-
Mtsogoleri Watsopano ndi Azimayi Awiri Olimba MtimaZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 32
Mtsogoleri Watsopano Komanso Azimayi Awiri Olimba Mtima
Atatsogolera anthu a Yehova kwa zaka zambiri, Yoswa anamwalira ali ndi zaka 110. Pa nthawi imene iye anali moyo, Aisiraeli ankalambira Yehova. Koma atangomwalira, iwo anayamba kulambira mafano ngati mmene anthu a ku Kanani ankachitira. Chifukwa cha zimenezi, Yehova analola kuti mfumu ina ya ku Kanani dzina lake Yabini izipondereza Aisiraeli. Iwo anapempha kuti Yehova awathandize. Choncho Yehova anawapatsa mtsogoleri wina dzina lake Baraki. Iye anathandiza Aisiraeli kuti ayambirenso kulambira Yehova.
Ndiyeno mneneri wina wamkazi dzina lake Debora anatumizira Baraki uthenga wochokera kwa Yehova. Uthengawo unali wakuti: ‘Tenga amuna 10,000, ndipo upite kukakumana ndi asilikali a Yabini kumtsinje wa Kisoni. Kumeneko ukagonjetsa Sisera mkulu wa asilikali a Yabini.’ Baraki anauza Debora kuti: ‘Ndipita ngati iweyo ungapite nane.’ Iye anati: ‘Ndipita nawe. Koma dziwa kuti si iweyo amene ukaphe Sisera. Yehova wanena kuti amene akamuphe ndi mzimayi.’
Debora anapita limodzi ndi Baraki ndi asilikali a Barakiyo kuphiri la Tabori kukakonzekera nkhondo. Sisera atamva zimenezi, anasonkhanitsa magaleta ndi asilikali ake. Debora anauza Baraki kuti: ‘Lero Yehova akuthandiza kuti upambane pa nkhondoyi.’ Baraki ndi asilikali ake 10,000 anatsika m’phiri muja kukakumana ndi Sisera ndi asilikali ake amphamvu.
Ndiyeno Yehova anachititsa kuti mtsinje wa Kisoni usefukire. Choncho magaleta a Sisera ankangolowa m’matope. Sisera ataona kuti zavuta, anangotsika pagaleta lake n’kuyamba kuthawa. Baraki ndi asilikali ake anagonjetsa adani awo koma Sisera anathawa ndipo anakabisala mutenti ya mzimayi wina dzina lake Yaeli. Mzimayiyo anam’patsa mkaka kuti amwe ndiponso anamufunditsa bulangete. Sisera anagona tulo. Zitatero, Yaeli anayenda mwakachetechete n’kukamukhoma m’mutu ndi chikhomo cha tenti. Sisera anafera pomwepo.
Baraki anafika akusakasaka Sisera. Yaeli anatuluka mutenti yake n’kumuuza kuti: ‘Lowani mom’muno ndikuonetseni munthu amene mukufunayo.’ Baraki atalowa anaona Sisera atagona poteropo atafa. Baraki ndi Debora anaimba nyimbo yotamanda Yehova chifukwa chothandiza Aisiraeli kugonjetsa adani awo. Kwa zaka 40 zotsatira, Aisiraeli anali pa mtendere.
“Akazi amene akulengeza uthenga wabwino ndi gulu lalikulu.”—Salimo 68:11
-
-
Rute ndi NaomiZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 33
Rute ndi Naomi
Pa nthawi ina, ku Isiraeli kunali njala. Ndiyeno Naomi ananyamuka ndi mwamuna wake komanso ana ake aamuna awiri kupita ku Mowabu. Kenako mwamuna wa Naomi anamwalira. Ana ake aja anakwatira akazi a Chimowabu ndipo akaziwo anali Rute ndi Olipa. Koma patapita nthawi, anawo anamwaliranso.
Naomi atamva kuti njala ku Isiraeli yatha, anaganiza zobwerera kwawo. Rute ndi Olipa ananyamuka naye limodzi koma ali panjira, Naomi anawauza kuti: ‘Ndinu akazi abwino kwambiri. Munkathandiza ana anga komanso ineyo. Koma bwererani kwanu ku Mowabu ndipo mukhoza kukakwatiwanso.’ Rute ndi Olipa anati: ‘Timakukondani kwambiri ndipo sitikufuna kuti tisiyane.’ Naomi anawaumiriza kuti abwerere. Pamapeto pake, Olipa anabwerera koma Rute sanabwerere. Naomi anauza Rute kuti: ‘Iwe, taona Olipa akubwerera kwa anthu ake ndiponso kwa milungu yake. Bwerera naye limodzi, pita kunyumba kwa mayi ako.’ Koma Rute anati: ‘Sindingakusiyeni. Anthu anu adzakhala anthu anga ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.’ Kodi ukuganiza kuti Naomi anamva bwanji Rute atanena zimenezi?
Naomi ndi Rute anafika ku Isiraeli nthawi yokolola balere itangoyamba. Tsiku lina Rute anapita kukakunkha balere wotsalira m’munda mwa bambo wina dzina lake Boazi. Bamboyu anali mwana wa Rahabi. Atamva zoti Rute anali wa ku Mowabu koma ankakhalabe ndi Naomi, anauza antchito ake kuti azimusiyira barele wina kuti atenge.
Tsiku lina Rute atabwerera madzulo, Naomi anamufunsa kuti: ‘Kodi lero unakakunkha kuti balere?’ Rute anayankha kuti: ‘M’munda mwa bambo enaake dzina lawo a Boazi.’ Ndiyeno Naomi anati: ‘Amenewotu ndi achibale a mwamuna wanga. Nthawi zonse uzipita m’munda wawo limodzi ndi atsikana ena. Sangakuchite chipongwe.’
Rute ankapitadi kumunda wa Boazi mpaka pamene nyengo yokolola inatha. Boazi anaona kuti Rute ankagwira ntchito mwakhama ndipo anali mkazi wabwino kwambiri. Nthawi imeneyo munthu akamwalira wopanda mwana, wachibale wake ankakwatira mkazi wamasiyeyo. Choncho Boazi anakwatira Rute. Iwo anabereka mwana dzina lake Obedi amene anadzakhala agogo ake a Mfumu Davide. Anzake a Naomi anasangalala kwambiri. Iwo ankanena kuti: ‘Yehova anakupatsa Rute ndipo wakhala akukuthandiza kwambiri. Tsopano wakupatsa chidzukulu. Yehova atamandike.’
“Pali mnzako amene amakhala nawe pafupi nthawi zonse kuposa mʼbale wako.”—Miyambo 18:24
-