Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • th phunziro 19 tsamba 22
  • Kuwafika Pamtima Anthu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuwafika Pamtima Anthu
  • Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Nkhani Yofanana
  • Kulankhula ndi Mtima Wonse
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Yesetsani Kuwafika Pamtima Anthu
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Kusonyeza Kuti Nkhaniyo Ndi Yothandiza
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Kulankhula Molimbikitsa
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
Onani Zambiri
Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
th phunziro 19 tsamba 22

PHUNZIRO 19

Kuwafika Pamtima Anthu

Lemba

Miyambo 3:1

MFUNDO YAIKULU: Thandizani anthu kumvetsa zimene mukunena komanso kuzigwiritsa ntchito.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Muzithandiza anthu kuti azidzifufuza. Muzifunsa mafunso othandiza anthu kudzifufuza mumtima.

  • Muzithandiza anthu kukhala ndi zolinga zabwino. Thandizani anthu kudzifufuza kuti adziwe chifukwa chimene amachitira zinthu zabwino. Athandizeni kuti azichita zinthu chifukwa chokonda Yehova, anzawo komanso Mawu a Mulungu. Muzikambirana ndi anthu osati kuwauza zochita. Nkhani yanu ikamatha, anthu azikhala atalimbikitsidwa osati atachititsidwa manyazi. Azifunitsitsa kuchita zonse zimene angathe.

  • Muzithandiza anthu kuganizira za Yehova. Nkhani yanu izithandiza anthu kuona kuti malamulo komanso mfundo za m’Baibulo zimasonyeza makhalidwe a Yehova monga chikondi. Muzithandiza anthu kudziwa kuti zochita zawo zimakhudza Yehova ndipo azifunitsitsa kumusangalatsa.

    Mfundo yothandiza

    Kumbukirani kuti Yehova ndi amene amakoka anthu. Choncho muzigwiritsa ntchito Mawu ake polimbikitsa anthu.

MU UTUMIKI

Ngati n’zotheka, muzifunsa mafunso kuti mudziwe zimene munthu amakhulupirira. Muzimuyang’ana nkhope komanso kumva mmene akulankhulira kuti muzindikire zimene zili mumtima mwake. Koma muzikhala oleza mtima. Nthawi zina zimatenga nthawi kuti munthu ayambe kukukhulupirirani n’kufotokoza zimene zili mumtima mwake.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena