-
Miliri Inanso 6Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 20
Miliri Inanso 6
Mose ndi Aroni anapita kwa Farao kukamuuza uthenga wochokera kwa Mulungu, wakuti: ‘Ngati sulola kuti anthu anga apite, nditumiza ntchentche zoluma m’dzikoli.’ Ndiyeno ntchentche zolumazo zinadzaza m’nyumba za Aiguputo onse, olemera ndi osauka omwe moti zinali mbwee paliponse. Koma ku Goseni kumene Aisiraeli ankakhala kunalibe ntchentchezi. Kuyambira ndi mliri wa nambala 4 umenewu, miliriyi inkangokhudza Aiguputo okha. Choncho Farao anachonderera Mose kuti: ‘Ukandipemphere kwa Yehova kuti achotse ntchentchezi. Zikatero ndikulolani kuti mupite.’ Koma Yehova atangochotsa ntchentchezo, Farao anasintha maganizo. Iye sanaphunzirepo kanthu.
Yehova anati: ‘Farao akapanda kulola kuti anthu anga apite, ziweto zonse za Aiguputo ziyamba kudwala n’kufa.’ Tsiku lotsatira, ziweto za Aiguputo zinayamba kufa. Koma ziweto za Aisiraeli sizinafe. Ngakhale zinali choncho, Farao sanalolebe kuti Aisiraeli azipita.
Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti apitenso kwa Farao ndipo akaponye phulusa m’mwamba. Phulusalo linasanduka fumbi ndipo linadzaza dziko lonselo moti Aiguputo onse anali fumbi lokhalokha. Fumbilo likagwera munthu kapena ziweto, linkayambitsa zilonda zopweteka kwambiri. Komabe Farao sanalole kuti Aisiraeli apite.
Yehova anatuma Mose kuti apitenso kwa Farao n’kukanena kuti: ‘Kodi sukufunabe kuti anthu anga apite? Mawa ndibweretsa mvula yamphamvu kwambiri yamatalala.’ Tsiku lotsatira, Yehova anabweretsa mvula yamatalala, mabingu ndi moto. Ku Iguputo kunali kusanagwepo chimvula ngati chimenecho chiyambire. Chimvulacho chinawononga mitengo komanso mbewu zonse kupatulapo za ku Goseni. Farao anati: ‘Kandipemphere kwa Yehova kuti aletse chimvulachi ndipo ndikulolani kuti muzipita.’ Koma matalalawo ndi chimvulacho zitangosiya, Farao anasinthanso maganizo.
Kenako Mose anati: ‘Tsopano kugwa dzombe ndipo lidya zomera zonse zimene sizinawonongedwe ndi matalala.’ Choncho kunagwa dzombe lambiri moti linadya mbewu zonse komanso masamba onse a mitengo. Farao anachondereranso kuti: ‘Kandipemphere kwa Yehova kuti achotse dzombeli.’ Koma Yehova atachotsa dzombelo, Farao anakanabe kulola kuti Aisiraeli apite.
Yehova anauza Mose kuti: ‘Tambasula dzanja lako ndipo uloze kumwamba.’ Nthawi yomweyo, kunachita mdima wandiweyani. Kwa masiku atatu, Aiguputo sankatha kuona munthu aliyense kapena chinthu chilichonse. Koma m’nyumba za Aisiraeli munkawala.
Zitatero Farao anauza Mose kuti: ‘Pitani, koma ziweto zanu muzisiye.’ Koma Mose anati: ‘Tizitenga chifukwa tikufuna kukapereka nsembe kwa Mulungu wathu.’ Farao anakwiya kwambiri n’kunena kuti: ‘Choka! Ndisadzakuonenso. Ndipo ukadzangobweranso ndidzakupha.’
“Mudzaonanso kusiyana pakati pa munthu wolungama ndi woipa ndiponso pakati pa munthu amene akutumikira Mulungu ndi amene sakumutumikira.”—Malaki 3:18
-
-
Mliri wa 10Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 21
Mliri wa 10
Mose anauza Farao kuti sadzapitanso kukaonana naye. Koma asananyamuke, anamuuza kuti: ‘Lero pakati pa usiku ana onse aamuna oyamba kubadwa a Aiguputo afa, kuyambira mwana wa Farao mpaka ana a akapolo.’
Yehova anauza Aisiraeli kuti adye chakudya chapadera. Anawauza kuti: ‘Mupeze mwana wankhosa kapena wambuzi. Akhale wamphongo komanso wachaka chimodzi. Mumuphe ndipo magazi ake mupake pamafelemu a zitseko zanu. Nyama yakeyo muiwotche ndipo muidye limodzi ndi mikate yopanda zofufumitsa. Mudye mutavala zovala zanu komanso nsapato pokonzekera ulendo. Usiku wa lero mutuluka mu Iguputo.’ Kodi ukuganiza kuti Aisiraeli anamva bwanji atauzidwa zimenezi?
Pakati pa usiku, mngelo wa Yehova anapita kunyumba zonse za mu Iguputo. Nyumba iliyonse imene inalibe magazi pafelemu, mwana woyamba anafa. Koma mngeloyo sankapha ana a m’nyumba zimene anapaka magazi pamafelemu. M’banja lililonse la Aiguputo, kaya lolemera kapena losauka, munafa mwana woyamba. Koma palibe mwana ngakhale mmodzi wa Aisiraeli amene anafa.
Mwana woyamba wa Farao weniweniyo anafanso. Apa m’pamene makani a Farao anathera. Nthawi yomweyo anauza Mose ndi Aroni kuti: ‘Nyamukani. Chokani kuno. Pitani mukalambire Mulungu wanu. Mutengenso ziweto zanu n’kumapita.’
Usiku womwewo, Aisiraeli ananyamuka ndipo kunja kunali kukuwala kwambiri chifukwa mwezi unali wathunthu. Mabanja komanso mafuko ankayendera limodzi. Panali amuna 600,000 komanso akazi ndi ana ambiri. Panalinso anthu a mitundu ina amene anapita nawo kuti akalambirenso Yehova. Apa m’pamene panathera ukapolo wa Aisiraeli.
Pofuna kukumbukira zimene Yehova anachita powapulumutsa, Aisiraeliwa ankadya chakudya chapadera chija chaka chilichonse. Mwambowu ankautchula kuti Pasika.
“Ndakusiya ndi moyo kuti ndikusonyeze mphamvu zanga komanso kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.”—Aroma 9:17
-