Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
SEPTEMBER 6-12
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | DEUTERONOMO 33-34
“Muzithawira ‘M’manja a Yehova Amene Adzakhalapo Mpaka Kalekale’”
it-2 51
Yesuruni
Linali dzina la ulemu la Aisiraeli. M’Baibulo la Chigiriki la Septuagint dzina lakuti “Yesuruni” ndi dzina losonyeza kunyadira winawake ndipo linamasuliridwa kuti “wokondedwa.” Dzina lakuti “Yesuruni” linkakumbutsa Aisiraeli kuti anachita mgwirizano wapadera ndi Yehova, choncho ankafunika kukhalabe olungama. (De 33:5, 26; Yes 44:2) Pa Deuteronomo 32:15 dzina lakuti Yesuruni linagwiritsidwa ntchito pofotokoza zimene Aisiraeli analephera kuchita. M’malo moti Aisiraeli azichita zinthu mogwirizana ndi tanthauzo la dzina lakuti Yesuruni, iwo anakhala anthu osamvera, anakana yemwe anawapanga komanso ananyoza Mpulumutsi wawo.
Mfundo Zothandiza
it-2 439 ¶3
Mose
Mose anamwalira ali ndi zaka 120. Potsimikizira kuti iye anali adakali ndi mphamvu, Baibulo limati: “Diso lake silinachite mdima ndipo anali adakali ndi mphamvu.” Yehova anamuika m’manda pa malo amene sadziwika mpaka pano. (De 34:5-7) N’kutheka kuti zimenezi zinathandiza Aisiraeli kuti asakodwe mumsampha n’kuyamba kulambira konyenga ngati akanati azilambira manda ake. Ndipo zikuoneka kuti zimenezi ndi zomwe Mdyerekezi ankafuna kuchita ndi mtembo wa Mose. Yuda, m’bale wake wa Yesu Khristu, analemba kuti: “Pamene Mikayeli mkulu wa angelo anasemphana maganizo ndi Mdyerekezi ndipo anakangana naye za mtembo wa Mose, sanayese n’komwe kumuweruza ndi mawu onyoza, m’malomwake anati: ‘Yehova akudzudzule.’” (Yuda 9) Aisiraeli asanalowe m’dziko la Kanani motsogoleredwa ndi Yoswa, analira maliro a Mose kwa masiku 30.—De 34:8.
SEPTEMBER 20-26
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOSWA 3-5
“Yehova Amadalitsa Anthu Achikhulupiriro”
it-2 105
Yorodano
Mtsinje wa Yorodano ukatuluka m’nyanja ya Galileya, m’madera ambiri ndi wakuya pakati pa mita imodzi ndi mamita atatu ndipo kuchoka tsidya lina kuwolokera ku tsidya lina ndi waukulu mamita pakati pa 27 ndi 30. Koma m’nyengo ya mvula mtsinjewu umasefukira ndipo umakhala waukulu komanso wakuya kwambiri. (Yos 3:15) Pa nthawi yoti mtsinje wa Yorodano wasefukira zikanakhala zangozi kuti Aisiraeli, omwe analipo amuna, akazi komanso ana, awoloke mtsinjewo makamaka pafupi ndi mzinda wa Yeriko. Pafupi ndi mzindawo madzi amathamanga kwambiri, moti m’zaka zaposachedwapa anthu ena omwe ankasambira anakokoloka. Koma Yehova anachita zodabwitsa pophwetsa mtsinje wa Yorodano, zomwe zinachititsa kuti Aisiraeli awoloke panthaka youma. (Yos 3:14-17) Patapita zaka zambiri Eliya anachitanso chodabwitsa ngati chimenechi ali limodzi ndi Elisa ndipo pa nthawi ina Elisa anachichitanso ali yekha.—2Mf 2:7, 8, 13, 14.
SEPTEMBER 27-OCTOBER 3
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOSWA 6-7
“Musamaone Zinthu Zopanda Pake”
N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuulula Tchimo?
Chifukwa chimodzi chimene tiyenera kuululira tchimo n’chakuti zimathandiza kuti mpingo ukhalebe woyera. Yehova ndi Mulungu woyera. Iye amafuna kuti anthu onse omulambira akhale oyera mwauzimu komanso azikhala ndi makhalidwe abwino. Mawu ake ouziridwa amati: “Monga ana omvera, lekani kukhala motsatira zilakolako zimene munali nazo kale pamene munali osadziwa. Koma khalani motsanzira Woyera amene anakuitanani. Inunso khalani oyera m’makhalidwe anu onse, chifukwa Malemba amati: ‘Mukhale oyera, chifukwa ine ndine woyera.’” (1 Petulo 1:14-16) Anthu amene amachita zonyansa kapena machimo angadetse mpingo wonse, zomwe zingachititse kuti Yehova asamasangalale ndi anthu a mumpingowo. Chomwe chingafunike ndi chakuti anthu oterewa athandizidwe kuti asinthe kapena akhoza kuchotsedwa mumpingomo.—Yerekezerani ndi Yoswa, chaputala 7.
OCTOBER 4-10
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOSWA 8-9
“Zimene Tikuphunzira pa Nkhani ya Agibeoni”
it-1 930-931
Gibeoni
Kuchita Zinthu ndi Yoswa. M’nthawi ya Yoswa mumzinda wa Gibeoni munkakhala Ahivi, womwe unali umodzi mwa mitundu 7 ya Akanani yomwe inkafunika kuwonongedwa. (De 7:1, 2; Yos 9:3-7) Agibeoni ankatchedwanso kuti Aamori, chifukwa zikuoneka kuti dzina limeneli nthawi zina linkagwiritsidwa ntchito ponena za Akanani onse. (2Sa 21:2; yerekezerani ndi Ge 10:15-18; 15:16) Mosiyana ndi Akanani ena, Agibeoni anazindikira kuti ngakhale anali ndi asilikali amphamvu komanso mzinda wawo unali waukulu, sakanatha kulimbana ndi Aisiraeli chifukwa Yehova ankawamenyera nkhondo. Choncho mizinda ya Yeriko ndi Ai itawonongedwa, amuna a ku Gibeoni omwe zikuoneka kuti ankaimiranso anthu a m’mizinda ina itatu ya Ahivi yomwe ndi Kefira, Beeroti, ndi Kiriyati-yearimu (Yos 9:17), anatumiza nthumwi kwa Yoswa ku Giligala kuti akakambirane nawo za mtendere. Akazembe a ku Gibeoniwa anavala zovala zansanza, nsapato zakutha zosokererasokerera, ndipo ananyamula vinyo m’matumba achikopa akutha, omangamanga mong’ambika komanso mkate wouma ndi wofumbutuka. Pofuna kuti Aisiraeli asawawononge, anawauza kuti achokera ku dziko lakutali. Iwo ananena kuti amva zomwe Yehova anachita kwa Aiguputo komanso mafumu a Aamori, omwe ndi Sihoni ndi Ogi. Koma mochenjera, iwo sanatchule zimene zinachitikira mzinda wa Yeriko ndi Ai chifukwa nkhani ya kuwonongedwa kwa mizindayi inali itangochitika kumene moti sikanakhala itafika “kudziko lakutali kwambiri” kumene iwo ankati achokera. Atsogoleri a Isiraeli atayang’anitsitsa zinthuzo, anavomerezadi kuti achokera kutali ndipo anachita nawo pangano kuti asawaphe.—Yos 9:3-15.
Mfundo Zothandiza
it-1 1030
Kupachika
M’chilamulo chimene Yehova anapereka kwa Aisiraeli, anthu ena omwe apalamula milandu ankatha kupachikidwa pamtengo pambuyo poti aphedwa chifukwa anali ‘otembereredwa ndi Mulungu.’ Iwo ankapachikidwa kuti akhale chitsanzo chochenjeza kwa anthu amene ankawaona. Mtembo wa munthu amene wapachikidwa unkayenera kutsitsidwa ndi kuikidwa m’manda tsiku lomwelo, chifukwa kuusiya pamtengopo usiku wonse kukanatha kuipitsa nthaka imene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli. (De 21:22, 23) Aisiraeli ankatsatira lamuloli ngakhale kuti amene waphedwayo sanali Mwisiraeli.—Yos 8:29; 10:26, 27.
OCTOBER 11-17
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOSWA 10-11
“Yehova Anamenyera Nkhondo Aisiraeli”
it-1 50
Adoni-zedeki
Anali mfumu ya Yerusalemu pa nthawi imene Aisiraeli ankakalanda Dziko Lolonjezedwa. Adoni-zedeki anagwirizana ndi maufumu ena akumadzulo kwa Yorodano omwe anachita mgwirizano kuti akamenyane ndi Yoswa ndi gulu lake lankhondo. (Yos 9:1-3) Koma Ahivi omwe ankakhala ku Gibeoni anachita pangano la mtendere ndi Yoswa. Ndiye pofuna kubwezera Agibeoni pa zomwe anachitazi, Adoni-zedeki anaphatikiza gulu lake lankhondo ndi magulu ankhondo a mafumu 4 a Aamori kuti akamenyane ndi Agibeoniwo. Mafumu 5wo ataona mmene Yoswa anapulumutsira Agibeoni m’njira yodabwitsa kwambiri komanso mmene anaphera magulu awo ankhondo omwe anachita mgwirizanowo, anathawira ku Makeda komwe anakabisala kuphanga. Yoswa anapha yekha Adoni-zedeki limodzi ndi mafumu 4 enawo pamaso pa gulu lake lankhondo ndipo anawapachika pamtengo. Kenako mitembo yawo anakaiponya kuphanga konkuja ndipo amenewa anakhala manda awo.—Yos 10:1-27.
it-1 1020
Matalala
Yehova Ankawagwiritsa Ntchito. Nthawi zina, Yehova ankagwiritsa ntchito matalala pokwaniritsa mawu ake komanso kusonyeza mphamvu zake. (Sl 148:1, 8; Yes 30:30) Baibulo limasonyeza kuti nthawi yoyamba pamene matalala anagwa, inali pa mliri wa 7 omwe unagwera Aiguputo, ndipo anawononga zomera, mitengo komanso anapha anthu ndi nyama zomwe zinali kunja, koma sanakhudze Aisiraeli ku Goseni. (Eks 9:18-26; Sl 78:47, 48; 105:32, 33) Kenako, m’Dziko Lolonjezedwa, pamene Aisiraeli motsogoleredwa ndi Yoswa ankathandiza Agibeoni kumenyana ndi mafumu 5 a Aamori amene anachita mgwirizano, Yehova anagwiritsa ntchito matalala akuluakulu pomenyana ndi Aamoriwo. Pa nthawi imeneyi matalala anapha anthu ambiri kuposa amene anaphedwa ndi Aisiraeli.—Yos 10:3-7, 11.
Mfundo Zothandiza
it-1 902-903
Gebala
M’nthawi ya Yoswa, Yehova anaphatikiza “dziko la Agebala” pa mayiko amene Aisiraeli ankafunika kulanda. (Yos 13:1-5) Anthu otsutsa amanena kuti zimenezi ndi zosamvetsetseka chifukwa dziko la Gebala linali kutali kwambiri, kumpoto kwa Isiraeli (c. 100 km [60 mi] kumpoto kwa Dani) ndipo zikuoneka kuti Aisiraeli sanalilandepo. Akatswiri ena amanena kuti n’kutheka kuti Malemba Achiheberi omwe panali vesili anawonongeka, ndipo amaganiza kuti kalelo vesili linkanena kuti “dziko lomwe limafika ku Lebanoni,” kapena kuti ‘mpaka kukafika kumalire a Agebala.’ Komabe, kuti malonjezo a Yehova opezeka pa Yoswa 13:2-7 akwaniritsidwe, ankadalira zimene Aisiraeliwo akanachita. Choncho Aisiraeli sakanalanda dziko la Gebala chifukwa cha kusamvera kwawo.—Yerekezerani ndi Yos 23:12, 13.
OCTOBER 25-31
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOSWA 15-17
“Muziteteza Cholowa Chanu Chomwe Ndi Chamtengo Wapatali”
it-1 1083 ¶3
Heburoni
Pamene ntchito ya Aisiraeli yolanda madera a kummwera kwa Kanani inkapitirira, anthu okhala mumzinda wa Heburoni kuphatikizapo mfumu yawo (mosakayikira inali mfumu yomwe inalowa m’malo mwa Hohamu) anawonongedwa. (Yos 10:36, 37) Koma ngakhale kuti Aisiraeli omwe ankatsogoleredwa ndi Yoswa anagonjetsa Akanani, zikuoneka kuti iwo sanaike mwamsanga asilikali olondera omwe akanathandiza kuti adani awowo asabwererenso. Zikuonekanso kuti pamene Aisiraeli ankamenya nkhondo kwina, Aanaki anabwereranso ku Heburoni komwe ankakhala, zomwe zinapangitsa kuti Kalebe (kapena ana a Yuda omwe ankatsogoleredwa ndi Kalebe) adzamenye nawo nkhondo n’kulandanso mzindawo m’manja mwawo pambuyo pake. (Yos 11:21-23; 14:12-15; 15:13, 14; Owe 1:10) Poyamba mzinda wa Heburoni unaperekedwa kwa Kalebe yemwe anali wa fuko la Yuda, ndipo kenako unapatulidwa kuti ukhale mzinda wothawirako. Unkagwiritsidwanso ntchito ngati mzinda wa ansembe. Komabe, ‘malo ozungulira mzinda wa [Heburoni]’ ndi midzi yake anawapereka kwa Kalebe kuti akhale cholowa chake.—Yos 14:13, 14; 20:7; 21:9-13.
it-1 848
Ntchito Yaukapolo
Kale, “ntchito yaukapolo” (Heb., mas) inali yofala kwambiri chifukwa anthu amene mitundu yawo yagonjetsedwa ankakhala akapolo mwalamulo. (De 20:11; Yos 16:10; 17:13; Est 10:1; Yes 31:8; Mlr 1:1) Aisiraeli omwe ankagwira ntchito yaukapolo yomanga mizinda yosungiramo zinthu ku Pitomu ndi ku Ramese, ankayang’aniridwa ndi akulu a ku Iguputo omwe ankawalamulira mwankhanza. (Eks 1:11-14) Kenako Aisiraeli atatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, m’malo motsatira lamulo la Yehova loti athamangitse Akanani onse omwe ankakhala m’dzikolo komanso kuwawononga, iwo anayamba kuwagwiritsa ntchito yaukapolo. Zimenezi zinabweretsa zotsatirapo zoipa kwa Aisiraeli, chifukwa anakopeka n’kuyamba kulambira milungu yonyenga. (Yos 16:10; Owe 1:28; 2:3, 11, 12) Mfumu Solomo inapitiriza kugwiritsa ntchito yaukapolo mbadwa za Akanani zomwe ndi Aamori, Ahiti, Aperezi, Ahivi, ndi Ayebusi.—1Mf 9:20, 21.
it-1 402 ¶3
Kanani
Ngakhale kuti Akanani ambiri anapulumuka m’manja mwa Aisiraeli ndipo sanagonjetsedwe, tinganenebe kuti “Yehova anapatsa Aisiraeli dziko lonse limene analumbira kuti adzapatsa makolo awo,” komanso anawapatsa “mpumulo pakati pa adani awo onse owazungulira,” ndipo “palibe lonjezo ngakhale limodzi limene silinakwaniritsidwe, pa malonjezo onse abwino amene Yehova analonjeza nyumba ya Isiraeli. Onse anakwaniritsidwa.” (Yos 21:43-45) Adani onse a Aisiraeli omwe anawazungulira ankakhala mwamantha, ndipo Aisiraeliwo sankaopa chilichonse kuchokera kwa adani awowo. Mulungu anali ataneneratu kuti adzathamangitsa Akanani “pang’onopang’ono” kuopera kuti zilombo zakutchire zingachulukane ndi kuwavutitsa. (Eks 23:29, 30; De 7:22) Ngakhale kuti Akanani anali ndi zida zankhondo zamphamvu zomwe zinkaphatikizapo magaleta ankhondo okhala ndi zitsulo zazitali zakuthwa za m’mawilo, silikanakhala vuto la Yehova kuti walephera kukwaniritsa lonjezo lake ngati Aisiraeli akanalephera kulanda madera ena amene ankafunika kulanda. (Yos 17:16-18; Owe 4:13) M’malomwake, Baibulo limasonyeza kuti Aisiraeli analephera kugonjetsa adani awo ena chifukwa cha kusakhulupirika kwawo.—Nu 14:44, 45; Yos 7:1-12.