Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ya February 2020
FEBRUARY 3-9
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 12-14
“Pangano Lomwe Limakukhudzani”
it-1 522 ¶4
Pangano
Pangano la Abulahamu. Zikuoneka kuti pangano la Abulahamu linayamba kugwira ntchito Abulamu (Abulahamu) atawoloka mtsinje wa Firate popita ku Kanani. Pangano la Chilamulo linakhazikitsidwa patatha zaka 430. (Agal. 3:17) Yehova analankhula ndi Abulahamu pamene ankakhala ku Mesopotamiya mumzinda wa Uri. Anamuuza kuti anyamuke n’kupita kudziko limene Mulungu akamuonetse. (Mac. 7:2, 3; Gen. 11:31; 12:1-3) Lemba la Ekisodo 12:40, 41 (LXX) limasonyeza kuti Aisiraeli anakhala ku Iguputo komanso ku Kanani kwa zaka 430. “Pa tsiku lomwe [zakazi] zinatha,” Aisiraeli omwe anali paukapolo ku Iguputo anamasulidwa. Tsiku lomwe Mulungu anawatulutsa ku Iguputo linali Nisani 14 m’chaka cha 1513 B.C.E., lomwenso linali tsiku la Pasika. (Eks. 12:2, 6, 7) Zimenezi zikusonyeza kuti Abulahamu ayenera kuti anawoloka mtsinje wa Firate kupita ku Kanani pa Nisani 14, mu 1943 B.C.E., ndipo mwachidziwikire pangano la Abulahamu linayamba kugwira ntchito patsikuli. Abulahamu atalowa mu Kanani mpaka kukafika ku Sekemu, Mulungu anaonekeranso kwa iye ndipo anapitiriza kumulonjeza kuti, “Ndidzapereka dziko ili kwa mbewu yako.” Zimenezi zikusonyeza kuti panali kugwirizana pakati pa panganoli ndi Lonjezo la mu Edeni ndipo zinali zoonekeratu kuti “mbewu” imene inkatchulidwayo idzabadwa kudzera mwa munthu. (Gen. 12:4-7) Malonjezo ena omwe Yehova anapereka, amapezeka pa Genesis 13:14-17; 15:18; 17:2-8, 19; 22:15-18.
Chifukwa Chake Muyenera Kudziwa Zoona Zokhudza Abulahamu
Lonjezoli linali lodabwitsa kwambiri ndipo Abulahamu anauzidwa zimenezi maulendo enanso awiri. (Genesis 18:18; 22:18) Kuti lonjezoli lidzakwaniritsidwe, Mulungu adzaukitsa anthu omwe anamwalira kuchokera m’mitundu yosiyanasiyana. Kuukitsidwa kwa anthuwa lidzakhala dalitso lalikulu chifukwa pa nthawiyo dziko lidzakhala malo abwino kwambiri ngati mmene unalili munda wa Edeni. Kenako adzaphunzitsidwa zomwe adzachite kuti adzakhale ndi moyo wosatha.—Genesis 2:8, 9, 15-17; 3:17-23.
it-2 213 ¶3
Lamulo
Mogwirizana ndi maumboni akale, akatswiri amakhulupirira kuti kale anthu akamagulitsana malo, wogula ankaonetsedwa malire ake onse. Wogulayo akakhutira n’kunena kuti “malowa ndawaona,” ankasonyeza kuti wavomereza kugula malowo motsatira malamulo. Yehova atalonjeza zopereka dziko la Kanani kwa Abulahamu, choyamba anaonetsa kaye Abulahamu zigawo zonse 4 za dzikolo. Komabe Abulahamu sananene kuti “malowa ndawaona.” Mwina sananene mawuwa chifukwa Mulungu anali atalonjeza kale kuti adzapereka Dziko Lolonjezedwalo kwa mbewu yake. (Gen. 13:14, 15) Mose yemwe ankaimira Aisiraeli mogwirizana ndi lamulo, anauzidwa kuti ‘aone’ dzikolo. Ngati zomwe akatswiri aja anafotokoza zilidi zoona, ndiye kuti zomwe zinachitika pa nthawiyi zinasonyeza kuti dzikolo linaperekedwa kwa Aisiraeli mogwirizana ndi malamulo. Mose anapereka dzikolo m’manja mwa Yoswa yemwe anamulowa m’malo potsogolera Aisiraeli. (Deut. 3:27, 28; 34:4; yerekezeraninso ndi zomwe anachita Satana pamene ankayesa Yesu pa Mat. 4:8.) Zinanso zomwe zinkachitika ngati njira yovomerezeka mogwirizana ndi malamulo, zinali kuyendera kaye dzikolo m’mbali zake zonse kapenanso kulowamo lisanatengedwe. (Gen. 13:17; 28:13) Pazikalata zina zakale, pankalembedwanso kuchuluka kwa mitengo yomwe inali pamalo omwe ankagulitsidwawo.—Yerekezerani ndi Gen. 23:17, 18.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-2 683 ¶1
Wansembe
Melekizedeki mfumu ya ku Salemu anali wansembe (ko·henʹ) wapadera kwambiri. Baibulo silifotokoza chilichonse chokhudza makolo ake, za nthawi imene anabadwa komanso kufa kwake. Iye sanabadwire m’banja la ansembe komanso unsembe wake sanachite kuulandira kuchokera kwa munthu wina ndiponso sanalowedwe m’malo ndi aliyense. Melekizedeki anali mfumu komanso wansembe. Unsembe wake unali wapamwamba kuposa ansembe a m’banja la Levi, chifukwa mwanjira ina Levi anapereka chakhumi kwa Melekizedeki. Tikutero chifukwa Abulahamu yemwe anali kholo lawo, anapereka chakhumi kwa Melekizedeki ndipo iye anadalitsa Abulahamu. (Gen. 14:18-20; Aheb. 7:4-10) Zimene zinachitika pa moyo wa Melekizedeki zinkachitira chithunzi Yesu Khristu yemwe ndi “wansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melekizedeki.”—Aheb. 7:17.
FEBRUARY 10-16
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 15-17
it-1 817
Zolakwa, Kupezera Ena Zolakwa
Mwanjira ina, zochita za anthu nthawi zambiri zimakhala zolakwika. Anthu onse anatengera uchimo kuchokera kwa Adamu. (Aroma 5:12; Sal. 51:5) Koma Yehova amene salakwitsa kanthu “akudziwa bwino mmene anatiumbira, amakumbukira kuti ndife fumbi” ndipo amatichitira chifundo. (Sal. 103:13, 14) Iye ankaona Nowa, yemwe anali wokhulupirika, kukhala munthu “wopanda cholakwa pakati pa anthu a m’nthawi yake.” (Gen. 6:9) Yehova anauza Abulahamu kuti: “Yenda pamaso panga ndipo ukhale wolungama.” (Gen. 17:1) Ngakhale kuti Nowa komanso Abulahamu sanali angwiro komanso anamwalira, Yehova yemwe “amaona mmene mtima ulili,” anawaona kukhala opanda cholakwa. (1 Sam. 16:7; yerekezerani ndi 2 Maf. 20:3; 2 Mbiri 16:9) Mulungu analamulanso Aisiraeli kuti: “Ukhale wopanda cholakwa pamaso pa Yehova Mulungu wako.” (Deut. 18:13; 2 Sam. 22:24) Iye anapereka Mwana wake yemwe analibe uchimo (Aheb. 7:26) ngati nsembe ya dipo. Pogwiritsa ntchito nsembe imeneyi, Mulungu amatchula anthu omvera komanso omwe ali ndi chikhulupiriro kukhala ‘olungama.’ Zimenezi zimachititsanso kuti Mulungu akhale Woweruza wolungama ndiponso wopanda cholakwa.—Aroma 3:25, 26.
it-1 31 ¶1
Abulahamu
Nthawi inadutsa ndipo tsopano Abulahamu anali atakhala ku Kanani kwa zaka 10. Koma Sara anali asanakhalebe ndi mwana. Kenako anauza mwamuna wake kuti atenge Hagara, kapolo wake wa ku Iguputo kuti amuberekere mwana. Abulahamu anagwirizana ndi maganizowa. Choncho mu 1932 B.C.E., Abulahamu ali ndi zaka 86, Isimaeli anabadwa. (Gen. 16:3, 15, 16) Kenako panadutsanso zaka zambiri. Mu 1919 B.C.E., Abulahamu ali ndi zaka 99, Yehova analamula kuti amuna onse a m’nyumba ya Abulahamu adulidwe monga chizindikiro cha pangano lapadera pakati pa Yehova ndi Abulahamu. Pa nthawiyo Yehova anasinthanso dzina la Abulamu kukhala Abulahamu ponena kuti “chifukwa ndidzakupangitsa kukhala tate wa mitundu yambiri.” (Gen. 17:5, 9-27; Aroma 4:11) Patapita nthawi yochepa, angelo atatu omwe anali ndi matupi ngati a anthu anafika. Abulahamu anawalandira bwino m’dzina la Yehova ndipo angelowo ananena kuti Sara adzakhala ndi pakati ndipo adzabereka mwana wamwamuna m’chaka chotsatira.—Gen. 18:1-15.
Kufufuza Mfundo Zothandiza
it-1 460-461
Nthawi
Yehova anauza Abulamu (Abulahamu) kuti: “Udziwe ndithu kuti mbewu yako idzakhala mlendo m’dziko la eni, ndipo idzatumikira eni dzikolo. Iwo adzasautsa mbewu yako kwa zaka 400.” (Gen. 15:13; onaninso Mac. 7:6, 7.) Mawuwa ananenedwa Isaki yemwe anali wolandira cholowa komanso “mbewu” yalonjezo asanabadwe. Mu 1932 B.C.E., Hagara anabereka Isimaeli ndipo mu 1918 B.C.E., Sara anabereka Isaki. (Gen. 16:16; 21:5) Tikawerengetsera zaka 400 kudzafika pa nthawi yomwe Aisiraeli anamasuka ku ukapolo, (Gen. 15:14) zimatifikitsa m’chaka cha 1913 B.C.E., Isaki ali ndi zaka 5. N’kutheka kuti pa nthawiyi Isaki anali atasiyitsidwa kale kuyamwa komanso atakhala kale “mlendo” m’dziko la eni m’njira yakuti anali atayamba kale kukumana ndi mavuto omwe analoseredwa kale pomwe Isimaeli yemwe anali ndi zaka pafupifupi 19 ‘ankamuseka.’ (Gen. 21:8, 9) Ngakhale kuti zimene Isimaeli ankachita poseka mbewu ya Abulahamu zingaoneke ngati nkhani yaing’ono masiku ano, komabe pa nthawi imeneyo inali nkhani yaikulu kwambiri. Umboni wa zimenezi ukuonekera ndi zimene Sara anachita komanso chifukwa chakuti Mulungu anavomereza maganizo a Sara akuti Hagara ndi mwana wake Isimaeli athamangitsidwe. (Gen. 21:10-13) Chifukwa chakuti nkhaniyi inalembedwa mwatsatanetsatane m’Mawu a Mulungu, zimatithandiza kudziwa nthawi imene ulosi wa zaka 400 wonena za kuzunzidwa kwa anthu a Mulungu unayamba kukwaniritsidwa.—Agal. 4:29.
it-1 778 ¶4
Ulendo wa Aisiraeli Wopita ku Kanani
“M’badwo wachinayi.” Tiyenera kukumbukira kuti Yehova anauza Abulahamu kuti mbadwa zake zidzabwerera ku Kanani mu m’badwo wachinayi. (Gen. 15:16) Pa zaka 430 zomwe pangano la Abulahamu linayamba kugwira ntchito, kudzafika nthawi imene Aisiraeli anayamba ulendo wobwerera kwawo, mibadwo yawo inali itapitirira 4. Zimenezi zinakhaladi choncho ngakhale tikaganizira zimene mbiri imafotokoza kuti anthu a m’nthawi imeneyo ankakhala ndi moyo kwa zaka zambiri. Komabe Aisiraeli anakhala ku Iguputo kwa zaka 215 zokha. Mibadwo 4 yomwe inakhalapo atalowa m’dziko la Iguputo tingaiwerengetsere motere, mwachitsanzo ponena za fuko limodzi lokha la Levi: (1) Levi, (2) Kohati, (3) Amuramu, ndi (4) Mose.—Eks. 6:16, 18, 20.
FEBRUARY 17-23
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 18–19
Kufufuza Mfundo Zothandiza
Kodi Pali Amene Anaonapo Mulungu?
Tsopano tingathe kumvetsa chifukwa chake Abulahamu polankhula ndi mngelo amene anaonekera kwa iye ankalankhula ngati kuti akulankhula ndi Yehova Mulungu mwiniwakeyo. Chifukwa chakuti mngeloyo ankalankhula ndendende zimene Mulungu ankafuna kuuza Abulahamu, komanso chifukwa chakuti ankaimira Mulungu, n’zosadabwitsa kuti Baibulo limanena kuti, “Yehova anaonekera kwa Abulahamu.”—Gen. 18:1.
Muyenera kukumbukira kuti mngelo amene angalankhule m’malo mwa Mulungu angathe kupereka uthenga wochokera kwa Mulungu popanda kusintha uthengawo ngakhale pang’ono ngati mmene zingakhalire ndi uthenga woperekedwa kwa munthu wina pogwiritsa ntchito foni kapena wailesi. Choncho tingathe kumvetsa chifukwa chake Abulahamu, Mose, Manowa komanso anthu ena analankhula ndi angelo ngati kuti ankalankhula ndi Mulungu. Ngakhale kuti ndi zoona kuti anthuwa ankatha kuona angelo amene ankalankhula nawo komanso kuona ulemerero wa Yehova kudzera mwa angelowo, komabe sanathe kuona Mulungu. Zimenezi sizikutsutsana ndi zimene mtumwi Yohane ananena kuti: “Palibe munthu anaonapo Mulungu ndi kale lonse.” (Yoh. 1:18) Anthuwa anangoona angelo omwe ankaimira Mulungu osati Mulunguyo.
FEBRUARY 24–MARCH 1
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 20-21
Abulahamu ndi Chitsanzo Chabwino kwa Onse Ofuna Kukhala Paubwenzi ndi Mulungu
9 Abulahamu anachita zinthu zosonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro. Nkhaniyo imafotokoza kuti: “Iye anamanga pamalopo guwa lansembe la Yehova.” (Gen. 12:7) N’zosakayikitsa kuti pa nthawiyi Abulahamu anapereka nsembe ya nyama. Tikutero chifukwa mawu a Chiheberi akuti “guwa,” amatanthauza “malo operekera nsembe.” Kuchokera pamenepa, Abulahamu anapitiriza kupereka nsembe kwa Yehova kulikonse komwe ankapita. Kuwonjezera pamenepo, iye ‘ankaitana pa dzina la Yehova.’ (Genesis 12:8; 13:18; 21:33) Mawu a Chigiriki akuti “kuitana pa dzina,” angatanthauze “kulengeza (kulalikira) za dzina.” N’zosakayikitsa kuti anthu a m’banja la Abulahamu komanso Akanani ankamva Abulahamu akulengeza molimba mtima za dzina la Mulungu wake, Yehova. (Genesis 14:22-24) Masiku anonso, onse amene akufuna kukhala paubwenzi ndi Mulungu ayenera kuitana pa dzina lake mwachikhulupiriro. Tingachite zimenezi tikamalalikira anthu osiyanasiyana ndipo “nthawi zonse tizitamanda Mulungu. Tizichita zimenezi monga nsembe imene tikupereka kwa Mulungu, yomwe ndi chipatso cha milomo yathu. Timagwiritsa ntchito milomo imeneyi polengeza dzina lake kwa anthu ena.”—Aheb. 13:15; Aroma 10:10.