Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • th phunziro 6 tsamba 9
  • Kufotokoza Bwino Malemba

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kufotokoza Bwino Malemba
  • Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Nkhani Yofanana
  • Kunena Mawu Oyenera Musanayambe Kuwerenga Lemba
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Kugwiritsa Ntchito Malemba Moyenerera
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Mawu Omaliza Abwino
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Kusonyeza Kuti Nkhaniyo Ndi Yothandiza
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
Onani Zambiri
Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
th phunziro 6 tsamba 9

PHUNZIRO 6

Kufotokoza Bwino Malemba

Lemba

Yohane 10:33-36

MFUNDO YAIKULU: Musamangoti kuwerenga lemba ili, basi kupita pa lemba lina. Muzithandiza anthu kuona kugwirizana pakati pa lemba limene mwawerenga ndi nkhani imene mukukamba.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Sankhani mawu ofunika. Mukawerenga lemba, muzisankhapo mawu amene akugwirizana kwambiri ndi mfundo yaikulu yamunkhani yanu. Mungabwereze kutchula mawuwo, kapena kufunsa funso limene lingachititse anthu kuganizira mawuwo.

    Mfundo yothandiza

    Ngati mukugwiritsa ntchito mawu ena pofotokozera lemba, muzitsimikizira kuti anthu akuona kugwirizana pakati pa mawu a m’Baibulo ndi mfundo imene mukufotokoza.

  • Tsindikani mfundo. Ngati munatchula chifukwa chowerengera lemba, mukaliwerenga muzisonyeza mmene mawu amulembalo akuperekera chifukwacho.

    Mfundo yothandiza

    Mukamafotokozera lemba, Baibulo lanu lizikhala lotsegula. Izi zimathandiza kuti anthu azigwirizanitsa zimene mukunena ndi mavesi amene mwawerenga.

  • Fotokozani mwachidule mmene tingagwiritsire ntchito. Pewani kunena zambirimbiri pa mawu amene sakugwirizana ndi mfundo yanu yaikulu. Ganizirani zimene anthu akudziwa kale pa lembalo. Kenako fotokozani mwachidule mmene anthu angagwiritsire ntchito mfundoyo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena