-
Rahabi Anabisa Aisiraeli Okafufuza DzikoZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 30
Rahabi Anabisa Aisiraeli Okafufuza Dziko
Aisiraeli awiri amene anatumidwa kukafufuza mzinda wa Yeriko anakafikira m’nyumba ya mayi wina dzina lake Rahabi. Mfumu ya kumeneko itazindikira, inatumiza asilikali kunyumbako. Koma Rahabi anabisa Aisiraeliwo padenga n’kuuza asilikaliwo kuti alowere njira ina. Kenako anauza Aisiraeliwo kuti: ‘Ndikukuthandizani chifukwa ndikudziwa kuti Yehova akukumenyerani nkhondo ndipo mugonjetsa mzindawu. Chonde, lonjezani kuti simudzapha ineyo ndi abale anga.’
Aisiraeliwo anauza Rahabi kuti: ‘Tikulonjeza kuti aliyense amene adzakhale m’nyumba yakoyi sadzaphedwa.’ Ndiyeno anamuuza kuti: ‘Umangirire chingwe chofiira pawindo kuti iwe ndi abale ako mudzatetezeke.’
Rahabi anagwiritsa ntchito chingwe potulutsira Aisiraeliwo pawindo kuti azipita. Iwo anakabisala m’mapiri kwa masiku atatu asanabwerere kumene kunali Yoswa. Kenako Aisiraeli anawoloka mtsinje wa Yorodano ndipo anayamba kukonzekera kuti alande dzikolo. Mzinda woyamba kuugonjetsa unali wa Yeriko. Yehova anawauza kuti azizungulira mzindawo kamodzi pa tsiku kwa masiku 6. Koma pa tsiku la 7 anawauza kuti auzungulire maulendo 7 ansembe akuimba malipenga, kenako asilikali anayamba kuchita phokoso kwambiri. Zitatero, mpanda wa mzindawo unagwa. Koma nyumba ya Rahabi yomwe inalumikizana ndi mpandawo, sinagwe. Rahabi ndi anthu a m’banja lake anapulumuka chifukwa chakuti ankakhulupirira kwambiri Yehova.
“Mofanana ndi zimenezi, kodi Rahabi . . . sanaonedwenso kuti ndi wolungama chifukwa cha ntchito zake, atalandira bwino anthu amene ankafufuza dziko lawo nʼkuwathandiza kuti athawe kudzera njira ina?”—Yakobo 2:25
-
-
Yoswa ndi anthu a ku GibiyoniZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 31
Yoswa ndi Anthu a ku Gibiyoni
Anthu ena a ku Kanani anamva zimene zinachitika ku Yeriko. Ndiyeno mafumu angapo anagwirizana kuti amenyane ndi Aisiraeli. Koma anthu a ku Gibiyoni anaganizira pulani ina. Anapita kwa Yoswa atavala zovala zong’ambika n’kunena kuti: ‘Tachokera kudziko lakutali kwambiri. Tamva za Yehova komanso zimene anakuchitirani ku Iguputo ndi ku Mowabu. Lonjezani kuti simudzamenyana nafe ndipo ife tikhala akapolo anu.’
Yoswa anakhulupirira zimene ananenazi ndipo analonjeza kuti sadzamenyana nawo. Patangodutsa masiku atatu, anazindikira kuti anthuwo sanali akutali. Anali a m’dziko la Kanani lomwelo. Ndiyeno Yoswa anafunsa anthuwo kuti: ‘N’chifukwa chiyani munatinamiza?’ Iwo anayankha kuti: ‘Timaopa, chifukwa tikudziwa kuti Yehova Mulungu wanu ndi amene akukumenyerani nkhondo. Chonde musatiphe.’ Yoswa anasunga lonjezo lake ndipo sanawaphe.
Pasanapite nthawi yaitali, mafumu 5 a ku Kanani anakonza zoti amenyane ndi anthu a ku Gibiyoni. Ndiyeno Yoswa ndi asilikali ake anayenda usiku wonse kupita kukawathandiza. Nkhondo inayamba m’mawa ndipo Akananiwo anayamba kuthawa n’kubalalikira mbali zonse. Ndiyeno kulikonse kumene ankathawirako Yehova ankawagwetsera zimatalala zikuluzikulu. Kenako Yoswa anapempha Yehova kuti aimitse dzuwa. N’chifukwa chiyani iye anapempha zimenezi chikhalirecho dzuwa linali lisanaimepo? N’chifukwa choti ankakhulupirira kwambiri Yehova. Yehova anayankha ndipo dzuwa silinalowe kwa tsiku lonse mpaka Aisiraeli atagonjetsa mafumu onsewo ndi asilikali awo.
“Tangotsimikizani kuti mukati ‘Indeʼ akhaledi inde, ndipo mukati ‘Ayiʼ akhaledi ayi, chifukwa mawu owonjezera pamenepa ndi ochokera kwa woipayo.”—Mateyu 5:37
-