Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr23 January tsamba 1-13
  • Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Timitu
  • JANUARY 2-8
  • w05 8/1 12 ¶1
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
mwbr23 January tsamba 1-13

Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

JANUARY 2-8

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MAFUMU 22-23

“N’chifukwa Chiyani Kudzichepetsa N’kwabwino?”

w00 9/15 29-30

Yosiya Wodzichepetsayo Anayanjidwa Ndi Yehova

Kuchokera m’mamawa, okonza kachisi amenewa akugwira ntchito mwakhama. Ndithudi Yosiya akuthokoza Yehova kuti ogwira ntchito akukonza mbali za nyumba ya Mulungu zimene makolo ake ena oipa anawononga. Ntchito ili m’kati, Safani akubwera kudzamuuza zina zake. Nanga chimene wanyamulacho n’chiyani? Wanyamula mpukutu! Akufotokoza kuti Hilikiya Mkulu wa Ansembe wapeza “buku la chilamulo la Yehova mwa dzanja la Mose.” (2 Mbiri 34:12-18) Limene anapezalo mosakayikira linali buku lenileni la Chilamulo.

Yosiya akufunitsitsa kumva mawu onse a bukulo. Pamene Safani akuwerenga, mfumuyo ikuyesetsa kuona mmene lamulo lililonse likugwirira ntchito kwa iye ndi kwa anthu ake. Makamaka akukondwera ndi mmene bukulo likufotokozera kwambiri za kulambira koona ndi kuneneratu za miliri ndi kuchotsedwa m’dziko zimene zingadze ngati anthu adzilowetsa m’chipembedzo chonyenga. Podziwa tsopano kuti malamulo ena a Mulungu sanatsatiridwe, Yosiya akung’amba chovala chake nalamula Hilikiya, Safani, ndi ena kuti: ‘Funsirani kwa Yehova za mawu a buku ili; pakuti mkwiyo wa Yehova wotiyakira ife ndi waukulu; popeza atate athu sanamvera mawu a buku ili.’​—2 Mafumu 22:11-13; 2 Mbiri 34:19-21.

w00 9/15 30 ¶2

Yosiya Wodzichepetsayo Anayanjidwa Ndi Yehova

Amithenga a Yosiya apita kwa Hulida mneneri wamkazi ku Yerusalemu ndipo abwerako ndi mawu. Hulida wawauza mawu a Yehova, kunena kuti masoka amene analembedwa m’buku limene langopezedwa kumenelo adzagweradi mtundu wopandukawo. Komabe, chifukwa cha kudzichepetsa kwake pamaso pa Yehova Mulungu, Yosiya sadzaona masokawo. Adzam’sonkhanitsa kukhala ndi makolo ake ndipo adzatengedwa alowe m’manda mwake mwamtendere.​—2 Mafumu 22:14-20; 2 Mbiri 34:22-28.

Mfundo Zothandiza

w01 4/15 26 ¶3-4

Mungachite Moyenera Ngakhale Sanakulereni Bwino

Ngakhale kuti panachitika zoipa panthawi ya ubwana wake, Yosiya anachita zoyenera pamaso pa Yehova. Ulamuliro wake unali wopambana ndipo Baibulo limati: “Asanabadwe iye panalibe mfumu [y]olingana naye, imene inatembenukira kwa Yehova ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse, ndi mphamvu yake yonse, monga mwa chilamulo chonse cha Mose; atafa iyeyu sanaukanso wina wolingana naye.”​—2 Mafumu 23:19-25.

Zimene Yosiya anachita n’chitsanzo cholimbikitsa kwa amene anakumana ndi zoipa paubwana wawo. Kodi chitsanzo chimenechi chingatiphunzitse chiyani? N’chiyani chinathandiza Yosiya kusankha njira yoyenera ndi kupitirizabe kuitsatira?

JANUARY 9-15

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 MAFUMU 24-25

“Musamaiwale Kuti Muli mu Nthawi Yamapeto”

w01 2/15 12 ¶2

Tsiku la Yehova Lopereka Chiweruzo Layandikira!

2 Mosakayikira, kulosera kwa Zefaniya kunachititsa Yosiya wachinyamatayo kuzindikira kwambiri za kufunika kochotsa kulambira konyansa m’dziko la Yuda. Komabe, zimene mfumu inachita poyesetsa kufafaniza chipembedzo chonyenga m’dzikolo sizinathetse kuipa konse pakati pa anthuwo kapena kufafaniza machimo a agogo ake aamuna, Mfumu Manase, amene “anadzaza Yerusalemu ndi mwazi wosachimwa.” (2 Mafumu 24:3, 4; 2 Mbiri 34:3) Chotero, tsiku la Yehova lopereka chiweruzo linali kudzafika ndithu.

w07 3/15 11 ¶10

Mfundo Zazikulu za M’buku la Yeremiya

Chaka cha 607 B.C.E., chinali chaka cha 11 mu ulamuliro wa mfumu Zedekiya. Ndipo mfumu ya ku Babulo, Nebukadinezara inali itazinga Yerusalemu kwa miyezi 18 tsopano. Patsiku la 7 la mwezi wachisanu, m’chaka cha 19 cha ulamuliro wa Nebukadinezara, mkulu wa asilikali oteteza mfumu dzina lake Nebuzaradani, “anadza,” kapena kuti anafika ku Yerusalemu. (2 Mafumu 25:8) Mwina Nebuzaradani ankachokera ku misasa imene anamanga kunja kwa mpanda wa Yerusalemu, n’kumakazonda mzindawo kuti adziwe mmene angaugonjetsere. Patangopita masiku atatu okha, patsiku la khumi la mweziwu, Nebuzaradani “anadza,” kapena kuti analowa mu Yerusalemu, ndipo anatentha mzindawu ndi moto.​—Yeremiya 52:12, 13.

Mfundo Zothandiza

w05 8/1 12 ¶1

Mfundo Zazikulu za M’buku la Mafumu Wachiwiri

24:3, 4. Chifukwa choti Manase anali ndi mlandu wopha anthu, Yehova “sanafuna kukhululukira” Yuda. Mulungu amaona kuti mwazi wa anthu osalakwa n’ngofunika. Tisamakayikire m’pang’ono pomwe kuti Yehova adzabwezera anthu okhetsa mwazi wosalakwa powawononga.​—Salmo 37:9-11; 145:20.

JANUARY 16-22

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MBIRI 1-3

“Baibulo Ndi Buku Limene Limanena Zoona”

w09 9/1 14 ¶1

Kodi Adamu ndi Hava Anali Anthu Enieni?

Mwachitsanzo, onani ndandanda ya makolo achiyuda otchulidwa m’Baibulo m’buku la 1 Mbiri chaputala 1 mpaka 9, ndiponso Uthenga Wabwino wa Luka chaputala 3. Buku la 1 Mbiri limatchula mwatsatanetsatane makolo a mibadwo 48 ndipo Luka amatchula makolo a mibadwo 75. Buku la Luka limatchula m’badwo wa makolo a Yesu Khristu, pomwe buku la 1 Mbiri limatchula mibadwo ya ansembe a mtundu wa Isiraeli. Mabuku onsewa amatchula maina a anthu odziwika bwino monga Solomo, Davide, Yakobo, Isake, Abulahamu ndi Nowa ndipo pomalizira pake amatchula Adamu. Maina onse a m’mabuku amenewa ndi a anthu enieni, ndipo Adamu anali munthu weniweni pa m’ndandanda uliwonse.

w08 6/1 3 ¶4

Chigumula cha Nowa Chinachitikadi Kapena Ndi Nthano?

Nkhani ziwiri za m’Baibulo zotchula mzera wobadwira wa anthu, zimasonyeza kuti Nowa anali munthu weniweni. (1 Mbiri 1:4; Luka 3:36) Ezara ndi Luka, amene analemba nkhani zimenezi anali anthu odziwa kufufuza bwino nkhani. Luka anafufuza ndi kupeza kuti Nowa anali m’gulu la makolo a Yesu Khristu.

w09 9/1 14-15

Kodi Adamu ndi Hava Anali Anthu Enieni?

Mwachitsanzo, taonani nkhani ya m’Baibulo yokhudza dipo imene anthu ambiri opemphera amaona kuti ndi yofunika kwambiri. Mawu akuti dipo amatanthauza kuti Yesu Khristu anapereka moyo wake wangwiro monga nsembe yopulumutsa anthu ku uchimo. (Mateyo 20:28; Yohane 3:16) Monga tikudziwira, dipo ndi mtengo wokwanira kuwombolera kapena kugulanso chinthu chomwe chinatayika kapena kuwonongedwa. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti Yesu ndi ‘dipo lolingana.’ (1 Timoteyo 2:6) Koma tingafunse kuti, kodi ndi dipo lolingana ndi chiyani? Baibulo limayankha kuti: “Pakuti monga mwa Adamu onse akufa, momwemonso mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo.” (1 Akorinto 15:22) Moyo wangwiro umene Yesu anapereka kuti awombole anthu omvera unali wolingana ndi moyo wangwiro umene Adamu anataya pamene anachimwa m’munda wa Edene. (Aroma 5:12) Ndithudi, ngati Adamu sanali munthu weniweni, ndiye kuti nsembe ya dipo imene Khristu anapereka ikanakhala yopanda tanthauzo.

Mfundo Zothandiza

it-1 911 ¶3-4

Mzere wa Mibadwo ya Makolo

Mayina a Akazi. Nthawi zina akazi ankatchulidwa m’Baibulo ngati akufuna kuti asonyeze mbiri ya anthu pa nthawi inayake. Zimaoneka kuti Sarai (Sara) anatchulidwa pa Genesis 11:29, 30, chifukwa chakuti Mbewu yolonjezedwa inali kudzachokera mwa iyeyo, osati mwa mkazi wina wa Abulahamu. Milika ayenera kuti anatchulidwa pa vesili chifukwa chakuti anali agogo ake a Rabeka yemwe anali mkazi wa Isaki, zomwe zinasonyeza kuti Rabeka anali mumzera wa achibale ake a Abulahamu, chifukwa paja Isaki sankayenera kukwatira mkazi yemwe anali wa mtundu wina. (Ge 22:20-23; 24:2-4) Pa Genesis 25:1, anatchulapo za mkazi wina wa Abulahamu dzina lake Ketura. Zimenezi zikusonyeza kuti Sara atamwalira, Abulahamu anakwatiranso ndipo anali adakali ndi mphamvu zoti akhoza kubereka ngakhale kuti pa nthawiyi panali patadutsa zaka zoposa 40 kuchokera pomwe Yehova anamupatsanso mphamvuzi. (Aro 4:19; Ge 24:67; 25:20) Zinasonyezanso ubale umene unalipo pakati pa Aisiraeli ndi Amidiyani komanso mafuko ena a Aluya.

Leya, Rakele komanso adzakazi a Yakobo anatchulidwa limodzi ndi ana awo. (Ge 35:21-26) Zimenezi zimatithandiza kumvetsa mmene Mulungu anachitira zinthu ndi anawa patapita nthawi. Akazi enanso anatchulidwa m’Baibulo pa zifukwa zofananazi. Iwo ankatchulidwa mayina ngati anali oyenera kulandira cholowa. (Nu 26:33) Komabe Tamara, Rahabi, ndi Rute anali apadera. Akazi onsewa anachita chinachake chapadera chimene chinachititsa kuti akhale mumzere umene Mesiya, Yesu Khristu anabadwira. (Ge 38; Ru 1:3-5; 4:13-15; Mt 1:1-5) Malemba ena amene amatchula mayina a akazi m’Baibulo ndi 1Mbiri 2:35, 48, 49; 3:1-3, 5.

JANUARY 23-29

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MBIRI 4-6

“Kodi Mapemphero Anga Amasonyeza Kuti Ndine Wotani?”

w10 10/1 23 ¶3-7

“Wakumva Pemphero”

Yabezi anali munthu wokonda kupemphera. Iye anayamba pemphero lake ndi kupempha madalitso kwa Mulungu. Kenako anapempha zinthu zitatu zimene zikusonyeza kuti iye anali ndi chikhulupiriro cholimba.

Poyamba, Yabezi anapempha Mulungu kuti: ‘Mukulitse dziko langa.’ (Vesi 10) Munthu wolemekezekayu sankalanda malo a anthu kapena kusirira zinthu za eni. N’kutheka kuti iye ankaganizira za anthu osati malo. Mwina ankapempha kuti dera lake likule mwamtendere n’cholinga choti mukhale anthu ambiri olambira Mulungu woona.

Chachiwiri, Yabezi anapempha kuti “dzanja” la Mulungu likhale naye. Mawu ophiphiritsa akuti dzanja la Mulungu amatanthauza mphamvu zimene Mulungu amagwiritsa ntchito pothandiza anthu amene amamulambira. (1 Mbiri 29:12) Kuti alandire zimene anapempha kuchokera pansi pa mtima, Yabezi anadalira Mulungu yemwe dzanja lake silifupika kwa anthu amene amamukhulupirira.​—Yesaya 59:1.

Chachitatu, Yabezi anapemphera kuti: ‘Munditeteze ku tsoka, kuti lisandivulaze.’ Mawu akuti, ‘kuti lisandivulaze’ akusonyeza kuti Yabezi sanapemphe kuti asakumane ndi tsoka koma kuti asade nkhawa kwambiri ndi tsokalo kapena kugonja pokumana ndi zoipa.

Pemphero la Yabezi limasonyeza kuti iye ankaganizira kwambiri za kulambira koona ndipo ankakhulupirira ndi kudalira Wakumva pemphero. Kodi Yehova anamuyankha bwanji? Nkhani yachiduleyi imatha ndi mawu akuti: “Choncho Mulungu anakwaniritsa zimene iye anapempha.”

Mfundo Zothandiza

w05 10/1 9 ¶7

Mfundo Zazikulu za M’buku Loyamba la Mbiri

5:10, 18-22. M’masiku a Mfumu Sauli, mafuko amene anali kum’mawa kwa Yordano anagonjetsa Ahagiri ngakhale kuti chiwerengero cha Ahagiri chinali chochuluka kuwirikiza kawiri pochiyerekeza ndi cha mafukowa. Izi zinali choncho chifukwa chakuti amuna amphamvu a mafuko amenewa anadalira Yehova kuwathandiza. Tiyeni tidalire Yehova ndi mtima wonse pamene tikupitiriza kumenya nkhondo yauzimu ndi adani omwe ali ochuluka kutiposa.​—Aefeso 6:10-17.

JANUARY 30–FEBRUARY 5

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MBIRI 7-9

“Yehova Angakuthandizeni Kuti Mukwanitse Kuchita Utumiki Wovuta”

w05 10/1 9 ¶8

Mfundo Zazikulu za M’buku Loyamba la Mbiri

9:26, 27. Alevi oyang’anira zipata anali ndi udindo wofunika kwambiri. Iwo anapatsidwa makiyi otsegulira malo opatulika osiyanasiyana a pakachisi. Anali okhulupirika potsegula zipata tsiku lililonse. Tapatsidwa udindo wofikira anthu m’gawo lathu ndi kuwathandiza kuyamba kupembedza Yehova. Kodi sitiyenera kukhala odalirika ndi okhulupirika monga mmene Alevi oyang’anira zipata anachitira?

w11 9/15 32 ¶7

Khalani Olimba Mtima Ngati Pinihasi

Pinihasi anali ndi udindo waukulu mu Isiraeli wakale koma anathana ndi mavuto bwinobwino chifukwa cha kulimba mtima, kumvetsa zinthu ndiponso kudalira Mulungu. Komanso zimene Pinihasi anachita posamalira mpingo wa Mulungu zinasangalatsa kwambiri Yehova. Patapita zaka 1,000, Ezara anauziridwa kulemba kuti: “Pinihasi mwana wa Eleazara ndiye anali mtsogoleri wawo kalekale, ndipo Yehova anali naye.” (1 Mbiri 9:20) Mawu amenewa ayeneranso kugwira ntchito kwa amene amatsogolera anthu a Mulungu masiku ano komanso Akhristu onse amene amatumikira Mulungu mokhulupirika.

Mfundo Zothandiza

w10 12/15 21 ¶6

Imbirani Yehova

6 Kudzera mwa aneneri ake, Yehova analamula kuti anthu amene amamulambira azimutamanda ndi nyimbo. Anthu oimba nyimbo ochokera m’fuko la ansembe sankaloledwa kugwira ntchito zina zimene Alevi ena ankagwira n’cholinga choti akhale ndi nthawi yokwanira yokonza nyimbo n’kuyesa kuziimba.​—1 Mbiri 9:33.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

w21.06 3-4 ¶3-8

Muzithandiza Ophunzira Baibulo Kuti Abatizidwe

3 Wophunzira Baibulo asanabatizidwe, ayenera kumagwiritsa ntchito zimene amaphunzira. (Werengani Mateyu 28:19, 20.) Akamachita zimenezi angafanane ndi “munthu wochenjera” wa m’fanizo la Yesu, yemwe anakumba kwambiri pansi kuti amange nyumba yake pathanthwe. (Mat. 7:24, 25; Luka 6:47, 48) Ndiye kodi tingathandize bwanji wophunzira Baibulo kuti azigwiritsa ntchito zimene akuphunzira. Tiyeni tikambirane zinthu zitatu zimene tingachite.

4 Muzithandiza wophunzira wanu kuti azikhala ndi zolinga. N’chifukwa chiyani muyenera kuchita zimenezi? Taganizirani izi: Ngati mukuyenda pa ulendo wautali, mumatha kuima pamalo ena osangalatsa kuti mupume. Zimenezo zingakuthandizeni kuti musaone kutalika ulendowo. Mofanana ndi zimenezi, wophunzira Baibulo akamakhala ndi zolinga zing’onozing’ono n’kumazikwaniritsa angazindikire kuti akhoza kukwaniritsa cholinga chake chofuna kubatizidwa. Mungagwiritse ntchito tizigawo takuti “Zolinga” m’buku lakuti, Mungakhale ndi Moyo Mpaka Kalekale pothandiza wophunzira wanu. Pa mapeto pa phunziro lililonse, muzikambirana ndi wophunzirayo kugwirizana kumene kulipo pakati pa zolinga zimene zatchulidwa ndi zimene waphunzira. Ngati mukuganizira zolinga zina zimene mukufuna wophunzira wanu azikwaniritse, mungalembe pa kagawo kakuti “Zina.” Nthawi zambiri muzigwiritsa ntchito kagawo kameneka pokambirana ndi wophunzira wanu zolinga zimene angazikwaniritse kwa nthawi yochepa kapena kwa nthawi yaitali

5 Muzithandiza wophunzira wanu kusintha zinthu pa moyo wake. (Werengani Maliko 10:17-22.) Yesu ankadziwa kuti zikanakhala zovuta kuti munthu wina wolemera agulitse zinthu zake zonse. (Maliko 10:23) Komabe iye anamuuza kuti achite zimenezi ngakhale kuti kunali kusintha kwakukulu pa moyo wake. Yesu anamuuza izi chifukwa ankamukonda kwambiri. Nthawi zina tingalephere kulimbikitsa wophunzira wathu kuti asinthe zinthu zina pa moyo wake poganiza kuti sanakonzeke kuchita zimenezi. Zingatenge nthawi yaitali kuti anthu ena asiye zimene anazolowera n’kuvala umunthu watsopano. (Akol. 3:9, 10) Koma mukakambirana naye mofulumira zinthu zimene afunika kusintha, wophunzirayo amayambanso kusintha mofulumira. Mukamakambirana naye nkhani ngati zimenezi mumasonyeza kuti mumamuganizira.​—Sal. 141:5; Miy. 27:17.

6 N’zofunika kuti tizifunsa wophunzira wathu mafunso omuthandiza kufotokoza maganizo ake pa nkhani inayake. Muzifunsa mafunso oterewa kuti muzidziwa zimene wophunzira wanu amadziwa komanso kukhulupirira. Mukamachita zimenezi kawirikawiri zidzakhala zosavuta kuti m’tsogolo mudzathe kukambirana naye nkhani zimene n’zovuta kuti azivomereze. Mu buku la Mungakhale ndi Moyo Mpaka Kalekale, muli mafunso ambiri angati amenewa. Mwachitsanzo, m’phunziro 04 muli funso lakuti: “Ndiye mukuona kuti Yehova amamva bwanji mukamagwiritsa ntchito dzina lake?” M’phunziro 09 muli funso lakuti: “Tchulani zinthu zina zimene mungakonde kupempherera.” Poyamba wophunzira wanu angamatenge nthawi yaitali kuti ayankhe mafunso amenewa. Mungamuthandize kuti aziganiza pogwiritsa ntchito zithunzi komanso Malemba.

7 Wophunzira wanu akamvetsa zimene ayenera kuchita, muzigwiritsa ntchito nkhani zofotokoza zimene zinachitikira anthu ena pomulimbikitsa kuti azichita zimene waphunzira. Mwachitsanzo, ngati wophunzira wanu zimamuvuta kupezeka pamisonkhano mungamuonetse vidiyo yakuti Yehova Anandisamalira, yomwe ili pa kagawo kakuti “Onani Zinanso,” muphunziro 14. M’mitu yambiri m’buku lakuti Mungakhale ndi Moyo Mpaka Kalekale, mungapeze zitsanzo za zimene zinachitikira anthu ena pa kagawo kakuti “Fufuzani Mozama,” komanso kakuti “Onani Zinanso.” Muzisamala kuti musamayerekezere wophunzira wanu ndi anthu ena pomuuza kuti, “Ngati uyu anakwanitsa ndiye kuti inunso mungakwanitse.” Muzilola wophunzira wanu kuti aziona yekha zimenezo. Inuyo muzingokambirana naye mfundo zimene zinathandiza munthu amene watchulidwa muvidiyoyo. Mwina mungatchule lemba kapena zinthu zina zimene zinamuthandiza. Ndipo ngati n’zotheka muzifotokoza mmene Yehova anathandizira munthuyo.

8 Muzithandiza wophunzira wanu kuti ayambe kukonda Yehova. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Mukamaphunzira naye muziyesetsa kupeza mipata yomuthandiza kudziwa makhalidwe a Yehova. Muzimuthandiza kuona kuti Yehova ndi Mulungu wachimwemwe amene amathandiza anthu omwe amamukonda. (1 Tim. 1:11; Aheb. 11:6) Muzimufotokozera kuti zinthu zingamuyendere bwino kwambiri akamagwiritsa ntchito zimene akuphunzirazo, ndipo muzimuuza kuti umenewo ndi umboni woti Yehova amamukonda. (Yes. 48:17, 18) Wophunzirayo akamakonda kwambiri Yehova m’pamene angathe kusintha zinthu pa moyo wake.​—1 Yoh. 5:3.

FEBRUARY 6-12

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MBIRI 10-12

“Muzikhala Wofunitsitsa Kuchita Zimene Mulungu Amafuna”

w12 11/15 6 ¶12-13

“Ndiphunzitseni Kuchita Chifuniro Chanu”

12 Davide anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani yofunitsitsa kutsatira mfundo za m’Chilamulo. Mwachitsanzo, taganizirani zimene zinachitika Davide atanena kuti ankafunitsitsa kumwa “madzi a m’chitsime cha ku Betelehemu.” Asilikali atatu a Davide anakalowa mwamphamvu mumzindawo, womwe pa nthawiyo unali utalandidwa ndi Afilisiti. Iwo anakatunga madzi m’chitsimecho n’kubwera nawo. Koma “Davide anakana kumwa madziwo. M’malomwake anawapereka kwa Yehova mwa kuwathira pansi.” N’chifukwa chiyani sanamwe? Iye anafotokoza kuti: “Sindingachite zimenezo chifukwa ndimalemekeza Mulungu wanga. Kodi ndimwe magazi a anthuwa omwe anaika moyo wawo pachiswe? Iwowa akanataya moyo wawo pokatunga madziwa.”​—1 Mbiri 11:15-19.

13 Davide anadziwa kuti Chilamulo chimanena kuti magazi sayenera kudyedwa koma kuperekedwa kwa Yehova. Iye ankadziwa kuti “moyo wa nyama [kapena munthu] uli m’magazi.” Komatu Davide anakana madzi osati magazi. Ndiye anakaniranji? Iye anakana chifukwa ankadziwa mfundo ya m’lamulolo. Davide ankaona kuti madziwo anali amtengo wapatali ngati magazi a amuna atatuwa. Choncho ankaona kuti n’kulakwa kwambiri kumwa madziwo. Chotero sanamwe koma anawathira pansi.​—Lev. 17:11; Deut. 12:23, 24.

w18.06 17 ¶5-6

Muziphunzitsa Chikumbumtima Chanu ndi Malamulo Komanso Mfundo za Mulungu

5 Kuti malamulo a Mulungu azitithandiza, tiyenera kuchita zambiri osati kungowawerenga n’kuwadziwa. Tiziwakonda kwambiri komanso kuwalemekeza. Paja Mawu a Mulungu amati: “Danani ndi choipa ndipo muzikonda chabwino.” (Amosi 5:15) Koma kodi tingachite bwanji zimenezi? Chofunika ndi kuona zinthu mmene Yehova amazionera. Tiyerekeze kuti muli ndi vuto losowa tulo. Kenako dokotala akukuuzani kuti muzichita masewera olimbitsa thupi, muzidya zakudya zabwino komanso musinthe zinthu zina pa moyo wanu. Ndiyeno mutatsatira malangizowo mukuona kuti mwayamba kupeza tulo bwinobwino. Mukhoza kuthokoza kwambiri dokotalayo chifukwa chokuthandizani.

6 Nayenso Mlengi wathu watipatsa malamulo otithandiza kuti tikhale ndi moyo wabwino komanso tisamakumane ndi mavuto chifukwa cha uchimo. Tangoganizirani mmene timapindulira tikamatsatira malamulo a m’Baibulo pa nkhani ya kunama, chiwembu, kuba, chiwerewere, chiwawa ndiponso kuchita zamizimu. (Werengani Miyambo 6:16-19; Chiv. 21:8) Tikazindikira ubwino woyenda m’njira za Yehova, timayamba kumukonda kwambiri komanso kukonda malamulo ake.

Mfundo Zothandiza

it-1 1058 ¶5-6

Mtima

Kutumikira Ndi “Mtima Wonse.” Mtima weniweni umafunika kukhala wathunthu kuti uzigwira bwino ntchito, koma mtima wophiphiritsa ukhoza kukhala wogawanika. Davide anapemphera kuti: “Ndipatseni mtima wosagawanika kuti ndiope dzina lanu,” kusonyeza kuti mtima wa munthu ukhoza kukhala wogawanika chifukwa cha zimene umakonda komanso kuopa. (Sl 86:11) Munthu wotereyu akhoza kukhala ndi ‘mitima iwiri’ kapenanso kukhala wofunda polambira Mulungu. (Sl 119:113; Chv 3:16) Akhoza kumatumikira ambuye awiri kapena mwachinyengo kumanena zinthu zina pomwe akuganiza zinthu zina. (1Mb 12:33; Sl 12:2) Yesu anadzudzula mwamphamvu anthu achinyengo omwe amakhala ndi mitima iwiri.​—Mt 15:7, 8.

Munthu amene akufuna kusangalatsa Mulungu sayenera kukhala ndi mtima wogawanika kapena kuti mitima iwiri koma ayenera kumutumikira ndi mtima wonse. (1Mb 28:9) Zimenezitu zimafuna khama chifukwa mtima ndi wonyenga ndipo umafunitsitsa kuchita zoipa. (Yer 17:9, 10; Ge 8:21) Zinthu zimene zingatithandize kuti tizitumikira ndi mtima wonse ndi: kupemphera mochokera pansi pamtima (Sl 119:145; Mlr 3:41), kuphunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse (Eza 7:10; Miy 15:28), kugwira nawo mwakhama ntchito yolalikira uthenga wabwino (yerekezerani ndi Yer 20:9), komanso kuchita zinthu ndi anthu amene amatumikira Yehova ndi mtima wonse.​—Yerekezerani ndi 2Mf 10:15, 16.

FEBRUARY 13-19

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MBIRI 13-16

“Zinthu Zimatiyendera Bwino Tikamatsatira Malangizo”

w03 5/1 10-11

Kodi Mumafunsa Kuti, “Ali Kuti Yehova?”

12 Likasa la chipangano litabwerera ku Israyeli ndipo litakhala zaka zambiri ku Kiriyati-Yearimu, Mfumu Davide inafuna kusamutsira Likasalo ku Yerusalemu. Anakambirana ndi akulu amene anali kutsogolera anthu ndipo anawauza kuti Likasa lisamutsidwa ‘chikakomera iwo, ndipo chikachokera kwa Yehova.’ Koma sanafufuze mokwanira kuti adziwe maganizo a Yehova pankhaniyi. Akanakhala kuti anachita zimenezo, sibwenzi atanyamulira Likasalo pa galeta. Alevi Achikohati ndi amene akananyamula pa mapewa pawo, monga momwe Mulungu analangizira momveka bwino. Ngakhale kuti Davide nthawi zonse ankafunsira kwa Yehova, analephera kuchita zimenezo moyenera panthawi imeneyi. Zotsatira zake zinali zomvetsa chisoni zedi. Patapita nthawi Davide anavomereza kuti: “Yehova Mulungu wathu anachita chotipasula, popeza sitinam’funafuna Iye monga mwa chiweruzo.”​—1 Mbiri 13:1-3; 15:11-13; Numeri 4:4-6, 15; 7:1-9.

w03 5/1 11 ¶13

Kodi Mumafunsa Kuti, “Ali Kuti Yehova?”

13 Tsopano Alevi atasamutsa Likasa ku Obedi-Edomu kupita nalo ku Yerusalemu, anthu anaimba nyimbo imene Davide analemba. Ena mwa mawu a m’nyimboyo anali mawu ochokera pansi pamtima owakumbutsa, akuti: “Funsirani kwa Yehova ndi mphamvu yake; funani nkhope yake nthawi zonse. Kumbukirani zodabwiza zake adazichita, zizindikiro zake, ndi maweruzo a pakamwa pake.”​—1 Mbiri 16:11, 12.

Mfundo Zothandiza

w14 1/15 10 ¶14

Lambirani Yehova, Mfumu Yamuyaya

14 Davide anabweretsa ku Yerusalemu likasa la pangano lomwe linali lopatulika. Pa nthawiyi anthu anasangalala kwambiri ndipo Alevi anaimba nyimbo yotamanda Mulungu. M’nyimboyo munali mawu amene ali pa 1 Mbiri 16:31 akuti: “Anene pakati pa anthu a mitundu ina kuti: ‘Yehova wakhala mfumu!’” Apatu ena angadabwe kuti, ‘Popeza Yehova ndi Mfumu yamuyaya, zikutheka bwanji kuti anakhala Mfumu pa nthawiyo?’ Yehova amakhala Mfumu akachita zinthu zosonyeza kuti iye ndi amene akulamulira kapena akasankha wina kuti amuimire pa nthawi inayake kapena pothana ndi vuto linalake. Mfundo imeneyi ingatithandize kumvetsa mfundo zina zokhudza ulamuliro wake. Davide asanamwalire, Yehova anamulonjeza kuti ufumu wake sudzatha. Ananena kuti: “Ndidzautsa mbewu yako yobwera pambuyo pako, imene idzatuluka m’chiuno mwako. Ndipo ndidzakhazikitsadi ufumu wake.” (2 Sam. 7:12, 13) Ndiyeno mawuwa anadzakwaniritsidwa patadutsa zaka zoposa 1,000. Kodi ndani anadzakhala “mbewu” yolonjezedwayo, nanga anayamba liti kulamulira?

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

w16.01 13-14 ¶7-10

Tiziyamikira ‘Mphatso Yaulere’ Imene Mulungu Anatipatsa

7 Choyamba, tiyenera kuchita zinthu zimene mtumwi Paulo ananena. Iye anati “chikondi chimene Khristu ali nacho chimatikakamiza” kuchita zimene Khristuyo angasangalale nazo. (Werengani 2 Akorinto 5:14, 15.) Paulo ankadziwa kuti munthu akamayamikira chikondi chimene Yesu anasonyeza, amayamba kukonda kwambiri Yesuyo. Tikamaganizira ndi kumvetsa bwino zimene Yehova anatichitira, timayamikira kwambiri chikondi chake. Komanso timafunitsitsa kukhala ndi moyo wogwirizana ndi zimene Yesu amafuna. Koma kodi tingasonyeze bwanji zimenezi?

8 Popeza timakonda Yehova, timayesetsa kutsatira chitsanzo cha Yesu mosamala kwambiri komanso kuchita zimene Mulungu ndi Khristu amafuna. (1 Pet. 2:21; 1 Yoh. 2:6) Yesu anati: “Amene ali ndi malamulo anga ndipo amawasunga, ameneyo ndiye amene amandikonda. Komanso wondikonda ine, Atate wanga adzamukondanso. Inenso ndidzamukonda ndipo ndidzadzionetsera bwinobwino kwa iye.”​—Yoh. 14:21; 1 Yoh. 5:3.

9 Nyengo ya Chikumbutso ndi nthawi yabwino kuganizira kwambiri zinthu zimene timachita. Tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndi zinthu ziti zimene ndimachita bwino potsanzira Yesu? Nanga ndi zinthu ziti zimene ndiyenera kusintha?’ Tiyenera kudzifunsa mafunso amenewa chifukwa nthawi zonse timakakamizidwa kutsatira zimene anthu a m’dzikoli amachita. (Aroma 12:2) Ngati sitingasamale, tikhoza kuyamba kutsatira anthu am’dzikoli amene amaoneka anzeru, otchuka kapena akatswiri amasewera. (Akol. 2:8; 1 Yoh. 2:15-17) Kodi tingapewe bwanji zimenezi?

10 Pa nyengo ya Chikumbutso tingachitenso bwino kuona zinthu zomwe tili nazo. Mwachitsanzo, tingaone bwinobwino zovala zathu ndiponso nyimbo ndi mafilimu amene tili nawo. Ndi bwinonso kuona zinthu zimene timasunga pakompyuta, pafoni kapena patabuleti yathu. Mukamayang’ana zovala zanu muzidzifunsa kuti: ‘Zitakhala kuti Yesu alipo, kodi ndikhoza kucheza naye momasuka nditavala zovala zimenezi?’ (Werengani 1 Timoteyo 2:9, 10.) ‘Ndikavala zovala zimenezi, kodi anthu amazindikira kuti ndine wotsatira wa Yesu?’ Pa nkhani ya mafilimu, nyimbo komanso zipangizo zamakono, tingadzifunsenso mafunso ngati awa: ‘Kodi Yesu angaonere filimu kapena kumvera nyimbo imeneyi? Kodi ndikhoza kumubwereka foni kapena tabuleti yanga ndi kumulola kuti aone zimene ndinaikamo?’ Ndipo ngati mumakonda masewera apakompyuta, mungadzifunsenso kuti: ‘Kodi ndingavutike kufotokozera Yesu chifukwa chimene ndimakondera masewera amenewa?’ Ngati timakonda kwambiri Yehova, tidzataya chilichonse chimene Khristu sangasangalale nacho, ngakhale zitakhala kuti tinachigula modula. (Mac. 19:19, 20) Pamene tinkadzipereka kwa Yehova tinamulonjeza kuti sitidzachitanso zofuna zathu koma za Mwana wake. Choncho sitiyenera kukakamira chilichonse chimene chingatilepheretse kutsatira mosamala chitsanzo cha Yesu.​—Mat. 5:29, 30; Afil. 4:8.

FEBRUARY 20-26

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MBIRI 17-19

“Muzikhalabe Wosangalala Ngakhale Pamene Zinthu Sizikuyenda Bwino”

w06 7/15 19 ¶1

Ganizirani za Ubwino wa Gulu la Yehova

DAVIDE wa ku Isiraeli wakale ndi mmodzi mwa anthu odziwika kwambiri ofotokozedwa m’Malemba a Chiheberi. Munthuyu yemwe anali mbusa, woimba, mneneri ndi mfumu, ankakhulupirira kwambiri Yehova Mulungu. Ubwenzi wolimba umene Davide anali nawo ndi Yehova unam’limbikitsa kukhala ndi chikhumbo chofuna kumangira Mulungu nyumba. Nyumba kapena kachisi ameneyu anadzakhala likulu la kulambira koona m’Israyeli. Davide ankadziwa kuti kachisi ndiponso ntchito yomwe inkachitika pakachisipo idzabweretsa chimwemwe ndi madalitso kwa anthu a Mulungu. Motero, Davide anaimba kuti: “Wodala munthuyo [amene inu Yehova] mum’sankha, ndi kum’yandikizitsa, akhale m’mabwalo anu: Tidzakhuta nazo zokoma za m’nyumba yanu, za m’malo oyera a Kachisi wanu.”​—Salmo 65:4.

w21.08 22-23 ¶11

Muzisangalala ndi Utumiki Wanu

11 Mofanana ndi zimenezi, ifenso tingamasangalale kwambiri ngati titakhala akhama pa chilichonse chimene timachita potumikira Yehova. Nthawi zonse ‘tizitanganidwa kwambiri’ ndi ntchito yolalikira ndipo tizidzipereka ndi mtima wonse pogwira ntchito zamumpingo. (Mac. 18:5; Aheb. 10:24, 25) Muzikonzekera bwino misonkhano n’cholinga choti muzikapereka ndemanga zolimbikitsa. Muzikonzekeranso bwino mukapatsidwa nkhani za ophunzira pamisonkhano ya mkati mwa mlungu. Mukapemphedwa kuti mugwire ntchito inayake mumpingo, muzisunga nthawi komanso muzikhala odalirika. Musamaone kuti zimene mwapemphedwa n’zosafunika kapena kungotaya nthawi. Muziyesetsa kuwonjezera luso lanu. (Miy. 22:29) Mukamadzipereka kwambiri pa utumiki wanu, m’pamenenso mumapita patsogolo mofulumira ndipo mumasangalala. (Agal. 6:4) Zimenezi zingakuthandizeninso kuti muzisangalala ndi ena akapatsidwa utumiki umene inuyo mumaulakalaka.​—Aroma 12:15; Agal. 5:26.

Mfundo Zothandiza

w20.02 12, bokosi

Timakonda Kwambiri Atate Wathu Yehova

Kodi Yehova Amandiwerengera?

Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti, ‘Pa anthu mabiliyoni ambiri padzikoli, kodi Yehova angandiwerengere ineyo?’ Ngati zili choncho, simuli nokha. Paja Mfumu Davide analemba kuti: “Inu Yehova, munthu ndani kuti mumuganizire? Kodi mwana wa munthu wochokera kufumbi ndani kuti mumuwerengere?” (Sal. 144:3) Koma Davide sankakayikira kuti Yehova ankamudziwa bwino. (1 Mbiri 17:16-18) Yehova amagwiritsa ntchito Mawu ake komanso gulu lake potitsimikiziranso kuti amayamikira chikondi chimene timamusonyeza. Mawu a m’Baibulo otsatirawa angatithandize kuti tisamakayikire mfundo imeneyi.

• Yehova anakuonani ngakhale musanabadwe.​—Sal. 139:16.

• Yehova amadziwa zimene zili mumtima mwanu komanso zimene mukuganiza.​—1 Mbiri 28:9.

• Yehova amamvetsera pemphero lanu lililonse.​—Sal. 65:2.

• Zochita zanu zimakhudza Yehova.​—Miy. 27:11.

• Yehova wakukokani kuti mubwere kwa iye.​—Yoh. 6:44.

• Yehova amakudziwani bwino kwambiri moti ngakhale mutafa sangadzavutike kukuukitsani. Iye adzapanganso thupi lanu n’kukuthandizani kukhala ndi maganizo komanso makhalidwe amene muli nawo. Mudzathanso kukumbukira zinthu zonse zimene mukuzidziwa panopa.​—Yoh. 11:21-26, 39-44; Mac. 24:15.

FEBRUARY 27–​MARCH 5

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 MBIRI 20-22

“Muzithandiza Achinyamata Kuti Azichita Zambiri”

w17.01 29 ¶8

‘Zinthu Zimenezo Uziziphunzitsa kwa Anthu Okhulupirika’

8 Werengani 1 Mbiri 22:5. Davide akanatha kuganiza kuti Solomo wachepa nayo ntchitoyo. Pajatu kachisiyo anafunika kukhala ‘wokongola ndiponso waulemerero wosaneneka.’ Kuwonjezera pamenepo, Solomo anali adakali “wamng’ono komanso wosakhwima.” Koma Davide ankadziwa kuti Yehova adzathandiza Solomo kuti agwire bwino ntchitoyo. Choncho Davide anangochita zimene akanatha ndipo anamuthandiza kukonzekera ntchito yaikuluyo.

w17.01 29 ¶7

‘Zinthu Zimenezo Uziziphunzitsa kwa Anthu Okhulupirika’

7 Davide akanatha kukhumudwa kwambiri chifukwa choti ankafunitsitsa kumanga kachisi wa Yehova. Koma anathandiza kwambiri pokonzekera ntchito imene Solomo adzagwireyo. Anapeza zitsulo, mkuwa, siliva, golide matabwa komanso anthu oti adzagwire ntchitoyo. Iyeyo sanadandaule kuti akapanda kumanga kachisiyo sadzatamandidwa. Ndipotu atamangidwa ankatchedwa kachisi wa Solomo. M’malomwake analimbikitsa Solomo kuti: “Tsopano mwana wanga, Yehova akhale nawe, ndipo zinthu zikuyendere bwino kuti umange nyumba ya Yehova Mulungu wako, monga mmene iye analankhulira za iwe.”​—1 Mbiri 22:11, 14-16.

w18.03 11-12 ¶14-15

Makolo, Kodi Mukuthandiza Ana Anu Kuti Ayenerere Kubatizidwa

14 Akulu mumpingo omwe ndi abusa, angathandize makolo akamalimbikitsa ana kuti akhale ndi zolinga zauzimu. Mlongo wina amene anachita upainiya kwa zaka zoposa 70 ananena mmene M’bale Charles T. Russell anamulimbikitsira iye ali ndi zaka 6 zokha. Mlongoyo anati: “M’baleyu anakambirana nane kwa maminitsi 15 zokhudza zolinga zanga zauzimu.” Apa n’zoonekeratu kuti mawu abwino komanso olimbikitsa angathandize anthu kwa nthawi yaitali. (Miy. 25:11) Akulu angapemphenso makolo ndi ana awo kuti azithandiza pa ntchito za pa Nyumba ya Ufumu. Angapereke ntchito kwa ana mogwirizana ndi msinkhu komanso luso lawo.

15 Abale ndi alongo ena mumpingo angathandizenso makolo akamalimbikitsa ana awo. Kuti achite zimenezi, ayenera kukhala tcheru kuti aone zimene ana akuchita mumpingo. Mwachitsanzo, mwina mwana angapereke ndemanga yochokera pansi pa mtima, kukamba nkhani kapena kuchita chitsanzo pamisonkhano yampingo. Kapena mwina wakhalabe wokhulupirika atakumana ndi mayesero kapenanso walalikira kwa anzake kusukulu. Mukaona zimenezi musamachedwe kuwayamikira ndi mtima wonse. Mungachitenso bwino kukhala ndi cholinga choti muzicheza ndi mwana mmodzi misonkhano isanayambe kapena itatha. Mukamachita zinthu ngati zimenezi, mungathandize ana kuzindikira kuti ndi ofunika kwambiri mu “mpingo waukulu.”​—Sal. 35:18.

Mfundo Zothandiza

w05 10/1 11 ¶6

Mfundo Zazikulu za M’buku Loyamba la Mbiri

21:13-15. Yehova analamula mngelo kuletsa mliri chifukwa chakuti Iye amakhudzidwa kwambiri anthu Ake akamavutika. Ndithudi, “zifundo zake zichulukadi.”

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

w16.03 10-11 ¶10-15

Achinyamata, Kodi Mungakonzekere Bwanji Kubatizidwa

10 Baibulo limati: “Chikhulupiriro pachokha, ngati chilibe ntchito zake, ndi chakufa.” (Yak. 2:17) Zimene mumachita zimasonyeza ngati chikhulupiriro chanu ndi cholimba kapena ayi. Baibulo limanena kuti ‘muyenera kukhala ndi khalidwe loyera ndiponso kuchita ntchito zosonyeza kuti ndinu odzipereka kwa Mulungu.’​—Werengani 2 Petulo 3:11.

11 Kuti musonyeze kuti muli ndi khalidwe loyera, nthawi zonse muyenera kupewa kuchita zoipa. Mwachitsanzo, taganizirani zimene mwachita pa miyezi 6 yapitayi. Ngati munayesedwa kuti muchite zoipa, kodi munaiganizira bwinobwino nkhaniyo n’kuzindikira zoyenera kuchita? (Aheb. 5:14) Kodi mukukumbukira nthawi ina pamene munakana mayesero kapena kutengera zochita za anzanu? Nanga kodi zimene mumachita kusukulu zimathandiza anthu kuti azilemekeza Yehova? Kodi mumakhala okhulupirika kwa Yehova kapena mumachita zofuna za anthu akusukulu kwanu n’cholinga choti asakunyozeni? (1 Pet. 4:3, 4) N’zoona kuti tonsefe timalakwitsa zinthu nthawi zina. Ngakhale anthu amene atumikira Mulungu kwa zaka zambiri, nthawi zina amachita mantha kulalikira kwa ena. Komabe munthu aliyense amene anadzipereka kwa Yehova ayenera kunyadira kuti ndi wa Mboni za Yehova ndipo ayenera kuyesetsa kukhala ndi khalidwe loyera.

12 Koma kodi “ntchito zosonyeza kuti ndinu odzipereka kwa Mulungu” ndi ziti? Izi ndi zinthu monga kusonkhana komanso kulalikira. Palinso zinthu zina zomwe anthu ambiri sangaone monga kupemphera komanso kuphunzira Baibulo panokha. Munthu amene anadzipereka kwa Yehova ndi mtima wonse saona zinthu zimenezi ngati zotopetsa. Koma amakhala ndi maganizo ofanana ndi a Mfumu Davide amene anati: “Ndimakondwera ndi kuchita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga, ndipo chilamulo chanu chili mumtima mwanga.”​—Sal. 40:8.

13 Buku lachiwiri la Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, lingakuthandizeni kuti muzichita “ntchito zosonyeza kuti ndinu odzipereka kwa Mulungu.” Patsamba 308 ndi 309 m’bukuli, pali mafunso amene mungayankhe. Mafunso ake ndi monga akuti: “Mukamapemphera, kodi mumatchula mwachindunji zimene mukufuna? Nanga mapemphero anuwo amasonyeza kuti mumakondadi Yehova?” “Kodi mumachita zotani paphunziro lanu laumwini?” “Kodi mumalowa mu utumiki ngakhale ngati makolo anu sanalowe?” Ndiyeno patsamba 309 palinso malo amene mungalembepo zimene mukufuna kuchita pa nkhani ya kupemphera, kuphunzira panokha komanso kulalikira.

14 Achinyamata ambiri amene akuganiza zobatizidwa amaona kuti zimene zili pamasambawa n’zothandiza kwambiri. Mtsikana wina dzina lake Tilda ananena kuti: “Ndinkagwiritsa ntchito masamba amenewa kulembapo zimene ndinkafuna kuchita. Ndiyeno pang’ono ndi pang’ono ndinakwaniritsa zimene ndinalembazo. Patangotha chaka chimodzi, ndinali wokonzeka kubatizidwa.” Mnyamata wina dzina lake Patrick ananenanso kuti: “Ndinkadziwa zimene ndinkafuna kuchita, komabe kulemba zinthuzo kunandithandiza kuchita khama kuti ndizikwaniritse.”

15 Patsamba 309 pali funso lina lofunika kwambiri lakuti: “Kodi mungapitirize kutumikira Yehova ngakhale makolo anu ndiponso anzanu atasiya kum’tumikira?” Muyenera kukumbukira kuti munthu aliyense adzayankha yekha kwa Mulungu. Choncho aliyense ayenera kusankha yekha kuti adzipereke kwa iye ndiponso kubatizidwa. Sayenera kudalira makolo ake kapenanso anthu ena potumikira Mulungu. Mukakhala ndi khalidwe loyera ndiponso mukamachita zinthu zosonyeza kuti ndinu wodzipereka kwa Yehova, mumasonyeza kuti mumamukonda komanso mumakonda mfundo zake. Komanso mumasonyeza kuti mukhoza kubatizidwa pasanapite nthawi yaitali.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena