NYIMBO 40
Kodi Ndife A Ndani?
Losindikizidwa
1. Iwe ndi wandani?
Umvera m’lungu uti?
Amene umamulambira
Iye ndiye m’lungu wako.
Milungu iwiri
Sungaitumikire.
Sungalambire iwiri yonse
Sankhapo mmodzi yekha.
2. Iwe ndi wandani?
Umvera m’lungu uti?
Zili ndi iweyo kusankha
Woona kaya wonama.
Kodi Kaisara
Udakamukondabe?
Kapena udzamvera Yehova
Ndikumutumikira?
3. Ine ndi wandani?
Ndidzamvera Yehova.
Ndikufuna kusangalatsa
Atate wanga kumwamba.
Anandigulatu.
Ndidzamutumikira.
Ndizimulambira iye yekha
Ndi kumulemekeza.
(Onaninso Yos. 24:15; Sal. 116:14, 18; 2 Tim. 2:19.)