NYIMBO 70
Fufuzani Anthu Oyenerera
Losindikizidwa
1. Ambuye wathu anatisonyeza
Njira yolalikirira.
‘Fufuzani anthu oyenerera
Ofuna kumva choonadi.
Muziwapatsa moni eni nyumba
Ndi kuwafunira mtendere.
Ngati sanakulandireni
Sansani fumbi m’mapazi muchoke.’
2. Onse amene akulandirani
Alandiranso Ambuye.
Athandizeni kudziwa Yehova
Ngati ali oyenerera.
Musadere nkhawa zoti munene,
Yehova akuthandizani.
Mawu anu akakhala okoma,
Ofatsa adzasangalala.
(Onaninso Mac. 13:48; 16:14; Akol. 4:6.)