Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kapolo Amene Ankamvera Mulungu
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
    • Yosefe akuthawa mkazi wa Potifara

      MUTU 14

      Kapolo Amene Ankamvera Mulungu

      Yosefe anali wachiwiri kwa mwana womaliza wa Yakobo. Azichimwene ake anaona kuti bambo awo ankamukonda kwambiri. Kodi ukuganiza kuti iwo ankasangalala ndi zimenezi? Ayi. Ankamuchitira nsanje komanso ankadana naye. Pa nthawi ina Yosefe analota maloto odabwitsa. Atawauza azichimwene akewo, iwo anaganiza kuti malotowo akutanthauza kuti tsiku lina adzamugwadira. Izi zinangowonjezera chidani chija.

      Azichimwene ake a Yosefe akumuponyera m’chitsime

      Tsiku lina azichimwene ake a Yosefe ankadyetsa ziweto pafupi ndi mzinda wotchedwa Sekemu. Ndiyeno Yakobo anatuma Yosefe kuti akawaone ngati ali bwino. Koma iwo atamuona akubwera anayamba kuuzana kuti: ‘Wolota uja suyo akubwera apoyo? Tiyeni timuphe.’ Atatero anamugwira n’kumuponyera m’chitsime chakuya. Koma mmodzi mwa azichimwene akewo dzina lake Yuda, anati: ‘Ayi tisamuphe. Tiyeni tingomugulitsa kuti akhale kapolo.’ Choncho anamugulitsa ndi ndalama zasiliva zokwana 20 kwa amalonda a Chimidiyani omwe ankapita ku Iguputo.

      Kenako azichimwene akewo anatenga mkanjo wa Yosefe n’kuuviika m’magazi a mbuzi. Ndiyeno atafika kunyumba anapatsa bambo awo mkanjowo n’kunena kuti: ‘Kodi mkanjo uwu si wa mwana wanu?’ Yakobo atauona, anaganiza kuti Yosefe wadyedwa ndi chilombo. Choncho anamva chisoni kwambiri n’kuyamba kulira ndipo sankatonthozeka.

      Yosefe ali m’ndende

      Amalonda aja atafika ku Iguputo, anagulitsa Yosefe kwa munthu wina waudindo dzina lake Potifara kuti akhale kapolo wake. Koma Yehova anali naye. Potifara anaona kuti Yosefe anali wolimbikira ntchito komanso wodalirika. Pasanapite nthawi, Yosefe anaikidwa kuti aziyang’anira zinthu zonse za Potifara.

      Mkazi wa Potifara anaona kuti Yosefe anali wooneka bwino komanso wamphamvu. Tsiku lililonse ankamukakamiza kuti agone naye. Kodi Yosefe anatani? Iye ankakana ndipo anamuuza kuti: ‘Ayi, zimenezo si zabwino. Abwana anga amandikhulupirira ndipo inuyo ndinu mkazi wawo. Ndikagona nanu ndichimwira Mulungu.’

      Tsiku lina mkazi wa Potifara anakakamizanso Yosefe kuti agone naye. Moti anamugwira malaya koma Yosefe anathawa. Potifara atabwera, mkaziyo ananena kuti Yosefe amafuna kumugwiririra. Koma zimenezi sizinali zoona. Choncho Potifara anakwiya kwambiri ndipo anaika Yosefe m’ndende. Koma Yehova sanaiwale Yosefe.

      “Choncho dzichepetseni pamaso pa Mulungu wathu wamphamvu kuti adzakukwezeni nthawi yake ikadzakwana.”​—1 Petulo 5:6

      Mafunso: Kodi azichimwene ake a Yosefe anamuchitira zotani? Kodi chinachititsa n’chiyani kuti Yosefe apezeke ali m’ndende?

      Genesis chaputala 37 ndi 39; Machitidwe 7:9

  • Yehova Sanamuiwale Yosefe
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
    • Yosefe akufotokoza tanthauzo la maloto a Farao

      MUTU 15

      Yehova Sanaiwale Yosefe

      Yosefe ali m’ndende, Farao yemwe anali mfumu ya ku Iguputo, analota maloto. Palibe amene ankadziwa tanthauzo la malotowo. Wantchito wina wa Farao ananena kuti Yosefe akhoza kufotokoza tanthauzo lake. Nthawi yomweyo, Farao anatuma anthu kuti akatenge Yosefe.

      Atafika, Farao anamufunsa kuti: ‘Kodi ungandiuze tanthauzo la maloto anga?’ Yosefe anayankha kuti: ‘Pa zaka 7 zikubwerazi, mu Iguputo muno mukhala chakudya chambirimbiri koma kenako kudzabwera zaka zina 7 za njala. Musankhe munthu wanzeru kuti asonkhanitse chakudya kuti anthu anu asadzafe ndi njala.’ Farao anayankha kuti: ‘Ndakusankha iweyo. Ukhala woyangʼanira dziko lonse la Iguputo. Ine ndekha ndikhala wamkulu kwa iwe.’ Kodi Yosefe anadziwa bwanji tanthauzo la maloto a Farao? Yehova ndi amene anamuthandiza.

      Yosefe akulangiza anthu kuti asunge chakudya

      Ndiyeno Yosefe anasonkhanitsa chakudya kwa zaka 7. Kenako padziko lonse panali njala mogwirizana ndi zimene Yosefe ananena. Anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana ankabwera kudzagula chakudya kwa Yosefe. Ndiyeno bambo ake atamva kuti ku Iguputo kuli chakudya, anatuma ana awo 10 kuti apite kukagula chakudyacho.

      Ana a Yakobo anapita kwa Yosefe ndipo iye atangowaona anawazindikira. Koma azichimwene akewo sanamuzindikire. Iwo anamugwadira ndipo izi zinali zogwirizana ndi maloto amene Yosefe analota ali wamng’ono. Koma iye ankafuna kudziwa ngati abale akewo anali adakali ndi chidani. Choncho anawauza kuti: ‘Inu ndinu akazitape! Mwabwera kuno kudzafufuza malo amene dziko lathu lili lofooka.’ Iwo anayankha kuti: ‘Ayi si choncho. Tachokera ku Kanani ndipo m’banja lathu tinalimo amuna 12. M’bale wathu wina anamwalira ndipo wamng’ono watsala ndi bambo athu.’ Kenako Yosefe anati: ‘Mukabwere ndi mng’ono wanuyo kuti ndikukhulupirireni.’ Zitatero azichimwene ake a Yosefewo anabwerera kwawo.

      Ndiyeno chakudya chija chitatha, Yakobo anauza ana akewo kuti apitenso ku Iguputo. Pa ulendowu anatenga mng’ono wawo uja ndipo dzina lake linali Benjamini. Pofuna kuwayesa abale akewo, Yosefe anabisa kapu yake m’thumba la Benjamini n’kuwauza kuti aba kapuyo. Antchito a Yosefe anapeza kapuyo m’thumba la Benjamini ndipo izi zinadabwitsa kwambiri abale akewo. Iwo anapempha Yosefe kuti awalange iwowo m’malo mwa Benjamini.

      Apa Yosefe anadziwa kuti abale akewo anasintha kwambiri. Iye analephera kudzigwira moti anayamba kulira n’kunena kuti: ‘Ndine Yosefe, m’bale wanu uja. Kodi bambo anga adakali ndi moyo?’ Abale akewo anadabwa kwambiri. Koma iye anawauza kuti: ‘Musadandaule ndi zimene munandichitira zija. Mulungu ndi amene ananditumiza kuno kuti akupulumutseni. Bwererani kwa bambo anga msanga ndipo mukawatenge n’kubwera nawo kuno.’

      Abale akewo anapita kukauza bambo awo nkhani yabwinoyi ndipo anawatenga n’kupita nawo ku Iguputo. Yosefe ndi bambo akewo atakumananso anasangalala kwambiri chifukwa panali patadutsa zaka zambiri asanaonane.

      Yosefe wakumana ndi bambo ake, a Yakobo ndipo akupatsana moni

      “Ngati simukhululukira anthu machimo awo, Atate wanu sadzakukhululukiraninso machimo anu.”​—Mateyu 6:15

      Mafunso: Kodi Yehova anathandiza bwanji Yosefe? Kodi Yosefe anasonyeza bwanji kuti anakhululukira abale ake?

      Genesis chaputala 40 mpaka 45; 46:1-7, 26-34; Salimo 105:17-19; Machitidwe 7:9-15

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena