-
‘Tetezani Mtima Wanu’Nsanja ya Olonda—2012 | May 1
-
-
‘Tetezani Mtima Wanu’
Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova
MUTU WA LACHISANU
“Yehova Amaona Mmene Mtima Ulili”—1 SAMUELI 16:7.
MUTU WA LOWERUKA
“Pakamwa Pamalankhula Zosefukira Mumtima”—MATEYU 12:34.
MUTU WA LAMLUNGU
‘M’tumikireni Yehova Ndi Mtima Wathunthu’—1 MBIRI 28:9.
Baibulo limatchula mtima pafupifupi ka 1,000. Kawirikawiri Malemba akamanena za mtima, amanena mtima wophiphiritsira osati weniweni. Kodi mtima wophiphiritsira umenewu ndi chiyani? Nthawi zambiri mawu amenewa amatanthauza zimene munthu amaganiza, mmene amamvera komanso zimene amalakalaka.
N’chifukwa chiyani tiyenera kuteteza mtima wathu wophiphiritsira? Mulungu anauzira Mfumu Solomo kulemba kuti: “Uteteze mtima wako kuposa zonse zimene ziyenera kutetezedwa, pakuti mumtimamo ndiye muli akasupe a moyo.” (Miyambo 4:23) Kuti tikhale ndi moyo wabwino panopo komanso kuti tidzapeze moyo wosatha m’tsogolo zimadalira mmene mtima wathu wophiphiritsira ulili. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa Mulungu amaona zimene zili mumtima mwathu. (1 Samueli 16:7) Mulungu akafuna kudziwa kuti ndife munthu wotani amayang’ana “munthu wobisika wamumtima” kapena kuti zimene zili mumtima mwathu.—1 Petulo 3:4.
Ndiyeno kodi tingateteze bwanji mtima wathu? Funso limeneli lidzayankhidwa pa Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova. Msonkhano umenewu udzachitika padziko lonse lapansi kuyambira kumayambiriro a mwezi uno. Mukuitanidwa kuti mudzapezeke pa msonkhano umenewu kwa masiku onse atatu.a Zimene mudzaphunzire pa msonkhanowu zidzakuthandizani kuti muzichita zinthu zomwe zingakondweretse mtima wa Yehova Mulungu.—Miyambo 27:11.
-
-
Kodi Mungafune Kukuchezerani?Nsanja ya Olonda—2012 | May 1
-
-
Kodi Mungafune Kukuchezerani?
Ngakhale m’dziko lamavutoli, mungakhalebe osangalala podziwa zenizeni zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani ya Mulungu, Ufumu wake, ndi cholinga chimene iye ali nacho chakuti anthu adzakhale ndi moyo wabwino kwambiri. Ngati mukufuna kudziwa zambiri kapena kuti wina aziphunzira nanu Baibulo panyumba panu kwaulere, Pitani pa Webusaiti yawo pa Intaneti pa adiresi ya www.pr2711.com/ny.
-