Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwhf nkhani 4
  • Mmene Mungathandizire Ana Anu pa Nkhani ya Mowa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Mungathandizire Ana Anu pa Nkhani ya Mowa
  • Mfundo Zothandiza Mabanja
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene muyenera kudziwa
  • Zimene mungachite
  • Mmene Kumwa Mowa Mopitirira Muyeso Kumakhudzira Thanzi la Munthu
    Galamukani!—2005
  • Mowa Umafunika Kusamala Nawo
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kodi Mumayendera Maganizo a Yehova pa Nkhani ya Mowa?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Khalani ndi Maganizo Oyenera Pankhani ya Kumwa Mowa
    Nsanja ya Olonda—2010
Onani Zambiri
Mfundo Zothandiza Mabanja
ijwhf nkhani 4
Kamtsikana kakuyang’anitsitsitsa makolo ake akumwa mowa

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA

Mmene Mungathandizire Ana Anu pa Nkhani ya Mowa

Bambo wina dzina lake Alexander ananena kuti: “Pamene mwana wathu wamkazi anali ndi zaka 6, tinakambirana naye koyamba nkhani ya mowa. Koma tinadabwa kwambiri kuona kuti akudziwa zambiri zokhudza mowa zomwe sitinkayembekezera.”

  • Zimene muyenera kudziwa

  • Zimene mungachite

  • Zimene Baibulo limanena pa nkhani ya mowa

Zimene muyenera kudziwa

Kukambirana ndi ana anu zokhudza mowa n’kofunika.Musamadikire kuti mwana wanu akule kaye kuti mudzakambirane naye za nkhaniyi. Bambo wina wa ku Russia dzina lake Khamit ananena kuti: “Ndimaona kuti sitinachite bwino kumulekerera mwana wathu osamuuza zokhudza mowa pa nthawi imene anali wamng’ono. Ndinazindikira kuti anali atayamba kale kumwa kwambiri ali ndi zaka 13. Ndinaphunzirapo kanthu koma zinthu zinali zitaipa kale.”

N’chifukwa chiyani kukambirana ndi mwana za nkhaniyi n’kofunika?

  • Anzake a kusukulu, otsatsa malonda komanso zimene amaona pa TV zingachititse mwana wanu kusintha mmene amaonera nkhani ya kumwa mowa.

  • Kafukufuku amene bungwe lina ku United States linachita, anasonyeza kuti pa ana aang’ono 100, pali 11 omwe amamwa mowa.​—U.S. Centers for Disease Control and Prevention.

Mpake kuti akuluakulu a zaumoyo amanena kuti makolo ayenera kuphunzitsiratu ana awo adakali aang’ono za kuopsa kwa mowa. Tiyeni tione mmene makolo angathandizire ana awo.

Zimene mungachite

Muzikhala okonzeka kuyankha mafunso omwe mwana wanu angafunse. Ana amakhala ndi mtima wofuna kudziwa zinthu ndipo akamakula amafunanso kudziwa zambiri. Choncho mumafunika kukonzekereratu mmene mungawayankhire. Mwachitsanzo:

  • Ngati mwana wanu akufuna kudziwa mmene mowa umamvekera, mungamuuze kuti pali mowa wina umawawasirako pomwe wina umawawa kwambiri.

  • Ngati mwana wanu akufuna kulawako mowa, mungamuuze kuti mowa si wabwino kwa ana. Mwachitsanzo, n’zoona kuti munthu akamwako mowa amasangalala komanso amamasuka. Koma akaumwa mopitirira malire, amapanga chizungulire, saganiza bwinobwino pochita zinthu ndiponso amachita kapena kulankhula zinthu zomwe kenako amadzanong’oneza nazo bondo.​—Miyambo 23:29-35.

Muzidziwiratu zokhudza mowa. Baibulo limanena kuti: “Aliyense wochenjera amachita zinthu mozindikira.” (Miyambo 13:16) Choncho muyenera kufufuza ndi kudziwiratu mavuto amene amakhalapo munthu akamwa, zimene malamulo a m’dziko lanu amanena pa nkhani ya mowa ndiponso kuchuluka kwa mowa womwe munthu amayenera kumwa. Mukadziwa zimenezi simungavutike kuthandiza mwana wanu.

Muziyamba ndi inuyo kukambirana ndi mwana wanu zokhudza mowa. Bambo wina wa ku Britain dzina lake Mark ananena kuti: “Mowa umasokoneza kwambiri ana. Tsiku lina ndinafunsa mwana wanga wamwamuna wa zaka 8 kuti afotokozepo maganizo ake ngati kumwa mowa n’kwabwino kapena ayi. Ndinkalankhula naye momasuka ngati kuti tikungocheza ndipo zimenezi zinathandiza kuti nayenso amasuke kunena maganizo ake pa nkhani ya mowa.”

Ngati nthawi zambiri mumakonda kunena za mavuto amene amakhalapo chifukwa cha mowa, zingathandize ana anu kudziwa kuopsa kwa mowa. Choncho potengera msinkhu wa mwana wanu, mukamakambirana nkhani zofunika pa moyo monga kupewa ngozi pamsewu komanso nkhani zokhudza kugonana, mungakambirane nayenso zokhudza kuopsa kwa mowa.

Muzikhala chitsanzo chabwino. Ana ali ngati thonje. Thonje likaviikidwa m’madzi, kaya akuda kapena oyera, limayamwa komanso kutengera mtundu wa madziwo. Ochita kafukufuku anapeza kuti nawonso ana amatengera kwambiri zimene makolo awo amakonda kuchita. Izi zikutanthauza kuti ngati inuyo mumaona kuti kumwa mowa ndi njira yokhayo yabwino yochepetsera nkhawa kapena mavuto anu, mwana wanunso amatengera zomwezo. Choncho muzikhala chitsanzo chabwino. Ndipo ngati mumamwa, muziyesetsa kumwa moyenera.

Kamtsikana kakuchita chidwi pamene mayi ake akukana kupatsidwa mowa wowonjezera kumalo odyera

Ana anu amatengera zimene mumachita pa nkhani ya kumwa mowa

Zimene Baibulo limanena pa nkhani ya mowa

‘[Yehova] . . . amatulutsa vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu.’ (Salimo 104:14, 15) Izi zikusonyeza kuti mowa si woipa ndipo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.

“Vinyo ndi wonyoza. Chakumwa choledzeretsa chimasokosera ndipo aliyense wosochera nacho alibe nzeru.” (Miyambo 20:1) Choncho ndi bwino kumwa mowa moyenera.

‘Zidakwa . . . sizidzalowa mu Ufumu wa Mulungu.’ (1 Akorinto 6:10) Apa mfundo ndi yakuti Mulungu amadana ndi kumwa mowa kwambiri osati kumwa mowako pakokha.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena