NYIMBO 59
Tamandani Ya
Losindikizidwa
1. Titamande
Ya mokweza.
Amatipatsa zonse zabwino.
Tsiku lonse
Tim’tamande.
Ndi wachikondi ndi wamphamvunso
Ndipo tilengeze dzina lake.
2. Titamande
Ya chifukwa
Amatimva tikamapemphera.
Dzanja lake
Ndi lamphamvu.
Amalimbikitsa ofooka.
Timalengeza za mphamvu zake.
3. Titamande
Ya limodzi.
Iye ndi Mulungu wolungama.
Adzakonza Zolakwika
Ndipo tonse
tidzadalitsidwa.
Timutamande mosangalala.
(Onaninso Sal. 94:18, 19; 145:21; 147:1; 150:2; Mac. 17:25.)