Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • th phunziro 13 tsamba 16
  • Kusonyeza Kuti Nkhaniyo Ndi Yothandiza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusonyeza Kuti Nkhaniyo Ndi Yothandiza
  • Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Nkhani Yofanana
  • Mawu Oyamba Abwino
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Kuwafika Pamtima Anthu
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Kulankhula ndi Mtima Wonse
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Nkhani Yophunzitsadi Anthu
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
Onani Zambiri
Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
th phunziro 13 tsamba 16

PHUNZIRO 13

Kusonyeza Kuti Nkhaniyo Ndi Yothandiza

Lemba

Miyambo 3:21

MFUNDO YAIKULU: Thandizani anthu kudziwa mmene mfundo zimene mukuphunzitsa zingawathandizire ndiponso zimene angachite potsatira zimene mukuphunzitsazo.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Muziganizira anthu. Muzidzifunsa kuti, Kodi nkhani yangayi ingathandize bwanji anthuwa, nanga mbali zimene zingawathandize kwambiri ndi ziti?

  • Munkhani yanu yonse, muzithandiza anthu kudziwa zoyenera kuchita. Mukangoyamba nkhani yanu, aliyense azizindikira kuti, ‘Nkhaniyitu indithandiza.’ Mukatchula mfundo yaikulu iliyonse, muziwasonyeza mmene angaigwiritsire ntchito. Muzipewa kukamba nkhani mongolambalala popanda kusonyeza zoyenera kuchita.

    Mfundo yothandiza

    Muzifotokoza mmene anthu angagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulo koma muzichita zimenezi mwachikondi ndiponso mokoma mtima. Musamachititse anthu kuganiza kuti akulakwitsa zinazake koma muziwathandiza kuti awonjezere chikondi ndi chikhulupiriro ndipo musamakayikire kuti azichita zinthu zoyenera.

MU UTUMIKI

Mukamakonzekera ulaliki muziganizira nkhani zimene zangochitika kumene komanso zimene anthu a m’gawo lanu angafune kumva. Muzisintha ulaliki wanu kuti ugwirizane ndi mmene zinthu zilili pa moyo wawo. Muzifunsa mafunso amene angathandize munthu kufotokoza maganizo ake. Muzimvetsera pamene akufotokoza maganizo akewo ndipo muzisintha ulaliki wanu kuti ugwirizane ndi zimene akunenazo ngati pangafunike kutero.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena