Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu
© 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
JULY 7-13
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 21
Mfundo Zothandiza Kuti Banja Lizikhala Losangalala
Kodi Mungatani Kuti Muzisankha Zochita Mwanzeru?
Sitingasankhe zochita mwanzeru ngati tisankha mopupuluma. Miyambo 21:5 imachenjeza kuti: “Zoganizira za wakhama zichulukitsadi katundu; koma yense wansontho angopeza umphawi.” Mwachitsanzo, achinyamata amene ali m’chikondi chongotengeka maganizo sayenera kupupuluma kumanga banja. Apo phuluzi, adzaona zimene William Congreve, wolemba masewero achingelezi m’zaka za m’ma 1700 ananena, kuti: “Ukafulumira kulowa m’banja, umadzanong’oneza bondo pambuyo pake.”
Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Liziyenda Bwino
Dzichepetseni. “Musachite kanthu kalikonse ndi mzimu wandewu kapena wodzikuza, koma modzichepetsa, mukumaona ena kukhala okuposani.” (Afilipi 2:3) Kawirikawiri, mikangano m’banja imayamba chifukwa chakuti pakabuka vuto, kudzikuza kumachititsa kuti wina aziimba mlandu mnzake m’malo modzichepetsa n’kupeza njira zothetsera vutolo mokomera aliyense. Koma kudzichepetsa kungakuthandizeni kuchotsa maganizo odziona kuti olakwa siinu.
‘Ukondwere ndi Mkazi Wokula Naye’
13 Kodi zingakhale bwanji ngati banja likukumana ndi mavuto chifukwa cha zimene mwamuna ndi mkazi amachitirana? Zikatero, m’pofunika khama kuti apeze njira yothetsera mavutowo. Mwachitsanzo, n’kutheka kuti m’banja mwawomo munalowa mzimu wosalankhulana bwino ndipo tsopano kulankhulana kotero kwakhala chizolowezi chawo. (Miyambo 12:18) Monga momwe taonera m’nkhani yapitayi, zimenezi zingathe kusokoneza kwambiri banja. Mwambi wina m’Baibulo umati: “Kukhala m’chipululu kufunika kuposa kukhala ndi mkazi wolongolola ndi wong’ung’udza.” (Miyambo 21:19) Ngati ndinu mkazi m’banja loterolo, dzifunseni kuti, ‘Kodi khalidwe langa limapangitsa mwamuna wanga kuvutika kucheza nane?’ Baibulo limauza amuna kuti: “Kondani akazi anu, ndipo musawawire mtima iwo.” (Akolose 3:19) Ngati ndinu mwamuna, dzifunseni kuti, ‘Kodi sindisonyeza chikondi, moti mpaka mkazi wanga amaganiza zofuna kulimbikitsidwa ndi anthu ena?’ N’zoona kuti palibe chifukwa chomveka chochitira chiwerewere. Komabe, popeza kuti n’zotheka kuti zimenezi zichitike, ndi bwino kuti mabanja azikambirana mosapita m’mbali za mavuto awo.
Mfundo Zothandiza
Masomphenya a Ufumu wa Mulungu Asanduka Zenizeni
9 Yesu tsopano si munthu wamba wokwera pa mwana wa bulu, koma ndi Mfumu yamphamvu. Baibulo limafotokoza kuti wakwera pa kavalo, chomwe m’Baibulo chili chizindikiro cha nkhondo. (Miyambo 21:31) “Taonani, kavalo woyera,” likutero lemba la Chivumbulutso 6:2, “ndipo wom’kwerayo anali nawo uta; ndipo anam’patsa korona; ndipo anatulukira wolakika kuti alakike.” Komanso ponena za Yesu, wamasalmo Davide analemba kuti: “Yehova adzatumiza ndodo ya mphamvu yanu kuchokera ku Ziyoni; Chitani ufumu pakati pa adani anu.”—Salmo 110:2.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira
ijwfq nkhani na. 54
Kodi a Mboni za Yehova Amaiona Bwanji Nkhani Yothetsa Banja?
Timatsatira kwambiri zimene Baibulo limanena pa nkhani ya ukwati komanso kuthetsa banja. Pamene Mulungu ankayambitsa ukwati, ankafuna kuti mwamuna ndi mkazi azikhala limodzi kwa moyo wawo wonse. Baibulo limanena kuti banja likhoza kutha pokhapokha ngati wina m’banjamo wachita chigololo.—Mateyu 19:5, 6, 9.
Kodi a Mboni amathandiza mabanja amene akukumana ndi mavuto?
Inde, ndipo amachita zimenezi pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana monga:
Mabuku. Nthawi zambiri mabuku athu amakhala ndi nkhani zimene zingathandize mabanja, ngakhale amene akuoneka ngati sangayambenso kuyenda bwino. Mwachitsanzo, onani nkhani yakuti “Khalanibe Okhulupirika Muukwati Wanu,” “Kodi Mungatani Kuti Muzikhululukirana,” komanso yakuti “Zimene Mungachite Kuti Muyambirenso Kukhulupirirana.”
Misonkhano. Kumisonkhano yathu ya mpingo, yadera komanso yachigawo, timaphunzira malangizo a m’Baibulo amene angathandize mabanja.
Akulu. Akulu amathandiza mabanja amene akukumana ndi mavuto ndipo amachita zimenezi pogwiritsa ntchito malemba monga Aefeso 5:22-25.
Kodi akulu ayenera kuvomereza ngati wa Mboni akufuna kuthetsa banja?
Ayi. Ngati banja limene likukumana ndi mavuto litapempha akulu kuti alithandize, akuluwo sakuyenera kusankhira zochita banjalo.(Agalatiya 6:5) Komabe, ngati munthu angathetse banja pa zifukwa zosagwirizana ndi zimene Baibulo limanena, sangakhale ndi mwayi wochita utumiki wapadera mu mpingo komanso alibe ufulu wokwatira kapena kukwatiwanso.—1 Timoteyo 3:1, 5, 12.
Kodi a Mboni amaiona bwanji nkhani yopatukana?
Baibulo limalimbikitsa anthu okwatirana kuti ayenera kukhalabe limodzi ngakhale pamene zinthu sizikuyenda bwino. (1 Akorinto 7:10-16) Mavuto ambiri akhoza kuthetsedwa popemphera mochokera pansi pa mtima, kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo komanso kusonyezana chikondi.—1 Akorinto 13:4-8; Agalatiya 5:22.
Komabe, Akhristu ena amasankha kupatukana ngati akukumana ndi mavuto aakulu kwambiri monga:
Kulephera kusamalira banja mwadala.—1 Timoteyo 5:8.
Nkhanza—Salimo 11:5.
Ngati moyo wauzimu uli pangozi. Mwachitsanzo, mwamuna kapena mkazi yemwe si wa Mboni angakakamize mnzake wa mu ukwati yemwe ndi wa Mboni kuti achite zina zake zosemphana ndi malamulo a Mulungu. Zikatero, amene akukakamizidwayo akhoza kusankha kuti apatukane ndi mnzakeyo chifukwa kuchita zimenezi ndi njira yokhayo imene ingamuthandize kuti ‘amvere Mulungu monga wolamulira, osati anthu.’—Machitidwe 5:29.
JULY 14-20
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 22
Mfundo Zothandiza Polera Ana
Kodi Ana Anu Akadzakula Azidzatumikira Mulungu?
7 Ngati muli pabanja ndipo mumafuna mutakhala ndi ana mungadzifunse kuti: ‘Kodi ndife anthu odzichepetsa komanso timakonda Yehova ndi Mawu ake? Kodi Yehova angatisankhe kuti tikhale makolo a ana omwe amawaona kuti ndi amtengo wapatali?’ (Sal. 127:3, 4) Ngati ndinu kholo mungadzifunse kuti: ‘Kodi ndimaphunzitsa ana anga kuti aziona kufunika kogwira ntchito mwakhama?’ (Mlal. 3:12, 13) Kodi ndimayesetsa kuteteza ana anga ku zinthu zoopsa zimene angakumane nazo m’dziko la Satanali?’ (Miy. 22:3) Simungathe kuteteza ana anu ku mavuto onse amene angakumane nawo. Zimenezo n’zosatheka. Koma mungawathandize kukonzekera mavuto amene angakumane nawo popitiriza kuwaphunzitsa mwachikondi kuti azidalira malangizo opezeka m’Mawu a Mulungu. (Werengani Miyambo 2:1-6.) Mwachitsanzo, ngati wachibale wanu wina wasiya kutumikira Yehova, muzithandiza ana anu pogwiritsira ntchito Baibulo kuti adziwe kufunika kopitirizabe kukhala okhulupirika kwa Yehova. (Sal. 31:23) Kapena ngati munthu wina amene mumamukonda wamwalira muzisonyeza ana anu mavesi a m’Baibulo amene angawathandize kupirira chisoni chimene ali nacho komanso kuti akhale ndi mtendere.—2 Akor. 1:3, 4; 2 Tim. 3:16.
Kuphunzitsa Mwana Kuyambira Ali Wakhanda
17 Muziyamba kuphunzitsa ana adakali aang’ono. Zinthu zimayenda bwino makolo akayamba kuphunzitsa ana awo adakali aang’ono. (Miy. 22:6) Chitsanzo ndi Timoteyo, amene ankayenda ndi mtumwi Paulo. Mayi ake a Timoteyo dzina lawo a Yunike ndi agogo ake dzina lawo a Loisi ankamuphunzitsa kuyambira ali “wakhanda.”—2 Tim. 1:5; 3:15.
18 M’bale wina dzina lake Jean-Claude ndi mkazi wake Peace, omwenso amakhala ku Côte d’Ivoire, anathandiza ana awo onse 6 kuti azikonda Yehova komanso kumutumikira. Kodi n’chiyani chinawathandiza? Iwo anatsatira chitsanzo cha Yunike ndi Loisi. Banjali linati: “Tinayamba kukhomereza Mawu a Mulungu mwa ana athu pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene anabadwa.”—Deut. 6:6, 7.
19 Kodi mawu akuti “kukhomereza” Mawu a Mulungu mwa ana amatanthauza chiyani? “Kukhomereza” kumatanthauza “kuphunzitsa ndi kukumbutsa mobwerezabwereza.” Kuti zimenezi zitheke, makolo ayenera kukhala ndi nthawi yambiri yocheza ndi ana awo. Nthawi zina, kulangiza ana mobwerezabwereza kungaoneke kotopetsa. Komabe makolo ayenera kuona kuti imeneyi ndi njira yothandizira ana awo kumvetsa Mawu a Mulungu komanso kuwagwiritsa ntchito.
Makolo Khalani Chitsanzo Chabwino kwa Ana Anu
Inde, ana ndi ana basi, ndipo ena n’ngosamva ndipo mwinanso amatha kulowerera. (Genesis 8:21) Kodi makolo angatani? Baibulo limati: “Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana; koma ntyole yom’langira idzauingitsira kutali.” (Miyambo 22:15) Anthu ena amaona kuti kulanga mwana m’njira imeneyi ndi nkhanza ndipo kuti n’kwachikale. N’zoona kuti Baibulo limadana ndi zachiwawa ndiponso kuzunza munthu m’njira ina iliyonse. Komano nthawi zina mawu akuti “ntyole” amatanthauza udindo umene makolo ali nawo womwe amaugwiritsa ntchito mosalekerera koma mwachikondi komanso moyenerera pofuna kuti ana awo adzakhale ndi moyo wosatha.—Ahebri 12:7-11.
Mfundo Zothandiza
Muzisangalala ndi Utumiki Wanu
11 Mofanana ndi zimenezi, ifenso tingamasangalale kwambiri ngati titakhala akhama pa chilichonse chimene timachita potumikira Yehova. Nthawi zonse ‘tizitanganidwa kwambiri’ ndi ntchito yolalikira ndipo tizidzipereka ndi mtima wonse pogwira ntchito zamumpingo. (Mac. 18:5; Aheb. 10:24, 25) Muzikonzekera bwino misonkhano n’cholinga choti muzikapereka ndemanga zolimbikitsa. Muzikonzekeranso bwino mukapatsidwa nkhani za ophunzira pamisonkhano ya mkati mwa mlungu. Mukapemphedwa kuti mugwire ntchito inayake mumpingo, muzisunga nthawi komanso muzikhala odalirika. Musamaone kuti zimene mwapemphedwa n’zosafunika kapena kungotaya nthawi. Muziyesetsa kuwonjezera luso lanu. (Miy. 22:29) Mukamadzipereka kwambiri pa utumiki wanu, m’pamenenso mumapita patsogolo mofulumira ndipo mumasangalala. (Agal. 6:4) Zimenezi zingakuthandizeninso kuti muzisangalala ndi ena akapatsidwa utumiki umene inuyo mumaulakalaka.—Aroma 12:15; Agal. 5:26.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Nkhani
ijwyp nkhani na. 100
Kodi Ndingatani Ngati Sindinamvere Lamulo la Makolo Anga?
Zimene zingathandize
Muzivomereza zimene mwalakwitsa. Baibulo limanena kuti: “Wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino.” (Miyambo 28:13) Makolo anu amadziwa kuti si inu wangwiro. Koma funso n’kumati, Kodi mumachita zinthu moona mtima?
“Makolo adzakuchitira chifundo ngati unena zoona zake. Ukavomereza zimene wachita, adzayamba kukhulupirira kuti ndiwe woona mtima komanso wokhulupirika.”—Olivia.
Muzipepesa. Baibulo limanena kuti: “Muzichitirana zinthu modzichepetsa.” (1 Petulo 5:5) Kunena kuti “pepani” komanso kupewa kupereka zifukwa zodzikhululukira kumafuna kudzichepetsa.
“Anthu amene nthawi zonse amapereka zifukwa zodzikhululukira akhoza kuwononga chikumbumtima chawo. Kenako akhoza kusiyiratu kudziimba mlandu akachita zinthu zoipa.”—Heather.
Muzivomereza chilango chimene mwalandira. Baibulo limanena kuti: “Mverani malangizo.” (Miyambo 8:33) Muzipewa kudandaula ndipo muzichita zinthu mogwirizana ndi chilango chimene makolo anu akupatsani.
Ukamangodandauladandaula ndi chilango chimene walandira, zinthu zikhoza kuipa kwambiri. Uziyesetsa kungovomereza chilangocho m’malo mochiganizira kwambiri.”—Jason.
Muziyesetsa kukhala wodalirika. Baibulo limanena kuti: “Muvule umunthu wakale umene umagwirizana ndi khalidwe lanu lakale.” (Aefeso 4:22) Muyambe kuchita zinthu zosonyeza kuti ndinu wodalirika.
“Nthawi zonse ukamayesetsa kusankha zochita mwanzeru n’kumasonyeza makolo ako kuti sudzachitsanso zimene unalakwitsazo, iwo adzayambanso kukukhulupirira.”—Karen.
ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI: Muzichita zonse zimene mungathe posonyeza kuti ndinu wodalirika. Mwachitsanzo, mukachoka pakhomo, muziuza makolo pamene muli m’njira yobwerera kunyumba ngakhale ngati simufika mochedwa. Izi zingawasonyeze kuti mukufuna kuti iwo azikukhulupirirani.
JULY 21-27
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 23
Mfundo Zothandiza pa Nkhani ya Mowa
Mowa Umafunika Kusamala Nawo
5 Bwanji ngati munthu amamwa mowa koma mosamala moti ena sangam’zindikire kuti waledzera? Anthu ena sadziwika kwenikweni kuti aledzera ngakhale atamwa mowa wambiri. Koma, kuganizira kuti palibe vuto lililonse ngati achita zimenezi, n’kudzinyenga chabe. (Yeremiya 17:9) M’kupita kwanthawi ndiponso pang’ono ndi pang’ono, munthu akhoza kufika mpaka pomadwala akapanda kumwa mowa ndiponso angathe ‘kukodwa nacho chikondi cha pavinyo.’ (Tito 2:3) Ponenapo za mmene munthu amakhalira chidakwa, mayi wina wolemba mabuku, dzina lake Caroline Knapp, anati: “Chizolowezichi chimayamba pang’onopang’ono, mosadziwika bwinobwino ndiponso moti munthu sangathe kufotokoza.” Kumwa kwambiri ndi msampha woopsadi kwambiri.
6 Komanso, taganizirani chenjezo la Yesu lakuti: “Koma mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha; pakuti lidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pankhope padziko lonse lapansi.” (Luka 21:34, 35) Munthu amaodzera ndiponso kufooka ndi mowa asanafike poledzera nawo, ndipo izi zingasokonezenso moyo wake wauzimu. Kodi zingakhale bwanji tsiku la Yehova litam’peza ali choncho?
it-1 656
Kuledzera
Baibulo Limaletsa. Kumwa zakumwa zaukali mpaka kufika poledzera ndi koletsedwa m’Baibulo. Munthu wanzeru yemwe analemba buku la Miyambo anafotokoza momveka bwino kwambiri komanso molondola zomwe zimachitikira munthu yemwe wamwa mowa kwambiri. Iye ananena kuti: “Ndi ndani amene akuvutika? Ndi ndani amene ali ndi nkhawa? Ndi ndani amene ali pa mikangano? Ndi ndani amene ali ndi madandaulo? Ndi ndani amene ali ndi mabala popanda chifukwa? Ndi ndani amene ali ndi maso ofiira? Ndi amene amakhala nthawi yaitali akumwa vinyo, amene amafunafuna vinyo wosakaniza. Usakopeke ndi kufiira kwa vinyo, pamene akunyezimira m’kapu [pamene amaoneka wokopa] n’kumatsetserekera kukhosi mwamyaa! Chifukwa pamapeto pake amaluma ngati njoka, ndipo amatulutsa poizoni ngati mphiri [amayambitsa matenda ngati a chiwindi komanso matenda ena okhudza kusokonezeka ubongo, monga kunjenjemera ndi kuona zinthu zimene palibepo, ndipo nthawi zinanso munthu akhoza kufa]. Maso ako adzaona zinthu zachilendo [mowa umayamba kulamulira ubongo wa munthu ndipo amasiya kuona zinthu moyenera, amaona zinthu zimene palibepo, m’mutu mwake mumadzaza nkhani zosangalatsa za zinthu zimene zamuchitikira komanso amachita zinthu mosadziletsa], ndipo mtima wako udzalankhula zinthu zokhota [zomwe ankaganiza komanso zomwe ankalakalaka koma sizinkabwera poyera, amayamba kuzitulutsa].”—Miy 23:29-33; Ho 4:11; Mt 15:18, 19.
Wolembayu anapitiriza kufotokoza zimene zimachitikira munthu woledzera: “Udzakhala ngati munthu amene wagona pakatikati pa nyanja, [amamva ngati mmene munthu amamvera akamamira m’madzi kenako n’kukomoka] komanso ngati munthu amene wagona pansonga ya mtengo wa ngalawa [mofanana ndi ngalawa imene ikuwindukawinduka chifukwa cha mafunde, moyo wa munthu woledzera umakhala pachiopsezo chifukwa akhoza kuchita ngozi, kufa ziwalo, kuchita ndewu ndi zina zambiri]. Udzanena kuti: ‘Andimenya koma sindinamve kupweteka. Andikuntha koma sindinadziwe chilichonse [amatero munthu woledzera ngati kuti akudzilankhulira yekha; amakhala kuti sakudziwa zimene zinamuchitikira ndipo saphunzirapo kanthu]. Kodi ndidzuka nthawi yanji? Ndikufuna ndikamwenso wina [amagona kaye kuti mowawo umuthere m’mutu, koma chifukwa choti amaukondetsetsa, amakhala kapolo ndipo amaona kuchedwa kuti akamwenso wina].’” Amasauka chifukwa amawononga ndalama zambiri pogulira mowa ndipo amakhala wosadalirika chifukwa amalephera kugwira ntchito bwinobwino.—Miy 23:20, 21, 34, 35.
Mfundo Zothandiza
Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Mwachitsanzo, kunenepa mopyola muyeso kungathe kukhala chizindikiro cha kususuka, koma sikuti ndi mmene zimakhalira nthawi zonse. Munthu angathe kunenepa kwambiri chifukwa cha matenda. Mwinanso zingakhale zotengera kwa makolo. Tiyeneranso kukumbukira kuti tikamanena kuti munthu ndi wonenepa mopyola muyeso timakhala tikunena za thupi lake, pamene tikanena za kususuka timakhala tikunena za maganizo ake. Kunenepa mopyola muyeso amati ndi “kuchuluka mafuta m’thupi,” pamene kususuka ndi “umbombo kapena kudya mosadziletsa.” Motero, kukula kwa thupi la munthu sichizindikiro cha kususuka. Chizindikiro chake ndi mmene munthuyo amaonera chakudya. Munthu angathe kukhala wathupi labwinobwino kapena wochepa thupi koma ali wosusuka. Komanso, mmene anthu a m’dera lina amaonera nkhani ya kunenepa moyenerera kapena kuumbika kwabwino kwa thupi zimasiyana kwambiri ndi mmene anthu a m’dera linanso angaonere nkhanizi.
JULY 28–AUGUST 3
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 24
Muzikonzekera Mavuto
it-2 610 ¶8
Chizunzo
Akhristu amazindikiranso mphoto imene anthu omwe akupirira adzalandire. Ponena za mphotoyo, Yesu anenana kuti: “Osangalala ndi anthu amene azunzidwa chifukwa cha chilungamo chifukwa Ufumu wakumwamba ndi wawo.” (Mt 5:10) Kudziwa za chiyembekezo chakuti akufa adzauka komanso kudziwa bwino amene amapereka chiyembekezo chimenechi kumawathandiza kukhala olimba. Kumawathandizanso kukhala okhulupirika kwambiri kwa Mulungu ngakhale pamene akuopsezedwa ndi anthu ankhanza kuti awapha. Chifukwa chokhulupirira zimene imfa ya Yesu inakwaniritsa, iwo saopanso kuphedwa mwankhanza. (Ahe 2:14, 15) Kuti Mkhristu akhalebe wokhulupirika pamene akutsutsidwa, amafunika kukhala ndi maganizo oyenera. ‘Khalani ndi maganizo amenenso Khristu Yesu anali nawo. Iye anakhala womvera mpaka imfa, inde imfa yapamtengo wozunzikirapo.’ (Afi 2:5-8) “Chifukwa chodziwa kuti adzasangalala m’tsogolo, anapirira mtengo wozunzikirapo. Iye sanasamale kuti zochititsa manyazi zimuchitikira.”—Ahe 12:2; onaninso 2Ak 12:10; 2At 1:4; 1Pe 2:21-23.
Khalanibe ndi Chimwemwe Mukamakumana ndi Mavuto
12 Lemba la Miyambo 24:10 limanena kuti: “Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako ichepa.” Mwambi winanso umati: “Moyo umasweka ndi zowawa za m’mtima.” (Miy. 15:13) Akhristu ena amakhumudwa kwambiri mpaka kusiya kuwerenga Baibulo ndi kusinkhasinkha Mawu a Mulungu. Mapemphero awo amangokhala amwambo ndipo amasiya kucheza ndi olambira anzawo. N’zoonekeratu kuti kukhala wokhumudwa kwanthawi yaitali kungativulaze.—Miy. 18:1, 14.
13 Komabe kukhala ndi maganizo abwino kungatithandize kuika maganizo athu pa zinthu zimene zingatichititse kukhala osangalala pa moyo wathu. Davide analemba kuti: “Kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga.” (Sal. 40:8) Tikamakumana ndi mavuto, tisamayerekeze n’komwe kusiya kuchita zinthu zauzimu. Ndipotu njira yabwino yothetsera kukhumudwa ndiyo kuchita zinthu zimene zingatithandize kukhala osangalala. Yehova amatiuza kuti tingakhale osangalala mwa kuwerenga Mawu ake ndi kuwasinkhasinkha nthawi zonse. (Sal. 1:1, 2; Yak. 1:25) M’Baibulo ndiponso pamisonkhano yachikhristu timalandira “mawu okoma” amene angatilimbikitse komanso kutithandiza kukhala osangalala.—Miy. 12:25; 16:24.
Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Lemba la Miyambo 24:16 limati: “Wolungama akhoza kugwa ngakhale nthawi 7 ndipo ndithu adzadzukanso.” Kodi pamenepa akunena za munthu amene amachita machimo mobwerezabwereza koma kenako Mulungu n’kumukhululukira?
Zimenezi si zimene lembali limatanthauza. M’malomwake lembali likutanthauza kuti munthu akakumana ndi mavuto ambiri amakhala ngati wagwa, ndipo akakwanitsa kuwapirira zimakhala ngati wadzukanso.
Choncho zonsezi zikusonyeza kuti lemba la Miyambo 24:16, silikunena za kuchita tchimo koma likunena za kukumana ndi mavuto mobwerezabwereza. M’dziko loipali munthu wolungama angakumane ndi mavuto a thanzi, kapenanso mavuto ena. Akhozanso kuzunzidwa ndi boma chifukwa cha chikhulupiriro chake. Koma amakhulupirira kuti Mulungu angamuthandize kuti athe kupirira komanso kuti zinthu zimuyendere bwino. Mwina mungadzifunse kuti: ‘Kodi sindimaona kuti nthawi zambiri atumiki a Mulungu zinthu zimawayendera bwino?’ N’zolimbikitsa kuti “Yehova amachirikiza amene ali pafupi kugwa, ndipo amaweramutsa onse amene awerama chifukwa cha masautso.”—Sal. 41:1-3; 145:14-19.
Mfundo Zothandiza
Mafunso Ochokera kwa Owerenga
M’nthawi za m’Baibulo, ngati munthu akufuna “kumanga nyumba” yake kapena kuti kukhazikika pokwatira n’kukhala ndi ana, anayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndine wokonzeka kusamalira ndi kuthandiza mkazi ndiponso ana amene tingakhale nawo?’ Asanakhale ndi banja, anayenera kugwira kaye ntchito kumunda. N’chifukwa chake Baibulo la Today’s English Version linamasulira vesili motere: “Usamange nyumba yako n’kukhala ndi banja pamene sunakonzeke kumunda kwako, ndipo sunatsimikize kuti uzidzapeza zofunika pa moyo.” Kodi mfundo imeneyi imagwiranso ntchito masiku ano?
Inde. Mwamuna amene akufuna kukwatira ayenera kukonzekera bwino udindo umenewo. Ngati angathe, ayenera kugwira ntchito. N’zoona kuti ntchito imene mwamuna ayenera kuchita posamalira banja lake, siyenera kukhala yongodyetsa kapena kuveka banjalo basi. Mawu a Mulungu amasonyeza kuti mwamuna amene sakonda banja lake ndiponso salisamalira mwakuthupi ndi mwauzimu, amaipa kuposa munthu wopanda chikhulupiriro. (1 Tim. 5:8) Motero, pokonzekera ukwati ndiponso moyo wabanja, mwamuna ayenera kudzifunsa mafunso monga akuti: ‘Kodi ndine wokonzeka kupezera banja langa zinthu zofunikira mwakuthupi? Kodi ndine wokonzeka kukhala mutu wa banja pa nkhani zauzimu? Kodi ndidzakwanitsa udindo wochita phunziro la Baibulo mokhazikika ndi mkazi komanso ana anga?’ Mawu a Mulungu amagogomezera kwambiri maudindo amenewa.—Deut. 6:6-8; Aef. 6:4.
Motero mnyamata amene akufuna kukwatira ayenera kuganizira bwino mfundo ya pa Miyambo 24:27. Mtsikananso ayenera kudzifunsa ngati ali wokonzeka kukwaniritsa udindo wokhala mkazi ndiponso mayi. Komanso achinyamata amene angokwatirana kumene ayenera kudzifunsa mafunso omwewa ngati akuganiza zokhala ndi ana. (Luka 14:28) Anthu a Mulungu akatsatira malangizo amenewa, amapewa mavuto ambiri ndipo amasangalala ndi moyo wabanja.
AUGUST 4-10
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 25
Mfundo Zothandiza Kuti Tizilankhula Bwino
Muzigwiritsa Ntchito Bwino Lilime Lanu
6 Lemba la Miyambo 25:11 limasonyeza kufunika kosankha bwino nthawi yolankhula. Limati: “Mawu olankhulidwa pa nthawi yoyenera ali ngati zipatso za maapozi agolide m’mbale zasiliva.” Zinthu zagolide zimakhala zokongola ndipo mukaziika m’mbale zasiliva zimaoneka bwino kwambiri. Choncho lembali likusonyeza kuti tikasankha mawu abwino n’kuwalankhulanso pa nthawi yoyenera, tingalimbikitse amene tikulankhula naye. Koma kodi tingachite bwanji zimenezi?
7 Zimene tikufuna kunena zikhoza kukhala zolimbikitsa, komabe ngati sitinazilankhule pa nthawi yoyenera sizingathandize. (Werengani Miyambo 15:23.) Mwachitsanzo mu March 2011, ku Japan kunachitika chivomerezi komanso kunasefukira madzi ndipo mizinda yambiri inawonongeka. Anthu oposa 15,000 anafa. Ngakhale kuti abale ndi alongo akuderali nawonso anakhudzidwa ndi vutoli, anayesetsa kulimbikitsa anzawo pogwiritsa ntchito Baibulo. Komabe anthu ambiri akumeneko ndi achipembedzo chachibuda moti sadziwa mfundo za m’Baibulo ndipo amakhulupirira zosiyana kwambiri ndi zimene limaphunzitsa. Choncho abale anadziwa kuti nthawiyi sinali yabwino kuti auze anthu amene anaferedwa zoti Mulungu adzaukitsa akufa. M’malomwake anangowalimbikitsa n’kuwauza kuchokera m’Baibulo chifukwa chake anthu abwino nawonso amakumana ndi mavuto
Muzigwiritsa Ntchito Bwino Lilime Lanu
15 Tikafuna kulankhula zinazake, tiyeneranso kuganizira mmene tingalankhulire. Pamene Yesu ankalankhula m’sunagoge wa kwawo ku Nazareti, anthu ambiri ‘anadabwa ndi mawu ake ogwira mtima.’ (Luka 4:22) Tikamalankhula mwaulemu, mawu athu amakhala ogwira mtima ndipo anthu savutika kutsatira zimene tanena. (Miy. 25:15) Tingatsanzire Yesu polankhula mokoma mtima ndiponso kuchita zinthu moganizira ena. Pa nthawi ina, anthu anayesetsa kupita kumene kunali Yesu, n’cholinga choti akamve mawu ake. Iye atawaona, anawamvera chifundo ndipo “anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.” (Maliko 6:34) Ngakhale pamene anthu ankamunyoza, sanabwezere ndi mawu achipongwe.—1 Pet. 2:23.
16 Nthawi zina zimakhala zovuta kulankhula mwaulemu kwa achibale kapena anzathu mu mpingo chifukwa choti tinawazolowera. Tingaganize kuti tikhoza kuwalankhula mawu alionse ndipo sangakhumudwe. Koma kodi Yesu ankaona kuti akhoza kulankhula mawu alionse kwa ophunzira ake chifukwa choti anali anzake? Ayi. Mwachitsanzo, atumwi ake atakangana pa nkhani yakuti wamkulu ndani, Yesu anawathandiza mokoma mtima pogwiritsa ntchito chitsanzo cha mwana wamng’ono. (Maliko 9:33-37) Nawonso akulu angachite bwino kutsanzira Yesu popereka malangizo “ndi mzimu wofatsa.”—Agal. 6:1.
Fulumizanani ku Chikondano ndi Ntchito Zabwino—Motani?
8 Potumikira Mulungu wathu, tonsefe tingalimbikitsane mwa chitsanzo chathu. Yesu analimbikitsa amene ankamumvetsera. Iye ankakonda ntchito yolalikira ndipo ankaiona kuti ndi yofunika kwambiri. Iye anati inali ngati chakudya chake. (Yohane 4:34; Aroma 11:13) Ena sangachedwe kutengera khama loterolo. Kodi nanunso mungachititse kuti anthu aziona kuti mukusangalala ndi utumiki wanu? Muzifotokozera ena mumpingo zokumana nazo zanu zabwino, koma muzipewa kudzitamandira. Mukamapempha ena kuti agwire nanu ntchito yolalikira, muziona ngati mungawathandize kuti azisangalala kwambiri kuuza ena zokhudza Mlengi wathu Wamkulu, Yehova.—Miyambo 25:25.
Mfundo Zothandiza
it-2 399
Kufatsa
Munthu wofatsa amakwanitsa kukhala ndi khalidweli chifukwa choti amakhala ndi chikhulupiriro komanso mphamvu. Ndi munthu woti sasunthika mosavuta moti ena sangamuchititse kuti asiye kuona zinthu moyenera. Munthu amene sachita zinthu mofatsa, amatero chifukwa choti akudzimva kuti ndi wosatetezeka, wakwiya, alibe chikhulupiriro kapena chiyembekezo mwinanso wasowa mtengo wogwira. Buku la Miyambo limafotokoza za munthu amene si wofatsa kuti: “Munthu wosaugwira mtima ali ngati mzinda umene mpanda wake wagumulidwa.” (Miy 25:28) Zimakhala zosavuta kuti ayambe kuganiza zinthu zolakwika zomwe zingamupangitse kuti achite zinthu zolakwika.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Nkhani
ijwyp nkhani na. 23
Kodi Ndingatani Ngati Anthu Ena Akukonda Kunena za Ine?
1: Mukhoza kungozisiya. Nthawi zambiri zimakhala bwino kungozisiya makamaka ngati nkhaniyo si yaikulu kwenikweni. Mungagwiritse ntchito malangizo a m’Baibulo akuti: “Usamafulumire kukwiya mumtima mwako.”—Mlaliki 7:9.
“Anthu anayamba kufalitsa kuti ndinali pachibwenzi ndi mnyamata winawake woti sindinakumanepo naye. Zinandiseketsa kwambiri moti ndinangozisiya.”—Elise.
“Ngati munthu uli ndi mbiri yabwino sudandaula. Ngakhale anthu atafalitsa zinthu zoipa zokhudza iweyo, ndi anthu ochepa kwambiri amene angakhulupirire. Ndipo pamapeto pake zoona zake zimadziwika.”—Allison.
Yesani izi: Lembani (1) zimene zinanenedwa zokhudza inuyo ndi (2) mmene zinakukhudzirani. Mukalankhula “mumtima mwanu” mmene mukumvera, zimakhala zosavuta kungozisiya.—Salimo 4:4.
2: Mukhoza kulankhula ndi munthu yemwe wayambitsa nkhaniyo. Nthawi ina zimapezeka kuti anthu akufalitsa nkhani yaikulu yokhudza inuyo. Pamenepa mungachite bwino kulankhula ndi munthu amene anayambitsa nkhaniyo.
“Kulankhula ndi anthu amene anayambitsa nkhaniyo kungathandize anthuwo kudziwa kuti mumamva zimene amakunenani. Komanso kungathandize kuti zoona zake za nkhaniyo zidziwike kenako n’kuthetsa mabodzawo.”—Elise.
Mungachite bwino kuganizira mfundo za m’Baibulo zotsatirazi komanso kudzifunsa mafunsowo musanakalankhulane ndi munthu amene amakunenani.
“Munthu aliyense woyankhira nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa.” (Miyambo 18:13) ‘Kodi ndikudziwa zonse zokhudza nkhaniyi? Kodi munthu amene wandiuza kuti ndimanenedwayu anamvetsadi zimene anthuwo amanena?’
“Munthu aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula, wosafulumira kukwiya.” (Yakobo 1:19) ‘Kodi ino ndi nthawi yoyenera kulankhula ndi munthu amene amandinenayu? Kodi zimene ndikufuna kuchitazi ndi zoyenereradi? Kapena kodi ndikufunika kudikira kaye kuti mtima wanga ukhale m’malo?’
“Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.” (Mateyu 7:12) ‘Zikanakhala kuti ineyo ndi amene ndimamunena munthuyu, kodi ndikanafuna kuti andilankhule bwanji? Kodi ndikanakonda kuti andilankhule pamalo otani? Kodi ndikanakonda kuti andilankhule mawu otani komanso kuti nkhope yake izioneka bwanji?’
Yesani izi: Musanakalankhule ndi munthu amene amakunenani, lembani zimene mukufuna mukanene. Kenako dikirani kwa mlungu umodzi kapena iwiri, werenganinso zimene munalembazo ndipo muone ngati mukufunika kusintha zina ndi zina. Mungachitenso bwino kukambirana ndi makolo anu kapena mnzanu woganiza bwino kuti akupatseni malangizo.
Mfundo yoona: Kunenedwa kuli m’gulu la zinthu zimene simungazipeweretu pa moyo wanu. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti palibe chomwe mungachite.
AUGUST 11-17
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 26
Muzipewa “Munthu Wopusa”
it-2 729 ¶6
Mvula
Nyengo. Nyengo zina ziwiri zomwe zinali ku Dziko Lolonjezedwa, zomwe ndi nyengo yotentha ndi yozizira, zingatchulidwenso kuti nyengo ya dzuwa ndi ya mvula. (Yerekezerani ndi Sl 32:4; Nym 2:11) Kuyambira chapakati pa mwezi wa April kufika chapakati pa mwezi wa October, sikunkagwa mvula yambiri. Mvula inkagwa yochepa pa nthawi imeneyi, yomwenso anthu ankakolola. Lemba la Miyambo 26:1, limasonyeza kuti anthu ankadabwa akaona mvula ikugwa munyengo yokolola. (Yerekezerani ndi 1Sa 12:17-19.) Munyengo ya mvula, sikuti mvulayo inkangokhalira kugwa ayi, koma nthawi zina kunkakhala kopanda mitambo n’komwe. Chifukwa choti imeneyi inkakhalanso nthawi yozizira, munthu akanyowa ndi mvula ankazizidwa kwambiri. (Eza 10:9, 13) Choncho anthu ankafunikira kukhala ndi malo abwino okhala.—Yes 4:6; 25:4; 32:2; Yob 24:8.
Chilango Chimabala Chipatso cha Mtendere
12 Anthu ena angafunikire chilango champhamvu monga mmene lemba la Miyambo 26:3 likusonyezera: “Chikwapu n’chokwapulira hatchi, zingwe n’zomangira pakamwa pa bulu, ndipo ndodo ndi yokwapulira msana wa anthu opusa.” Nthawi zina Yehova ankalola kuti Aisiraeli agonjetsedwe chifukwa cha zoipa zimene achita: “Chifukwa anapandukira mawu a Mulungu, ananyoza malangizo a Wam’mwambamwamba. Choncho Mulungu anawagwetsera mavuto kuti akhale ndi mtima wodzichepetsa. Iwo anapunthwa ndipo panalibe wowathandiza. Iwo anaitana Yehova kuti awathandize m’masautso awo, ndipo iye anawapulumutsa ku mavuto awo.” (Salimo 107:11-13) Komabe anthu ena opusa amakhala okanika moti palibe chilango chimene chingawathandize: “Munthu amene amaumitsa khosi lake pambuyo podzudzulidwa mobwerezabwereza adzathyoledwa mwadzidzidzi ndipo sadzachira.”—Miyambo 29:1.
it-2 191 ¶4
Kulumala
Mmene amagwirira ntchito m’buku la Miyambo. Mfumu yanzeru Solomo inanena kuti: “Munthu amene amasiya ntchito yake m’manja mwa munthu wopusa ali ngati munthu amene wapundula mapazi ake n’kudzivulaza yekha.” Kunena zoona, munthu amene amauza munthu wopusa kuti amugwirire ntchito, amakhala kuti sakuifunira zabwino ntchitoyo. N’zosakayikitsa kuti akhoza kuona ntchitoyo ikuwonongeka, ndipo zingamupweteke kwambiri.—Miy 26:6.
Mfundo Zothandiza
it-1 846
Wopusa
Kuyankha munthu wopusa “mogwirizana ndi uchitsiru wake” pofuna kubwezera mawu achipongwe amene akulankhula pamene mukukangana naye, kumapangitsa nonse awiri kuoneka kuti simuganiza bwino ndipo mulibe nzeru. Posafuna kufanana ndi munthu wopusa, lemba la Miyambo 26:4 limapereka malangizo akuti: “Usayankhe aliyense wopusa mogwirizana ndi uchitsiru wake.” Pomwe lemba la Miyambo 26:5 limasonyeza kuti kuyankha munthu wopusa “mogwirizana ndi uchitsiru wake” pofuna kutsutsana ndi zimene akunena, kumusonyeza kuti zimene akunenazo ndi zopanda nzeru komanso kumusonyeza kuti zimene akunenazo ndi zosiyana ndi zimene akuganiza, kukhoza kukhala kothandiza.
AUGUST 18-24
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 27
Anzathu Abwino Amatithandiza
Yehova Amaona Kuti Atumiki Ake Odzichepetsa Ndi Amtengo Wapatali
12 Munthu wodzichepetsa amayamikira akapatsidwa malangizo. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti muli kumisonkhano. Ndiye mutacheza ndi abale ndi alongo angapo, munthu wina akukutengerani pambali n’kukuuzani kuti kachakudya kenakake katsalira m’mano. N’zosachita kufunsa kuti mungachite manyazi. Koma mungayamikire kuti wakuuzani zimenezo ndipo mwina mukanakonda ngati wina akanakuuzani mwamsanga. Mofanana ndi zimenezi, tiyenera kudzichepetsa n’kumayamikira ngati Mkhristu mnzathu walimba mtima n’kutipatsa malangizo. Tiyenera kuona kuti munthuyo ndi mnzathu osati mdani wathu.—Werengani Miyambo 27:5, 6; Agal. 4:16.
it-2 491 ¶3
Munthu Woyandikana Naye Nyumba
Buku la Miyambo limatipatsa malangizo kuti tiyenera kukhulupirira komanso kudalira mnzathu pa nthawi imene tikufunika thandizo. “Usasiye mnzako kapena mnzawo wa bambo ako, ndipo usalowe m’nyumba ya mchimwene wako pa tsiku limene tsoka lakugwera. Munthu woyandikana naye nyumba amene ali pafupi ali bwino kuposa mchimwene wako amene ali kutali.” (Miy 27:10) Lembali likusonyeza kuti mnzako woyandikana naye amene mumagwirizana, ndi amene uyenera kumuona kuti ndi wofunika kwambiri ndipo ndi amene angakuthandize pamene ukufunika thandizo ngati m’bale wako weniweni amakhala kutali. M’bale wakoyo sangakhale wokonzeka kapena sangakwanitse kukuthandiza chifukwa choti ali kutali.
Achinyamata, Kodi Mudzachita Chiyani pa Moyo Wanu?
7 Nkhani ya Yehoasi ikutiphunzitsa kuti tizisankha anzathu omwe angatithandize kuti tizichita zabwino. Tizisankha anthu omwe amakonda Yehova komanso amafuna kumusangalatsa. Tisamangocheza ndi anthu amsinkhu wathu okha. Kumbukirani kuti Yehoasi anali wamng’ono kwambiri poyerekezera ndi mnzake Yehoyada. Mukamasankha anzanu muzidzifunsa kuti: ‘Kodi iwo amandithandiza kuti ndizikhulupirira kwambiri Yehova? Kodi amandilimbikitsa kuti ndizitsatira mfundo zake? Kodi amakonda kulankhula za Yehova komanso choonadi chake chamtengo wapatali? Kodi amalemekeza mfundo za Mulungu? Kodi iwo amangondiuza zinthu kuti andisangalatse kapena amalimba mtima n’kundiuza zimene ndikulakwitsa?’ (Miy. 27:5, 6, 17) Kunena zoona anthu amene sakonda Yehova sayenera kukhala anzanu. Koma ngati muli ndi anzanu omwe amakonda Yehova, pitirizani kucheza nawo chifukwa azikuthandizani.—Miy. 13:20.
Mfundo Zothandiza
bMfundo Zazikulu za M’buku la Miyambo
27:21. Zimene timachita akatiyamikira zimasonyeza kuti ndife anthu otani. Kutiyamikira kukatichititsa kudziwa kuti tatha kuchita zimenezo chifukwa cha Yehova ndi kutilimbikitsa kupitiriza kum’tumikira, timasonyeza kuti ndife odzichepetsa. Ngati tayamikiridwa ndiye n’kumadzimva ngati ndife opambana, timasonyeza kuti ndife odzitukumula.
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Nkhani
ijwyp nkhani na. 75
Ndingatani Ngati Mnzanga Atandikhumudwitsa?
Zimene mungachite
Mudzifufuze. Baibulo limati: “Usamafulumire kukwiya mumtima mwako, pakuti anthu opusa ndi amene sachedwa kupsa mtima.”—Mlaliki 7:9.
Alyssa ananena kuti: “Nthawi zina pakapita masiku m’pamene umaona kuti unangokhumudwa ndi zazing’ono.”
Zoti muganizire: Kodi mumangokhumudwa zilizonse? Kodi pali zimene mungachite kuti musamakhumudwe kwambiri ndi zomwe anzanu amachita?—Mlaliki 7:21, 22.
Muziganizira kufunika kokhululukira ena. Baibulo limati: ‘Kunyalanyaza cholakwa kumachititsa [munthu] kukhala wokongola.’—Miyambo 19:11.
Mallory ananena kuti: “Ngakhale utakhumudwa pa zifukwa zomveka, ndi bwino kukhululuka ndi mtima wonse. Ukatero siufunikanso kumangokumbutsa mnzakoyo zomwe analakwitsa kuti azingokhalira kukupepesa. Ukamukhululukira, nkhaniyo izitheranso pomwepo.”
Zoti muganizire: Kodi ndi nkhani yaikuludi? Kodi mungathe kungomukhululukira kuti mukhalenso pamtendere?—Akolose 3:13.
Muziganizira zofuna za mnzanuyo. Baibulo limati: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”—Afilipi 2:4.
Nicole ananena kuti: “Mukamakondana komanso kulemekezana, mumayesetsa kuti mugwirizanenso mwamsanga mukasemphana zochita. Mumakhala kuti munachitira limodzi zinthu zambiri choncho simungafune kuti musiyane.”
Zoti muganizire: Kodi mungathe kumvetsa chifukwa chimene chachititsa mnzanuyo kulankhula kapena kuchita zinthu zimenezo?—Afilipi 2:3.
Mfundo yofunika kwambiri: Muyenera kudziwiratu zimene mungachite anzanu akakukhumudwitsani ndipo zimenezi zidzakuthandizani mukadzakula. Yesetsani kuphunzira kuchita zimenezi panopa.
AUGUST 25-31
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU MIYAMBO 28
Kusiyana Pakati pa Munthu Woipa ndi Munthu Wolungama
Kodi Mumatsatira Yehova ndi Mtima Wonse?
“OLUNGAMA amakhala olimba mtima ngati mkango.” (Miyambo 28:1) Amasonyeza chikhulupiriro, amadalira Mawu a Mulungu ndipo amapitiriza kutumikira Yehova molimba mtima ngakhale pamene akukumana ndi zoopsa.
it-2 1139 ¶3
Kumvetsa Zinthu
Anthu amene asiya kumvera Yehova. Anthu amene ayamba kuchimwira Mulungu saganizira kaye zimene Mulunguyo amafuna akamasankha zochita kapena akamapanga mapulani pa moyo wawo. (Yob 34:27) Munthu woteroyo amalola kuti mtima wake uyambe kumupusitsa ndipo sazindikira kuti zimene akuchitazo ndi zoipa moti amasiya kuona zinthu moyenera. (Sl 36:1-4) Ngakhale atamanena kuti amalambira Mulungu, amaona kuti maganizo a anthu ndi ofunika kwambiri kuposa a Mulungu ndipo amakonda maganizo a anthuwo. (Yes 29:13, 14) Akamachita khalidwe lochititsa manyazi, amadzikhululukira n’kumanena kuti zili ngati “masewera” chabe (Miy 10:23) komanso amayamba kuganiza mwachinyengo ndi mwauchitsiru mpaka kufika pomaganiza kuti Mulungu sakuona kapena sakuzindikira zinthu zoipa zimene akuchitazo, ngati kuti Mulunguyo alibenso mphamvu zotha kuzindikira zinthu. (Sl 94:4-10; Yes 29:15, 16; Yer 10:21) Zochita ndi zolankhula zake, zimakhala ngati akunena kuti, “Kulibe Yehova” (Sl 14:1-3) ndipo saganiza n’komwe za Yehovayo. Chifukwa choti satsatira mfundo za Mulungu, sangasankhe zinthu zoyenera, sangaone zinthu moyenera, sangaganizire mfundo zonse za nkhani imene akufunika kusankha komanso sangasankhe zinthu mwanzeru.—Miy 28:5.
it-1 1211 ¶4
Kukhulupirika
N’zotheka kukhala okhulupirika kwa Yehova, osati ndi mphamvu zathu, koma pokhapokha ngati timakhulupirira ndi kudalira mphamvu zake zopulumutsira. (Sl 25:21) Mulungu amalonjeza kuti adzakhala “chishango” komanso “malo achitetezo” kwa anthu okhulupirika. (Miy 2:6-8; 10:29; Sl 41:12) Chifukwa choti anthu okhulupirikawa nthawi zonse amayesetsa kuchita zinthu zosangalatsa Yehova, amakhala ndi moyo wosangalala zomwe zimawathandiza kuti azitha kukwaniritsa zolinga zawo. (Sl 26:1-3; Miy 11:5; 28:18) Komabe, Yobu anakhumudwa atazindikira kuti anthu abwino amakumana ndi mavuto chifukwa cha zochita za anthu oipa ndipo akhoza kufa pamodzi ndi anthu oipawo. Koma anazindikiranso kuti ngakhale zili choncho, Yehova amakhala akuona zimene munthu wosalakwayo akukumana nazo ndipo amamutsimikizira kuti adzalandira cholowa chake, adzakhala mwamtendere m’tsogolo, komanso adzalandira zinthu zabwino. (Yob 9:20-22; Sl 37:18, 19, 37; 84:11; Miy 28:10) Monga mmene zinalili ndi Yobu, munthu amaonedwa kuti ndi wofunika kwa Mulungu ngati ali wokhulupirika, osati ngati ali ndi chuma. (Miy 19:1; 28:6) Ana amene bambo awo ndi okhulupirika chonchi, amakhala ndi mwayi waukulu ndipo amakhala osangalala (Miy 20:7), komanso amalemekezedwa chifukwa cha chitsanzo chabwino ndi mbiri yabwino ya bambo awo.
Mfundo Zothandiza
Mungathe Kupewa Matenda a Mtima Wauzimu
Kudzidalira mopambanitsa. Anthu ambiri amene anadwalapo mtima anali kudzidalira kwambiri kuti thanzi lawo linali bwino asanayambe kudwala. Nthawi zambiri, ananyalanyaza kukapimitsa ku chipatala ndipo anaona ngati n’kosafunika n’komwe kuti achite zimenezo. N’chimodzimodzinso ndi ena amene amaganiza kuti popeza akhala Mkhristu kwa nthawi yaitali, palibe chingawachitikire. Mwina anganyalanyaze kuti adzipime mwauzimu mpaka tsoka litawagwera. N’kofunika kwambiri kukumbukira langizo labwino la Paulo lakuti tipewe kudzidalira mopambanitsa. Iye anati: “Iye wakuyesa kuti ali chilili, ayang’anire kuti angagwe.” N’kwanzeru kuzindikira kupanda kwathu ungwiro ndi kudzipima mwauzimu nthawi zonse.—1 Akorinto 10:12; Miyambo 28:14.