Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr23 September tsamba 1
  • Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Timitu
  • SEPTEMBER 4-​10
  • SEPTEMBER 11-​17
  • SEPTEMBER 18-​24
  • SEPTEMBER 25–OCTOBER 1
  • OCTOBER 2-8
  • OCTOBER 9-​15
  • OCTOBER 16-​22
  • OCTOBER 23-​29
  • OCTOBER 30–NOVEMBER 5
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
mwbr23 September tsamba 1

Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

© 2023 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania

SEPTEMBER 4-​10

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | ESITERE 1-2

“Yesetsani Kukhala Odzichepetsa Ngati Esitere”

w17.01 25 ¶11

Kodi Tingatani Kuti Nthawi Zonse Tizikhala Odzichepetsa?

11 Kudzichepetsa kumakhalanso kovuta ngati tikutamandidwa. Taganizirani zimene zinachitikira Esitere. Iye anali wokongola kwambiri. Ndiyeno anatengedwa kuti akakhale m’gulu la atsikana oti asamaliridwe bwino kwa chaka chathunthu. Kumeneko ankakhala ndi atsikana ambiri ochokera m’madera osiyanasiyana amene ankalamuliridwa ndi ufumu wa Perisiya. Pa nthawiyo anthu ankafuna kupeza mkazi amene angasangalatse mfumu. Koma Esitere anakhalabe waulemu komanso wodzichepetsa. Anapitiriza kuchita zimenezi ngakhale pamene anasankhidwa kuti akhale mfumukazi.​—⁠Esitere 2:​9, 12, 15, 17.

ia 130 ¶15

Analimba Mtima Kuteteza Anthu a Mulungu

15 Ndiyeno nthawi itakwana yoti Esitere akaonekere kwa mfumu, anapatsidwa ufulu woti anene chilichonse chimene akufuna kuti am’patse, mwina kuti awonjezere kudzikongoletsa. Modzichepetsa, iye sanapemphe chilichonse chowonjezera pa zimene Hegai anatchula. (Esitere 2:15) Ayenera kuti anadziwa kuti kukongola pakokha sikungachititse kuti mfumuyo imusankhe. Ankadziwa kuti chofunika kwambiri n’kukhala wodzichepetsa. Koma kodi zimenezi zinathandizadi?

w17.01 25 ¶12

Kodi Tingatani Kuti Nthawi Zonse Tizikhala Odzichepetsa?

12 Kudzichepetsa kumathandizanso kuti tizivala komanso kudzikongoletsa mwaulemu. Munthu wodzichepetsa amapewa kudzionetsera kapena kudzitama koma amasonyeza “mzimu wabata ndi wofatsa.” (Werengani 1 Petulo 3:​3, 4; Yer. 9:​23, 24) Zimene timachita komanso kulankhula zimasonyeza zimene zili mumtima mwathu. Mwachitsanzo, anthu ena amakonda kulankhula zosonyeza kuti akusangalala chifukwa choti ali ndi udindo winawake, akudziwa zinsinsi zina kapena chifukwa choti amagwirizana ndi abale ena audindo. Ena amakonda kulankhula zosonyeza kuti zinthu zina zinayenda bwino chifukwa cha iwowo kuiwala kuti ena anathandizaponso. Koma Yesu anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani ya kudzichepetsa. Mfundo zambiri zimene ankalankhula zinali zochokera m’Malemba Achiheberi kapena zokhudza Malembawo. Iye ankachita zimenezi n’cholinga choti anthu adziwe kuti zimene ankalankhula zinali zochokera kwa Yehova osati nzeru zake.​—⁠Yoh. 8:⁠28.

Mfundo Zothandiza

w22.11 31 ¶3-6

Kodi Mukudziwa?

Ofufuza anapeza dzina lakuti Marduka (m’Chichewa Moredekai) pazolembedwa za pamwala za ku Perisiya. Iye anali ndi udindo m’boma, ndipo n’kutheka kuti anali wowerengera chuma ku Susani. Arthur Ungnad, yemwe ndi katswiri wa mbiri ya Kum’mawa, ananena kuti “kupatula pa Baibulo, ndi zolemba pamwala umenewu zokha zomwe zimatchulanso za Moredekai.”

Kungochokera pamene Arthur ananena zimenezi, akatswiri akhala akumasulira zolembedwa pamiyala zambiri za ku Perisiya. Ina mwa miyalayi anaipeza m’mabwinja a nyumba yosungiramo zinthu pafupi ndi mpanda wa mzinda. Miyala imeneyi inalembedwa pa nthawi ya Sasta Woyamba. Zolembedwazi zili m’chilankhulo cha Chielami ndipo zili ndi mayina angapo opezeka m’buku la Esitere.

Miyala ingapo imatchula za dzina la Marduka, yemwe anali mlembi kunyumba yachifumu ku Susani pa nthawi ya ulamuliro wa Sasta Woyamba. Mwala wina umanena kuti Marduka anali womasulira. Zimenezi zikugwirizana ndi zomwe Baibulo limanena zokhudza Moredekai. Iye anali munthu waudindo m’khoti la Mfumu Ahasiwero (Sasta Woyamba) ndipo ankalankhula zilankhulo zosachepera ziwiri. Nthawi zambiri Moredekai ankakhala pageti kunyumba yachifumu ku Susani. (Esitere 2:​19, 21; 3:⁠3) Pagetili panali nyumba imene munkagwira ntchito anthu audindo panyumba yachifumuyi.

Pali kufanana kochititsa chidwi pakati pa Marduka wotchulidwa pamiyalayi ndi Moredekai wotchulidwa m’Baibulo. Anakhalapo pa nthawi yofanana, pamalo ofanana ndiponso ankagwira ntchito pamaudindo ofanana. Kufanana kumeneku kukusonyeza kuti zimene ofukula zakale apeza zingakhale zikunena za Moredekai wotchulidwa m’buku la Esitere.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

w20.11 13-14 ¶3-7

Limbani Mtima Chifukwa Yehova Akuthandizani

3 Paulo ankafunika kuthandizidwa. Cha m’ma 56 C.E., khamu la anthu linamukokera kunja kwa kachisi ku Yerusalemu ndipo linkafuna kumupha. Tsiku lotsatira, pamene Paulo anamubweretsa ku Khoti Lalikulu la Ayuda, adani ake anatsala pang’ono kumukhadzulakhadzula. (Mac. 21:​30-32; 22:30; 23:​6-10) Pa nthawiyi mwina Paulo ankadzifunsa kuti, ‘Kodi ndipirira mavuto amenewa mpaka liti?’

4 Kodi Yesu anathandiza bwanji Paulo? Tsiku limene Paulo anamangidwa, usiku “Ambuye” Yesu anaimirira pambali yake ndi kunena kuti: “Limba mtima! Pakuti wandichitira umboni mokwanira mu Yerusalemu, ndipo ukandichitiranso umboni ku Roma.” (Mac. 23:11) Zimenezitu zinalimbikitsa kwambiri Paulo. Yesu anayamikira Paulo chifukwa cha ntchito yochitira umboni imene anagwira ku Yerusalemu. Ndipo analonjeza kuti Paulo akafika bwinobwino ku Roma kuti akapitirize kugwira ntchito yochitira umboni kumeneko. Atamva zimenezi, Paulo anayamba kuona kuti ndi wotetezeka ngati mwana amene ali m’manja mwa bambo ake.

5 Kodi Paulo anakumananso ndi mavuto ena ati? Patadutsa zaka pafupifupi ziwiri kuchokera pa nthawi imene adani anamuukira ku Yerusalemu, Paulo anakwera ngalawa pa ulendo wopita ku Italiya. Ngalawayi inakumana ndi mphepo yamkuntho ndipo oyendetsa komanso anthu amene anali mmenemo ankaganiza kuti afa. Koma Paulo sankachita mantha. Chifukwa chiyani? Iye anauza anthu amene anali m’ngalawayo kuti: “Usiku mngelo wa Mulungu wanga, amene ndikumuchitira utumiki wopatulika, anaima pafupi nane, ndi kunena kuti, ‘Usaope Paulo. Uyenera kukaima pamaso pa Kaisara, ndipo taona! Chifukwa cha iwe, Mulungu mokoma mtima adzapulumutsa onse amene uli nawo pa ulendowu.’ ” Yehova anagwiritsa ntchito mngelo kuti alimbikitse Paulo ngati mmene anamulimbikitsira m’mbuyomu pogwiritsa ntchito Yesu. Paulo anakafikadi ku Roma monga mmene Yehova anamulonjezera.​—⁠Mac. 27:​20-25; 28:⁠16.

6 Kodi Yesu amatithandiza bwanji? Yesu adzatithandiza ngati mmene anathandizira Paulo. Mwachitsanzo, Yesu analonjeza otsatira ake onse kuti: “Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:20) Mawu a Yesuwa ndi olimbikitsa. Chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti masiku ena timakumana ndi zinthu zovuta kupirira. Mwachitsanzo, munthu amene timam’konda akamwalira timakhala achisoni, osati kwa masiku ochepa, koma mwina kwa zaka zambiri. Enanso amavutika tsiku ndi tsiku chifukwa cha ukalamba. Ndipo ena amavutika chifukwa cha nkhawa. Ngakhale zili choncho, timapeza mphamvu kuti tithe kupirira chifukwa tikudziwa kuti Yesu alinafe “masiku onse” kuphatikizapo nthawi zovuta kwambiri pa moyo wathu.​—⁠Mat. 11:​28-30.

7 Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti Yehova amatithandiza pogwiritsa ntchito angelo. (Aheb. 1:​7, 14) Mwachitsanzo, angelo amatithandiza ndi kutitsogolera tikamalalikira “uthenga wabwino wa Ufumu” kwa anthu ochokera “kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse.”​—⁠Mat. 24:​13, 14; werengani Chivumbulutso 14:⁠6.

SEPTEMBER 11-​17

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | ESITERE 3-5

“Muzithandiza Ena Kuti Azichita Zambiri”

it-2 431 ¶7

Moredekai

Anakana kuweramira Hamani. Pambuyo pake, Hamani Mwagagi anaikidwa kukhala nduna yaikulu ndi Mfumu Ahasiwero, yemwe analamula kuti atumiki onse a mfumu omwe anali kuchipata azigwadira Hamani chifukwa cha udindo waukulu womwe anamupatsa. Moredekai anakana molimba mtima kuchita zimenezi chifukwa anali Myuda. (Est 3:​1-4) Chifukwa chimene anaperekachi chimasonyeza kuti ankaona kuti ubwenzi wake ndi Yehova ndi womwe unali wofunika kwambiri. Iye ankadziwa kuti kuweramira Hamani kukanaphatikiza zambiri osati kungowerama mpaka nkhope yake pansi, ngati mmene Aisiraeli ankachitira akakumana ndi munthu wa udindo waukulu. (2Sa 14:4; 18:28; 1Mf 1:16) Moredekai anali ndi zifukwa zomveka zomwe anakanira kugwadira Hamani. Zimaoneka kuti Hamani anali Mwamaleki ndipo Yehova anali atanena kale kuti adzakhala ali pankhondo ndi Aamaleki “ku mibadwomibadwo.” (Eks 17:16) Kwa Moredekai nkhani inali kukhala wokhulupirika kwa Mulungu osati kutenga nawo mbali pa zinthu za ndale.

it-2 431 ¶9

Moredekai

Anagwiritsidwa Ntchito Populumutsa Aisiraeli. Pataperekedwa lamulo lakuti Ayuda onse aphedwe mu ufumuwo, Moredekai anasonyeza kuti ankakhulupirira kuti Mulungu ndi amene anachititsa kuti Esitere akhale mfumukazi pa nthawiyi kuti Ayuda apulumutsidwe. Iye anathandiza Esitere kudziwa udindo waukulu womwe anali nawo ndipo anamuuza kuti apite kwa mfumu kukapempha kuti iwachitire chifundo komanso iwathandize. Ngakhale kuti zimenezi zinaika moyo wake pangozi, Esitere anavomera ndipo anachitadi zomwe anauzidwazo.—⁠Est 4:7–​5:⁠2.

ia 133 ¶22-​23

Analimba Mtima Kuteteza Anthu a Mulungu

22 Esitere ayenera kuti anachita mantha kwambiri atamva uthengawo. Pamenepa chikhulupiriro chake chinayesedwa kwambiri. Zimene Esitere anayankha Moredekai zinasonyeza kuti anali ndi mantha kwambiri. Iye anakumbutsa Moredekai za lamulo loletsa kukaonekera kwa mfumu usanaitanidwe lija. Munthu akaphwanya lamulo limeneli ankatha kuphedwa. Ankapulumuka pokhapokha ngati mfumu yamuloza ndi ndodo yake yagolide. Ndipo akaganizira zimene zinachitikira Vasiti atakana kukaonekera kwa mfumuyo, Esitere ankaona kuti ngakhale kuti ndi mkazi wa mfumu, n’kutheka kuti mfumuyi singamuchitire chifundo. Esitere anauza Moredekai kuti panali patatha masiku 30 asanaitanidwe kuti akaonekere kwa mfumu. Zimenezi ziyenera kuti zinachititsa Esitere kuyamba kukayikira ngati mfumuyi, yomwe sinkachedwa kupsa mtima, inkamukondabe.​—⁠Esitere 4:​9-11.

23 Moredekai anayankhanso Esitere ndi mawu amphamvu kuti chikhulupiriro chake chilimbe. Anamutsimikizira kuti ngati sangachitepo kanthu, chipulumutso cha Ayuda chichokera kwina. Koma kodi Esitere akanapulumuka ngati lamulo loti Ayuda aphedwe likanayamba kugwira ntchito? Apa Moredekai anasonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri Yehova, yemwe sangalole kuti anthu ake onse awonongedwe kapena kulola kuti malonjezo ake asakwaniritsidwe. (Yos. 23:14) Kenako Moredekai anafunsa Esitere kuti: “Ndani akudziwa? Mwina iwe wakhala mfumukazi kuti uthandize pa nthawi ngati imeneyi.” (Esitere 4:​12-14) Moredekai ankakhulupirira Yehova Mulungu ndi mtima wonse. Kodi ifenso timatero?​—⁠Miy. 3:​5, 6.

Mfundo Zothandiza

kr 160 ¶14

Kumenyera Ufulu Wolambira Mulungu Momasuka

14 Mofanana ndi mmene anachitira Esitere ndi Moredekai, anthu a Yehova a masiku ano amamenyera ufulu wolambira Yehova m’njira imene mwiniwake anatilamula. (Esitere 4:​13-16) Kodi nanunso mungathandize nawo pomenyera ufuluwu? Inde. Mukhoza kupempherera mobwerezabwereza abale ndi alongo omwe akuzunzika chifukwa cha malamulo amene ali m’dziko lawo. Mapemphero ngati amenewo angathandize kwambiri abale ndi alongo omwe akuzunzidwa. (Werengani Yakobo 5:16.) Koma kodi Yehova amayankha mapemphero otero? Milandu imene takhala tikuwina ikusonyeza kuti Yehova amayankhadi mapemphero amenewa.​—⁠Aheb. 13:​18, 19.

SEPTEMBER 18-​24

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | ESITERE 6-8

“Zimene Tikuphunzira pa Nkhani ya Kulankhulana Bwino”

ia 140 ¶15-​16

Anachita Zinthu Mwanzeru, Molimba Mtima Ndiponso Moganizira Ena

15 Chifukwa chakuti Esitere anadikiranso tsiku lina asanauze mfumuyo pempho lake, zinachititsa kuti Hamani achite zinthu zomwe zinamubweretsera yekha mavuto. N’kutheka kuti Yehova Mulungu ndi amene anachititsa kuti mfumuyo isowe tulo. (Miy. 21:⁠1) N’chifukwa chake Mawu a Mulungu amatilimbikitsa ‘kuyembekezera moleza mtima.’ (Werengani Mika 7:⁠7.) Tikamayembekezera kuti Mulungu atithandize pa mavuto athu, tidzaona kuti iye amapeza njira yabwino yothetsera mavuto yoposa imene ifeyo tikanatsatira.

Analankhula Molimba Mtima

16 Esitere anaona kuti si bwino kuti mfumuyo izingodikirabe kuti aiuza zotani. Choncho, paphwando lotsatira, iye anaona kuti ayenera kufotokoza zonse. Koma kodi akanayambira pati? Mwamwayi, mfumuyo inamufunsanso kuti afotokoze pempho lake. (Esitere 7:⁠2) Esitere anaona kuti tsopano imeneyi ndi “nthawi yolankhula.”

ia 140 ¶17

Anachita Zinthu Mwanzeru, Molimba Mtima Ndiponso Moganizira Ena

17 N’kutheka kuti Esitere anapemphera chamumtima kwa Mulungu wake asanauze mfumu mawu awa: “Ngati mungandikomere mtima mfumu, ndipo ngati zingakukomereni, ndikupempha kuti mupulumutse moyo wanga komanso kuti musawononge anthu a mtundu wanga.” (Esitere 7:⁠3) Onani kuti iye anasonyeza kuti ankalemekeza zimene mfumuyo ingalamule malinga ndi zomwe iyoyo yaona kuti n’zoyenera. Zimene Esitere anachitazi zinasonyeza kuti anali wosiyana kwambiri ndi Vasiti, mkazi wakale wa mfumuyi, amene anachititsa manyazi mfumuyi mwadala. (Esitere 1:​10-12) Komanso, Esitere sananyoze mfumuyi chifukwa chokhulupirira zinthu zabodza zimene Hamani anaiuza. M’malomwake, anapempha mfumuyo kuti imuteteze kuti asaphedwe.

ia 141 ¶18-​19

Anachita Zinthu Mwanzeru, Molimba Mtima Ndiponso Moganizira Ena

18 Pempho limeneli linadabwitsa kwambiri mfumuyo komanso inaona kuti iyeneradi kuchitapo kanthu. Ndipotu palibe mwamuna amene angalekerere kuti mkazi wake aphedwe. Esitere anapitiriza kufotokoza kuti: “Ine ndi anthu a mtundu wanga tagulitsidwa kuti tiwonongedwe, tiphedwe ndi kufafanizidwa. Ngati tikanagulitsidwa kukhala akapolo aamuna ndi akapolo akazi ndikanakhala chete. Koma musalole kuti tsoka limeneli lichitike chifukwa liwonongetsa zinthu zambiri za mfumu.” (Esitere 7:⁠4) Onani kuti Esitere anafotokoza zokhudza chiwembucho momveka bwino koma ananenanso kuti zikanakhala kuti iwo anangokhala akapolo chabe, iye sakanadandaula chilichonse. Komano popeza kuti kupha mtundu wonse kukanakhudzanso kwambiri mfumuyo, iye anaona kuti si bwino kungokhala chete.

19 Chitsanzo cha Esitere chikutiphunzitsa njira yabwino yofotokozera maganizo athu mogwira mtima. Ngati mukufuna kufotokoza vuto linalake kwa munthu amene mumam’konda kapena kwa munthu waudindo, kuchita zinthu moleza mtima, mwaulemu, komanso kutchula vutolo mosapita m’mbali, kungakuthandizeni kwambiri.​—⁠Miy. 16:​21, 23.

Mfundo Zothandiza

w06 3/1 11 ¶1

Mfundo Zazikulu za M’buku la Estere

7:4—⁠Kodi kuwonongedwa kwa Ayuda kukanabweretsa bwanji “kusowa kwa mfumu”? Mwa kufotokoza mwanzeru kuti iye sakanavutika Ayuda akanagulitsidwa kukhala akapolo, Estere anatsindika mmene kuwonongedwa kwawo kukanapwetekera mfumu. Ndalama za siliva 10,000 zimene Hamani anali atalonjeza sizinali zaphindu pa chuma cha mfumu kuyerekeza ndi chuma chimene chikanapezeka Hamani akanakhala kuti anakonza chiwembu chogulitsa Ayuda kukhala akapolo. Chiwembu cha Hamani chikanatheka, mfumu ikanataya mkazi wake.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

w22.01 10-11 ¶8-10

Zimene Tingaphunzire Kuchokera kwa Mng’ono Wake wa Yesu

8 Yakobo sanapite patali ndi sukulu. Mpake kuti atsogoleri achipembedzo a munthawi yake ankamuona mofanana ndi mmene ankaonera mtumwi Petulo ndi Yohane kuti anali “osaphunzira ndiponso anthu wamba.” (Mac. 4:13) Komabe iye anadzakhala mphunzitsi waluso monga mmene timaonera tikamawerenga buku limene limadziwika ndi dzina lake. Mofanana ndi Yakobo n’kutheka kuti ifenso sitinaphunzire kwambiri. Ngakhale zili choncho, mothandizidwa ndi Yehova komanso maphunziro amene timalandira m’gulu lake, ifenso tingakhale aphunzitsi abwino. Tiyeni tikambirane chitsanzo cha Yakobo monga mphunzitsi komanso zimene tingaphunzire kwa iye.

9 Yakobo sankagwiritsa ntchito mawu ogometsa kapena kufotokoza zinthu m’njira yovuta kumvetsa. Choncho anthu amene ankamumvetsera ankadziwa zoyenera kuchita komanso mmene angazichitire. Mwachitsanzo, taganizirani mmene iye anaphunzitsira mosavuta mfundo yakuti Akhristu ayenera kukhala okonzeka kuvutika chifukwa cha zinthu zopanda chilungamo popanda kusungira ena zifukwa. Yakobo analemba kuti: “Anthu amene anapirira timawatcha odala. Munamva za kupirira kwa Yobu ndipo mwaona zimene Yehova anamupatsa, mwaona kuti Yehova ndi wachikondi chachikulu ndi wachifundo.” (Yak. 5:11) Onani kuti iye akamaphunzitsa ankagwiritsa ntchito Malemba. Anagwiritsa ntchito Mawu a Mulungu pothandiza omvera ake kudziwa kuti Yehova nthawi zonse amapereka mphoto kwa anthu amene mofanana ndi Yobu amakhala okhulupirika kwa iye. Yakobo anaphunzitsa mfundo imeneyi pogwiritsa ntchito mawu osavuta kumva komanso motsatirika. Pochita zimenezi iye anathandiza anthu kuti aziganizira kwambiri za Yehova osati iyeyo.

10 Zimene tikuphunzirapo: Uthenga wathu uzikhala wosavuta kumva ndipo tiziphunzitsa pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu. Cholinga chathu chisamakhale kugometsa anthu ndi zimene tikudziwa, koma kuwathandiza kudziwa zimene Yehova amadziwa komanso mmene amawasamalirira. (Aroma 11:33) Tingathe kukwaniritsa cholinga chathuchi ngati nthawi zonse zomwe timanena zimachokera m’Malemba. Mwachitsanzo, m’malo mouza ophunzira Baibulo zimene ifeyo tikanachita tikanakhala iwowo, tiziwathandiza kuganizira zitsanzo za m’Baibulo ndiponso kumvetsa mmene Yehova amaganizira komanso mmene amamvera. Tikatero tidzawathandiza kuti azifunitsitsa kusangalatsa Yehova osati ifeyo.

SEPTEMBER 25–OCTOBER 1

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | ESITERE 9-​10

“Anagwiritsa Ntchito Udindo Wake Pothandiza Anthu Ena”

it-2 432 ¶2

Moredekai

Tsopano Moredekai anakhala nduna yaikulu m’malo mwa Hamani ndipo mfumu inamupatsa mphete yake yodindira. Esitere anaika Moredekai kuti aziyang’anira nyumba ya Hamani yomwe mfumu inamupatsa. Kenako Moredekai anagwiritsa ntchito mphamvu zomwe mfumu inamupatsa polemba lamulo lopita kwa Ayuda lowapatsa ufulu wodziteteza. Ayuda anasangalala kwambiri podziwa kuti tsopano apulumutsidwa. Anthu ambiri mu ufumuwo anakhala kumbali ya Ayuda ndipo pamene tsiku la Adara 13 linakwana, lomwe linali tsiku loti malamulowa agwire ntchito, Ayuda anali atakonzeka. Akuluakulu aboma analinso kumbali yawo chifukwa Moredekai anali ndi udindo waukulu. Kumenyanako kunafika mpaka tsiku lotsatira ku Susani. Adani a Ayuda oposa 75,000 a ku Perisiya anaphedwa, kuphatikizapo ana 10 a Hamani. (Est 8:1–​9:​18) Esitere atapereka chilolezo, Moredekai analamula Ayuda kuti chaka ndi chaka azichita chikondwerero pa tsiku la 14 ndi la 15 la Adara, omwe anali “masiku a Purimu,” kuti azisangalala, kuchita phwando, kutumizirana chakudya ndi kupereka mphatso kwa osauka. Ayuda anavomera ndipo analamula ana awo komanso anthu onse omwe ankafuna kukhala kumbali yawo kuti azichita nawo chikondwererochi. Monga wachiwiri mu ufumuwo, Moredekai ankalemekezedwa kwambiri ndi Ayuda omwe anali odzipereka kwa Mulungu ndipo iye anapitiriza kuwatumikira.​​—⁠Est 9:​19-​22, 27-​32; 10:​2, 3.

it-2 716 ¶5

Purimu

Cholinga Chake. Anthu ena amanena kuti chikondwerero cha Purimu cha Ayuda, chimene anthu amachita masiku ano ndi chachikunja ndipo nthawi zambiri anthu amachita zinthu monyanyira, koma si mmene zinthu zinkachitikira m’mbuyomu. Moredekai ndi Esitere anali atumiki a Mulungu woona, ndipo anakhazikitsa chikondwererochi kuti azimulemekeza. Ayuda anapulumutsidwa ndi Yehova Mulungu chifukwa nkhani yoti aphedwe inayambika chifukwa cha kukhulupirika kwa Moredekai pa nkhani yolambira Yehova. Zimaoneka kuti Hamani anali Mwamaleki, mtundu umene Yehova anautemberera ndipo anati adzauwononga. Moredekai anamvera lamulo la Mulungu ndipo anakana kugwadira Hamani. (Est 3:​2, 5; Eks 17:​14-16) Mawu amene Moredekai anauza Esitere (Est 4:​14) amasonyeza kuti ankakhulupirira kuti apulumutsidwa ndi munthu wamphamvu kwambiri, komanso kusala kudya komwe Esitere anachita asanakaonekere kwa mfumu kukaipempha kuti iwathandize ndi kuiitanira kuphwando, zinasonyeza kuti ankadalira kwambiri Yehova.​​—⁠Est 4:​16.

cl 101-​102 ¶12-​13

‘Khalani Otsanzira Mulungu’ Pamene Mukugwiritsa Ntchito Mphamvu

12 Yehova wapereka oyang’anira kuti azitsogolera mu mpingo wachikristu. (Ahebri 13:17) Amuna okhoza kutsogolera amenewa amayenera kugwiritsa ntchito udindo womwe Mulungu wawapatsa pothandiza gulu la nkhosa ndi kuchititsa nkhosazo kukhala ndi moyo wabwino. Kodi udindo wawowo umapatsa akulu ufulu wochita umbuye pa okhulupirira anzawo? M’pang’onong’ono pomwe! Akulu afunika kuona ntchito imene ali nayo mu mpingo mosamala bwino ndi modzichepetsa. (1 Petro 5:​2, 3) Baibulo limauza oyang’anira kuti: “Muwete Eklesia wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa iye [“Mwana wake,” NW] yekha.” (Machitidwe 20:28) Chimenechitu ndi chifukwa champhamvu kwabasi chochitira zinthu mokoma mtima ndi nkhosa iliyonse m’gululo.

13 Tingachitire fanizo motere. Bwenzi lanu lapamtima lakupemphani kuti mulisungire katundu wamtengo wapatali. Inu mukudziwa kuti bwenzi lanu linalipira ndalama zambiri pogula katunduyo. Kodi simungamugwire mosamala kwambiri kuti asawonongeke? Mofananamo, Mulungu wapatsa akulu udindo wosamalira katundu wamtengo wapatali zedi: mpingo, womwe anthu ake amafanizidwa ndi nkhosa. (Yohane 21:​16, 17) Yehova amazikonda nkhosa zake; amazikondatu kwambiri moti anazigula ndi magazi amtengo wapatali a Mwana wake wobadwa yekha, Yesu Khristu. Panalibenso mtengo wina wokwera kuposa pamenepa umene Yehova akanalipirira nkhosa zake. Akulu odzichepetsa amakumbukira zimenezi ndipo amasamalira nkhosa za Yehova moyenerera.

Mfundo Zothandiza

w06 3/1 11 ¶4

Mfundo Zazikulu za M’buku la Esitere

9:​10, 15, 16—⁠Ngakhale kuti lamulo linalola kulanda zofunkha, n’chifukwa chiyani Ayuda sanachite zimenezo? Kusachita kwawo zimenezo unali umboni wakuti cholinga chawo chinali kuteteza mtundu wawo osati kudzilemeretsa ayi.

OCTOBER 2-8

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 1-3

“Pitirizani Kusonyeza Kuti Mumakonda Kwambiri Yehova”

w18.02 6 ¶16-​17

Tizikhala Okhulupirika Komanso Omvera Ngati Nowa, Danieli ndi Yobu

16 Mavuto amene Yobu anakumana nawo. Zinthu zambiri zinasintha pa moyo wa Yobu. Iye asanakumane ndi mayesero ake, anali “munthu wolemekezeka kwambiri pa anthu onse a Kum’mawa.” (Yobu 1:⁠3) Yobu anali wolemera, wotchuka komanso anthu ambiri ankamulemekeza. (Yobu 29:​7-16) Ngakhale zinali choncho, sankadziona kuti ndi wapamwamba kwambiri kapena kuona kuti sakufunikira thandizo la Mulungu. Ndipotu Yehova anatchula Yobu kuti “mtumiki wanga” ndipo anati: “Iyetu ndi munthu wopanda cholakwa ndi wowongoka mtima, woopa Mulungu ndi wopewa zoipa.”​—⁠Yobu 1:⁠8.

17 Koma pa nthawi yochepa kwambiri, zinthu pa moyo wa Yobu zinasinthiratu. Zinthu zake zonse zinawonongeka ndipo anakhumudwa kwambiri moti ankangolakalaka atafa. Tikudziwa kuti Satana ndi amene anayambitsa zonsezi pamene ananama kuti Yobu ankalambira Mulungu chifukwa chongofuna kupeza phindu basi. (Werengani Yobu 1:​9, 10.) Yehova sanangonyalanyaza zimene Satana ananena. Koma anapereka mwayi kwa Yobu kuti asonyeze zoti ankamutumikira chifukwa chomukonda ndi mtima wonse osati chifukwa chofuna kupeza phindu.

w19.02 5 ¶10

Pitirizani Kukhala ndi Mtima Wosagawanika

10 Satana amatsutsanso zoti aliyense wa ife angapitirize kukhala ndi mtima wosagawanika. Kodi zimenezi zimakukhudzani bwanji inuyo? Tingati Satana amanena kuti simukonda kwenikweni Yehova Mulungu, mudzasiya kumutumikira moyo wanu ukadzakhala pa ngozi komanso simungapitirize kukhala ndi mtima wosagawanika. (Yobu 2:​4, 5; Chiv. 12:10) Kodi mumamva bwanji mukaganizira zimenezi? Muyenera kuti mumakhumudwa. Koma taganizirani mfundo iyi: Yehova amakukhulupirirani kwambiri moti amalola kuti Satana akuyeseni. Iye amadziwa kuti mukhoza kukhalabe ndi mtima wosagawanika ndipo mudzasonyeza kuti Satana ndi wabodza. Komanso Yehova walonjeza kuti adzakuthandizani kuchita zimenezi. (Aheb. 13:⁠6) Kunena zoona, ndi mwayi waukulu kwambiri kuti Yehova amatikhulupirira chonchi. Kukhala ndi mtima wosagawanika n’kofunika kwambiri. Zili choncho chifukwa timasonyeza kuti Satana ndi wabodza, timalemekeza dzina labwino la Atate wathu komanso timasonyeza kuti tili kumbali ya ulamuliro wake. Koma kodi n’chiyani chingatithandize kukhala ndi mtima wosagawanika?

Mfundo Zothandiza

w21.04 11 ¶9

Zimene Tingaphunzire pa Mawu Omaliza a Yesu

9 Kodi Yesu ananena kuti chiyani? Atatsala pang’ono kufa, Yesu ananena kuti: “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?” (Mat. 27:46) Baibulo silifotokoza chifukwa chake Yesu ananena zimenezi. Koma tiyeni tione zimene tingaphunzire pa mawu amenewa. Ponena mawuwa Yesu anakwaniritsa ulosi wopezeka pa Salimo 22:⁠1. Komanso mawuwa akusonyeza kuti Yehova ‘sanam’tchinge’ kapena kum’teteza Mwana wakeyu. (Yobu 1:10) Yesu ankadziwa kuti Atate ake analola kuti adani ake amuyese mokwanira mpaka imfa yake, ndipo palibe munthu amene anakumana ndi mayesero amene iye anakumana nawo. Kuonjezera pamenepo, mawuwa akusonyeza kuti Yesu sanapalamule mlandu uliwonse woti mpaka ankafunika kuphedwa.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

w22.01 11-12 ¶11-14

Zimene Tingaphunzire Kuchokera kwa Mng’ono Wake wa Yesu

11 Yakobo ankapereka malangizo mosapita m’mbali. Malinga ndi kalata yake, n’zoonekeratu kuti Yakobo ankadziwa mavuto amene Akhristu anzake ankakumana nawo ndipo anawapatsa malangizo omveka bwino omwe akanawathandiza. Mwachitsanzo Akhristu ena ankachedwa kutsatira malangizo. (Yak. 1:22) Ena ankakondera anthu olemera. (Yak. 2:​1-3) Ndiye panalinso ena omwe ankavutika kulamulira lilime lawo. (Yak. 3:​8-10) Akhristuwa anali ndi mavuto akulu koma Yakobo ankakhulupirira kuti iwo akhoza kusintha. Iye anawapatsa malangizo mokoma mtima koma mosapita m’mbali ndipo analimbikitsa Akhristu omwe ankakumana ndi mavutowo kuti azipempha akulu kuti awathandize.​—⁠Werengani Yakobo 5:​13-15.

12 Zimene tikuphunzirapo: Tizipereka malangizo mosapita m’mbali ndipo tiziona ena moyenera. N’kutheka kuti ambiri amene tikuphunzira nawo Baibulo zingamawavute kutsatira malangizo ake. (Yak. 4:​1-4) Mwina zingawatengere nthawi kuti asiye makhalidwe oipa n’kuyamba kukhala ndi makhalidwe ngati a Khristu. Mofanana ndi Yakobo tiyenera kukhala olimba mtima kuti tizitha kuuza ophunzira Baibulo zimene ayenera kusintha. Tiyeneranso kukhala ndi maganizo oyenera n’kumakhulupirira kuti Yehova adzakokera kwa iye anthu amene ndi odzichepetsa ndipo adzawapatsa mphamvu zowathandiza kusintha zinthu pa moyo wawo.​—⁠Yak. 4:⁠10.

13 Yakobo ankadziona moyenera. Yakobo sankaona kuti ndi wofunika kwambiri kuposa abale ndi alongo ake chifukwa cha banja limene anakulira komanso utumiki umene anapatsidwa. Iye ankatchula Akhristu anzake kuti “abale anga okondedwa.” (Yak. 1:​16, 19; 2:⁠5) Sankachititsa anthu ena kuganiza kuti iyeyo salakwitsa zinthu. M’malo mwake iye anadziphatikizamo pamene ananena kuti: “Tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.”​—⁠Werengani Yakobo 3:⁠2.

14 Zimene tikuphunzirapo: Tizikumbukira kuti tonsefe ndi ochimwa. Sitiyenera kuganiza kuti timaposa mwa njira ina yake anthu amene timawaphunzitsa. Chifukwa chiyani? Chifukwa ngati tingachititse wophunzira Baibulo wathu kuona kuti sitilakwitsa kalikonse, angayambe kuganiza kuti sangakwanitse kutsatira malangizo a Mulungu. Koma ngati moona mtima tingamufotokozere kuti si nthawi zonse pamene zinali zophweka kuti tizitsatira mfundo za m’Malemba, komanso kumuuza mmene Yehova watithandizira kusintha moyo wathu, tingamuthandize kuona kuti nayenso angathe kutumikira Yehova.

OCTOBER 9-​15

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 4-5

“Samalani ndi Nkhani Zabodza”

it-1 713 ¶11

Elifazi

2. wl19Mmodzi mwa anzake atatu a Yobu. (Yob 2:11) Anali wa mtundu wa Atemani ndipo zimaoneka kuti anali mwana wa mwana woyamba kubadwa wa Esau zomwe zikutanthauza kuti anali mbadwa ya Abulahamu komanso anali pachibale chapatali ndi Yobu. Iye komanso anthu amtundu wake ankadzitama chifukwa cha nzeru zawo. (Yer 49:⁠7) Pa anzake atatu a Yobu omwe anabwera kudzamulimbikitsa aja, zimaoneka kuti Elifazi anali wofunika, ndipo n’kutheka kuti iye anali wamkulu pa onsewo. Iye ndi amene anayambirira kulankhula ndipo analankhula mawu ambiri.

w05 9/15 26 ¶2

Pewani Maganizo Olakwika

Pokumbukira masomphenya odabwitsa amene anaona nthawi ina, Elifazi anati: “Panapita mzimu pamaso panga; tsitsi la thupi langa lidati nyau nyau.” (Yobu 4:15) Kodi ndi mzimu wotani umene unam’sokoneza maganizo Elifazi? Mawu osalimbikitsa amene ananena pambuyo ponena zimenezi amasonyeza kuti mzimuwo sunali mzimu wochokera kwa Mulungu. (Yobu 4:​17, 18) Mzimu umenewu unali chiwanda. N’chifukwa chaketu Yehova anadzudzula Elifazi ndi anzake awiri aja kuti ananena zabodza. (Yobu 42:⁠7) Inde Elifazi anasokonezedwa maganizo ndi ziwanda. Mawu amene ananena anasonyeza kuti maganizo ake sanali maganizo a Mulungu.

w10 2/15 19 ¶5-6

Musalole Mabodza a Satana Kukusokonezani Maganizo

Satana anagwiritsira ntchito Elifazi, mmodzi wa anthu atatu amene anapita kukazonda Yobu, kunena mfundo yabodza yakuti anthu sangalimbelimbe akakumana ndi ziyeso za Satana. Iye ananena kuti anthu ndi ‘okhala m’nyumba zadothi,’ ndipo anauza Yobu kuti ‘maziko awo ali m’fumbi. Angothudzulidwa ngati gulugufe. Kuyambira m’mawa kufikira madzulo athudzuka; awonongeka kosatha, osasamalirako munthu.’​—⁠Yobu 4:​19, 20.

wl19Malemba ena amayerekezera anthu ndi “zotengera zadothi,” zomwe sizichedwa kusweka. (2 Akor. 4:⁠7) N’zoona kuti uchimo umene tinatengera kwa makolo athu oyambirira komanso kupanda ungwiro zimachititsa kuti tikhale ofooka. (Aroma 5:12) Moti patokha sitingathe kulimbana ndi Satana. Komabe, poti ndife Akhristu, Yehova amatithandiza. Ngakhale kuti tili ndi zofooka, ndife amtengo wapatali kwambiri pamaso pa Mulungu. (Yes. 43:⁠4) Komanso Yehova amapereka mzimu woyera kwa amene am’pempha. (Luka 11:13) Mzimu wake ungathe kutipatsa “mphamvu yoposa yachibadwa,” yomwe ingatithandize kulimbana ndi mavuto aliwonse amene Satana amatibweretsera. (2 Akor. 4:7; Afil. 4:13) Tikamayesetsa kulimbana ndi Mdyerekezi, n’kukhala “olimba m’chikhulupiriro,” Mulungu angathe kutilimbitsa n’kukhala amphamvu. (1 Pet. 5:​8-10) Motero sitiyenera kumuopa Satana Mdyerekezi.

mrt 32 ¶13-​17

Samalani Kuti Musamapusitsike Ndi Nkhani Zabodza

● Muziganizira kumene nkhaniyo yachokera komanso zimene imanena

Zimene Baibulo limanena: “Tsimikizirani zinthu zonse.”​—⁠1 Atesalonika 5:⁠21.

wl19Musanakhulupirire nkhani inayake kapena kuitumiza, ngakhale imene ndi yodziwika kapena imene yalengezedwa pa nyuzi, mutsimikizire kaye kuti ndi yoona. Kodi mungachite bwanji zimenezi?

wl19Muziganizira ngati nkhani yachokera kwa munthu kapena kumalo odalirika. Makampani kapena mabungwe ofalitsa nkhani akhoza kusintha nkhanizo chifukwa cha maganizo awo andale kapena okhudza zinthu zina. Muziyerekezera nkhani zochokera kwa ofalitsa nkhani ena ndi nkhani zomwezo zochokera kwa ofalitsa nkhani anzawo. Nthawi zina, anzanu angakutumizireni mameseji abodza mosadziwa. Choncho musamakhulupirire nkhani iliyonse kusiyapo ngati mungadziwe kumene yachokera.

Muzitsimikiziranso ngati zimene nkhani imanena n’zatsopano komanso zoona. Muziona madeti, mfundo zotsimikizirika komanso umboni wamphamvu wosonyeza kuti nkhaniyo ndi yoona. Muzisamala kwambiri ngati nkhani ikufotokoza zinthu zovuta m’njira yosavuta kwambiri kapena ngati yalembedwa mokufikani pamtima kwambiri.

Mfundo Zothandiza

w03 5/15 22 ¶5-6

Khalani Okhazikika Kuti Mudzapambane pa Mpikisano wa Moyo

Kukhala m’gulu la padziko lonse la olambira oona kungatilimbitse kwambiri. Ndi dalitso lalikulu kukhala pakati pa abale achikondi a padziko lonse amenewa! (1 Petro 2:17) Ndipo ngakhale ifeyo tikhoza kulimbitsanso okhulupirira anzathu.

Taganizirani ntchito zothandiza zimene munthu wolungama Yobu ankachita. Ngakhale Elifazi, amene anali wotonthoza wabodza, anavomereza kuti: “Mawu ako anachirikiza iye amene akadagwa, walimbitsanso maondo otewa.” (Yobu 4:⁠4) Kodi ife timathandiza anzathu? Aliyense wa ife ali ndi udindo wothandiza abale ndi alongo athu auzimu kuti apirire potumikira Mulungu. Tikamachita nawo zinthu, tizichita mogwirizana ndi mawu awa: “Limbitsani manja opanda mphamvu, ndi kulimbitsa maondo agwedegwede.” (Yesaya 35:⁠3) Choncho, bwanji osakhala n’cholinga cholimbikitsa Mkhristu mnzanu mmodzi kapena awiri nthawi iliyonse imene mwakumana? (Ahebri 10:​24, 25) Mawu owalimbikitsa ndi owayamikira chifukwa chopitirizabe kusangalatsa Yehova angawathandize kuti akhale okhazikika kuti adzapambane pa mpikisano wa moyo.

OCTOBER 16-​22

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 6-7

“Moyo Ukafika Povuta”

w06 3/15 14 ¶10

Mfundo Zazikulu za M’buku la Yobu

7:1; 14:14—⁠Kodi mawu oti “nkhondo” kapena “ntchito” [ntchito yokakamiza, NW ] akuimira chiyani? Yobu anali atavutika kwambiri moti moyo wake ankangouna ngati ntchito yokakamiza. (Yobu 10:17) Popeza kuti munthu sakhala mu Shelo mwa kufuna kwake, kuchokera panthawi imene wamwalira n’kufika panthawi imene adzaukitsidwe, Yobu anaiyerekezera ndi ntchito yochita kukakamizidwa.

w20.12 16 ¶1

Yehova Amapulumutsa Anthu a Mtima Wosweka

MOYO wathu ndi waufupi komanso “wodzadza ndi masautso.” (Yobu 14:⁠1) Zimenezi nthawi zina zimachititsa kuti tikhale osweka mtima. Atumiki ena a Yehova m’mbuyomu zimenezi zinawachitikirapo, moti ena anafika poona kuti bola angofa. (1 Maf. 19:​2-4; Yobu 3:​1-3, 11; 7:​15, 16) Koma nthawi zonse Yehova amene ankamukhulupirira ankawalimbikitsa komanso kuwapatsa mphamvu. Nkhani za anthu amenewa zinalembedwa kuti zizitilimbikitsa komanso kutilangiza.​—⁠Aroma 15:⁠4.

g 1/12 16 ¶2-4

Kodi Mungatani Mukakhala ndi Maganizo Ofuna Kudzipha?

Ngakhale kuti mungamaone kuti mavuto amene mukukumana nawo ndi osapiririka, muzikumbukira kuti siinu nokha amene mukukumana ndi mavuto komanso pafupifupi aliyense akulimbana ndi vuto linalake. Baibulo limanena kuti: “Chilengedwe chonse chikubuula limodzi ndi kumva zowawa mpaka pano.” (Aroma 8:22) Ngakhale kuti panopa mungamaone kuti mavuto anuwo sadzatha, zoona zake n’zakuti zinthu zimasintha pakapita nthawi. Ndiyeno kodi panopa muyenera kuchita chiyani?

Uzani Mnzanu Wodalirika Mavuto Amene Mukukumana Nawo. Baibulo limanena kuti: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo ilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.” (Miyambo 17:17) Baibulo limasonyeza kuti Yobu, yemwe anali munthu wokhulupirika, ankafotokozera anzake mavuto ake. Pa nthawi yomwe ‘ankanyansidwa ndi moyo wake,’ iye ananena kuti: “Ndilankhula mwamphamvu za nkhawa zanga. Ndilankhula chifukwa cha kuwawa kwa moyo wanga.” (Yobu 10:⁠1) Mukauzako anthu ena za mavuto anu, mumamvako bwino mumtima ndipo zingakuthandizeni kuti muyambe kuona mavuto anuwo mwanjira ina.

Pempherani kwa Yehova. Anthu ena amaganiza kuti pemphero limangothandiza anthu kuti azingomvako bwino pang’ono, koma Baibulo limafotokoza zosiyana ndi zimenezo. Lemba la Salimo 65:2 limati Yehova Mulungu ndi “Wakumva pemphero” komanso lemba la 1 Petulo 5:7 limati: “Amakuderani nkhawa.” Baibulo limanena mobwerezabwereza za kufunika kodalira Mulungu. Taonani malemba otsatirawa:

“Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalire luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukira m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola njira zako.”—⁠MIYAMBO 3:​5, 6.

“Anthu amene amamuopa [Yehova] adzawachitira zokhumba zawo, adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo ndipo adzawapulumutsa.”​​—⁠SALIMO 145:⁠19.

“Ifetu timamudalira kuti chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.”​​—⁠1 YOHANE 5:⁠14.

“Yehova amakhala kutali ndi anthu oipa, koma amamva pemphero la anthu olungama.”​​—⁠MIYAMBO 15:⁠29.

Mukamauza Mulungu mavuto amene mukukumana nawo, iye adzakuthandizani. N’chifukwa chake Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Mukhulupirireni nthawi zonse, . . . Mukhuthulireni za mumtima mwanu.”​​—⁠Salimo 62:⁠8.

Mfundo Zothandiza

w20.04 16 ¶10

Tizimvetsera Anthu, Kuwadziwa Komanso Kuwachitira Chifundo

10 Nafenso tiyenera kutsanzira Yehova poyesetsa kuwamvetsa anzathu. Tiziyesetsa kuti tiwadziwe bwino abale ndi alongo athu. Tizicheza nawo misonkhano isanayambe komanso ikatha, tiziyenda nawo mu utumiki ndipo ngati n’kotheka, tiziwaitanira chakudya. Mukatero mwina mudzadabwa kuona kuti mlongo amene amaoneka ngati wosachezeka ali ndi vuto la manyazi, m’bale amene amaoneka ngati wokonda ndalama ali ndi mtima wochereza kapena banja limene limachedwa kumisonkhano limatsutsidwa. (Yobu 6:29) N’zoona kuti tiyenera kupewa ‘kulowerera nkhani za eni.’ (1 Tim. 5:13) Koma ndi bwino kudziwa zinthu zina zokhudza abale ndi alongo athu komanso zimene akumana nazo pa moyo wawo.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

w22.01 12-13 ¶15-18

Zimene Tingaphunzire Kuchokera kwa Mng’ono Wake wa Yesu

15 Yakobo ankagwiritsa ntchito mafanizo ogwira mtima. N’zosakayikitsa kuti mzimu woyera unkamuthandiza, koma n’kutheka kuti iye anaphunzira mmene angaphunzitsire mwaluso poona mafanizo amene mchimwene wake Yesu ankagwiritsa ntchito. Mafanizo amene Yakobo anagwiritsa ntchito m’kalata yake ndi osavuta kumva ndipo mfundo zake ndi zomveka bwino.​—⁠Werengani Yakobo 3:​2-6, 10-12.

16 Zimene tikuphunzirapo: Tizigwiritsa ntchito mafanizo ogwira mtima. Mukamagwiritsa ntchito bwino mafanizo mumathandiza omvera kuti aziona m’maganizo mwawo zimene akuphunzirazo. Zimene amaona m’maganizo mwawozo zimawathandiza kuti azikumbukira mosavuta mfundo za choonadi za m’Baibulo. Yesu anali katswiri pankhani yogwiritsa ntchito mafanizo ndipo mchimwene wake Yakobo anatengera chitsanzo chake. Tiyeni tione fanizo limodzi limene Yakobo anagwiritsa ntchito ndiponso chifukwa chake tinganene kuti linali labwino kwambiri.

17 Werengani Yakobo 1:​22-25. Fanizo la Yakobo lonena za galasi ndi logwira mtima pazifukwa zingapo. M’fanizoli iye ankafuna kuphunzitsa mfundo yofunika kwambiri yakuti, kuti tipindule ndi Mawu a Mulungu tiyenera kuchita zambiri kuposa kungowawerenga. Tifunika kumachita zinthu mogwirizana ndi zimene timawerengazo. Yakobo anagwiritsa ntchito fanizo la munthu wodziyang’anira pagalasi lomwe omvera ake sakanavutika kulimvetsa. Kodi mfundo yafanizoli inali yotani? Mfundo yake ndi yakuti kungakhale kupusa ngati munthu atadziyang’anira pagalasi n’kuona penapake pofunika kukonza koma osakonzapo. Mofanana ndi zimenezi, kungakhalenso kupusa ngati titawerenga Mawu a Mulungu n’kuona kuti tifunika kusintha makhalidwe athu koma osachitapo kanthu.

18 Mukamagwiritsa ntchito mafanizo mungatsanzire Yakobo pochita zinthu zitatu izi: (1) Muzionetsetsa kuti fanizo lanu likugwirizana ndi mfundo imene mukufotokoza. (2) Muzigwiritsa ntchito fanizo limene omvera anu angalimvetse mosavuta. (3) Muzifotokoza mfundo ya fanizolo momveka bwino. Ngati zimakuvutani kuganizira mafanizo oyenera oti mugwiritse ntchito, mungafufuze mu Watch Tower Publications Index. Pamutu wakuti “Illustrations,” mungapezepo zitsanzo zambiri za mafanizo amene mungagwiritse ntchito. Komabe muzikumbukira kuti mafanizo ali ngati maikolofoni ndipo amangothandiza kuti mfundo yanu imveke bwino. Choncho muzigwiritsa ntchito mafanizo pa mfundo zofunika zokhazo zimene mukufuna kuphunzitsa. N’zoona kuti cholinga chathu chachikulu pokulitsa luso lathu lophunzitsa, sikuchititsa ena kuti aziganizira kwambiri za ifeyo koma kuthandiza anthu ambiri mmene tingathere kuti akhale mbali ya banja losangalala la Yehova.

OCTOBER 23-​29

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 8-​10

“Chikondi Chokhulupirika cha Mulungu Chimatiteteza ku Mabodza a Satana”

w15 7/1 12 ¶3

Kodi Anthufe Tingasangalatsedi Mulungu?

Yobu anakumana ndi mavuto ambiri motsatizana ndipo mavutowa ankaoneka kuti samayenera kukumana nawo. Izi zinamuchititsa kuti aganize molakwika n’kumaona kuti Mulungu analibe nazo ntchito zakuti iyeyo ndi munthu wokhulupirika. (Yobu 9:​20-22) Yobu ankadziona kuti anali munthu wolungama kwambiri moti anthu ena ankaganiza kuti Yobuyo akunena kuti ndi wolungama kuposa Mulungu.​—⁠Yobu 32:​1, 2; 35:​1, 2.

w21.11 6 ¶14

Kodi Timapindula Bwanji ndi Chikondi Chokhulupirika cha Yehova?

14 Chikondi chokhulupirika cha Mulungu chimatiteteza mwauzimu. Popemphera kwa Yehova, Davide anati: “Ndinu malo anga obisalamo, mudzanditeteza ku masautso. Mudzachititsa kuti chisangalalo chindizungulire pamene mukundipulumutsa. . . . Wokhulupirira Yehova amazunguliridwa ndi kukoma mtima kosatha.” (Sal. 32:​7, 10) Mofanana ndi mipanda imene inkateteza mizinda kalelo, chikondi chokhulupirika cha Yehova chimatitchinga n’kumatiteteza ku zinthu zimene zingawononge ubwenzi wathu ndi iye. Kuwonjezera pamenepo, chikondi chimenechi chimamuchititsa kuti atikokere kwa iye.​—⁠Yer. 31:⁠3.

Mfundo Zothandiza

w10 10/15 6-7 ¶19-​20

“Ndani Akudziwa Maganizo a Yehova?”

19 Kodi taphunzira chiyani pa nkhani ya “maganizo a Yehova”? Tiyenera kulola kuti Mawu a Mulungu azitithandiza kudziwa bwino maganizo a Yehova. Popeza kuti anthufe sitidziwa zambiri, tisamaweruze Yehova malinga ndi mfundo ndiponso maganizo amene timayendera. Yobu anati: “[Mulungu] si munthu ngati ine kuti ndimuyankhe, kapena kuti tizengane mlandu.” (Yobu 9:32) Mofanana ndi Yobu tikayamba kudziwa bwino maganizo a Yehova tidzafuula kuti: “Zimenezi ndi kambali kakang’ono chabe ka zochita zake, ndipo timangomva kunong’ona kwapansipansi kwa mawu ake. Koma kodi mabingu ake amphamvu, angawamvetse ndani?”​—⁠Yobu 26:⁠14.

20 Tikamawerenga Malemba, kodi tiyenera kutani ngati tapeza nkhani yovuta kuimvetsa makamaka yokhudza mmene Yehova amaganizira? Ngati tafufuza nkhaniyo koma osapeza yankho lomveka bwino, tiyenera kuona kuti umenewu ndi mwayi wathu wosonyeza kuti timakhulupirira kwambiri Yehova. Tisaiwale kuti mfundo zina zimatithandiza kusonyeza kuti timakhulupirira kuti Yehova ali ndi makhalidwe abwino. Tiyeni tikhale odzichepetsa n’kuvomereza kuti sitingamvetse zochita zake zonse. (Mlal. 11:⁠5) Izi zidzatithandiza kuvomereza mawu a mtumwi Paulo akuti: “Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri. Nzeru zake n’zozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri. Ziweruzo zake ndi zosasanthulika, ndipo ndani angatulukire njira zake? Pakuti ‘ndani akudziwa maganizo a Yehova, kapena ndani angakhale phungu wake?’ Kapenanso, ‘Ndani anayamba kumupatsa kanthu, kuti amubwezere?’ Chifukwa zinthu zonse zimachokera kwa iye ndipo iye ndi amene anazipanga ndiponso ndi zake. Ulemerero ukhale wake kwamuyaya. Ame.”​​—⁠Aroma 11:​33-36.

OCTOBER 30–NOVEMBER 5

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOBU 11-​12

“Njira Zitatu Zomwe Tingapezere Nzeru N’kumazigwiritsa Ntchito”

w09 4/15 6 ¶17

Yobu Analemekeza Dzina la Yehova

Kodi n’chiyani chinamuthandiza Yobu kusungabe umphumphu wake? N’zodziwikiratu kuti iye anali atalimbitsa kale ubwenzi wake ndi Yehova masoka asanamugwere. Ngakhale kuti tilibe umboni wosonyeza kuti Yobu ankadziwa kuti Satana anali atatsutsa Yehova, iye anatsimikiza mtima kukhalabe wokhulupirika. Iye anati: “Mpaka kufa ine sinditaya ungwiro [“umphumphu,” NW ] wanga.” (Yobu 27:⁠5) Kodi Yobu anachita chiyani kuti akhale pa ubwenzi wolimba choncho ndi Mulungu? Mosakayikira, iye anamva zimene Mulungu anachitira Abulahamu, Isake ndi Yakobo omwe anali abale ake ndipo ankazikhulupirira. Ndiponso iye anaphunzira za makhalidwe ambiri a Yehova poona chilengedwe.​​—⁠Werengani Yobu 12:​7-9, 13, 16.

w21.06 10 ¶10-​12

Yehova Ali Nanu, Simuli Nokha

10 Muzigwirizana ndi Akhristu okhulupirika. Muzipeza anzanu mumpingo omwe mungaphunzire zinthu kwa iwo ngakhale mutakhala kuti mukusiyana msinkhu komanso kochokera. Baibulo limatikumbutsa kuti okalamba “amakhala ndi nzeru.” (Yobu 12:12) Achikulire angaphunzirenso zambiri kuchokera kwa achinyamata okhulupirika. Davide anali wamng’ono poyerekezera ndi Yonatani koma zimenezi sizinachititse kuti asakhale mabwenzi. (1 Sam. 18:⁠1) Iwo ankathandizana potumikira Yehova ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto aakulu. (1 Sam. 23:​16-18) Mlongo wina dzina lake Irina, amene m’banja lawo alipo yekha wa Mboni ananena kuti: “Abale ndi alongo akhoza kukhala ngati makolo athu komanso achibale athu enieni. Yehova akhoza kuwagwiritsa ntchito kuti azitithandiza.”

11 Kupeza anzanu atsopano si kophweka makamaka mukakhala kuti ndinu amanyazi. Mlongo wina dzina lake Ratna, yemwe ndi wamanyazi ndipo anaphunzira choonadi ngakhale kuti ankatsutsidwa, anafotokoza kuti: “Ndinkayenera kuvomereza kuti ndinkafunika kuthandizidwa ndi abale ndi alongo mumpingo.” Zikhoza kukhala zovuta kuti mufotokozere munthu wina mmene mukumvera, koma mukamumasukira zingachititse kuti muyambe kugwirizana. Anzanu amafuna kukulimbikitsani komanso kukuthandizani, koma mumafunika kuti muwafotokozere kuti adziwe mmene angakuthandizireni.

12 Njira imodzi imene ingakuthandizeni ndi kulalikira ndi Akhristu ena. Carol yemwe tamutchula kale uja anati: “Ndapeza anzanga ambiri abwino polalikira ndi alongo ena komanso pogwira nawo ntchito zina m’gulu la Mulungu. Pa zaka zonsezi Yehova wakhala akundithandiza pogwiritsa ntchito anzangawa.” Kugwirizana ndi Akhristu okhulupirika n’kothandiza kwambiri. Yehova amagwiritsa ntchito anzanu amenewa pokuthandizani kulimbana ndi maganizo ofooketsa, monga odziona kuti muli nokhanokha.​—⁠Miy. 17:⁠17.

it-2 1190 ¶2

Nzeru

Nzeru za Mulungu. Yehova ndi Mulungu ‘yekhayo amene ndi wanzeru’ ndipo nzeru zake ndi zambiri. (Aro 16:27; Chv 7:12) Nzeru zimayendera limodzi ndi kudziwa zolondola ndipo popeza Yehova ndi Mlengi, yemwe wakhalako “kuyambira kalekale mpaka kalekale” (Sl 90:​1, 2), iye yekha ndi amene amadziwa zinthu zonse zokhudza chilengedwe komanso mbiri yake yonse. Malamulo a m’chilengedwe, mmene zinthu zimayendera komanso malamulo amene anthu amagwiritsa ntchito akafuna kufufuza zinthu zatsopano, zonsezi zinapangidwa ndi Mulungu. Pakanakhala kuti zinthu zimenezi panalibe, sibwenzi anthu atapeza chilichonse chokhudza chilengedwe. (Yob 38:​34-38; Sl 104:24; Miy 3:19; Yer 10:​12, 13) Kunena zoona, mfundo zake za makhalidwe abwino n’zofunika kwambiri kuti zinthu ziziyenda bwino, kuti anthu azisankha zinthu mwanzeru komanso kuti anthu azikhala ndi moyo wabwino. (De 32:​4-6) Palibe chilichonse chimene iye sachimvetsa. (Yes 40:​13, 14) Ngakhale kuti nthawi zina iye amalola kuti zinthu zosemphana ndi mfundo zake zolungama ziyambe kuchitika mwinanso kukhalitsa kwa kanthawi, ndi iye yekha amene akudziwa mmene zinthu za m’tsogolo zichitikire kuti zigwirizane ndi cholinga chake ndipo “adzakwaniritsadi” mawu onse amene analankhula.​​—⁠Yes 55:​8-11; 46:​9-11.

Mfundo Zothandiza

w08 8/1 11 ¶5

▪ ‘Kodi ndimamvetsa tanthauzo la zimene akunena?’ Lemba la Yobu 12:11 (Malembo Oyera) limati: “Kodi khutu silizindikira mawu? Kodi m’kamwa simulawa zakudya?” Mosiyana ndi poyamba, muyenera ‘kuzindikira’ tanthauzo lenileni la zimene mwana wanu akunena. Achinyamata amakonda kukokomeza kwambiri zinthu moti akamafotokoza vuto linalake amalankhula ngati kuti limachitika nthawi zonse. Mwachitsanzo, mwana wanu anganene kuti: “Inu nthawi zonse mumanditenga ngati kamwana.” Kapena kuti: “Simumandimvetsa kuyambira kale.” M’malo molimbana ndi mawu amene wanena akuti “nthawi zonse” kapena akuti “kuyambira kale,” ndi bwino kudziwa zimene mwanayo akutanthauza. Mwachitsanzo mawu akuti “Inu nthawi zonse mumanditenga ngati kamwana,” angatanthauze kuti “Ndikuona kuti simumandikhulupirira.” Ndipo mawu akuti “Simumandimvetsa kuyambira kale,” angatanthauze kuti “Ndikufuna kukuuzani mmene ndikumvera.” Yesetsani kumvetsa tanthauzo la zimene mwana wanu akunena.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena