-
Anthu 12 Anapita Kukaona Dziko la KananiZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 26
Anthu 12 Anapita Kukafufuza Dziko la Kanani
Aisiraeli atachoka paphiri la Sinai anadutsa m’chipululu cha Parana n’kukafika pamalo otchedwa Kadesi. Ali pamalowa, Yehova anauza Mose kuti: ‘Sankha amuna 12 kuchokera mu fuko lililonse kuti apite kukaona dziko la Kanani limene ndikufuna kulipereka kwa Aisiraeli.’ Ndiyeno Mose anasankha amuna 12 n’kuwauza kuti: ‘Pitani ku Kanani mukaone ngati dzikolo ndi labwino kulimamo mbewu. Mukaonenso ngati anthu ake ali amphamvu kapena ofooka komanso ngati amakhala m’matenti kapena m’mizinda.’ Zitatero, anthuwo anauyamba ulendo wopita ku Kanani ndipo pa gululi panali Yoswa ndi Kalebe.
Patatha masiku 40, anthuwa anabwerera ndipo anatenga zipatso za nkhuyu, makangaza ndi mphesa. Iwo anati: ‘Dziko lake ndi labwino kwambiri koma anthu ake ndi amphamvu ndipo amakhala m’mizinda ya mipanda italiitali.’ Ndiyeno Kalebe anati: ‘Komabe tingathe kuwagonjetsa anthuwo. Tiyeni tipite pompano.’ Kodi ukudziwa chifukwa chake Kalebe ananena zimenezi? Chifukwa chakuti iye ndi Yoswa ankakhulupirira kwambiri Yehova. Koma anthu ena 10 aja anati: ‘Ayi tisapite. Anthu ake ndi akuluakulu komanso amphamvu moti ife timangooneka ngati tiziwala.’
Aisiraeli atamva zimenezi anakhumudwa kwambiri. Anayamba kudandaula kuti: ‘Tiyeni tisankhe mtsogoleri wina ndipo tibwerere ku Iguputo. Kodi pali chifukwa choti tipitire m’dziko limeneli n’kukaphedwa?’ Koma Yoswa ndi Kalebe anati: ‘Musapandukire Yehova ndipo musachite mantha. Yehova atiteteza.’ Komabe Aisiraeliwo sanamvere, moti mpaka ankafuna kupha Yoswa ndi Kalebe.
Kodi Yehova anatani? Iye anauza Mose kuti: ‘Aisiraeli ndawachitira zinthu zambirimbiri koma sakundimverabe. Chifukwa cha zimenezi, akhala m’chipululumu kwa zaka 40 ndipo onse afera momwemu. Anthu amene akalowe m’dziko limene ndalonjezali ndi ana awo okha limodzi ndi Yoswa komanso Kalebe.’
“N’chifukwa chiyani mukuchita mantha chonchi, anthu achikhulupiriro chochepa inu?”—Mateyu 8:26
-
-
Aisiraeli Ena Anaukira YehovaZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 27
Aisiraeli Ena Anaukira Yehova
Nthawi ina Aisiraeli ali m’chipululu, Kora, Datani, Abiramu ndi anthu ena okwana 250 anaukira Mose. Iwo anati: ‘Tatopa nawe tsopano! N’chifukwa chiyani ukufuna uzitilamulira ndipo wasankha Aroni kuti akhale mkulu wa ansembe? Yehova ali ndi tonsefe, osati iweyo ndi Aroni basi.’ Zimenezi sizinamusangalatse Yehova chifukwa ankaona kuti anthuwo akutsutsana ndi iyeyo.
Mose anauza Kora ndi anthu amene anali kumbali ya Korayo kuti: ‘Mawa mubwere kuchihema ndipo mudzatenge zofukizira ndipo mʼzofukizirazo mudzaikemo moto ndi zinthu zonunkhira zoti mukapereke nsembe. Yehova adzationetsa munthu amene wamusankha.’
Tsiku lotsatira, Kora ndi anthu 250 aja anapitadi kukakumana ndi Mose kuchihema. Kumeneko iwo anapereka nsembe ngakhale kuti sanali ansembe. Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: ‘Chokani musayandikane ndi Kora ndi anzakewo.’
Ngakhale kuti Kora anapita kukakumana ndi Mose kuchihema, Datani, Abiramu ndi mabanja awo anakana kupitako. Yehova anauza Aisiraeli kuti asayandikire matenti a Kora, Datani ndi Abiramu. Nthawi yomweyo Aisiraeli anapita kutali ndi matentiwo. Datani, Abiramu ndi mabanja awo anaima panja pa matenti awo. Ndiye nthawi yomweyo nthaka inang’ambika n’kuwameza. Nakonso kuchihema kuja, moto wochokera kwa Yehova unapsereza Kora ndi anzake 250 aja.
Zitatero Yehova anauza Mose kuti: ‘Tenga ndodo ya mtsogoleri wa fuko lililonse ndipo ulembepo dzina la mtsogoleriyo. Koma pandodo ya fuko la Levi, ulembepo dzina la Aroni. Ndodozi uziike m’chihema ndipo ndodo ya munthu amene ndasankha, idzachita maluwa.’
Tsiku lotsatira Mose anatenga ndodo zonse n’kuwaonetsa atsogoleri aja. Ndodo ya Aroni inali itachita maluwa n’kubereka zipatso zakupsa za amondi. Zimenezi zinatsimikizira kuti Yehova anali atasankha Aroni kuti akhale mkulu wa ansembe.
“Muzimvera amene akukutsogolerani ndipo muziwagonjera.”—Aheberi 13:17
-