Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • th phunziro 15 tsamba 18
  • Kulankhula Motsimikiza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulankhula Motsimikiza
  • Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Nkhani Yofanana
  • Kulankhula Motsimikiza
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kulankhula ndi Mtima Wonse
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Kulankhula Mokambirana ndi Anthu
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Nkhani Yophunzitsadi Anthu
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
Onani Zambiri
Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
th phunziro 15 tsamba 18

PHUNZIRO 15

Kulankhula Motsimikiza

Lemba

1 Atesalonika 1:5

MFUNDO YAIKULU: Muzisonyeza kuti mumakhulupirira kwambiri mfundo za choonadi ndipo simukukayikira kuti mfundo zimene mukunena n’zothandiza.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Muzikonzekera bwino. Pokonzekera muzidzifunsa kuti, Kodi mfundo za m’Malemba zingathandize bwanji munthu kufika pozindikira zoona zake pa nkhaniyi? Muzigwiritsa ntchito mawu osavuta pofotokoza mfundo zikuluzikulu. Muziganizira mmene zingathandizire anthu amene mukukambirana nawo. Muzipempha Mulungu kuti akupatseni mzimu woyera.

    Mfundo yothandiza

    Muziyeserera mokweza mawu kuti muizolowere nkhaniyo komanso kuti muzilankhula mosakayikakayika.

  • Muzigwiritsa ntchito mawu osonyeza kutsimikiza. M’malo monena ndendende mmene mawu anawalembera m’mabuku athu, muzigwiritsa ntchito mawu anuanu. Muzigwiritsa ntchito mawu osonyeza kuti simukukayikira zimene mukunena.

  • Muzilankhula mochokera pansi pa mtima komanso mosakayikira. Mawu anu asakwere kwambiri kapena kutsika kwambiri. Ngati n’zololeka kwanuko, muziyang’ana anthu amene mukukambirana nawo.

    Mfundo yothandiza

    Sitikutanthauza kuti muzilankhula mosaganizira anthu, moumirira maganizo anu kapena mokakamiza anthu kuti atsatire zimene mukunena. Ngakhale pamene mukulankhula ndi anthu mosapita m’mbali, muzichita zinthu mwachikondi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena