NYIMBO 36
Titeteze Mitima Yathu
Losindikizidwa
1. Titeteze mtima wathu
Tikhale ndi moyo.
M’lungu amadziwa bwino
Za mumtima mwathu.
Mtima ndi wonyenga
Ungamatisocheretse.
Choncho tiganize bwino
Timvere Yehova.
2. Timafunafuna M’lungu
Tikamapemphera.
Timathokozadi zonse
Zomwe amachita.
Zomwe amatiphunzitsa
Timazitsatira
Ndipo tikhulupirike,
Timusangalatse.
3. Titeteze mtima wathu
Tipewe zoipa.
Mawu a Yehova M’lungu
Atitsogolere.
Anthu okhulupirika
Amawakondadi.
Choncho tizimulambira
Monga bwenzi lathu.
(Onaninso Sal. 34:1; Afil. 4:8; 1 Pet. 3:4.)