-
Zimene Yefita AnalonjezaZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 36
Zimene Yefita Analonjeza
Aisiraeli anasiyanso kutumikira Yehova ndipo anayamba kulambira milungu yabodza. Pamene a Amoni anawaukira n’kuyamba kumenyana nawo, milungu yobodzayi siinawathandize. Aisiraeli anavutika kwa zaka zambiri. Kenako iwo anauza Yehova kuti: ‘Takuchimwirani, chonde tipulumutseni kwa adani athu.’ Atatero, Aisiraeli anachotsa mafano onse ndipo anayambiranso kulambira Yehova. Yehova sankafuna kuti iwo azingovutikabe.
Choncho anthuwo anasankha Yefita kuti awatsogolere pokamenyana ndi a Amoni. Yefita anauza Yehova kuti: ‘Mukakatithandiza n’kupambana nkhondoyi, ndikulonjeza kuti ndidzapereka kwa inu munthu aliyense wa m’nyumba yanga amene adzayambirire kutuluka kudzandichingamira.’ Yehova anayankha pemphero la Yefita ndipo Aisiraeli anapambanadi pa nkhondoyo.
Pamene Yefita ankabwerera kwawo, munthu woyamba kumuchingamira anali mwana wake wamkazi. Iye anali ndi mwana mmodzi yekhayu basi. Mwana wakeyu anamuchingamira akuvina komanso kuimba maseche. Kodi Yefita anatani? Iye anakumbukira zimene analonjeza zija ndipo anati: ‘Mayo ine mwana wanga! Wandikhumudwitsa. Ndinalonjeza kwa Yehova ndipo kuti ndikwaniritse lonjezolo, ndiyenera kukutumiza kuti uzikatumikira kuchihema ku Silo.’ Koma mwana wakeyo anati: ‘Bambo, ngati mwalonjeza kwa Yehova, muyenera kuchita zimene munalonjezazo. Ndikungopempha kuti mundilole ndipite kumapiri ndi anzanga kwa miyezi iwiri. Kenako ndidzapita kuchihemako.’ Mwana wa Yefita anatumikira pachihema mokhulupirika kwa moyo wake wonse. Chaka chilichonse anzake ankapita ku Silo kukamuona.
“Aliyense amene amakonda kwambiri bambo ake kapena mayi ake kuposa ine ndi wosayenera kuti akhale wophunzira wanga.”—Mateyu 10:37
-
-
Yehova Analankhula ndi SamueliZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 37
Yehova Analankhula ndi Samueli
Eli anali mkulu wa ansembe ndipo anali ndi ana awiri amene ankatumikira ngati ansembe kuchihema. Mayina awo anali Hofeni ndi Pinihasi. Anawa sankamvera malamulo a Yehova ndipo ankachitira anthu zoipa. Aisiraeli akabweretsa nsembe zoti apereke kwa Yehova iwo ankatengapo nyama yabwino n’kukadya. Eli anamva zimene ana akewa ankachita koma sanawathandize. Kodi Yehova anangoilekerera nkhaniyi?
Pa nthawiyo Samueli anali wamng’ono koma sanatengere makhalidwe oipawo ndipo Yehova ankasangalala naye. Tsiku lina atagona, Samueli anamva munthu akumuitana. Iye anadzuka n’kupita kwa Eli ndipo atafika anati: ‘Ndabwera.’ Koma Eli anati: ‘Inetu sindinakuitane. Pita ukagone.’ Samueli atabwerera anamvanso kuitana kachiwiri. Ulendo wachitatu, Eli anazindikira kuti amene akumuitana ndi Yehova. Ndiyeno anamuuza kuti akakamuitananso akayankhe kuti: ‘Lankhulani Yehova. Ine mtumiki wanu ndikumva.’
Samueli atapita kukagona anamvanso kuitana kuti: ‘Samueli! Samueli!’ Iye anayankha kuti: ‘Lankhulani, ine mtumiki wanu ndikumva.’ Ndiyeno Yehova anamuuza kuti: ‘Ukamuuze Eli kuti ndimulanga iyeyo ndi banja lake. Akudziwa zoipa zimene ana ake akuchita kuchihema koma akungowalekerera.’ Kutacha, Samueli anakatsegula zitseko za chihema ngati mmene ankachitira nthawi zonse. Iye ankaopa kuuza mkulu wa ansembe zimene Yehova ananena. Koma Eli anamuitana n’kumufunsa kuti: ‘Mwana wanga, kodi Yehova wakuuza kuti chiyani? Ndiuze chilichonse.’ Zitatero, Samueli anauza Eli zonse zimene Yehova ananena.
Yehova anapitirizabe kutsogolera Samueli. Anthu a m’dziko lonse la Isiraeli ankadziwa kuti Yehova anasankha Samueli kuti akhale mneneri komanso woweruza.
“Choncho kumbukira Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako.”—Mlaliki 12:1
-