Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr25 May tsamba 1-15
  • Malifalensi a “Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a “Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu”
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2025
  • Timitu
  • MAY 5-11
  • MAY 12-18
  • MAY 19-25
  • MAY 26–JUNE 1
  • JUNE 2-8
  • JUNE 9-15
  • JUNE 16-22
  • JUNE 23-29
  • JUNE 30–JULY 6
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2025
mwbr25 May tsamba 1-15

Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu

MAY 5-11

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 12

Kugwira Ntchito Mwakhama Kumapindulitsa

w16.06 31 ¶1

Khalidwe la Mtengo Wapatali Kuposa Dayamondi

Akhristu ena amavutika kwambiri kuti apeze zofunika pa moyo. Koma m’malo mochita chinyengo, amagwira ntchito mwakhama. Apa amasonyeza kuti kukhala ndi makhalidwe a Yehova monga kuona mtima, n’kofunika kwambiri kuposa chilichonse.​—Miy. 12:24; Aef. 4:28.

w15 2/1 5 ¶4-6

Kodi Mungatani Kuti Muzisangalala Ndi Ntchito Yanu?

Funso lomalizali ndi lofunikadi kuliganizira chifukwa munthu amasangalala kwambiri ndi ntchito yake, makamaka akaona kuti ikuthandizanso anthu ena. Yesu anati: “Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka kuposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Musaiwale kuti kuwonjezera pa makasitomala komanso mabwana anu, palinso anthu ena amene amapindula ndi ntchito yanu. Anthu amenewa ndi monga a m’banja lanu ndiponso ovutika.

Anthu a m’banja lanu. Bambo akamagwira ntchito mwakhama zimathandiza banja lake m’njira ziwiri. Choyamba, zimathandiza kuti azipeza zofunika pa banja lake monga chakudya, zovala komanso malo ogona. Akamachita zimenezi amakhala akukwaniritsa udindo umene Mulungu anamupatsa wosamalira “anthu amene ndi udindo wake kuwasamalira.” (1 Timoteyo 5:8) Chachiwiri, bambo amene amagwira ntchito mwakhama, amapereka chitsanzo chabwino kwa ana ake. Shane, yemwe tamutchula m’nkhani yoyamba ija, anati: “Bambo anga ndi chitsanzo chabwino pa nkhani yolimbikira ntchito. Iwo akhala akugwira ntchito ya ukalipentala kwa zaka zambiri. Zinthu zimene amapanga zimathandiza kwambiri anthu. Chitsanzo chawo chandiphunzitsa kuona kufunika kogwira ntchito ndi manja athu.”

Anthu ovutika. Mtumwi Paulo analangiza Akhristu kuti azigwira “ntchito molimbikira . . . kuti akhale ndi kanthu kena kopatsa munthu wosowa.” (Aefeso 4:28) Ngati timagwira ntchito n’kumapeza ndalama zothandizira banja lathu, zingakhale zosavuta kuti tikhalenso ndi ndalama zothandizira anthu ovutika. (Miyambo 3:27) Choncho, tikamagwira ntchito mwakhama timathanso kuthandiza ena. Kuchita zimenezi kumachititsa kuti tizikhala osangalala.

Mfundo Zothandiza

ijwyp nkhani na. 95 ¶10-11

Kodi Ndine Wopirira?

● Muziona mavuto anu moyenera. Muzitha kusiyanitsa pakati pa mavuto aakulu ndi mavuto aang’ono. Baibulo limanena kuti: “Munthu amene amasonyeza mkwiyo wake tsiku lomwelo ndi wopusa, koma wochenjera akachitiridwa chipongwe, amangozinyalanyaza.” (Miyambo 12:16) Choncho si mavuto onse amene ayenera kukusowetsani mtendere.

“Kusukulu, anzanga ambiri amakonda kudandaula pa zinthu zosafunika n’komwe. Ndiye anzawo akakawachemerera pa intaneti, amaganiza kuti akuchita bwino, m’malo moti aone zinthu moyenera n’kupeza njira yothetsera vutolo.”​—Joanne.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

ijwfq nkhani na. 3

Kodi a Mboni za Yehova amakhulupirira kuti chipembedzo cholondola n’chawo chokha?

Anthu amene amakonda kwambiri za chipembedzo ayenera kukhulupirira kuti Mulungu ndiponso Yesu amavomereza chipembedzo chawo. Ngati sakhulupirira kuti chipembedzo chawo n’cholondola ndiye kuti palibe chifukwa chokhalira m’chipembedzocho.

Yesu Khristu sanavomereze maganizo akuti pali zipembedzo zambiri, kapena kuti misewu yambiri yopita kumoyo wosatha. M’malomwake iye anati: “Chipata cholowera ku moyo n’chopapatiza komanso msewu wake ndi wopanikiza, ndipo amene akuupeza ndi owerengeka.” (Mateyu 7:14) A Mboni za Yehova amakhulupirira kuti anapeza msewu umenewu. Akanakhala kuti sanaupeze akanalowa chipembedzo china.

MAY 12-18

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 13

Musamapusitsike ndi “Nyale ya Anthu Oipa”

it-2 196 ¶2-3

Nyale

Imatchulidwanso Mophiphiritsa. Chimene chimathandiza munthu kudziwa kumene akupita chimayerekezeredwa ndi nyale. Pogwiritsa ntchito tanthauzo limeneli, buku la miyambo limasiyanitsa anthu abwino ndi anthu oipa ponena kuti, “Kuwala kwa nyale ya anthu olungama kukuwonjezeka kwambiri. Koma nyale ya anthu oipa idzazimitsidwa.” (Miy 13:9) Kuwala kwa anthu olungama kumapitiriza kuwonjezeka. Koma ngakhale nyale ya anthu oipa ioneke yowala kwambiri bwanji, kapena zochita zawo zioneke kuti zikuwayendera bwino bwanji, Mulungu adzaonetsetsa kuti mapeto awo ndi amdima, ndipo phazi lawo lidzapunthwa. Zimenezi ndi zomwe zimachitikiranso munthu amene amatemberera bambo komanso mayi ake.​—Miy 20:20.

‘Nyale ya munthu ikazimitsidwa,’ zimatanthauza kuti alibenso tsogolo. Mwambi wina umanena kuti: “Aliyense woipa alibe tsogolo, ndipo nyale ya anthu oipa idzazimitsidwa.”​—Miy 24:20.

w12 7/15 12 ¶3

Tumikirani Mulungu Amene Amapereka Ufulu

3 Ngati Satana anakwanitsa kunyengerera anthu awiri angwiro komanso angelo ena kuti akane ulamuliro wa Mulungu, ifenso akhoza kutinyengerera. Satana sanasinthe. Iye amayesetsa kutipusitsa kuti tiziganiza zoti mfundo za Mulungu ndi zolemetsa ndipo zimatiletsa kusangalala. (1 Yoh. 5:3) Anthu ambiri amaganiza choncho ndipo ngati timacheza nawo kwambiri, nafenso tikhoza kutengera maganizo amenewa. Mlongo wina wa zaka 24, amene anachita chiwerewere, anati: “Ndinayamba kutengera maganizo oipa a anzanga chifukwa chakuti sindinkafuna kuoneka wosiyana nawo.” Mwina nanunso mumavutika kukhala osiyana ndi anzanu.

w04 7/15 31 ¶6

“Yense Wochenjera Amachita Mwanzeru”

Munthu wanzeru ndiponso woongoka mtima amene amachita zinthu mozindikiradi amadalitsidwa. Solomo anatitsimikizira kuti: “Wolungama adya nakhutitsa moyo wake; koma mimba ya oipa idzasowa.” (Miyambo 13:25) Yehova amadziwa zimene zingatipindulitse m’njira zosiyanasiyana pa moyo wathu, kaya n’zokhudza moyo wathu wa m’banja, ubwenzi wathu ndi ena, utumiki wathu, kapenanso kupatsidwa malangizo. Ndipo tikachita mwanzeru potsatira malangizo a m’Mawu ake, ndithu tidzakhala ndi moyo wosangalala kwambiri.

Mfundo Zothandiza

it-2 276 ¶2

Chikondi

Chikondi china chikhoza kukhala chosayenera. Pa zifukwa zimenezi, zikuoneka kuti munthu akhoza kukhala ndi chikondi chenicheni komanso choyenera ngati amafufuza ndiponso kutsatira malangizo opezeka m’Mawu a Mulungu komanso ngati amatsogoleredwa ndi mzimu wake woyera. Mwachitsanzo, kholo likhoza kumakonda mwana wake. Koma ngati amangomupatsa chilichonse chimene akufuna ndipo samukaniza kanthu, chikondi chimenechi chikhoza kuyamba kuchepa kapena chikhoza kukhala chosayenera. Akhoza kukhala kuti samagwiritsa ntchito moyenera udindo wake monga kholo pomudzudzula mwanayo ndiponso nthawi zina kumupatsa chilango kumene. (Miy 22:15) Makolo oterewa amachita zimenezi ponena kuti akufuna kumusonyeza chikondi mwanayo, komatu chimenechi si chikondi, kumeneku ndi kudzikonda. Baibulo limanena kuti munthu amene amachita zimenezi sakukonda mwana wakeyo koma akudana naye, chifukwa zimenezi sizingapulumutse moyo wa mwanayo.​—Miy 13:24; 23:13, 14.

MAY 19-25

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 14

Muziganizira Zimene Mungachite Kukachitika Ngozi

w23.02 22-23 ¶10-12

Tiziyamikira Mphatso ya Moyo Imene Mulungu Anatipatsa

10 Nthawi zina sitingathe kupewa zochitika zina zomwe zingachititse kuti moyo wathu ukhale pangozi. Zimenezi zingachitike makamaka pa nthawi ya ngozi za m’chilengedwe, miliri komanso pamene kukuchitika ziwawa. Komabe zinthu ngati zimenezi zikachitika, tingathe kutetezeka komanso kupulumuka ngati titatsatira malangizo oti tichoke m’deralo kapenanso malangizo ena operekedwa ndi akuluakulu a boma. (Aroma 13:1, 5-7) Nthawi zina zingadziwike kuti kuchitika ngozi choncho tingachite bwino kutsatira malangizo a akuluakulu a boma otithandiza kukonzekera. Mwachitsanzo, zingakhale zothandiza kusunga madzi ndi zakudya zimene sizingawonongeke msanga komanso mankhwala ndi zinthu zina zothandizira munthu akavulala.

11 Kodi tingatani ngati matenda opatsirana akufalikira m’dera lomwe timakhala? Tiyenera kumvera malangizo omwe angatiteteze monga kusamba m’manja, kukhala motalikirana, kuvala masiki, komanso kukhala kwatokha. Tikamayesetsa kutsatira malangizowa, timasonyeza kuti timayamikira mphatso ya moyo imene Mulungu anatipatsa.

12 Pa nthawi ya ngozi zosiyanasiyana tingamve nkhani zabodza kuchokera kwa anzathu, anthu oyandikana nawo nyumba komanso kwa ofalitsa nkhani. M’malo mokhulupirira “mawu alionse” amene tamva, tingachite bwino kumvera malangizo odalirika ochokera kuboma komanso kwa a zaumoyo. (Werengani Miyambo 14:15.) Bungwe Lolamulira komanso maofesi a nthambi, amayesetsa kufufuza mfundo zolondola asanapereke malangizo okhudza misonkhano yampingo komanso ntchito yolalikira. (Aheb. 13:17) Kutsatira malangizowa kumathandiza kuti ifeyo komanso anthu ena tikhale otetezeka. Timathandizanso kuti mpingo ukhale ndi mbiri yabwino m’dera lathu.​—1 Pet. 2:12.

w24.07 5 ¶11

Muzikhala Olimba Mtima Ngati Zadoki

11 Ngati mutapemphedwa kuti muthandize abale anu pa nthawi yovuta, kodi mungasonyeze bwanji kulimba mtima ngati Zadoki? (1) Muzitsatira malangizo. Pa nthawi ngati imeneyi, mumafunika kuchita zinthu mogwirizana. Muyenera kutsatira malangizo ochokera ku ofesi ya nthambi. (Aheb. 13:17) Nthawi ndi nthawi, akulu ayenera kumaonanso zimene anakonza pa nkhani yokonzekera ngozi komanso kutsatira malangizo a gulu pa nthawi ya ngoziyo. (1 Akor. 14:33, 40) (2) Muzikhala olimba mtima koma muzichita zinthu mosamala. (Miy. 22:3) Muziganiza kaye musanachite zinazake. Muziyesetsa kuti mukhale otetezeka. (3) Muzidalira Yehova. Muzikumbukira kuti Yehova amakukondani inuyo komanso abale anuwo. Choncho angakuthandizeni kuti mupereke thandizo kwa abale anuwo muli otetezeka.

Mfundo Zothandiza

it-2 1094

Kuganiza Bwino

Komabe, munthu amene amaganiza bwino akhozanso kuyamba kudedwa. N’kutheka kuti mfundo imeneyi ndi yomwe yafotokozedwa pa Miyambo 14:17 kuti: “Munthu amene amaganiza bwino amadedwa.” Nthawi zambiri anthu amene saganiza bwino samasangalala ndi anthu amene amagwiritsa ntchito mokwanira luso lawo loganiza. Komanso nthawi zambiri anthu amene amagwiritsa ntchito luso lawo loganiza pochita zimene Mulungu amafuna, anthu ena amawada. Monga mmene Yesu ananenera kuti: “Popeza simuli mbali ya dzikoli, koma ine ndinakusankhani kuchokera m’dziko, pa chifukwa chimenechi dziko likudana nanu.” (Yoh 15:19) Komabe, mawu a m’chilankhulo choyambirira omwe anawamasulira kuti ‘kuganiza bwino’ pa lemba la Miyambo 14:17, angatanthauzenso kuganiza zochitira ena chiwembu. Choncho vesili lingatanthauze kuti munthu amene amaganiza zochitira ena chiwembu amadedwa, ndipo umu ndi mmene Mabaibulo ena anamasulira lembali kuti: “Munthu wa ziwembu adzadedwa.”​—Buku Lopatulika Ndilo Mawu a Mulungu.

MAY 26–JUNE 1

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 15

Muzithandiza Ena Kukhala Osangalala

w10 11/15 31 ¶16

Tidzayenda Mogwirizana Ndi Mtima Wathu Wosagawanika

16 Yobu anali ndi mtima wochereza. (Yobu 31:31, 32) Ngakhale kuti sindife olemera, tikhoza ‘kukhala ochereza.’ (Aroma 12:13) Tikhoza kugawana ndi ena zinthu zochepa zimene tili nazo podziwa kuti, “ndi bwino kudya zamasamba koma pali chikondi, kusiyana ndi kudya nyama ya ng’ombe yamphongo yodyetsedwa bwino pali chidani.” (Miy. 15:17) Kudya chakudya chosalira zambiri koma pali mtendere ndi mtumiki mnzathu wokhulupirika kumakhala kosangalatsa ndiponso kopindulitsa mwauzimu.

w18.04 23-24 ¶16-18

Tizilimbikitsana Ndipo “Tiwonjezere Kuchita Zimenezi”

16 Si nzeru kuganiza kuti ifeyo sitingalimbikitse munthu chifukwa choti timasowa chonena pocheza ndi anthu. Tikutero chifukwa chakuti kulimbikitsa munthu sikufuna zambiri. Ngakhale tikangomwetulira popereka moni kwa munthu timakhala titamulimbikitsa. Ngati munthu winayo wayankha moniyo popanda kumwetuliranso zingasonyeze kuti mwina pali vuto linalake. Ndiyeno kumumvetsera munthu woteroyo kungamulimbikitse kwambiri.​—Yak. 1:19.

17 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi m’bale wina wachinyamata dzina lake Henri. Iye anakhumudwa kwambiri abale ake ena komanso bambo ake, omwe anali mkulu, atasiya choonadi. Henri anasangalala kwambiri pamene woyang’anira dera anamutengera kumalo enaake kukamugulira kachakudya kenako n’kuyamba kucheza naye kuti adziwe zimene zili mumtima mwake. Henri anazindikira kuti akhoza kuthandiza abale akewo kubwerera m’choonadi ngati iyeyo angakhalebe wokhulupirika. Analimbikitsidwa kwambiri atawerenga lemba la Salimo 46; Zefaniya 3:17 ndiponso Maliko 10:29, 30.

18 Nkhani ya Marthe komanso ya Henri zikusonyeza kuti n’zotheka kulimbikitsa munthu amene akuda nkhawa. Paja Mfumu Solomo analemba kuti: “Mawu onenedwa pa nthawi yoyenera ndi abwino kwambiri. Maso owala amapangitsa mtima kusangalala. Uthenga wabwino umanenepetsa mafupa.” (Miy. 15:23, 30) Kuwerenga magazini a Nsanja ya Olonda komanso nkhani zapawebusaiti yathu kukhoza kulimbikitsa munthu amene ali ndi nkhawa. Paulo anasonyeza kuti kuimba nyimbo za Ufumu limodzi kumalimbikitsanso. Iye analemba kuti: “Pitirizani kuphunzitsana ndi kulangizana [kapena kuti “kulimbikitsana”] mwa masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu, ndi nyimbo zauzimu zogwira mtima. Pitirizani kuimbira Yehova m’mitima yanu.”​—Akol. 3:16; Mac. 16:25.

Mfundo Zothandiza

ijwbq nkhani na. 39 ¶3

Kodi Mkhristu Angalandire Chithandizo cha Mankhwala Akadwala?

2. Kodi ndifunse maganizo madokotala ena ndisanalandire chithandizochi? Kumva maganizo a anthu ambiri kukhoza kukuthandizani kusankha bwino, makamaka ngati matenda anuwo ndi aakulu.​—Miyambo 15:22.

JUNE 2-8

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 16

Mafunso Atatu Othandiza Kusankha Zinthu Mwanzeru

w14 1/15 19-20 ¶11-12

Achinyamata, Muzisankha Zochita Mwanzeru

11 Timakhala osangalala kwambiri tikamatumikira Yehova. (Miy. 16:20) Zikuoneka kuti Baruki, yemwe anali mlembi wa Yeremiya, anaiwala mfundo imeneyi. Pa nthawi ina, kutumikira Yehova sikunkamusangalatsanso. Ndiyeno Yehova anamuuza kuti: “Iwe, ukufunafunabe zinthu zazikulu. Leka kuzifunafuna. Anthu onse ndikuwagwetsera tsoka ndipo iwe ndidzakupatsa moyo wako monga chofunkha chako kulikonse kumene ungapite.” (Yer. 45:3, 5) Kodi mukuona kuti n’chiyani chimene chikanathandiza Baruki kukhala wosangalala? Kodi ndi kufunafuna zinthu zazikulu kapena kutumikira Mulungu mokhulupirika n’kupulumuka pamene Yerusalemu akuwonongedwa?​—Yak. 1:12.

12 M’bale wina dzina lake Ramiro anaona kuti kutumikira ena n’kosangalatsa kwambiri. Iye anati: “Ndimachokera m’banja losauka limene limakhala kumudzi wina kumapiri a Andes. Choncho unali mwayi waukulu pamene mkulu wanga ananena kuti andilipirira kuti ndipite kuyunivesite. Koma ndinali nditangobatizidwa kumene ndipo mpainiya wina anali atandipempha kuti ndikalalikire naye kukatauni kena. Ndinapita kukatauni kameneka ndipo ndinaphunzira kumeta tsitsi. Kenako ndinatsegula malo anga ometera tsitsi kuti ndizipeza kangachepe. Pamene tinkapempha anthu kuti tiziphunzira nawo Baibulo, ambiri ankavomera ndiponso kuyamikira. Patapita nthawi, ndinayamba kusonkhana ndi mpingo wa chinenero cha kumeneko umene unali utangokhazikitsidwa kumene. Panopa ndakhala ndikuchita upainiya kwa zaka 10. Palibe ntchito ina imene ingandisangalatse kuposa kuthandiza anthu kumva uthenga wabwino m’chinenero chawo.”

w13 9/15 17 ¶1-3

Kodi Mwasandulika?

TONSEFE timachita zinthu malinga ndi kumene tinakulira komanso kumene tikukhala. Ndipo timasiyana pa nkhani ya zovala, chakudya komanso makhalidwe. Izi zingachitike chifukwa timatengera anthu amene timakhala nawo ndiponso chifukwa cha mmene zinthu zilili pa moyo wathu.

2 Koma timasiyananso pa zinthu zofunika kwambiri kuposa zovala ndi zakudya. Mwachitsanzo, malinga ndi mmene tinakulira, pali zinthu zina zimene timaona kuti ndi zoyenera pomwe zina timaona kuti ndi zolakwika. Timachitanso zinthu zina potsatira chikumbumtima chathu. Baibulo limanena kuti nthawi zambiri ‘anthu a mitundu amene alibe chilamulo amachita mwachibadwa zinthu za m’chilamulo.’ (Aroma 2:14) Kodi izi zikutanthauza kuti ngati Mulungu sanapereke lamulo loletsa zinthu zina ndiye kuti tikhoza kutsatira zimene ifeyo kapena anthu ena a m’dera lathu amaona kuti n’zoyenera?

3 Akhristu oona sayenera kungotsatira maganizo awo kapena a anthu ena. Tikutero pa zifukwa ziwiri. Choyamba, Baibulo limatiuza kuti: “Pali njira yooneka ngati yowongoka kwa munthu, koma mapeto ake ndi imfa.” (Miy. 16:25) Popeza si ife angwiro, patokha sitingasankhe bwinobwino zinthu zimene zingatithandize pa moyo wathu. (Miy. 28:26; Yer. 10:23) Chachiwiri, Baibulo limasonyeza kuti dziko lonse lili m’manja mwa Satana. Choncho maganizo ndiponso mfundo zimene anthu ambiri amayendera m’dzikoli zimachokera kwa Satanayo, yemwe ndi “mulungu wa nthawi ino.” (2 Akor. 4:4; 1 Yoh. 5:19) Ndiyetu ngati tikufuna kuti Yehova atidalitse tiyenera kutsatira malangizo a pa Aroma 12:2.​—Werengani.

Mfundo Zothandiza

it-1 629

Chilango

Zotsatira za Kumvera Kapena Kusamvera. Anthu oipa, zitsiru komanso anthu opanda khalidwe amasonyeza kuti amadana ndi malangizo ochokera kwa Yehova posawamvera ngakhale pang’ono. (Sl 50:16, 17; Miy 1:7) Zotsatirapo zoipa zomwe zimabwera chifukwa cha uchitsiru umenewu zimapangitsa kuti nthawi zina munthu alandire chilango chopweteka kwambiri. Zimenezi ndi zomwe mwambi wina umanena kuti: “Zitsiru zimalangidwa ndi kupusa kwawo komwe.” (Miy 16:22) Anthu amenewa akhoza kudzibweretsera umphawi, kuchita manyazi, kutenga matenda mwinanso kufa msanga kumene. Zomwe zinachitikira Aisiraeli zimasonyeza bwino mavuto amene amakhalapo chifukwa chosamvera malangizo. Iwo sanamvere ngakhale pang’ono pamene aneneri ankawapatsa malangizo komanso kuwadzudzula. Iwo sanamverebe Yehova ngakhale pamene anawapatsa chilango posiya kuwateteza komanso kuwadalitsa. Pamapeto pake, iwo anapatsidwa chilango chopweteka kwambiri chomwe anawauziratu, chakuti adzagonjetsedwa kenako adzapita ku ukapolo.​—Yer 2:30; 5:3; 7:28; 17:23; 32:33; Ho 7:12-16; 10:10; Zef 3:2

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

ijwbv nkhani na. 40

Miyambo 16:3:​—“Pereka Zochita Zako kwa AMBUYE”

Tanthauzo la Miyambo 16:3

Mwambi umenewu umatsimikizira anthu omwe amalambira Mulungu woona kuti mapulani awo adzayenda bwino ngati angamadalire Mulunguyo komanso kutsatira malangizo ake.

“Zochita zako zonse uzisiye mʼmanja mwa Yehova.” Anthu omwe amalambira Yehova amatsatira malangizo ake modzichepetsa asanasankhe zochita. (Yakobo 1:5) N’chifukwa chiyani amatero? Chifukwa chimodzi n’chakuti nthawi zambiri anthufe sitingathe kudziwa kapena kulamulira zochitika pa moyo wathu. (Mlaliki 9:11; Yakobo 4:13-15) Komanso timasowa nzeru zoyendetsera mapulani athuwo. Pa zifukwa zimenezi anthu ambiri amaona kuti ndi nzeru kusiya m’manja mwa Mulungu zochita zawo. Iwo amachita zimenezi popemphera kwa iye kuti awatsogolere komanso kuchita zinthu mogwirizana ndi chifuniro chake monga mmene Baibulo, lomwe ndi Mawu ake, limanenera.​—Miyambo 3:5, 6; 2 Timoteyo 3:16, 17.

Mawu akuti “pereka zochita zako kwa AMBUYE” m’chilankhulo choyambirira amatanthauza “kupereka ntchito zako kwa AMBUYE.” Malinga ndi buku lina, mawuwa amanena za “munthu yemwe amachotsa katundu pamsana pake n’kumuika pamsana pa munthu wina wamphamvu kuposa iyeyo amenenso angakwanitse kunyamula katunduyo.” Anthu odzichepetsa amadalira Mulungu ndipo samakayikira kuti awathandiza.​—Salimo 37:5; 55:22.

Mawu akuti “zochita zako zonse” sakutanthauza kuti Mulungu adzavomereza kapena kudalitsa mapulani alionse amene anthu angakhale nawo. Kuti Mulungu azitidalitsa, mapulani athu ayenera kukhala ogwirizana ndi zimene iye amafuna komanso mfundo zake. (Salimo 127:1; 1 Yohane 5:14) Mulungu samadalitsa anthu osamvera. Zoona zake n’zakuti, “amasokoneza mapulani a anthu oipa.” (Salimo 146:9) Koma amathandiza anthu amene amasonyeza kuti ndi odzichepetsa pomvera mfundo zomwe iye anakhazikitsa zimene zimapezeka m’Baibulo.​—Salimo 37:23.

“Ndipo mapulani ako adzayenda bwino.” Mabaibulo ena anamasulira mawu amenewa kuti “mapulani ako adzakhazikika.” M’Malemba a Chiheberi kapena kuti Chipangano Chakale, mawu omwe m’Chingelezi anamasuliridwa kuti “adzakhazikika” amafotokoza za kuyala maziko ndipo nthawi zambiri amanena za kukhazikika kwa ntchito zimene Mulungu analenga. (Miyambo 3:19; Yeremiya 10:12) Mofanana ndi zimenezi, Mulungu amakhazikitsa mapulani a anthu amene iye amawaona kuti akuchita zinthu mwachilungamo, amawateteza komanso amawathandiza kuti akhazikike ndiponso azikhala ndi moyo wosangalala.​—Salimo 20:4; Miyambo 12:3.

JUNE 9-15

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 17

Muzikhala Mwamtendere M’banja Lanu

g 9/14 11 ¶2

Mungatani Kuti Musamasunge Chakukhosi?

Dzifufuzeni moona mtima. Baibulo limasonyeza kuti anthu ena ‘amakonda kukwiya’ komanso ‘amakonda kupsa mtima.’ (Miyambo 29:22) Kodi ndi mmene inuyo mulili? Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndine munthu wosachedwa kupsa mtima? Kodi sindichedwa kukhumudwa? Nanga kodi ndimakhumudwa ngakhale pa nkhani yaing’ono?’ Baibulo limati, “amene amangokhalira kulankhula za nkhani inayake amalekanitsa mabwenzi apamtima.” (Miyambo 17:9; Mlaliki 7:9) Zimenezi zingachitikenso m’banja. Choncho ngati mumakonda kusunga chakukhosi, mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndingatani kuti ndizileza mtima mwamuna kapena mkazi wanga akandikhumudwitsa?’​—Lemba lothandiza: 1 Petulo 4:8.

w08 5/1 10 ¶6–11 ¶1

Kuthetsa Mavuto

1. Sankhani nthawi yoti mukambirane vutolo. “Kanthu kali konse kali ndi nthawi yake . . . mphindi yakutonthola ndi mphindi yakulankhula.” (Mlaliki 3:1, 7) Monga mmene taonera mu mkangano umene uli koyambirira kwa nkhani ino, mavuto ena angachititse kuti mupsetsane mitima. Pokambirana vuto linalake, mukaona kuti mwayamba kupsetsana mitima, siyani kaye kukambirana nkhaniyo. Kugwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo otsatirawa kungateteze ukwati wanu. “Chiyambi cha ndewu chifanana ndi kutsegulira madzi; tsono kupikisana kusanayambe tasiya makani.”​—Miyambo 17:14.

Komabe, palinso “mphindi yakulankhula.” Mofanana ndi udzu m’munda, mavuto amakula kwambiri mukawalekerera. Choncho musanyalanyaze vutolo poganiza kuti litha lokha. Ngati mwagwirizana kuti musiye kaye nkhaniyo, lemekezani mnzanuyo mwa kusankha nthawi ina yoyenera yoti mukambirane. Kuchita zimenezi kungakuthandizeni nonse kuti mutsatire malangizo a m’Baibulo akuti: “Dzuwa lisalowe muli chikwiyire.” (Aefeso 4:26) Motero, yesetsani kukwaniritsa zimene mwagwirizanazo.

Mfundo Zothandiza

it-1 790 ¶2

Diso

Zomwe munthu amachita ndi maso ake zimasonyeza bwino mmene akumvera mumtima. Maso angasonyeze kuti munthu akumva chisoni kapena ayi. (De 19:13) Munthu ‘akapsinyira’ kapena ‘kutsinzinira’ ena, zingasonyeze kuti akuwanyodola kapena akufuna kuwachitira zoipa. (Sl 35:19; Miy 6:13; 16:30) Anthu amene safuna kuchita chidwi ndi anthu ena kapena safuna kuthandiza anthu ena amatchulidwa kuti atseka maso awo. (Mt 13:15; Miy 28:27) Munthu wopusa amatchulidwa kuti maso ake “amangoyendayenda mpaka kumalekezero a dziko lapansi,” amangomwazamwaza maso kutanthauza kuti maganizo ake sakhazikika pa chinthu chimodzi. (Miy 17:24) Mmene maso a munthu akuonekera akhoza kusonyeza mmene thanzi lake lilili, mphamvu zake kapena mmene akusangalalira. (1Sa 14:27-29; De 34:7; Yob 17:7; Sl 6:7; 88:9) Mfumu Yehosafati anauza Yehova kuti: “Maso athu ali pa inu.”​—2Mb 20:12.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

ijwbv nkhani na. 60

Miyambo 17:17​—“Bwenzi Limakonda Nthawi Zonse”

Anzathu enieni amakhala odalirika. Mofanana ndi anthu obadwira m’banja limodzi, anzathuwa amakhala okhulupirika komanso amatithandiza, makamaka tikakumana ndi mavuto.

“Mnzako weniweni amakusonyeza chikondi nthawi zonse.” Mawu amenewa angamasuliridwenso kuti “mabwenzi amakondana nthawi zonse.” Mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti “chikondi” palembali, amaphatikizapo zambiri osangoti mmene munthu amamvera mumtima mwake. Amatanthauza chikondi chopanda dyera chimene munthu amasonyeza mnzake kudzera mu zochita. (1 Akorinto 13:4-7) Anthu omwe amakondana chonchi amagwirizanabe pakakhala kusamvetsetsana kapena mavuto ena. Amakhululukirananso ndi mtima wonse. (Miyambo 10:12) Ndiponso sachitirana nsanje wina zikamuyendera bwino. M’malomwake, amasangalala naye.​—Aroma 12:15.

“Mnzako weniweni . . . ndi mʼbale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.” Mwambiwu unachokera pa mfundo yoti anthu obadwira m’banja limodzi ndi amene angakhale ogwirizana kwambiri. Choncho tikamachita zonse zomwe tingathe kuti tithandize mnzathu yemwe ali pa mavuto, timachita zinthu ngati mchimwene kapena mchemwali wake weniweni. Kuwonjezera pamenepa, chikondi chimene chimagwirizanitsa anthu oterewa sichichepa kaya akumane ndi vuto lotani. M’malomwake, anthuwa amagwirizanabe chifukwa chokondana komanso kulemekezana kwambiri.

JUNE 16-22

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 18

Muzilankhula Mawu Olimbikitsa kwa Anthu Amene Akudwala

w22.10 22 ¶17

Nzeru Yeniyeni Ikufuula

17 Tiziganiza kaye tisanalankhule. Ngati sitingasamale, zimene tingalankhule zingakhumudwitse kwambiri anthu ena. Baibulo limati: “Pali munthu amene amalankhula mosaganizira ndi mawu olasa ngati lupanga, koma lilime la anthu anzeru limachiritsa.” (Miy. 12:18) Timapitiriza kugwirizana ndi anthu ena tikamapewa kulankhula miseche pa zimene amalakwitsa. (Miy. 20:19) Kuti zolankhula zathu zizisangalatsa ena osati kuwakhumudwitsa, tiyenera kudzadza mumtima mwathu ndi mfundo za m’Mawu a Mulungu. (Luka 6:45) Tikamaganizira kwambiri zimene Baibulo limanena, mawu athu angakhale ngati “chitsime cha nzeru” ndipo angatsitsimule anthu ena.​—Miy. 18:4.

mrt nkhani na. 19 bokosi

Zimene Zingakuthandizeni Ngati Mwayamba Kudwala Mwadzidzidzi

Muzimvetsera akamalankhula. Njira yabwino kwambiri yothandizira mnzanu ndi kumvetsera akafuna kulankhula nanu. Musaganize kuti muyenera kuyankha pa chilichonse chimene wanena. Nthawi zambiri kungomvetsera n’kokwanira. Muzipewa kumuweruza koma muziyesetsa kumumvetsa. Musamangoganiza kuti mukudziwa mmene akumvera m’thupi, makamaka ngati sakuoneka kuti akudwala.​—Miyambo 11:2.

Muzinena zinthu zolimbikitsa. Mwina mungasowe choti munene. Koma m’malo mongokhala chete, munganene zinthu zochepa zosonyeza kuti mwamumvetsa. Zimenezi zingamulimbikitse. Mwachitsanzo, ngati mulibe zonena, yesetsani kungonena mawu osavuta koma ochokera mumtima ngati kuti “Sindidziwa zimene ndinganene, koma dziwani kuti ndimakukondani.” Koma musamanene mawu ngati akuti “Pali anthu ena omwe akuvutika kwambiri kuposa inuyo” kapena akuti “Bola inuyo chifukwa simukudwala matenda a . . . ”

Mungasonyeze kuti mumamufunira zabwino mukamayesetsa kudziwa zambiri zokhudza matenda ake. N’zosakayikitsa kuti adzayamikira zimenezi ndipo mudzatha kumuuza zinthu zothandiza. (Miyambo 18:13) Koma musamangopereka malangizo okhudza matenda ake ngati sanakupempheni.

Muzimuthandiza. M’malo mongoganiza zimene mungachite pomuthandiza, muzimufunsa zimene mungachite. Koma muzikumbukira kuti mwina mnzanuyo sangavomere kuti akufunikira kuthandizidwa chifukwa sakufuna kukuvutitsani. Ngati zili choncho, muzimuuza zinthu zimene mungachite monga kukamugulira zinthu zofunika, kumugwirira ntchito zapakhomo kapena zinthu zina.​—Agalatiya 6:2.

Musataye mtima. Mnzanu akamadwala, nthawi zina mwina sangakwanitse kuchita zimene munagwirizana kapenanso sangafune kucheza nanu. Muzimulezera mtima n’kumumvetsa. Pitirizani kumayesetsa kumuthandiza.​—Miyambo 18:24.

wp23.1 14 ¶3–15 ¶1

Mmene Mungathandizire Amene Akudwala Matenda Amaganizo

‘Muzilankhula molimbikitsa.’ ​—1 ATESALONIKA 5:14.

Mnzanuyo akhoza kukhala ndi nkhawa kapena angamalimbane ndi vuto lodziona kuti ndi wachabechabe. Mungamulimbikitse kwambiri komanso kumutonthoza, mukamamutsimikizira kuti mumamukonda ngakhale musakudziwa zoti munene.

“Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse.”​—MIYAMBO 17:17.

Muzichita zinazake pomuthandiza. M’malo moganiza kuti mukudziwa kale zoyenera kuchita kuti mumuthandize, muzimupempha kuti akuuzeni zomwe akufuna kuti mumuchitire. Ngati mnzanuyo akulephera kukufotokozerani zimene akufunikira, muziyesa kukambirana naye zinthu zimene mungachitire limodzi monga kukayendera limodzi kumalo enaake. Mwinanso mungamupemphe kuti mukamugulire zinthu kumsika, kumuthandiza ntchito zapakhomo kapenanso zinthu zina.​—Agalatiya 6:2.

‘Muzikhala oleza mtima.’​—1 ATESALONIKA 5:14.

Si nthawi zonse pamene mnzanuyo angakhale womasuka kufotokoza maganizo ake. Muzimutsimikizira kuti ndinu wokonzeka kumumvetsera pa nthawi ina iliyonse yomwe angafune kukufotokozerani maganizo ake. Chifukwa cha matenda amene akudwalawo, iye akhoza kuchita kapena kulankhula zinthu zina zimene zingakukhumudwitseni. Ndipo nthawi zina, akhoza kusintha zinthu zimene munapangana kuti muchitire limodzi kapenanso akhoza kukwiya zosadziwika bwino. Choncho, muzichita naye zinthu moleza mtima komanso kumumvetsa pa nthawi imene mukumuthandizayo.​—Miyambo 18:24.

Mfundo Zothandiza

it-2 271-272

Maere, I

Kale, anthu ankachita maere kuti adziwe zochita pa nkhani inayake. Pochita maere ankaponya timiyala kapena timatabwa “pachovala,” kapena mumtsuko kenako n’kukhutchumula. Amene amugwera ndi amene ankasankhidwa. Asanapange maere ankafunikanso kupereka pemphero monga mmene zinalili ndi lumbiro. Akapereka pempheroli, ankayembekezera kuti Yehova achitapo kanthu. M’Baibulo mawu akuti maere (Chiheberi, goh·ralʹ) amagwiritsidwa ntchito mwachindunji kapena mophiphiritsa pofuna kutanthauza “gawo” kapena “cholowa.”​—Yos 15:1; Sl 16:5; 125:3; Yes 57:6; Yer 13:25.

Mmene ankawagwiritsira ntchito. Lemba la Miyambo 16:33 limati: “Maere amaponyedwa pachovala, koma zonse zimene maerewo asonyeza zimachokera kwa Yehova.” Ku Isiraeli, cholinga cha maere chinali kuthetsa kusamvana. “Kuchita maere kumathetsa mikangano ndipo kumathetsa nkhani pakati pa anthu amphamvu.” (Miy 18:18) Maere sankagwiritsidwa ntchito pochita masewera, zosangalatsa kapena kutchova juga. Sankabetcha kuti pamapeto pake awine kapena aluze. Sankawagwiritsa ntchito kuti apeze zopereka ku kachisi kapena kwa ansembe kapenanso kuti athandize ovutika. Mosiyana ndi zimenezi, asilikali Achiroma anachita maere ndi zolinga zadyera, monga mmene lemba la Salimo 22:18 linaloserera, iwo anachita maere pa zovala za Yesu.​—Mt 27:35.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

ijwfq nkhani na. 29

Kodi a Mboni za Yehova Amakhulupirira Kuti Dziko Linalengedwa M’masiku 6 Enieni?

Ayi. N’zoona kuti a Mboni za Yehova amakhulupirira kuti Mulungu analenga zinthu zonse. Koma sitikhulupirira kuti Mulungu analenga zinthu zonse m’masiku 6 enieni chifukwa zinthu zina zokhudza chikhulupirirochi ndi zosemphana ndi zimene Baibulo limanena. Taonani zitsanzo zotsatirazi:

1. Kutalika kwa masiku 6 amene Mulungu analenga zinthu zonse. Anthu ena amakhulupirira kuti Mulungu analenga zinthu zonse m’masiku 6 enieni, tsiku lililonse lokhala ndi maola 24. Koma m’Baibulo, mawu akuti “tsiku” akhoza kutanthauza nthawi yaitali.​—Genesis 2:4; Salimo 90:4.

2. Kodi dzikoli lakhalapo kwa zaka zingati? Anthu ena amaphunzitsa kuti dzikoli langokhala zaka masauzande ochepa kuchokera nthawi imene linalengedwa. Komabe Baibulo limasonyeza kuti dziko lapansili komanso chilengedwe chonse zinalipo masiku 6 olenga amene amatchulidwa m’Baibulo asanafike. (Genesis 1:1) Pa chifukwa chimenechi, a Mboni za Yehova satsutsa zimene asayansi ena apeza, zoti dziko lapansili lakhalapo zaka mabiliyoni ambiri kuchokera nthawi imene linalengedwa.

Ngakhale kuti a Mboni za Yehovafe timakhulupirira kuti dzikoli linalengedwa ndi Mulungu, sititsutsa zimene asayansi ena amapeza. Timakhulupirira kuti zinthu zolondola zimene asayansi angapeze zimagwirizana ndi zimene Baibulo limanena.

JUNE 23-29

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 19

Muzikhala Bwenzi Lenileni kwa Abale ndi Alongo Anu

w23.11 12-13 ¶16-17

Kodi Tingatani Kuti Tizikondana Kwambiri?

16 Muziganizira kwambiri makhalidwe abwino amene abale ndi alongo ali nawo osati zimene amalakwitsa. Tiyerekeze kuti muli pagulu limodzi ndi abale ndi alongo. Mukucheza mosangalala ndipo pamapeto pake mukujambulitsa chithunzi. Ndiye mukujambula zithunzi ziwiri kapena zitatu kuopera kuti mwina choyambacho sichinaoneke bwino. Apa tsopano muli ndi zithunzi zitatu. Ndiye pachithunzi chimodzicho m’bale wina sakumwetulira bwino. Kodi zikatero mumatani? Mumangochidilita chifukwa muli ndi zithunzi zina ziwiri pamene aliyense akumwetulira bwino.

17 Zithunzizi zili ngati zinthu zosiyanasiyana zomwe timakumbukira zokhudza anthu ena. Pali zabwino zambiri zimene timakumbukira zomwe tinachita ndi abale ndi alongo athu. Koma bwanji ngati pa nthawi ina m’bale kapena mlongo analankhula kapena kuchita zinthu mosaganizira ena? Kodi tiyenera kutani? Ndi bwino kungozichotsa m’maganizo mwathu ngati mmene tingachitire ndi zithunzi zija. (Miy. 19:11; Aef. 4:32) Tikhoza kuchotsa zimenezi m’maganizo mwathu chifukwa pali zabwino zambiri zokhudza m’bale wathuyo zomwe tingamazikumbukire. Zinthu zabwinozo ndi zimene tiyenera kuzisunga m’maganizo mwathu.

w23.07 9-10 ¶10-11

Pitirizani Kukonda Yehova ndi Anthu

10 Ifenso timafunafuna njira zothandizira abale ndi alongo athu. (Aheb. 13:16) Taganizirani zimene zinachitikira Anna amene tamutchula munkhani yapita ija. Pambuyo pa mphepo ina yamkuntho, iye ndi mwamuna wake anapita kukaona banja lina la Mboni ndipo anapeza kuti denga la nyumba yawo linali litawonongeka. Chifukwa cha mphepoyo, zovala zawo zonse zinada. Anna ananena kuti: “Tinatenga zovala zawozo n’kukazichapa, ndipo tinakawapatsa titazisita komanso kuzipinda bwinobwino. Kwa ife, zimenezi sizinali nkhani yaikulu, koma zinathandiza kuti tizigwirizana nawo kwambiri mpaka pano.” Kukonda abale ndi alongo awo, kunachititsa Anna ndi mwamuna wake kuti awathandize.​—1 Yoh. 3:17, 18.

11 Tikamakonda komanso kukomera mtima anthu ena, nthawi zambiri iwo amaona zimene timachita potsanzira Yehova pa nkhani ya mmene amaganizira komanso kuchitira zinthu. Ndipo akhoza kuyamikira kwambiri zimene tingachite powasonyeza kukoma mtima kuposa mmene tingaganizire. Khanh yemwe tamutchula kale uja, amasangalala akakumbukira mmene ena anamuthandizira. Iye anati: “Ndimayamikira kwambiri alongo onse omwe ankanditenga akamakalalikira. Ankabwera kudzanditenga kunyumba, kundiitanira chakudya komanso kudzandisiya. Panopa ndi pamene ndimazindikira kuti ankafunika kuchita khama kuti azichita zimenezi ndipo ankazichita chifukwa cha chikondi.” N’zoona kuti si onse amene angayamikire zomwe tawachitira. Ponena za anthu amene ankamuthandiza, Khanh ananena kuti: “Ndimalakalaka nditawabwezera zabwino zomwe anandichitira, koma sindimadziwa kumene onsewa amakhala. Komabe, Yehova amadziwa ndipo ndimamupempha kuti aziwadalitsa.” Khanh ananena zoona. Yehova amadziwa ngakhale zinthu zing’onozing’ono zomwe timachita pokomera mtima ena. Iye amaona kuti zimenezi ndi nsembe yamtengo wapatali komanso ngongole yomwe adzabweze.​—Werengani Miyambo 19:17.

w21.11 9 ¶6-7

Pitirizani Kusonyezana Chikondi Chokhulupirika

6 Masiku ano timatha kunena za munthu amene wagwira ntchito zaka zambiri pakampani kuti ndi wokhulupirika kukampaniyo. Koma n’kutheka kuti pa zaka zonsezo sanakumanepo ndi eniake a kampaniyo ndipo mwinanso sagwirizana ndi malamulo ake. Iye samaikonda kampaniyo koma amasangalala chifukwa ntchitoyo imamupatsa ndalama zomwe amafunikira. Komabe akupitiriza kugwira ntchitoyo mpaka pamene adzapume kapena kupeza ntchito yabwino kwina.

7 Kusiyana kumene kulipo pakati pa kukhulupirika ndi chikondi chokhulupirika chimene chatchulidwa mundime 6 ndi zolinga zomwe zimachititsa munthu kuti azisonyeza makhalidwewa. Munkhani zimene timawerenga m’Baibulo, kodi ndi chiyani chimene chinkachititsa anthu a Mulungu kuti azisonyeza chikondi chokhulupirika? Iwo ankatero osati chifukwa chakuti ndi zimene ankafunika kuchita, koma ndi zimene ankafuna kuchita. Taganizirani chitsanzo cha Davide. Iye ankafunitsitsa kusonyeza chikondi chokhulupirika kwa mnzake wapamtima Yonatani ngakhale kuti bambo ake a Yonatani ankafuna kupha Davideyo. Patapita zaka zambiri Yonatani atamwalira, Davide anapitiriza kusonyeza chikondi chokhulupirika kwa Mefiboseti mwana wa Yonatani.​—1 Sam. 20:9, 14, 15; 2 Sam. 4:4; 8:15; 9:1, 6, 7

Mfundo Zothandiza

it-1 515

Malangizo, Mlangizi

Yehova yekha ndi amene ali ndi nzeru zopanda malire. Ndi iye yekha amene safunikira malangizo kuchokera kwa wina aliyense. (Yes 40:13; Aro 11:34) Mwana wake ndi “Mlangizi Wodabwitsa” ndipo amakwanitsa kutsogolera komanso kupereka malangizo chifukwa amalandira komanso kugwiritsa ntchito malangizo ochokera kwa Bambo ake ndiponso ali ndi mzimu woyera. (Yes 9:6; 11:2; Yoh 5:19, 30) Zimenezi zikusonyeza kuti, kuti malangizo akhale othandiza, amafunika akhale otsogoleredwa ndi Yehova. Malangizo alionse omwe ndi otsutsana ndi Wam’mwambamwamba ndi opanda phindu. Ndipo amenewo si malangizo n’komwe.​—Miy 19:21; 21:30.

JUNE 30–JULY 6

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 20

Mfundo Zothandiza Kuti Chibwenzi Chanu Chiyende Bwino

w24.05 26-27 ¶3-4

Kodi Mungatani Kuti Chibwenzi Chanu Chiziyenda Bwino?

3 Monga taonera, nthawi yomwe anthu ali pa chibwenzi ikhoza kukhala yosangalatsa. Koma kuwonjezera pamenepa, ndi nthawi yofunika kwambiri yomwe ingathandize anthu kuona ngati angadzakwatirane. Pa tsiku la ukwati wawo, anthu okwatiranawo amalumbira pamaso pa Yehova kuti azikondana komanso kulemekezana kwa moyo wawo wonse. Tisanalumbire pa nkhani iliyonse, tiyenera kuiganizira kaye mofatsa. (Werengani Miyambo 20:25.) Ndi mmenenso zilili pa nkhani ya lumbiro la ukwati. Kukhala pa chibwenzi kumathandiza awiriwo kuti adziwane bwino komanso kuti asankhe zinthu mwanzeru. Akhoza kusankha kukwatirana kapena kuthetsa chibwenzicho. Ngati asankha kuthetsa chibwenzi sizitanthauza kuti chibwenzicho sichinawathandize. M’malomwake, chinakwaniritsa cholinga chake chifukwa chinawathandiza kuti adziwe zoyenera kusankha.

4 Koma nkhani yokhala pa chibwenzi tiyenera kumaiona moyenera. N’chifukwa chiyani tikutero? Ngati munthu yemwe sali pa banja ali ndi maganizo oyenera, sangachite chibwenzi ndi munthu yemwe akudziwiratu kuti sadzakwatirana naye. Koma si anthu omwe sali pa banja okha amene ayenera kukhala ndi maganizo oyenera. Tonsefe tiyenera kukhala ndi maganizo oyenera pa nkhaniyi. Mwachitsanzo, ena amaganiza kuti ngati anthu ali pa chibwenzi, ndiye kuti basi akuyenera kudzakwatirana. Kodi maganizo amenewa amakhudza bwanji Akhristu omwe sali pa banja? Mlongo wina wosakwatiwa dzina lake Melissa, wa ku United States, anati: “A Mboni ena akaona m’bale ndi mlongo ali pa chibwenzi, amangoganiza kuti basi ndiye kuti adzakwatirana. Chifukwa cha zimenezi, ena amalephera kuthetsa chibwenzi ngakhale ataona kuti sichikuyenda bwino. Ndipo ena safuna n’komwe kukhala pa chibwenzi. Zimenezi zimachititsa kuti uzikhala ndi nkhawa.”

w24.05 22 ¶8

Kodi Mungatani Kuti Mupeze Munthu Wokwatirana Naye?

8 Kodi mungachite bwanji zinthu mosamala pamene mukufuna kumudziwa bwino munthu wina? Pamisonkhano yampingo kapena pocheza pagulu, mukhoza kuona mmene munthuyo amakondera Yehova, khalidwe lake komanso mmene amachitira zinthu. Kodi amacheza ndi anthu ati, nanga amakonda kukamba nkhani zotani? (Luka 6:45) Kodi zolinga zake zikufanana ndi zanu? Mungathenso kufunsa akulu mumpingo wake kapena Akhristu ena olimba mwauzimu amene akumudziwa bwino. (Miy. 20:18) Mungawafunse za mbiri yake komanso makhalidwe ake. (Rute 2:11) Pamene mukufuna kumudziwa bwino munthu, muyenera kusamala kuti musakhale ngati mukumulondalonda. Muzilemekeza maganizo ake, musamamupanikize ndipo musamayese kufufuza chilichonse chokhudza iyeyo.

w24.05 28 ¶7-8

Kodi Mungatani Kuti Chibwenzi Chanu Chiziyenda Bwino?

7 Kodi mungatani kuti mumudziwe bwino mnzanuyo? Mungachite zimenezi pomalankhulana momasuka komanso moona mtima, kufunsa mafunso ndiponso kumvetsera. (Miy. 20:5; Yak. 1:19) Kuti zimenezi zitheke, mwina mungakonze zochitira limodzi zinthu zina ngati kudyera limodzi, kukayenda kumalo opezeka anthu ambiri komanso kulalikira limodzi. Kuwonjezera pamenepo, muzikonza zochita zinthu zomwe zingakuthandizeni kudziwa mmene mnzanuyo amachitira zinthu pa nthawi zosiyanasiyana komanso akakhala ndi anthu osiyanasiyana monga anzanu ndi achibale anu. Taonani zimene Aschwin wa ku Netherlands ankachita pa nthawi yomwe anali pa chibwenzi ndi Alicia. Iye anati: “Tinkachitira limodzi zinthu zomwe zikanatithandiza kuti tidziwane bwino. Nthawi zambiri zimenezi zinkakhala zinthu zing’onozing’ono monga kuphikira limodzi chakudya kapena kugwirira limodzi ntchito zapakhomo. Tikamachita zimenezi, aliyense ankatha kudziwa zomwe mnzake amachita bwino komanso zimene zimamuvuta.”

8 Mungadziwanenso bwino mukamaphunzira limodzi mfundo za m’Baibulo. Mukadzakwatirana, mudzafunika kumapeza nthawi yochita kulambira kwa pa banja n’cholinga choti Mulungu azitsogolera banja lanulo. (Mlal. 4:12) Ndiye bwanji panopa pamene muli pa chibwenzi osakonza zoti nthawi zina muziphunzira limodzi? N’zoona kuti anthu akakhala pa chibwenzi sizitanthauza kuti ali pa banja, komanso m’baleyo sakhala mutu wa mlongoyo. Komabe kuphunzira limodzi pafupipafupi kungakuthandizeni kudziwa mmene mnzanuyo amakondera Yehova. Max ndi Laysa, omwe amakhala ku United States, anaona kuti zimenezi zimathandizanso mwa njira ina. Max anati: “Titangoyamba chibwenzi, tinayamba kuphunzira limodzi nkhani zokhudza chibwenzi komanso moyo wa banja. Kuphunzira limodzi nkhani zimenezi, kunatithandiza kuti tiyambe kukambirana zinthu zofunika kwambiri zomwe mwina zikanakhala zovuta kuti tiyambe kuzikambirana.”

Mfundo Zothandiza

it-2 196 ¶7

Nyale

Mogwirizana ndi Miyambo 20:27, “mpweya wa munthu ndi nyale ya Yehova. Imafufuza zinthu zamkati mwa mtima wake.” Mpweya wa munthu, kapena kuti zomwe amalankhula, kaya zabwino kapena zoipa, zimasonyeza umunthu wake, kapena kuti mmene munthuyo alili.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

ijwbq nkhani na. 159

Kodi Zinyama Zimapita Kumwamba?

Baibulo limaphunzitsa kuti pa zolengedwa zonse zomwe zili padziko lapansi, ndi anthu ochepa okha omwe adzapite kumwamba. (Chivumbulutso 14:1, 3) Anthuwo adzapita kumwamba kuti akalamulire limodzi ndi Yesu monga mafumu komanso ansembe. (Luka 22:28-30; Chivumbulutso 5:9, 10) Koma anthu ambiri adzaukitsidwa kuti akhale ndi moyo m’paradaiso padziko lapansi.​—Salimo 37:11, 29.

Baibulo silimanena kuti ziweto kapena agalu zidzapita kumwamba. Tikutero chifukwa choti zinyama sizingakwanitse kutsatira mfundo za m’Baibulo zozithandiza kuyenerera ‘kuitanidwa kumwamba.’ (Aheberi 3:1) Mfundozi zikuphatikizapo kuphunzira, kukhala ndi chikhulupiriro komanso kumvera malamulo a Mulungu. (Mateyu 19:17; Yohane 3:16; 17:3) Choncho anthu okha ndi amene anapatsidwa chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha.​—Genesis 2:16, 17; 3:22, 23.

Kuti zolengedwa zapadziko zipite kumwamba, zimafunika ziukitsidwe kaye. (1 Akorinto 15:42) M’Baibulo muli nkhani za anthu angapo omwe anaukitsidwa kwa akufa. (1 Mafumu 17:17-24; 2 Mafumu 4:32-37; 13:20, 21; Luka 7:11-15; 8:41, 42, 49-56; Yohane 11:38-44; Machitidwe 9:36-42; 20:7-12) Koma onsewa anali anthu, osati zinyama.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena