PHUNZIRO 12
Kulankhula Mwachikondi Komanso Mokoma Mtima
1 Atesalonika 2:7, 8
MFUNDO YAIKULU: Mukamalankhula, anthu aziona kuti mumawaganizira komanso mumawafunira zabwino.
MMENE MUNGACHITIRE:
Muziganizira anthu. Pokonzekera nkhani yanu muziganizira mavuto amene anthu akukumana nawo. Muziganiziranso mmene anthuwo akumvera chifukwa cha mavuto awo.
Muzisankha bwino mawu. Cholinga chanu chizikhala kuwalimbikitsa, kuwatonthoza komanso kuwapatsa mphamvu. Pewani kukhumudwitsa anthu, kudzudzula anthu omwe si Mboni kapena kutsutsa kwambiri mfundo zimene anthu ena amazikhulupirira kwambiri.
Muzisonyeza kuti mumakonda anthu. Mawu komanso nkhope yanu zizisonyeza kuti mumaganizira anthu. Muzikondanso kumwetulira.