Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya April 2018
APRIL 2-8
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 26
“Kufanana Komanso Kusiyana Komwe Kulipo Pakati pa Mwambo wa Pasika ndi Chikumbutso”
nwtsty zithunzi ndi mavidiyo
Mwambo wa Pasika
Pa mwambo wa Pasika pankakhala zakudya monga nyama ya nkhosa yowotcha (palibe fupa lililonse la nkhosayo lomwe linkathyoledwa kapena kuphwanyidwa) (1); mkate wopanda chofufumitsa (2); ndi masamba owawa (3). (Eks. 12:5, 8; Num. 9:11) Masamba owawa ayenera kuti ankakumbutsa Aisiraeli kuti anali ku ukapolo wowawa ku Iguputo. Yesu anagwiritsa ntchito mkate wopanda chofufumitsa monga chizindikiro cha thupi lake lopanda uchimo. (Mat. 26:26) Mtumwi Paulo ananena kuti Yesu ndi “nsembe yathu ya pasika.” (1 Akor. 5:7) Komanso nthawi ya atumwi isanafike, anthu anali atayamba kugwiritsa ntchito vinyo (4) pa mwambo wa Pasika. Yesu anagwiritsa ntchito vinyo ndipo vinyoyo ankaimira magazi ake, omwe ankayenera kukhetsedwa chifukwa cha anthu ambiri.—Mat. 26:27, 28.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 26:26
ukuimira: Mawu achigiriki akuti e·stinʹ (omwe tanthauzo lake lenileni ndi “ndi”) angatanthauze “kusonyeza; kuimira chinachake, kukhala m’malo mwa chinachake.” Atumwi sanavutike kumvetsa zimenezi chifukwa Yesu yemwe anali ndi thupi langwiro anali pomwepo komanso mkate wopanda chofufumitsawo womwe anali atangotsala pang’ono kuti adye unali pompo. Choncho, mkatewo sunkatanthauza thupi lenileni la Yesu. N’zochititsa chidwi kuti mawu achigiriki ofanana ndi omwewa amapezekanso pa Mat. 12:7, ndipo Mabaibulo ambiri amawamasulira kuti “kuimira.”
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 26:28
magazi a pangano: Pangano latsopano la pakati pa Yehova ndi Akhristu odzozedwa, linayamba kugwira ntchito chifukwa cha nsembe ya Yesu. (Aheb. 8:10) Pa lembali Yesu anagwiritsa ntchito mawu ofanana ndi amene Mose anagwiritsa ntchito pamene ankapereka Chilamulo monga mkhalapakati wa Mulungu ndi Aisiraeli. (Eks. 24:8; Aheb. 9:19-21) Mofanana ndi momwe magazi a ng’ombe ndi mbuzi anachititsira kuti pakhale pangano pakati pa Mulungu ndi Aisiraeli, magazi a Yesu anathandizanso kuti pangano latsopano la pakati pa Yehova ndi Isiraeli wauzimu liyambe kugwira ntchito. Pangano limeneli linayamba kugwira ntchito pa Pentekosite wa mu 33 C.E.—Aheb. 9:14, 15.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 26:17
Pa tsiku loyamba la chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa: Chikondwerero cha Pasika chikachitika pa Nisani 14, chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa chinkayamba pa Nisani 15 ndipo chinkachitika masiku 7. (Onani sdg mutu 19.) Koma m’nthawi ya Yesu, zikondwerero ziwirizi zinkangotengedwa ngati chikondwerero chimodzi moti masiku onse 8, nthawi zina ankatchulidwa kuti “chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa.” (Luka 22:1) Choncho mawu a palembali akuti “Pa tsiku loyamba la” angatchulidwenso kuti “lisanafike tsiku la.” Mogwirizana ndi tanthauzo la mawuwa m’Chigiriki komanso chikhalidwe cha Ayuda, zikuoneka kuti ophunzirawa anafunsa Yesu funso la pa Mateyu 26:17 pa Nisani 13. Masana a tsikuli, ophunzirawo anakonza zofunika pa mwambo wa Pasika womwe unayamba “chakumadzulo ndithu.” Madzulowo anali chiyambi cha tsiku la Nisani 14.—Maliko 14:16, 17.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 26:39
kapu iyi indipitirire: M’Baibulo, mawu akuti “kapu” kawirikawiri amagwiritsidwa ntchito mophiphiritsa ponena za chifuniro cha Mulungu, kapena “gawo la chinachake” chimene munthu wapatsidwa. N’zosachita kufunsa kuti Yesu sankafuna kuti imfa yake ibweretse chitonzo kwa Yehova chifukwa chophedwa pa mlandu woukira boma komanso kunyoza Mulungu. Zimenezi ndi zimene zinachititsa Yesu kupemphera kuti “kapu” imeneyi imupitirire.
APRIL 9-15
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 27-28
“Kodi Tingamvere Bwanji Lamulo Lakuti, Pitani Mukaphunzitse Anthu?”
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 28:19
mukaphunzitse: Mawu achigiriki akuti ma·the·teuʹo angatanthauzenso “kuphunzitsa” n’cholinga choti munthuyo akhale wophunzira kapena wotsatira wako. (Yerekezerani ndi Mat. 13:52 pomwenso anagwiritsa ntchito mawu akuti “akaphunzitsidwa.”) Mawu akuti “muziwabatiza” komanso akuti “kuwaphunzitsa” angatithandize kudziwa zimene tiyenera kuchita tikamatsatira lamulo la Yesu lakuti, “mukaphunzitse.”
anthu a mitundu yonse: Mawu ake enieni angamasuliridwe kuti “mitundu yonse,” koma tikawerenga nkhani yonse timaona kuti mawu amenewa akutanthauza munthu aliyense payekha kuchokera m’mitundu yonse. Tikutero chifukwa mawu akuti muziwabatiza amanena za munthu aliyense payekha osati mtundu wonse. Lamulo loti aziphunzitsa “anthu a mitundu yonse” linali latsopano. Yesu asanayambe utumiki wake, Malemba amasonyeza kuti anthu a mitundu ina ankalandiridwa ku Isiraeli akabwera mwakufuna kwawo kudzalambira Yehova. (1 Maf. 8:41-43) Ndiye popereka lamulo limeneli, Yesu ankauza ophunzira ake kuti azilalikiranso anthu a mitundu ina, osati Ayuda okha. Iye ankasonyeza kuti ntchito yopanga ophunzirayi iyenera kuchitika padziko lonse.—Mat. 10:1, 5-7; Chiv. 7:9.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 28:20
ndi kuwaphunzitsa: Mawu achigiriki akuti “kuwaphunzitsa” amatanthauza kuuza munthu malangizo, kumufotokozera komanso kumuonetsa umboni woti zimene akuuzidwazo ndi zoona. Kuwaphunzitsa anthu kusunga zinthu zonse zimene Yesu analamula inali ntchito yopitirira. Izi zinkaphatikizapo kuwaphunzitsa zimene Yesu ankaphunzitsa, kuwathandiza kuti azigwiritsira ntchito zimene aphunzirazo komanso kuwathandiza kuti azitengera chitsanzo chake.—Yoh. 13:17; Aef. 4:21; 1 Pet. 2:21.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 27:51
nsalu yotchinga: Nsaluyi inkakhala yokongola ndipo inkasiyanitsa Malo Oyera ndi Malo Oyera Koposa. Malinga ndi chikhalidwe cha Ayuda, nsaluyi yomwe inkakhala yolemera, inali mamita 18 m’litali, mamita 9 m’lifupi komanso masentimita 7.4 kuchindikala kwake. Pamene nsaluyi inang’ambika, Yehova anasonyeza kuti anali atakwiyira kwambiri anthu omwe anapha Mwana wake komanso zinasonyeza kuti tsopano anthu anali ndi mwayi woti atha kupita kumwamba.—Aheb. 10:19, 20.
m’nyumba yopatulika: Mawu achigiriki akuti na·osʹ angatanthauze chipinda chapakati chomwe chinali ndi Malo Oyera komanso Malo Oyera Koposa.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Mat. 28:7
mukauze ophunzira ake kuti wauka: Sikuti azimayiwa anangokhala oyamba kuuzidwa kuti Yesu wauka ayi, iwo anauzidwanso kuti akauze ophunzira ake. (Mat. 28:2, 5, 7) Malinga ndi miyambo ya Ayuda yomwe sinali yochokera m’malemba, umboni woperekedwa ndi mzimayi sunkaloledwa kubwalo lamilandu. Koma mosiyana ndi zimenezi, mngelo wa Yehova analemekeza azimayi aja powauza uthenga wosangalatsa umenewu kuti akauze ophunzira a Yesu.
APRIL 16-22
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MALIKO 1-2
“Machimo Ako Akhululukidwa”
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Maliko 2:9
Chapafupi n’chiti: Zikanakhala zosavuta kuti munthu anene kuti akhoza kukhululukira machimo, chifukwa sipangafunike umboni uliwonse wosonyeza kuti angachitedi zimenezo. Koma pamene Yesu ananena kuti, Nyamuka . . . uyende anafunika kuchita chozizwitsa chomwe chikanathandiza anthu kudziwa kuti anapatsidwanso mphamvu zokhululukira machimo. Nkhani imeneyi komanso zimene lemba la Yes. 33:24 limanena, zimasonyeza kuti timadwala chifukwa cha uchimo.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Maliko 1:11
panamveka mawu ochokera kumwamba: M’mabuku a uthenga wabwino pali malo atatu pomwe Baibulo limamufotokoza Yehova akuyankhula mwachindunji ndi anthu, ndipo poyamba ndi pa Maliko 1:11.
Iwe ndiwe Mwana wanga: Pa nthawi imene anali kumwamba, Yesu anali mwana wa Mulungu. (Yoh. 3:16) Atabadwa monga munthu padzikoli, Yesu analinso “Mwana wa Mulungu” ngati mmene analili Adamu yemwe anali wangwiro. (Luka 1:35; 3:38) Komabe n’zomveka kunena kuti mawu a Yehovawa sankangodziwitsa anthu kuti iye ndi mwana wake, koma kuti amamukonda kwambiri. Pamene Yehova anachita zimenezi komanso kupereka mzimu wake anasonyeza kuti Yesu anali mwana wake wauzimu, amene anali ‘atabadwanso’ mwatsopano ndipo anali ndi chiyembekezo chodzapitanso kumwamba. Izi zinasonyezanso kuti anali atasankha Yesu kuti adzakhale Mfumu komanso Mkulu wa Ansembe m’tsogolo.—Yerekezerani ndi Yoh. 3:3-6; 6:51; Luka 1:31-33; Aheb. 2:17; 5:1, 4-10; 7:1-3.
ndimakondwera nawe: Mawuwa angatanthauzenso “ndimasangalala nawe; ndimakunyadira.” Mawu omwewa akupezekanso pa Mat. 12:18 ndipo ndi ulosi wa pa Yes. 42:1 umene umanena za Mesiya kapena kuti Khristu. Pamene Yehova analankhula mawuwa komanso kupereka mzimu wake anasonyeza kuti Yesu anali Mesiya wolonjezedwa.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Maliko 2:28
Mbuye wa sabata: Yesu ankanena za iye mwini pamene ananena mawu amenewa (Mat. 12:8; Luka 6:5), ndipo ankasonyeza kuti akanatha kugwiritsa ntchito tsiku la sabata kuchita zimene atate wake wakumwamba anamulamula kuchita. (Yerekezerani ndi Yoh. 5:19; 10:37, 38.) Yesu anachita zozizwitsa zina monga kuchiritsa pa tsiku la sabata. (Luka 13:10-13; Yoh. 5:5-9; 9:1-14) Zimenezi zinkasonyeza zomwe Yesu adzachite mu Ufumu wake umene udzakhale ngati mpumulo wa sabata.—Aheb. 10:1.
APRIL 23-29
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MALIKO 3-4
“Anachiritsa Munthu pa Tsiku la Sabata”
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Maliko 3:5
mokwiya ndi kumva chisoni kwambiri: Ndi Maliko yekha amene anafotokoza mmene Yesu anamvera ataona kuuma mtima kwa atsogoleri achipembedzo. (Mat. 12:13; Luka 6:10) N’kutheka kuti Maliko anamva zimenezi kwa Petulo, yemwe amaoneka kuti nthawi zambiri ankakhudzidwa mumtima ndi zinthu.—Onerani vidiyo yakuti “Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Maliko.”
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Maliko 3:29
wanyoza mzimu woyera: Kunyoza mzimu woyera kumatanthauza kunenera Mulungu kapena zinthu zopatulika mawu oipa kapena achipongwe. Popeza mzimu woyera umachokera kwa Mulungu, kulimbana kapena kukana mzimuwo kumasonyeza kuti tikunyoza Mulungu yemwe amapereka mzimuwo. Malinga ndi Mat. 12:24, 28 komanso Maliko 3:22, atsogoleri achipembedzo Achiyuda anaona Yesu akuchita zozizwitsa mothandizidwa ndi mzimu woyera, koma ankanena kuti iye ankathandizidwa ndi mphamvu za Satana.
mlandu wa tchimo losatha: Zikuoneka kuti ili ndi tchimo limene munthu wachita mwadala ndipo sangakhululukidwe mpaka kalekale; palibe nsembe yomwe ingathe kuphimba tchimo limenelo.—Onaninso pa wanyoza mzimu woyera.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Amene Ali ndi Makutu Akumva, Amve”
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Maliko 4:9
Amene ali ndi makutu akumva, amve: Asananene fanizo la wofesa mbewu, Yesu anati: “Tamverani.” (Maliko 4:3) Kenako anamaliza fanizoli ndi mawu amene ali mu vesi 9 pofuna kusonyeza ophunzira ake kuti zinali zofunika kumvera ndi kutsatira malangizo ake mosamala. Mawu ofanana ndi amenewa amapezekanso pa Mat. 11:15; 13:9, 43; Maliko 4:23; Luka 8:8; 14:35; Chiv. 2:7, 11, 17, 29; 3:6, 13, 22; 13:9.
APRIL 30–MAY 6
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MALIKO 5-6
“Yesu Ali ndi Mphamvu Zoukitsa Anthu Amene Anamwalira”
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Maliko 5:39
sanamwalire ayi, koma akugona: M’Baibulo, nthawi zambiri imfa imayerekezedwa ndi tulo. (Sal. 13:3; Yoh. 11:11-14; Mac. 7:60; 1 Akor. 7:39; 15:51; 1 Ates. 4:13) Yesu ankadziwa kuti aukitsa mtsikana yemwe anamwalirayo, moti n’kutheka kuti ananena zimenezi chifukwa ankafuna kusonyeza anthuwo kuti anthu akufa adzaukitsidwa mofanana ndi mmene timadzutsira munthu yemwe anali mtulo. Mphamvu zomwe Yesu anagwiritsa ntchito poukitsa mtsikanayo zinali zochokera kwa Atate wake, “amene amapereka moyo kwa akufa ndipo amanena za zinthu zimene palibe ngati kuti zilipo”—Aroma 4:17.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Maliko 5:19
ukawauze: Mosiyana ndi malangizo amene ankakonda kupereka nthawi zonse oti munthu asalengeze zozizwitsa zimene zamuchitikira (Maliko 1:44; 3:12; 7:36), Yesu anauza munthuyo kuti akauze achibale ake zimene zinamuchitikira. N’kutheka kuti Yesu anachita zimenezi chifukwa anauzidwa kuti achoke m’deralo ndipo izi zikanachititsa kuti asalalikire yekha anthu a m’deralo. Komanso zimenezi zikanathandiza kuti azikamba za munthu wochiritsidwa uja m’malo momakamba za nkhumba zinafa zija.
nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Maliko 6:11
sansani fumbi kumapazi anu: Zimene atumwiwa ankachita zinkasonyeza kuti ankasambira m’manja anthu a mumzindawo pa chilango chomwe akanalandira kuchokera kwa Mulungu. Mawu ofanana ndi omwewa amapezekanso pa Mat. 10:14 ndi pa Luka 9:5. Maliko ndi Luka anawonjezera mawu akuti “kuti ukhale umboni wowatsutsa.” Paulo ndi Baranaba anatsatira malangizo amenewa pamene anali ku Antiokeya wa ku Pisidiya (Mac. 13:51). Komanso Paulo anachita zofanana ndi zimenezi ku Korinto. Iye anakutumula zovala zake n’kunena kuti: “Magazi anu akhale pamitu panu. Ine ndilibe mlandu.” (Mac. 18:6) Kuchita zimenezi sinali nkhani yachilendo kwa atumwiwo chifukwa Ayuda odzipereka pa chipembedzo chawo akamachokera m’madera a anthu a mitundu ina, ankakutumula zovala zawo komanso kusasa fumbi la nsapato zawo asanalowe m’dera la Ayuda. Koma zikuoneka kuti malangizo amene Yesu anapereka kwa ophunzira ake sankatanthauza zimene Ayudawa ankachita.