Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • th phunziro 14 tsamba 17
  • Kuthandiza Anthu Kuti Aone Mfundo Zazikulu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuthandiza Anthu Kuti Aone Mfundo Zazikulu
  • Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Nkhani Yofanana
  • Kuunika Mfundo Zazikulu
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kugogomeza Mutu wa Nkhani ndi Mfundo Zazikulu
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Kukonza Autilaini
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kutambasula Mutu wa Nkhani
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Onani Zambiri
Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
th phunziro 14 tsamba 17

PHUNZIRO 14

Kuthandiza Anthu Kuti Aone Mfundo Zazikulu

Lemba

Aheberi 8:1

MFUNDO YAIKULU: Thandizani anthu kuti azitsatira nkhani yanu komanso aziona kugwirizana pakati pa mfundo zazikulu ndi mutu wa nkhani yonseyo.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Muzikhala ndi cholinga. Muzidzifunsa kuti, Kodi cholinga cha nkhaniyi n’chiyani? Kodi ndi kuphunzitsa, kuthandiza anthu kuti asinthe maganizo kapena kuwalimbikitsa kuchita zinazake? Ndiyeno mfundo zikuluzikulu zizikuthandizani kukwaniritsa cholingacho.

    Mfundo yothandiza

    Muzidzifunsa kuti, ‘Kodi anthu ayenera kuti amadzifunsa mafunso ati, nanga sangagwirizane ndi zinthu ziti pa nkhaniyi? Kodi mafunso kapena mfundo zawozo angazisanje m’njira iti?’ Ndiyeno inuyo musanje mfundo zanu m’njira imeneyo kuti anthu akutsatireni bwino komanso avomereze mfundo zimene mukuphunzitsa.

  • Muzitsindika mutu wa nkhani yanu. Munkhani yanu yonse muzitsindika mutu potchula mawu ofunika kwambiri a m’mutuwo kapena kugwiritsa ntchito mawu ofanana nawo.

  • Muzithandiza anthu kuona mfundo zazikulu m’njira yosavuta. Muzisankha mfundo zikuluzikulu zimene zikugwirizana ndi mutu wa nkhani komanso zimene mungazifotokoze bwino popanda kudya nthawi. Mfundo zikuluzikulu zizikhala zochepa, muzitchula mfundo iliyonse momveka, muzipuma mukamachoka pa mfundo ina kupita pa ina kuti musawasiye anthu m’malere.

    Mfundo yothandiza

    Mungatchule mfundo zikuluzikuluzo m’mawu anu oyamba kuti anthu akutsatireni, kenako mungazitchulenso m’mawu omaliza kuti anthu azikumbukire.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena