PHUNZIRO 9
Kugwiritsa Ntchito Bwino Zinthu Zooneka
Genesis 15:5
MFUNDO YAIKULU: Muzigwiritsa ntchito zinthu zooneka kuti anthu amvetse mfundo zikuluzikulu.
MMENE MUNGACHITIRE:
Muzisankha zinthu zimene zingathandizedi pophunzitsa. Mungagwiritse ntchito zithunzi, mapu, matchati kapena zinthu zina pofuna kutsindika mfundo zofunika osati timfundo ting’onoting’ono. Mukamaliza, anthu azikumbukira mfundo yaikuluyo osati zinthu zooneka zokhazo.
Zinthuzo zizikhala zoti aliyense atha kuziona.