NYIMBO 6
Kumwamba Kumalengeza Ulemerero wa Mulungu
Losindikizidwa
1. Zakumwamba zimatamanda M’lungu.
Zomwe analenga
N’zochititsa chidwi.
Zimalengeza ulemerero.
Timazindikira kuti
Alidi ndi mphamvu.
2. Malamulo a M’lungu ndi abwino.
Mawu ake onse
Amatiteteza.
Amaweruzanso molungama.
Mawu ake ndi oona,
Amatithandiza.
3. Tiziopa Mulungu mpaka kale.
Malamulo ake
Ali ngati nyale
Ndipotu amatitsogolera.
Dzina lake loyeralo
Tililemekeze.
(Onaninso Sal. 111:9; 145:5; Chiv. 4:11.)