PHUNZIRO 16
Kodi Yesu Anachita Zotani Ali Padzikoli?
Anthu ambiri akaganizira za Yesu amamukumbukira ngati mwana wakhanda atagonekedwa modyeramo ziweto. Ena amamukumbukira ngati mneneri wanzeru, pamene ena amakumbukira mmene anafera. Koma kodi kuphunzira zokhudza moyo wa Yesu ali padziko lapansi kungatithandize bwanji kumudziwa bwino? M’phunziroli tikambirana zinthu zina zofunika kwambiri zimene Yesu anachita komanso mmene zingakuthandizireni.
1. Kodi ntchito yofunika kwambiri imene Yesu ankagwira inali yotani?
Ntchito yofunika kwambiri yomwe Yesu ankagwira inali ‘yolengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.’ (Werengani Luka 4:43.) Iye ankalalikira uthenga wabwino wakuti Mulungu adzakhazikitsa ufumu, kapena kuti boma, lomwe lidzathetse mavuto onse amene anthu akukumana nawo padzikoli.a Yesu anagwira mwakhama ntchito youza anthu uthenga wolimbikitsawu kwa zaka zitatu ndi hafu.—Mateyu 9:35.
2. N’chifukwa chiyani Yesu ankachita zodabwitsa?
Baibulo limafotokoza kuti ‘Mulungu anagwiritsa ntchito Yesu pochita ntchito zamphamvu, zodabwitsa komanso zizindikiro.’ (Machitidwe 2:22) Mulungu anapatsa Yesu mphamvu zotha kulamulira mphepo, kudyetsa anthu masauzande ambirimbiri, kuchiritsa odwala, ngakhalenso kuukitsa anthu amene anamwalira. (Mateyu 8:23-27; 14:15-21; Maliko 6:56; Luka 7:11-17) Zodabwitsa zimene Yesu ankachita ndi umboni woti iye anachita kutumidwa ndi Mulungu komanso wakuti Yehova ali ndi mphamvu zothetsa mavuto athu onse.
3. Kodi tingaphunzire chiyani kwa Yesu?
Yesu ankamvera Yehova pa chilichonse. (Werengani Yohane 8:29.) Yesu ankachita chilichonse chimene Atate wake anamutuma. Iye ankachita zimenezi pa nthawi yonse yomwe anali ndi moyo padziko lapansi ngakhale kuti anthu ena ankafuna kumulepheretsa. Zimene anachitazi zikusonyeza kuti n’zotheka kuti anthu azitumikirabe Mulungu mokhulupirika ngakhale kuti akukumana ndi mavuto. Choncho, Yesu ‘anatisiyira chitsanzo kuti titsatire mapazi ake mosamala kwambiri.’—1 Petulo 2:21.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani kuti muone zimene Yesu ankachita kuti alalikire uthenga wabwino komanso mmene anachitira zodabwitsa.
4. Yesu ankalalikira uthenga wabwino
Yesu ankayenda maulendo ataliatali kwambiri m’misewu yafumbi, n’cholinga choti akalalikire uthenga wabwino kwa anthu ambiri. Werengani Luka 8:1, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi Yesu ankalalikira kwa anthu okhawo amene asonkhana kuti amvetsere ulaliki wake?
Kodi Yesu ankachita chiyani kuti afikire anthu kulikonse komwe ali?
Mulungu ananeneratu kuti Mesiya adzalalikira uthenga wabwino. Werengani Yesaya 61:1, 2, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi Yesu anakwaniritsa bwanji ulosi umenewu?
Kodi mukuona kuti masiku ano anthu akufunika kumva uthenga wabwinowu?
5. Yesu anaphunzitsa mfundo zothandiza
Kuwonjezera pa kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu Yesu ankaphunzitsa mfundo zothandiza. Tiyeni tikambirane zitsanzo zingapo za mfundo zimene Yesu anaphunzitsa pa ulaliki wina wotchuka umene umadziwika kuti Ulaliki Wapaphiri. Werengani Mateyu 6:14, 34 ndi 7:12, kenako mukambirane mafunso awa:
M’mavesiwa kodi Yesu anapereka malangizo othandiza ati?
Kodi mukuona kuti malangizo amenewa angatithandize masiku ano?
6. Yesu anachita zodabwitsa
Yehova anapatsa Yesu mphamvu kuti azichita zodabwitsa zambiri. Kuti muone chitsanzo chimodzi, werengani Maliko 5:25-34 kapena onerani VIDIYO. Kenako mukambirane mafunso otsatirawa.
Muvidiyoyi, kodi mayi wodwalayu ankakhulupirira chiyani?
N’chiyani chimene chikukusangalatsani mukaganizira chodabwitsa chimenechi?
Werengani Yohane 5:36, kenako mukambirane funso ili:
Kodi zodabwitsa zimene Yesu anachita ‘zinamuchitira umboni’ wotani?
Kodi mukudziwa?
Zinthu zambiri zokhudza moyo wa Yesu zimapezeka m’mabuku 4 a m’Baibulo amene amadziwika kuti Uthenga Wabwino. Mabuku ake ndi Mateyu, Maliko, Luka komanso Yohane. Aliyense wa olemba mabukuwa anafotokoza mfundo zokhudza Yesu m’njira zosiyanasiyana. Choncho tikamawerenga mabukuwa timamvetsa bwino zomwe zinachitika pa moyo wa Yesu.
MATEYU
ndi amene anayamba kulemba buku loyamba la Uthenga Wabwino. Bukuli limatiuza zambiri zimene Yesu anaphunzitsa makamaka zokhudza Ufumu wa Mulungu.
MALIKO
ndi amene analemba buku lalifupi kwambiri pa mabuku a Uthenga Wabwino. Bukuli limatiuza zinthu zambiri zochititsa chidwi.
LUKA
anafotokoza kuti Yesu ankaona kuti pemphero ndi lofunika kwambiri komanso kuti ankachita zinthu mwachifundo ndi akazi.
YOHANE
ndi amene anafotokoza makhalidwe ambiri a Yesu. Tikutero chifukwa chakuti analemba zinthu zambiri zomwe Yesu ankakambirana ndi anzake apamtima komanso anthu ena.
ANTHU ENA AMANENA KUTI: “Yesu anangokhala munthu wabwino basi.”
Kodi inuyo mukuganiza bwanji?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Yesu ankalalikira zokhudza Ufumu wa Mulungu, ankachita zodabwitsa komanso ankamvera Yehova pa chilichonse.
Kubwereza
Kodi ndi ntchito yofunika kwambiri iti imene Yesu ankagwira ali padziko lapansi?
Kodi zodabwitsa zimene Yesu anachita zinkasonyeza chiyani?
Kodi ndi mfundo zothandiza ziti zimene Yesu anaphunzitsa?
ONANI ZINANSO
Kodi nkhani imene Yesu ankakonda kukambirana ndi anthu inali yokhudza chiyani?
“Yesu Ankaona Kuti Ufumu wa Mulungu Ndi Wofunika Kwambiri” (Nsanja ya Olonda, October 1, 2014)
Fufuzani kuti muone chifukwa chake sitikayikira kuti Yesu anachitadi zodabwitsa.
“Kodi pa Zozizwitsa za Yesu Mungaphunzirepo Chiyani?” (Nsanja ya Olonda, July 15, 2004)
Werengani nkhaniyi kuti muone mmene munthu wina yemwe anali ndi khalidwe lodzikonda anasinthira potengera chitsanzo cha Yesu.
“Ndinali Munthu Wodzikonda Kwambiri” (Nsanja ya Olonda, October 1, 2014)
Onani zochitika zikuluzikulu zokhudza utumiki wa Yesu potengera nthawi imene zinachitikira.
a Nkhani yokhudza Ufumu wa Mulungu idzafotokozedwa bwino kwambiri m’phunziro 31 mpaka 33.