PHUNZIRO 13
Zipembedzo Zabodza Zimaphunzitsa Zinthu Zonama Zokhudza Mulungu
Zipembedzo zimene zimati zimachita zinthu ndi kulankhula m’dzina la Mulungu, zakhala zikuchita zinthu zoipa zambiri. N’chifukwa chiyani zipembedzozi zimachita zimenezi? Zoona zake n’zakuti zipembedzozi ndi zabodza. Zimene zimaphunzitsa ndi kunena zimachititsa anthu kukhulupirira zabodza zokhudza Mulungu. Kodi zipembedzozi zimachita bwanji zimenezi? Kodi Mulungu amamva bwanji akamaona zimene zipembedzozi zimachita? Nanga kodi adzachita chiyani ndi zipembedzozi?
1. Kodi zimene zipembedzo zimaphunzitsa zimachititsa bwanji anthu kukhulupirira zabodza zokhudza Mulungu?
Zipembedzo zabodza zakhala ‘zikusinthanitsa choonadi chonena za Mulungu ndi bodza.’ (Aroma 1:25) Mwachitsanzo, zipembedzo zambiri sizimaphunzitsa anthu awo dzina la Mulungu. Komatu Baibulo limaphunzitsa kuti tiyenera kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu. (Aroma 10:13, 14) Atsogoleri ena azipembedzo amanena kuti chinachake choipa chikachitika, chimakhala kuti ndi cholinga cha Mulungu. Koma limeneli ndi bodza. Mulungu si amene amachititsa zinthu zoipa. (Werengani Yakobo 1:13.) N’zomvetsa chisoni kuti mabodza amene zipembedzozi zimaphunzitsa amachititsa kuti anthu asamakonde Mulungu.
2. Kodi zimene zipembedzo zabodza zimachita zimachititsa bwanji anthu kukhulupirira zinthu Zonama zokhudza Mulungu?
Mulungu ndi chikondi, koma n’zodabwitsa kuti zipembedzo zabodza zimachitira anthu zinthu zambiri zoipa pomwe Yehova sachita zimenezi. Baibulo limanena kuti “machimo ake [azipembedzo zabodza] aunjikana mpaka kumwamba.” (Chivumbulutso 18:5) Kwa zaka zambiri, zipembedzo zakhala zikuchita nawo ndale, kulimbikitsa nkhondo ndiponso kuchititsa kapena kuvomereza kuti anthu ambirimbiri aphedwe. Atsogoleri azipembedzo ena amafuna kulemera kwambiri ndipo amauza anthu a m’zipembedzo zawo kuti aziwapatsa ndalama. Zimene amachitazi ndi umboni wakuti Mulungu samudziwa ngakhale pang’ono, choncho alibe ufulu wonena kuti ndi atumiki ake.—Werengani 1 Yohane 4:8.
3. Kodi Mulungu amamva bwanji akamaona zimene zipembedzo zabodza zimachita?
Ngati inuyo mumakhumudwa ndi zimene zipembedzo zabodza zimachita, ndiye mukuganiza kuti Yehova amamva bwanji? Yehova amakonda anthu koma amadana ndi atsogoleri azipembedzo amene amaphunzitsa anthu zabodza zokhudza iyeyo komanso kuchitira zoipa anthu amene ali m’chipembedzo chawo. Choncho akulonjeza kuti zipembedzo zabodza zidzawonongedwa ndipo ‘sizidzapezekanso.’ (Chivumbulutso 18:21) Posachedwapa, Mulungu awononga zipembedzo zonse zabodza.—Chivumbulutso 18:8.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani kuti mudziwe zambiri zokhudza mmene Mulungu amamvera akaona zimene zipembedzo zabodza zimachita. Phunzirani zambiri zokhudza zimene zipembedzozi zachita komanso chifukwa chake zimenezi siziyenera kukuchititsani kusiya kuphunzira za Yehova.
4. Kodi Mulungu amavomereza zipembedzo zonse?
Anthu ambiri amakhulupirira kuti zipembedzo zonse zili ngati njira zosiyanasiyana zimene zimafikitsa anthu kwa Mulungu. Koma kodi zimenezi n’zoona? Werengani Mateyu 7:13, 14, kenako mukambirane funso ili:
Kodi Baibulo limanena zotani zokhudza njira yotsogolera anthu kumoyo?
Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali.
Kodi Baibulo limanena kuti pali zipembedzo zambiri zimene zimasangalatsa Mulungu?
5. Zimene zipembedzo zabodza zimachita sizisonyeza kuti Mulungu ndi wachikondi
Zipembedzo zakhala zikuchita zinthu zoipa zambiri zomwe zimachititsa anthu kuona kuti Mulungu alibe chikondi. Mwachitsanzo, zimalimbikitsa nkhondo komwe n’kulakwa kwakukulu. Kuti muone mmene zimachitira zimenezi, onerani VIDIYO. Kenako mukambirane mafunso otsatirawa.
Kodi matchalitchi ambiri anachita zotani pa nkhondo yachiwiri yapadziko lonse?
Kodi mukumva bwanji mukaganizira zimene anachitazi?
Werengani Yohane 13:34, 35 ndi 17:16. Kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi mukuganiza kuti Yehova amamva bwanji zipembedzo zikamathandiza nawo pa nkhondo?
Zipembedzo zabodza zimachita zinthu zoipa zambiri. Ndi zinthu ziti zimene mwaonapo zomwe zikusonyeza kuti zipembedzo zalephera kusonyeza chikondi cha Mulungu?
Zimene zipembedzo zabodza zimanena komanso kuchita sizisonyeza kuti Mulungu ndi wachikondi
6. Mulungu akufuna kuti anthu atuluke m’zipembedzo zabodza
Werengani Chivumbulutso 18:4,a kenako mukambirane funso ili:
Kodi mumamva bwanji mukaganizira zoti Mulungu akufuna kuthandiza anthu amene akhala akunamizidwa ndi zipembedzo zabodza?
7. Pitirizani kuphunzira zokhudza Mulungu woona
Zinthu zoipa zimene zipembedzo zabodza zimachita, zisakuchititseni kuti musiye kukhulupirira Mulungu n’kuyamba kumuona kuti ndi woipa. Taganizirani za mwana amene sakufuna kumvera bambo ake ndipo akusankha kuchoka pakhomo n’kukayamba kuchita makhalidwe oipa ambiri. Bambowo sakugwirizana ndi zochita za mwana wawoyo. N’chifukwa chiyani kungakhale kulakwa kuimba mlandu bambowo chifukwa cha zochita za mwanayo?
Kodi zingakhale zomveka kuimba mlandu Yehova n’kusiya kuphunzira za iyeyo chifukwa cha zoipa zimene zipembedzo zabodza zimachita?
ANTHU ENA AMANENA KUTI: “Sindikufuna kuphunzira za Mulungu chifukwa zipembedzo zayambitsa mavuto ambiri.”
Kodi inunso mumaona choncho?
N’chifukwa chiyani sitiyenera kusiya kukhulupirira Yehova chifukwa cha zochita za zipembedzo zabodza?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Zipembedzo zabodza zakhala zikunamiza anthu ponena za Mulungu pophunzitsa zinthu zabodza komanso kuchita zinthu zoipa kwambiri. Mulungu adzawononga zipembedzo zonse zabodza.
Kubwereza
Kodi mumamva bwanji mukaganizira zimene zipembedzo zabodza zakhala zikuphunzitsa ndi kuchita?
Kodi Yehova amamva bwanji ndi zimene zipembedzo zabodza zimachita?
Kodi Mulungu adzachita chiyani ndi zipembedzo zabodza?
ONANI ZINANSO
Onani njira ziwiri zosonyeza mmene zipembedzo zambiri zimachitira zinthu zimene sizisangalatsa Mulungu.
N’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti tizimulambira limodzi ndi anzathu?
Kodi Pali Vuto Ngati Munthu Atakhala Kuti Sali M’chipembedzo Chilichonse? (Nkhani yapawebusaiti)
Wansembe ankakayikira zimene chipembedzo chake chimachita. Koma zimenezi sizinamuchititse kusiya kuphunzira choonadi chokhudza Mulungu.
“N’chifukwa Chiyani Wansembe Anasiya Chipembedzo Chake?” (Galamukani!, February 2015)
Kwa zaka zambiri, zipembedzo zakhala zikuphunzitsa mabodza omwe amachititsa anthu kuona ngati Mulungu satikonda ndiponso ndi wankhanza. Dziwani zoona zake pa atatu mwa mabodza amenewa.
“Mabodza Amene Amalepheretsa Anthu Kukonda Mulungu” (Nsanja ya Olonda, November 1, 2013)
a Buku la Chivumbulutso limanena kuti mkazi yemwe amatchedwa Babulo Wamkulu amaimira zipembedzo zabodza. Kuti mudziwe chifukwa chake, onani Mawu Akumapeto 1.