Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr18 September tsamba 1-5
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya September 2018

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya September 2018
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu (2018)
  • Timitu
  • SEPTEMBER 3-9
  • SEPTEMBER 10-16
  • SEPTEMBER 17-23
  • SEPTEMBER 24-30
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu (2018)
mwbr18 September tsamba 1-5

Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya September 2018

SEPTEMBER 3-9

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOHANE 1-2

“Chozizwitsa Choyamba cha Yesu”

Kufufuza Mfundo Zothandiza

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 1:1

Mawu: M’chigiriki, mawu ake enieni ndi ho loʹgos. Mawu amenewa anagwiritsidwa ntchito palembali ngati dzina laudindo. Mawuwa amapezekanso pa Yoh. 1:14 ndi Chiv. 19:13. Yohane ananena kuti limeneli ndi dzina laudindo la Yesu. Yesu ankadziwika ndi dzinali asanabwere padziko lapansi, pamene ankachita utumiki wake padziko lapansi monga munthu wangwiro komanso atapita kumwamba. Yesu anali Mawu m’njira yakuti ankapereka uthenga komanso malangizo ochokera kwa Yehova kwa angelo komanso anthu. Choncho, n’zomveka kunena kuti Yesu asanabwere padziko lapansi, Yehova ankamugwiritsa ntchito ngati Mawu popereka mauthenga kwa anthu, ndipo anali ngati womulankhulira.​—Gen. 16:7-11; 22:11; 31:11; Eks. 3:2-5; Ower. 2:1-4; 6:11, 12; 13:3.

ndi: Mawu ake enieni, “kuyandikana.” M’vesili, mawu achigiriki akuti pros amasonyeza kuyandikira komanso kukhala mabwenzi. Amasonyezanso kuti pali anthu awiri moti malinga ndi zimene vesili likunena, Mawu ndi osiyana ndi Mulungu woona.

Mawuyo anali mulungu: Kapena kuti “Mawu anali waumulungu [kapena kuti wokhala ngati Mulungu].” Yohane ananena mawu amenewa pofotokoza zambiri zokhudza makhalidwe a “Mawu” (pachigiriki ho loʹgos; onani mfundo zimene ndikuphunzira pa Mawu) yemwe ndi Yesu Khristu. Dzina limeneli limasonyeza udindo wa Mwana woyamba kubadwa wa Mulungu, yemwe anamugwiritsa ntchito polenga zinthu zina zonse. Chimenechi n’chifukwa chake amatchulidwa kuti “mulungu, wofanana ndi Mulungu kapena waumulungu.” M’Mabaibulo ambiri, mawuwa anawamasulira kuti “Mawu ndiye Mulungu,” kutanthauza kuti ndi wofanana ndi Mulungu Wamphamvuyonse. Komabe pali zifukwa zomveka bwino zomwe zimasonyeza kuti Yohane sankatanthauza kuti “Mawu” anali wofanana ndi Mulungu Wamphamvuyonse. Choyamba, vesili limasonyeza kuti “Mawuyo anali ndi Mulungu.” Komanso mawu achigiriki akuti the·osʹ omwe amatanthauza mulungu, amapezeka maulendo atatu muvesi 1 ndi 2. Ulendo woyamba ndi wachitatu, mawu akuti the·osʹ ali ndi mawu otchulira dzina, pomwe achiwiriwo alibe mawuwa. Akatswiri ena amanena kuti kusapezeka kwa mawu otchulira dzina kumbuyo kwa mawu akuti the·osʹ pa mawu achiwiriwo kuli ndi tanthauzo lapadera. Malo omwe agwiritsa ntchito mawu otchulira dzina kumbuyo kwa mawu akuti the·osʹ palembali, akunena za Mulungu Wamphamvuyonse. Koma mawu otchulira dzina aja akapanda kuikidwa kumbuyo kwa mawu akuti the·osʹ amasanduka mfotokozi ndipo m’vesili akunena zokhudza makhalidwe a “Mawu.” Choncho, Mabaibulo ena achingelezi, achifulenchi komanso achijeremani anamasulira mawuwa mofanana ndi Baibulo la Dziko Latsopano. Baibuloli linamasulira mavesiwa kuti “Mawu” anali “mulungu; wofanana ndi Mulungu kapena waumulungu.” Mabaibulo akale kwambiri a Uthenga Wabwino wa Yohane, omwe anamasuliridwa m’chinenero cha Chisahidiki komanso Chibohariki zomwe ndi zinenero zing’onozing’ono zimene zimapanga chinenero cha Chikoputiki, nawonso anamasulira mofanana ndi Baibulo la Dziko Latsopano. Mabaibulowa ayenera anamasuliridwa m’zaka za m’ma 200 C.E. ndi 300 C.E., ndipo anamasulira mawu awiri akuti the·osʹ omwe ali pa Yoh. 1:1 mosiyana. Mabaibulo amenewa ankafotokoza makhalidwe a “Mawu,” kuti ndi wofanana ndi Mulungu, koma sananene kuti Mawuyo ndi Atate yemwe ndi Mulungu Wamphamvuyonse. Mofanana ndi vesi limeneli, lemba la Akol. 2:9 limafotokoza kuti Khristu anali ndi “makhalidwe a Mulungu.” Komanso malinga ndi 2 Pet. 1:4, ngakhale odzozedwa omwe adzalamulire limodzi ndi Khristu nawonso adzakhala “ndi makhalidwe a Mulungu.” Kuwonjezera pamenepa, m’Baibulo la Septuagint, mawu achigiriki akuti the·osʹ ndi ofanana ndi mawu achiheberi akuti ʼel ndi ʼelo·himʹ omwe amatanthauza “Mulungu.” Mawu amenewanso amatanthauza “Wamphamvu.” Mawuwa amagwiritsidwa ntchito ponena za Mulungu Wamphamvuyonse, milungu ina ngakhalenso anthu. Choncho kutchula Mawu kuti “mulungu” kapena “wamphamvu” kukufanana ndi zimene lemba la Yes. 9:6 linanena ponena za Mesiya kuti azidzatchedwa “Mulungu Wamphamvu” (koma osati “Mulungu Wamphamvuyonse”) ndiponso kuti adzakhala “Atate Wamuyaya” kwa anthu omwe azidzawalamulira. Iye adzakwanitsa kuchita zimenezi chifukwa “Yehova wa makamu” adzamuthandiza.​—Yes. 9:7.

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 1:29

Mwanawankhosa wa Mulungu: Yesu atangobatizidwa komanso kuyesedwa ndi Mdyerekezi, Yohane M’batizi anamutchula kuti “Mwanawankhosa wa Mulungu.” Mawu amenewa amapezeka palemba limeneli komanso pa Yoh. 1:36 basi. (Onani sgd 4-B) Kuyerekezera Yesu ndi Mwana wankhosa n’koyenera kwambiri. Tikutero chifukwa Baibulo limasonyeza kuti kale, anthu ankapereka nkhosa kuti machimo awo akhululukidwe komanso kuti akhale paubwenzi ndi Mulungu. Zimenezi zinkasonyeza kuti Yesu adzapereka moyo wake wangwiro kuti awombole anthu. Mawu akuti “Mwanawankhosa wa Mulungu” amafanana ndi zomwe zinafotokozedwa m’malo enanso m’Baibulo. Popeza Yohane M’batizi ankadziwa bwino Malemba Achiheberi, n’kutheka kuti ankaganizira za zinthu zotsatirazi: Nkhosa yamphongo yomwe Abulahamu anapereka m’malo mwa Isaki (Gen. 22:13), nkhosa ya Pasika yomwe inaphedwa ku Iguputo n’kuthandiza kuti Aisiraeli amasulidwe ku ukapolo (Eks. 12:1-13), kapenanso mwana wa nkhosa yemwe ankaperekedwa nsembe pa guwa la nsembe la Mulungu ku Yerusalemu m’mawa komanso madzulo aliwonse (Eks. 29:38-42). N’kuthekanso kuti Yohane ankaganizira ulosi wa Yesaya womwe umanena kuti “Mtumiki” wa Yehova ‘adzatengedwa ngati nkhosa yopita kokaphedwa.” (Yes. 52:13; 53:5, 7, 11) Pamene mtumwi Paulo ankalemba kalata yake yoyamba yopita ku Korinto, ananena kuti Yesu ndi “nsembe yathu ya pasika.” (1 Akor. 5:7) Nayenso mtumwi Petulo ananena kuti magazi a Khristu anali “amtengo wapatali, monga a nkhosa yopanda chilema ndi yopanda mawanga.” (1 Pet. 1:19) Komanso kwa maulendo oposa 25 m’buku la Chivumbulutso, Yesu anafotokozedwa mophiphiritsa kuti ndi “Mwanawankhosa.”​—Zitsanzo zinanso za mavesi amenewa ndi: Chiv. 5:8; 6:1; 7:9; 12:11; 13:8; 14:1; 15:3; 17:14; 19:7; 21:9; 22:1.

SEPTEMBER 10-16

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOHANE 3-4

“Yesu Analalikira Mayi Wachisamariya”

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 4:6

atatopa: Ndi malo okhawa m’Baibulo pamene amafotokoza kuti Yesu anali “atatopa.” Nthawi inali ili 12 koloko masana ndipo n’kutheka kuti Yesu anali atayenda ulendo wautali kuchokera ku chigwa cha Yorodano ku Yudeya kukafika m’tawuni ya Sukari ku Samariya. Pa ulendowu anakwera chitunda chachitali mamita 900 kapena kuposa.​—Yoh. 4:3-5; onani sgd 4-B.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 3:29

mnzake wa mkwati: Kale, mnzake wa mkwati ndi amene ankakhala ngati womuimira ndipo ndi amene ankayendetsa zambiri zokhudza ukwatiwo. Anthu ankaona kuti mnzake wa mkwati ndi amene ankathandiza kwambiri kuti mwamuna ndi mkazi akwatirane. Pa tsiku laukwati, anthu ankapita kunyumba kwa mkwati kapena kwa bambo ake komwe kunkakhala phwando laukwati. Paphwandoli, mnzake wa mkwati ankasangalala kwambiri akamva mkwati akulankhulana ndi mkwatibwi chifukwa ankaona kuti wakwaniritsa ntchito yake. Yohane M’batizi anaziyerekezera ndi “mnzake wa mkwati.” Choncho tinganene kuti Yesu anali mkwati ndipo ophunzira ake anali mkwatibwi wake. Monga wokonza njira ya Mesiya, Yohane M’batizi anapereka ena mwa anthu amene anali ngati “mkwatibwi” wa Yesu Khristu. (Yoh. 1:29, 35; 2 Akor. 11:2; Aef. 5:22-27; Chiv. 21:2, 9) Phwando laukwati likangotha, ntchito ya “mnzake wa mkwati” inkatheranso pomwepo. Mofanana ndi zimenezi, ponena za Yesu Yohane anati: “Ameneyo ayenera kumawonjezereka, koma ine ndiyenera kucheperachepera.”​—Yoh. 3:30.

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 4:10

madzi amoyo: M’chigiriki mawuwa angatanthauze madzi a mumtsinje kapena kasupe. Madzi amenewa ndi osiyana kwambiri ndi madzi a m’chitsime omwe amangokhala osayenda. Pa Lev. 14:5, mawu achiheberi omwe anawamasulira kuti “madzi otunga kumtsinje” anali akuti “madzi amoyo.” Pa Yer. 2:13 ndiponso 17:13, pamanena kuti Yehova ali ngati “kasupe wa madzi amoyo,” omwe ndi madzi ophiphiritsa opatsa moyo. Pamene Yesu ankalankhula ndi mayi wachisamariya uja anagwiritsa ntchito mawu akuti “madzi amoyo” mophiphiritsa koma zikuoneka kuti mayiyu ankaganiza kuti Yesu ankanena za madzi enieni.​—Yoh. 4:11.

SEPTEMBER 17-23

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOHANE 5-6

“Muzitsatira Yesu Muli ndi Zolinga Zabwino”

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 6:10

amuna pafupifupi 5,000 anakhaladi pansi: Mateyu yekha ndi amene anawonjezera mfundo yakuti panalinso “akazi ndi ana aang’ono.” (Mat. 14:21) N’kutheka kuti anthu amene anadyetsedwa ndi Yesu mozizwitsa anali oposa 15,000.

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 6:14

mneneri: Ayuda ambiri a m’nthawi ya atumwi ankayembekezera kuti kudzabwera mneneri wokhala ngati Mose, yemwe anatchulidwa pa Deut. 18:15, 18, amene adzakhale Mesiya. Mawu akuti adzabwera padziko omwe akupezeka pa Yoh. 6:14, amasonyeza kuti ankanena za kubwera kwa Mesiya. Yohane yekha ndi amene analemba zimenezi.

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 6:27, 54

chakudya chimene chimawonongeka . . . chopereka moyo wosatha: Yesu ankadziwa kuti anthu ena ankangomutsatira kuti awapatse chakudya. Ngakhale kuti chakudya chimathandiza kuti munthu akhale ndi moyo, “chakudya” chochokera m’Mawu a Mulungu chimathandiza kuti anthu adzapeze moyo wosatha. Yesu analimbikitsa anthu kuti aziyesetsa kuti apeze chakudya “chopereka moyo wosatha” zomwe zikutanthauza kuti ankayenera kuchita khama kuphunzira Mawu a Mulungu komanso kukhulupirira zimene ankaphunzirazo.​—Mat. 4:4; 5:3; Yoh. 6:28-39.

wakudya mnofu wanga ndi kumwa magazi anga: Zimene Yohane ananena zikusonyeza kuti anthu akanadya komanso kumwa magazi a Yesu Khristu mophiphiritsa, posonyeza kuti amamukhulupirira. (Yoh. 6:35, 40) Yesu analankhula mawuwa mu 32 C.E., choncho sankanena za mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, womwe anaukhazikitsa chaka chotsatira. Ndiponso ananena mawuwa “chikondwerero cha Ayuda cha pasika” chitangotsala pang’ono (Yoh. 6:4), choncho anthu amene ankamumvetsera akanakumbukira mosavuta za chikondwererochi komanso za kufunika kwa magazi a mwana wa nkhosa omwe anapulumutsa miyoyo ya anthu usiku umene Aisiraeli anachoka ku Iguputo. (Eks. 12:24-27) Apa Yesu ankatsindika mfundo yakuti magazi ake adzathandiza kuti otsatira ake adzapeze moyo wosatha ngati mmene magazi a nkhosa anathandizira Aisiraeli.

Kufufuza Mfundo Zothandiza

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 6:44

kukokedwa: Ngakhale kuti mawu achigiriki omwe amatanthauza “kukoka” amanena zimene zimachitika pokoka ukonde wa nsomba (Yoh. 21:6, 11), lembali silisonyeza kuti Yehova amakakamiza anthu kuchita zimene akufuna. Mawu amenewa angatanthauzenso “kukopa,” ndipo zimene Yesu ananenazi zikufanana ndi zomwe Yehova ananena kwa anthu ake kalelo pa Yer. 31:3, kuti: “Ndakukoka mwa kukoma mtima kwanga kosatha.” (Baibulo la Septuagint linagwiritsanso ntchito mawu omwewa.) Lemba la Yoh. 12:32 limasonyeza kuti Yesu amakokanso anthu osiyanasiyana mwa njira imeneyi. Malemba amanena kuti Yehova anapereka ufulu wosankha kwa anthu. Munthu aliyense angasankhe yekha kumutumikira kapena ayi. (Deut. 30:19, 20) Yehova amakoka mwachikondi anthu onse a mtima wabwino kuti abwere kwa iye. (Sal. 11:5; Miy. 21:2; Mac. 13:48) Amachita zimenezi pogwiritsa ntchito uthenga wa m’Baibulo komanso mzimu woyera. Pa Yoh. 6:45 anagwira mawu ulosi wa pa Yes. 54:13, ndipo amanena za anthu amene amakokedwa ndi Atate.​—Yerekezerani ndi Yoh. 6:65.

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 6:64

Yesu anadziwa . . . amene adzamupereka: Apa Yesu ankanena Yudasi Isikariyoti. Yesu anachezera usiku wonse kupemphera kwa Atate wake asanasankhe atumwi 12. (Luka 6:12-16) Choncho poyamba Yudasi anali wokhulupirika kwa Mulungu. Zikuoneka kuti Yesu anadziwa kuti adzaperekedwa ndi mnzake wapamtima kuchokera m’maulosi a m’Malemba achiheberi. (Sal. 41:9; 109:8; Yoh. 13:18, 19) Yudasi atayamba kukhala ndi mtima woipa, Yesu anazindikira zimenezi chifukwa ankatha kudziwa zimene munthu akuganiza. (Mat. 9:4) Popeza Yehova amatha kudziwiratu zam’tsogolo, anadziwa kuti mmodzi wa anzake a Yesu adzasintha n’kumupereka. Koma tikaganizira makhalidwe a Mulungu komanso zimene wakhala akuchita m’mbuyomu, sitinganene kuti anakonzeratu kuti Yudasi ndi amene adzasinthe n’kupereka Yesu.

kuchokera pa chiyambi: Mawuwa sakutanthauza kuyambira pamene Yudasi anabadwa. Sakutanthauzanso pamene anasankhidwa kukhala mtumwi, zimene zinachitika Yesu atapemphera usiku wonse. (Luka 6:12-16) M’malomwake, akutanthauza kuyambira pamene Yesu anazindikira kuti Yudasi wayamba kuchita zinthu mwachinyengo. (Yoh. 2:24, 25; Chiv. 1:1; 2:23) Zimenezi zikusonyeza kuti zimene Yudasi anachita sizinangochitika mwadzidzidzi, koma anali ataziganizira kwa nthawi yaitali. M’malemba Achigiriki, tanthauzo la mawu akuti “pa chiyambi” (m’Chigiriki, ar·kheʹ) limasinthasintha mogwirizana ndi nkhani imene ikufotokozedwayo. Mwachitsanzo, pa 2 Pet. 3:4 mawu akuti “pa chiyambi” amanena za nthawi imene Yehova anayamba kulenga zinthu. Koma nthawi zambiri amatanthauza zosiyana ndi zimenezi. Mwachitsanzo, Petulo ananena kuti mzimu woyera unagwera pa anthu amitundu ina “monga mmene unachitiranso pa ife poyamba paja.” (Mac. 11:15) Apa iye sankanena za nthawi imene anabadwa kapena imene anasankhidwa kukhala mtumwi. Koma ankanena zimene zinachitika pa Pentekosite mu 33 C.E., pomwe panali ngati “pa chiyambi” poti anthu ayambe kulandira mzimu woyera. (Mac. 2:1-4) Zitsanzo zinanso zosonyeza mmene mawuwa anagwiritsidwira ntchito m’njira yofanana ndi imeneyi zikupezeka pa Luka 1:2; Yoh. 15:27; ndi 1 Yoh. 2:7.

SEPTEMBER 24-30

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOHANE 7-8

“Yesu Ankalemekeza Atate Wake”

Kufufuza Mfundo Zothandiza

nwtsty mfundo zimene ndikuphunzira pa Yoh. 8:58

ine n’kuti ndilipo kale: Ayuda amene ankatsutsa Yesu ankafuna kumugenda ndi miyala chifukwa choti ananena kuti ‘anamuona Abulahamu.’ Iwo ankaona kuti zimenezi n’zosatheka chifukwa Yesu anali ‘asanakwanitse n’komwe zaka 50.’ (Yoh. 8:57) Yesu ankafuna kuwafotokozera kuti asanabwere padziko lapansi anali mngelo wamphamvu kumwamba ndipo iye anakhalapo kalekale kwambiri Abulahamu asanabadwe. Ena amanena kuti lemba limeneli limasonyeza kuti Yesu ndi Mulungu. Iwo amati mawu achigiriki amene anagwiritsidwa ntchito pa Yoh. 8:58, akuti e·goʹ ei·miʹ, (omwe m’Mabaibulo ena amawamasulira kuti “Ine ndine”), ndi ofanana ndi omwe ali pa Eks. 3:14 m’Baibulo la Septuagint ndipo amati mavesi onsewa amanena zofanana. Tikaganizira zimene Yesu ananenazi, mawu akuti ei·miʹ, akusonyeza kuti Yesu anali alipo “Abulahamu asanakhaleko.” Choncho n’zolondola kumasulira mawuwa kuti “ine n’kuti ndilipo” m’malo momasulira kuti “Ine ndine.” Kuwonjezera pamenepo, Mabaibulo akale komanso a masiku ano amamasulira mawuwa kuti “ine n’kuti ndilipo.” Ndipotu pa Yoh. 14:9, anagwiritsanso ntchito mawu omwe aja akuti ei·miʹ pofotokoza zimene Yesu ananena kuti: “Anthu inu, ndakhala nanu nthawi yonseyi, koma kodi iwe Filipo sunandidziwebe?” Palinso Mabaibulo ena ambiri omwe anagwiritsa ntchito mawu omwewa, zomwe zikusonyeza kuti n’zotheka kumasulira mawu akuti ei·miʹ mogwirizana ndi mmene nkhani yake ilili. (Zitsanzo zina za mmene mawuwa anagwiritsidwira ntchito zikupezeka pa Luka 2:48; 13:7; 15:29; Yoh. 1:9; 5:6; 15:27; Mac. 15:21; 2 Akor. 12:19; 1 Yoh. 3:8.) Komanso zimene Yesu ananena pa Yoh. 8:54, 55 zimatithandiza kudziwa kuti iye sankadziona kuti ndi Mulungu mofanana ndi Atate wake.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena