NYIMBO 112
Yehova Ndi Mulungu Wamtendere
Losindikizidwa
1. M’lungu wachikondi
Mwalonjeza mtendere.
Mutipatse mzimu wanu
Uzitithandizabe.
Chikhulupiriro
Chimatithandizadi
Kuti tikhale anzanu.
Tilidi pamtendere.
2. Timamvetsa zinthu,
Timaona kuwala.
Mumatitsogolera
M’dziko lomwe ndi lamdima.
Nthawi idzafika
Pomwe nkhondo zidzatha.
Dalitsani khama lathu
Tikhale amtendere.
3. Mulitu ndi gulu
Kumwamba ndi padziko,
Lomwe ndi logwirizana
Lolengeza Ufumu.
Mu Ufumu wanu
Simudzakhala nkhondo.
Tidzakhala mwamtendere
Padziko mpaka kale.
(Onaninso Sal. 4:8; Afil. 4:6, 7; 1 Ates. 5:23.)