kanyerere koma mumameza ngamila: Nyerere komanso ngamila zinali zinthu zodetsedwa kwa Aisiraeli. (Lev. 11:4, 21-24) Yesu anagwiritsa ntchito mawuwa mokokomeza ponena kuti atsogoleri achipembedzo ankasefa zakumwa zawo n’cholinga choti asadetsedwe ndi kanyerere pomwe ankanyalanyaza zinthu zikuluzikulu za m’Chilamulo, kumene kunali ngati kumeza ngamila.
MARCH 19-25
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 24
“Pitirizani Kukhala Maso M’masiku Otsiriza Ano”
it-2 279 ¶6
Chikondi
Chikondi cha Munthu Chikhoza Kuzilala: Pofotokozera ophunzira ake zinthu za m’tsogolo, Yesu ananena kuti chikondi (a·gaʹpe) cha anthu ambiri omwe amati amakhulupirira Mulungu chidzazilala. (Mat. 24:3, 12) Mtumwi Paulo ananena kuti, monga chizindikiro cha masiku otsiriza, anthu adzakhala “okonda ndalama.” (2 Tim. 3:1, 2) Zimenezi zikusonyeza kuti munthu akhoza kusiya kuona zinthu moyenera ndipo chikondi chomwe anali nacho poyamba chikhoza kuzilala. Izi zikusonyeza kuti n’zofunika kwambiri kuti tizikulitsa chikondi chathu poyesetsa kusinkhasinkha Mawu a Mulungu komanso kutsatira mfundo zake.—Aef. 4:15, 22-24.
Kodi Mumachita Zonse Zimene Mulungu Amafuna?
5 Ponena za masiku otsiriza ano, Yesu anati: “Pakuti monga mmene analili masiku a Nowa, ndi mmenenso kukhalapo kwa Mwana wa munthu kudzakhalire. M’masiku amenewo chigumula chisanafike, anthu anali kudya ndi kumwa. Amuna anali kukwatira ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikira tsiku limene Nowa analowa m’chingalawa. Anthu ananyalanyaza zimene zinali kuchitika mpaka chigumula chinafika n’kuwaseseratu onsewo. Zidzateronso ndi kukhalapo kwa Mwana wa munthu.” (Mateyu 24:37-39) Palibe vuto ndi kudya komanso kumwa ngati munthu atachita zimenezi mosapitirira malire. Komanso paja amene anayambitsa ukwati ndi Mulungu. (Genesis 2:20-24) Ndiye ngati mwazindikira kuti mukutanganidwa kwambiri ndi zinthu zatsiku ndi tsiku zimenezi, bwanji osapempha Yehova kuti akuthandizeni? Iye angatithandize kuti tiziika zinthu zokhudza Ufumu pamalo oyamba, tizichita zinthu zoyenera komanso kuti tizichita zimene amafuna.—Mateyu 6:33; Aroma 12:12; 2 Akorinto 13:7.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 24:8
chiyambi cha masautso: Mawuwa anachokera ku mawu achigiriki omwe amatanthauza ululu womwe munthu amamva pobereka. Ngakhale kuti palembali mawuwa agwiritsidwa ntchito ponena za masautso, zopweteka komanso mavuto, mawuwa akusonyezanso kuti mavuto omwe ananenedweratuwo adzayamba kuchitika pafupipafupi, adzakhala aakulu kwambiri komanso azidzatenga nthawi yaitali mofanana ndi zowawa za pobereka. Zimenezi zidzachitika chisautso chachikulu chotchulidwa pa Mateyu 24:21 chisanayambe.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 24:20
m’nyengo ya chisanu: Mvula, madzi osefukira komanso kuzizira zikanachititsa kuti kuyenda komanso kupeza chakudya ndi malo ogona kukhale kovuta.—Ezara 10:9, 13.
pa tsiku la sabata: M’madera a ku Yudeya, kunali malamulo oletsa kuchita zinthu zina pa tsiku la sabata. Choncho sizikanatheka kuti munthu ayende ulendo wautali atanyamula katundu. Komanso patsikuli, zipata zinkakhala zotseka.—Onani Mac. 1:12 ndi sgd mutu 16A.