Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwbr25 November tsamba 1-16
  • Malifalensi a “Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malifalensi a “Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu”
  • Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2025
  • Timitu
  • NOVEMBER 10-16
  • KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
  • Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani ya Kudziphoda Komanso Kuvala Zodzikongoletsera?
  • NOVEMBER 17-23
  • Nyimbo ya Solomo
  • NOVEMBER 24-30
  • Atate ndi Ana Ake Opanduka
  • Nyumba ya Yehova Ikwezedwa Pamwamba
  • KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
  • Yankho la m’Baibulo
  • DECEMBER 1-7
  • Tsoka Munda Wamphesa Wosakhulupirika!
  • DECEMBER 8-14
  • Yehova Mulungu Ali M’kachisi Wake Wopatulika
  • DECEMBER 15-21
  • ip-1 125-126 ¶16-17
  • Lonjezo la Kalonga wa Mtendere
  • ip-1 130 ¶23-24
  • Lonjezo la Kalonga wa Mtendere
  • KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
  • Kodi a Mboni za Yehova amadalira Baibulo la Dziko Latsopano pofuna kusonyeza kuti zimene amakhulupirira n’zochokeradi m’Baibulo?
  • DECEMBER 22-28
  • Chipulumutso ndi Kusangalala mu Ulamuliro wa Mesiya
  • DECEMBER 29–JANUARY 4
  • Yehova Anyazitsa Mzinda Wodzikuza
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Yesaya​—Gawo 1
  • KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
  • Yankho la m’Baibulo
  • Kodi aneneri ankalandira bwanji mauthenga ochokera kwa Mulungu?
  • Kodi nthawi zonse ulosi umaneneratuzam’tsogolo?
  • Zitsanzo za maulosi a m’Baibulo omwe sananeneretu zam’tsogolo
Malifalensi a Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2025
mwbr25 November tsamba 1-16

Malifalensi a Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu

© 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania

NOVEMBER 10-16

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU NYIMBO YA SOLOMO 3-5

Kukongola kwa Mumtima Ndi Kofunika

w00 11/1 11 ¶17

Mmene Mulungu Amaonera pa Nkhani Yokhala Ndi Khalidwe Loyera

Munthu wachitatu yemwe anakhalabe wokhulupirika anali Msulami. Anali wachitsikana komanso wokongola, ndipo m’busa anakopeka naye kuphatikizanso Mfumu Solomo wa ku Isiraeli, yemwe anali wolemera. Nkhani yonse yosangalatsa ya m’buku la Nyimbo ya Solomo, imasonyeza kuti Msulamiyo anakhalabe woyera, zomwe zinachititsa kuti anthu ambiri azimulemekeza. Ngakhale kuti Solomo anakanidwa ndi mtsikanayu, iye anauziridwa kulemba nkhani yake. M’busa yemwe mtsikanayu anakonda ankalemekeza khalidwe la mtsikanayu lodzisunga. Pa nthawi ina mnyamatayo ananena kuti Msulamiyo anali ngati “munda umene watsekedwa.” (Nyimbo ya Solomo 4:12) Mu Isiraeli wakale, minda yokongola inkakhala ndi ndiwo zosiyanasiyana zamasamba, maluwa onunkhira bwino, ndi mitengo yochititsa chidwi. Minda yoteroyo nthawi zambiri inkatchingidwa ndi maheji kapena khoma, lomwe linkakhala ndi geti lokhoma. (Yesaya 5:5) Khalidwe loyera la Msulami komanso chikondi chake zinali ngati munda wokongola kwambiri kwa mbusayo. Mtsikanayo anali wodzisunga. Chikondi chake anali kudzachisonyeza kwa mwamuna wake wam’tsogolo basi.

g05 1/8 25 ¶2-5

Kukongola Kofunika Kwambiri

Kodi kukongola kwa mumtima kungakope ena? Georgina, amene wakhala pabanja kwa zaka pafupifupi khumi, anati: “Zaka zonsezi, ndakhala ndikukopeka ndi mwamuna wanga chifukwa cha kuona mtima kwake akamachita nane zinthu. Chinthu chofunika kwambiri pamoyo wake ndi kusangalatsa Mulungu. Zimenezi zamuchititsa kukhala munthu woganizira ena ndiponso wachikondi. Asanachite chinthu amayamba wandifunsa kaye maganizo anga ndipo amandichititsa kumva kuti amayamikira zimene ndimachita. Ndikudziwa kuti amandikondadi.”

Daniel, amene anakwatira mu 1987, anati: “Ndimaona kuti mkazi wanga ndi wokongola. Sikuti ndimangokopeka ndi maonekedwe ake okha, koma khalidwe lake limandichititsa kumukonda kwambiri. Nthawi zonse amaganizira anthu ena ndipo amayesetsa kuwachitira zinthu zabwino. Ali ndi makhalidwe abwino kwambiri achikristu. Zimenezi zachititsa kuti ndizisangalala kukhala naye.”

M’dziko lino limene anthu amangoona zakunja zokha, tiyenera kuona mtima wa munthu. Tiyenera kuzindikira kuti kukhala ndi thupi labwino kwambiri n’kovuta, mwinanso kosatheka kumene, ndipo kuli ndi phindu lochepa kwambiri. Komabe, n’zotheka kukhala ndi makhalidwe abwino amene amachititsa munthu kukhala wokongola mumtima. Baibulo limati: “Kukongola kungonyenga, maonekedwe okoma ndi chabe; koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa.” Mosiyana ndi zimenezo, Malemba amachenjeza kuti: “Monga chipini chagolidi m’mphuno ya nkhumba, momwemo mkazi wokongola wosasinkhasinkha bwino.”​—Miyambo 11:22; 31:30.

Mawu a Mulungu amatithandiza kuyamikira “munthu wobisika wamtima, m’chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.” (1 Petulo 3:4) Zoonadi, kukongola kwa mumtima kumeneko n’kofunika kwambiri kuposa kukongola kwa thupi. Ndipo aliyense akhoza kukhala nako.

Mfundo Zothandiza

w06 11/15 18 ¶4

Mfundo Zazikulu za Nyimbo ya Solomo

2:7; 3:5​—N’chifukwa chiyani mtsikanayo akulumbirira akazi akumpanda wa mfumu pogwiritsa ntchito “mphoyo, ndi nswala ya kuthengo”? Mphoyo ndi nswala zili ndi maonekedwe ake ochititsa kaso ndiponso okongola kwambiri. Kwenikweni, Msulamiyu, akulumbirira akazi akumpanda wa mfumu kuti chilichonse chimene chili chochititsa kaso ndiponso chokongola chisautse chikondi mwa iye.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

ijwbq nkhani Na. 131

Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani ya Kudziphoda Komanso Kuvala Zodzikongoletsera?

Yankho la m’Baibulo

Ngakhale kuti Baibulo silifotokoza mwatsatanetsatane za nkhaniyi, silimaletsa kudziphoda, kuvala zibangili ndi ndolo, kapena kugwiritsa ntchito njira zina zodzikongoletsera. Komabe, m’malo mofotokoza kwambiri za kaonekedwe ka kunja, Baibulo limalimbikitsa kudzikongoletsa ndi “zovala zosawonongeka, ndizo mzimu wabata ndi wofatsa.”​—1 Petulo 3:3, 4.

Kudzikongoletsa sikoletsedwa

● Akazi okhulupirika otchulidwa m’Baibulo ankadzikongoletsa. Rabeka, yemwe anakwatiwa ndi mwana wa Abulahamu dzina lake Isaki, ankavala ndolo yagolide ya pamphuno, zibangili zagolide komanso zinthu zina za mtengo wapatali zomwe Abulahamu yemwe anali kudzakhala mpongozi wake anamupatsa monga mphatso. (Genesis 24:22, 30, 53) Nayenso Esitere analola kupakidwa “mafuta okongoletsa” pokonzekera udindo wake wodzakhala mfumukazi ya Ufumu wa Perisiya. (Esitere 2:7, 9, 12) Zodzikongoletserazi ziyenera kuti zinkaphatikizapo “zodzoladzola za mitundu yosiyanasiyana.”​—New International Version; Easy-to-Read Version.

● Mafanizo a m’Baibulo amayerekezera zibangili komanso ndolo ndi zinthu zabwino. Mwachitsanzo, limanena kuti munthu wanzeru amene akupereka malangizo kwa “munthu wa khutu lomvetsera, amakhala ngati ndolo yagolide.” (Miyambo 25:12) Komanso, Mulungu anayerekezera zimene iye ankachitira mtundu wa Isiraeli ndi mwamuna amene amakongoletsa mkwatibwi ndi zibangili, mkanda wa m’khosi, komanso ndolo. Zimenezi zinakongoletsa kwambiri mtunduwo “ndipo unakhala chiphadzuwa.”​—Ezekieli 16:11-13.

Maganizo olakwika pa nkhani yodziphoda ndi kuvala zodzikongoletsera

Maganizo olakwika: Pa lemba la 1 Petulo 3:3, Baibulo limaletsa ‘kumanga tsitsi ndi kuvala zodzikongoletsera zagolide.’

Zoona zake: Nkhaniyi ikusonyeza kuti Baibulo limalimbikitsa kwambiri kukongola kwa mkati poyerekezera ndi maonekedwe abwino akunja. (1 Petulo 3:3-6) Palinso mavesi ena m’Baibulo amene amasonyeza kuti chofunika kwambiri ndi maonedwe amkati osati akunja.​—1 Samueli 16:7; Miyambo 11:22; 31:30; 1 Timoteyo 2:9, 10.

Maganizo olakwika: Zimene Mfumukazi yoipa Yezebeli anachita “podzipaka utoto wakuda m’maso mwake” ndi umboni wakuti kuphoda n’kolakwika.​—2 Mafumu 9:30.

Zoona zake: Yehova anapha Yezebeli chifukwa cha zoipa zimene anachita osati chifukwa cha kudzikongoletsa.​—2 Mafumu 9:7, 22, 36, 37.

NOVEMBER 17-23

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU NYIMBO YA SOLOMO 6-8

Muzikhala Khoma, Osati Chitseko

it “Nyimbo ya Solomo” ¶11-mwbr

Nyimbo ya Solomo

Zikuoneka kuti pambuyo pake, Solomo analola kuti Msulami abwerere kwawo. Azichimwene ake atamuona akubwera, anayamba kufunsana kuti: “Kodi ndi ndani amene akuchokera kuchipululuyu, atakoleka dzanja lake m’khosi mwa wachikondi wake?” (Nym 8:5a) Azichimwene akewo sankadziwa kuti mchemwali wawo ali m’chikondi choncho. M’mbuyomu, mmodzi mwa azichimwene akewo ananenapo kuti: “Tili ndi mchemwali wathu wamngʼono ndipo alibe mabere.” (Nym 8:8) Kenako winanso ananena kuti: “Akakhala khoma, tim’mangira kampanda kasiliva pamwamba pake, koma akakhala chitseko, timʼkhomerera ndi thabwa la mkungudza.” (Nym 8:9) Koma popeza Msulami anakana mayesero onse omwe anakumana nawo, chifukwa anali wokhutiritsidwa ndi munda wake wa mpesa ndipo anakhalabe wokhulupirika kwa wokondedwa wake (Nym 8:6, 7, 11, 12), anakwanitsa kunena kuti: “Ine ndine khoma, ndipo mabere anga ali ngati nsanja. Choncho m’maso mwa wokondedwa wanga ndakhala ngati mkazi amene wapeza mtendere.”​—Nym 8:10.

yp 188 ¶2

Bwanji Ponena za Kugonana Ukwati Usanachitike?

Komabe, kukhala woyera, kumachita zochuluka kuposa kuthandiza wachichepere kupewa zotulukapo zoopsa. Baibulo limasimba za msungwana wina amene anakhalabe woyera mosasamala kanthu za chikondi chomwe anali nacho kwa mnyamata wake. Chifukwa cha chimenecho, iye akanakhoza kunena monyadira kuti: “Ndine khoma, maere anga akunga nsanje zake.” Iye sanali ngati ‘chitseko chomangotseguka’ chimene ‘chinatseguka’ mosavuta pa chitsenderezo cha chisembwere. Mwamakhalidwe, iye anaima monga khoma losagwedezeka la linga lokhala ndi misanje yosakwereka! Iye anayenera kumatchedwa “woyera” ndipo akanatha kunena ponena za woyembekezera kukhala mwamuna wakeyo kuti, “ndinafanana ngati wopeza mtendere.” Mtendere wake wa iye mwini wa maganizo unathandiza chikhutiro pakati pawo awiriwo.​—Nyimbo ya Solomo 6:9, 10; 8:9, 10.

yp2 33

Chitsanzo Chabwino​—Msulami

Mtsikana wachisulami ankadziwa kuti sayenera kungotengeka maganizo pankhani ya chikondi. Iye anauza anzake kuti: ‘Ndikulumbirirani . . . musautse, musagalamutse chikondi, chisanafune mwini.’ Msulamiyu anadziwa kuti munthu angalephere kuganiza bwino chifukwa chongotengeka maganizo. Mwachitsanzo, anazindikira kuti anthu ena akanatha kumulimbikitsa kukhala pachibwenzi ndi munthu amene sakuyenerana naye. Anazindikiranso kuti mtima wake ungamuchititsenso kusaganiza mwanzeru. Choncho Msulamiyu anapitiriza kukhala ngati “khoma.”​—Nyimbo ya Solomo 8:4, 10.

Kodi ndinu wokhwima maganizo moti mumaona nkhani ya chikondi ngati mmene Msulami anali kuionera? Kodi mumayamba mwaganiza kaye musanachite zinthu kapena mumangotsatira zimene mtima wanu wafuna? (Miyambo 2:10, 11) Nthawi zina ena angakulimbikitseni kukhala pachibwenzi inuyo musanafike poti n’kuchita zimenezo. Zochita zanunso zingakulowetseni m’vuto limeneli. Mwachitsanzo, mukaona mnyamata ndi mtsikana akuyenda atagwirana manja, kodi nanunso mumalakalaka mutachita zimenezo? Kodi mungafune munthu amene si wachipembedzo chanu? Pankhani zachikondi, mtsikana wachisulami anali wokhwima maganizo. Inunso mungakhale wotero.

Mfundo Zothandiza

w15 1/15 29 ¶3

Kodi N’zotheka Kukondana Mpaka Kalekale?

Werengani Nyimbo ya Solomo 8:6. Lembali likufotokoza kuti chikondi ndi “lawi la Ya.” Mawu amenewa ndi oyenera chifukwa chakuti Yehova ndi amene anayambitsa chikondi ngati chimenechi. Iye anapanga munthu m’chifaniziro chake, choncho anthu amatha kukondana. (Gen. 1:26, 27) Mulungu anapereka Hava kwa Adamu ndipo Adamuyo anasangalala kwambiri moti ananena ndakatulo. Hava anapangidwa kuchokera ku nthiti ya Adamu ndipo Adamuyo ayenera kuti ankamukonda kwambiri. (Gen. 2:21-23) Popeza Yehova analenga anthu kuti azikondana n’zotheka kuti mwamuna ndi mkazi azikondana mpaka kalekale.

A Mboni za Yehova amakhulupirira kuti mfundo ndiponso malamulo a m’Baibulo angatithandize kuti tizisankha zochita mwanzeru komanso tizisangalatsa Mulungu. (Yesaya 48:17, 18) Sikuti tinakhazikitsa mfundo ndiponso malamulowa koma timayesetsa kuwatsatira. Tiyeni tione malamulo ndiponso mfundo zina za m’Baibulo zokhudza chibwenzi.a

NOVEMBER 24-30

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 1-2

Chiyembekezo kwa “Olemedwa Ndi Zolakwa”

ip-1 14 ¶8

Atate ndi Ana Ake Opanduka

Yesaya akupitiriza uthenga wake mwa kuuza mtundu wa Yuda mawu amphamvu akuti: “Mtundu wochimwa inu, anthu olemedwa ndi mphulupulu, mbewu yakuchita zoipa, ana amene achita mowononga, iwo amusiya Yehova, iwo amunyoza Woyera wa Israyeli, iwo adana naye nabwerera m’mbuyo.” (Yesaya 1:4) Zochita zoipa zingaunjikane kufika pokhala ngati chikatundu chopsinja. M’masiku a Abrahamu Yehova anafotokoza machimo a Sodomu ndi Gomora kuti anali “kulemera.” (Genesis 18:20) Chinthu chofanana ndi zimenezo tsopano chikuoneka mwa anthu a Yuda, pakuti Yesaya akuti iwo ali “olemedwa ndi mphulupulu.” Ndiponso, iye akuwatcha kuti “mbewu yakuchita zoipa, ana amene achita mowononga.” Inde, Ayuda ali ngati ana opulupudza. Iwo ‘abwerera m’mbuyo,’ kapena malinga n’kunena kwa Baibulo la New Revised Standard Version, iwo “alekeratu kuyanjana” ndi Atate awo.

ip-1 28-29 ¶15-17

“Tiyeni Tikonze Zinthu”

Mawu a Yehova tsopano akumveka mwachikondi ndi mwachifundo kwambiri. “‘Bwerani, tsono, anthu inu, tiyeni tikonze zinthu pakati pathu,’ ati Yehova. ‘Ngakhale machimo a anthu inu akhale ofiira, adzakhala oyera ngati matalala; ngakhale akhale ofiira ngati kapezi, adzakhala ngati ubweya wa nkhosa.’” (Yesaya 1:18, NW) Kawirikawiri anthu amamva molakwa chiitano chimene chili koyambirira kwa vesili. Mwachitsanzo, Baibulo lachichewa lotchedwa Buku Lopatulika Ndilo Mawu a Mulungu limati, “tiweruzane”​—ngati kuti aliyense afunika kuvomereza zolakwa zake kuti agwirizane. Si choncho ayi! Yehova sali wolakwa m’pang’ono pomwe m’zochita zake ndi anthu amenewa opanduka ndi achinyengo. (Deuteronomo 32:4, 5) Vesili silikunena za kukambirana kwakuti wina anena mbali yake winanso mbali yake kwa anthu ofanana, koma kwa pabwalo la milandu pofuna kupeza chilungamo. Zili ngati kuti panopo Yehova akutengera Aisrayeli kukhoti.

Zimenezi zingakhale zovutitsa maganizo, koma Yehova ndi Woweruza wachifundo kwambiri zedi. Sitingayerekeze ndi wina aliyense mmene iye amakhululukira ena. (Salmo 86:5) Iye yekha ndi amene angatenge machimo a Israyeli amene ali “ofiira” n’kuwayeretsa, kuwapanga kukhala “oyera ngati matalala.” Kuthimbirira kwa uchimo sikungachotsedwe ndi zoyesayesa za anthu, kachitidwe kenakake ka zinthu, nsembe, kapena mapemphero. Machimo angatsukidwe kokha mwa kukhululukiridwa ndi Yehova. Mulungu amakhululukira moteromo pamlingo wa zimene amanena, zimene zimaphatikizapo kulapa koona kochokera pansi pa mtima.

Choonadi chimenechi chili chofunika kwambiri kwakuti Yehova akuchibwereza ngati kuti akunena ndakatulo​—machimo a “ofiira” adzakhala ngati ubweya woyera watsopano wosasinthidwa mtundu. Yehova amafuna kuti ife tizidziwa kuti iye alidi Wokhululukira machimo, ngakhale machimo akulu kwambiri, malinga ngati aona kuti ife tili olapadi zenizeni. Awo amene sakhulupirira kuti zimenezi zili choncho kwa iwowo angachite bwino kulingalira za zitsanzo za anthu ena monga Manase. Iye analakwa kwambiri​—kwa zaka zochuluka. Komatu, iye analapa ndipo anamukhululukira. (2 Mbiri 33:9-16) Yehova akufuna tonsefe, kuphatikizapo awo amene achita machimo aakulu kwambiri, kuti tidziwe kuti sitinachedwe ‘kukonza zinthu’ ndi iye.

Mfundo Zothandiza

ip-1 39 ¶9

Nyumba ya Yehova Ikwezedwa Pamwamba

Zoonadi, anthu a Mulungu lerolino sasonkhana pa phiri lenileni limene lili ndi kachisi wa miyala. Kachisi wa Yehova ku Yerusalemu anawonongedwa ndi asilikali achiroma mu 70 C.E. Komanso, mtumwi Paulo ananena momveka bwino kuti kachisi wa ku Yerusalemu ndiponso chihema chimene chinalipo kachisiyo asanamangidwe zinali zophiphiritsa. Zinaimira mkhalidwe wauzimu weniweni ndi wokulirapo, “chihema choona, chimene Ambuye anachimanga, si munthu ayi.” (Aheberi 8:2) Chihema chauzimu chimenecho chili makonzedwe ofikira Yehova polambira ozikidwa pa nsembe ya dipo ya Yesu Khristu. (Aheberi 9:2-10, 23) Mogwirizana ndi zimenezi, “phiri la nyumba ya Yehova” lotchulidwa pa Yesaya 2:2 limaimira kulambira kokwezeka koyera kwa Yehova m’masiku athu. Awo amene amayamba kulambira koyera sasonkhana kumalo ena ake apadera; amasonkhana mu umodzi wa kulambira.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

ijwbq nkhani Na. 96

Kodi Tchimo N’chiyani?

Yankho la m’Baibulo

Munthu amachimwa ngati akuchita kapena kuganiza zinthu zomwe Mulungu amadana nazo. Mwachitsanzo, amachimwa ngati sanatsatire mfundo kapena malamulo a Mulungu. (1 Yohane 3:4; 5:17) Koma Baibulo limanenanso kuti munthu amachimwa akalephera kuchita zinthu zoyenera.​—Yakobo 4:17.

M’zinenero zoyambirira zomwe anagwiritsa ntchito polemba Baibulo, mawu akuti tchimo amatanthauza “kuphonya.” Mwachitsanzo, ku Isiraeli wakale kunali asilikali omwe ankati akaponya mwala ndi gulaye, ‘sankaphonya.’ Ngati mawuwa atamasuliridwa mmene analili m’chinenero choyamba, angalembedwe kuti ‘sankachimwa.’ (Oweruza 20:16) Choncho, tchimo lingatanthauze kuphonya kapena kuti kulephera kuchita zimene Mulungu amafuna.

Popeza Mulungu ndi amene anatilenga, iye ndi woyenera kutipatsa mfundo zoti tiziyendera. (Chivumbulutso 4:11) Choncho tidzayankha mlandu kwa Mulungu ngati titamachita zinthu zolakwika.​—Aroma 14:12.

Kodi n’zotheka kupeweratu kuchita machimo?

Ayi. Tikutero chifukwa Baibulo limanena kuti: “Onse ndi ochimwa ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23; 1 Mafumu 8:46; Mlaliki 7:20; 1 Yohane 1:8) N’chifukwa chiyani zili choncho?

Poyamba Adamu ndi Hava anali anthu angwiro. Sankachimwa chifukwa analengedwa m’chifaniziro cha Mulungu. (Genesis 1:27) Koma kenako, iwo anakhala ochimwa chifukwa sanamvere Mulungu. (Genesis 3:5, 6, 17-19) Choncho pamene anayamba kubereka ana, anawapatsiranso uchimowo. (Aroma 5:12) N’chifukwa chake Mfumu Davide ya Isiraeli inanena kuti: ‘Ndinabadwa ndili wochimwa.’​—Salimo 51:5.

Kodi machimo ena ndi aakulu kuposa ena?

Inde. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti anthu a ku Sodomu anali “oipa, ndipo anali ochimwa kwambiri” komanso ‘tchimo lawo linali lalikulu kwambiri.’ (Genesis 13:13; 18:20) Tiyeni tione mfundo zitatu zomwe zingatithandize kudziwa ngati tchimo ndi lalikulu kapena ayi.

1. Mtundu wake. Baibulo limatilimbikitsa kuti tizipewa machimo aakulu monga chiwerewere, kulambira mafano, kuba, kuledzera, kupha munthu komanso kukhulupirira mizimu. (1 Akorinto 6:9-11; Chivumbulutso 21:8) Baibulo limasiyanitsa machimowa ndi machimo ena omwe munthu amachita mosaganizira monga kulankhula kapena kuchita zinthu zokhumudwitsa ena. (Miyambo 12:18; Aefeso 4:31, 32) Koma Baibulo limatilimbikitsa kuti tisamaone tchimo lililonse kukhala laling’ono chifukwa zingachititse kuti tiyambe kuchita machimo aakulu.​—Mateyu 5:27, 28.

2. Cholinga chake. Anthu ena amachita machimo chifukwa sadziwa zimene Mulungu amafuna. (Machitidwe 17:30; 1 Timoteyo 1:13) Baibulo silichepetsa machimo amenewa, koma limangowasiyanitsa ndi machimo amene anthu ena amachita mwadala. (Numeri 15:30, 31) Munthu amene amachita machimo mwadala amakhala ndi ‘mtima woipa.’​—Yeremiya 16:12.

3. Kuchita mobwerezabwereza. Baibulo limasiyanitsanso munthu amene wachita tchimo kamodzi kokha ndi munthu amene amachita mobwerezabwereza. (1 Yohane 3:4-8) Mulungu adzaweruza anthu amene amachita “machimo mwadala” pambuyo poti adziwa zolondola.​—Aheberi 10:26, 27.

Anthu amene anachita machimo aakulu akhoza kumva chisoni kwambiri ndi zimene anachitazo. Mwachitsanzo, Mfumu Davide inanena kuti: “Zolakwa zanga zakwera kupitirira mutu wanga. Zandilemera kwambiri ngati katundu wolemera.” (Salimo 38:4) Komabe Baibulo limanena kuti: “Munthu woipa asiye njira yake ndipo wopweteka anzake asiye maganizo ake. Iye abwerere kwa Yehova ndipo adzamuchitira chifundo. Abwerere kwa Mulungu wathu, pakuti amakhululuka ndi mtima wonse.”​—Yesaya 55:7.

DECEMBER 1-7

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 3-5

Yehova Ankayembekezera Kuti Anthu Ake Azimumvera

ip-1 73-74 ¶3-5

Tsoka Munda Wamphesa Wosakhulupirika!

Kaya Yesaya akuwaimbiradi fanizo limeneli omvetsera ake kapena ayi, koma ndithudi likuwakopa chidwi. Ambiri anazolowera kulima minda yamphesa, ndipo kulongosola kwa Yesaya n’komveka bwino komanso n’zimene zingachitikedi. Mofanana ndi anthu amene amalima mphesa masiku ano, mwini wake wa munda wamphesawo wabzala, osati njere za mphesa, koma “mpesa wosankhika,” kapena kuti wambambande​—mtengo wampesa wodulidwa kapena nsonga ya mpesa wina. Moyenerera, walima munda wamphesa umenewu “m’chitunda cha zipatso zambiri,” malo amene mphesa zingabale bwino.

Pamakhala ntchito yaikulu kuti munda wamphesa ubale zipatso. Yesaya akulongosola kuti mwiniyo ‘anakumba mcherenje kuzungulira kwete natolatola miyala’​—ntchito yowawa komanso yotopetsa! Ayenera kuti miyala ikuluikulu ‘anamangira nsanja.’ M’nthawi zakale pansanja zoterozo ndipo panali kukhala alonda amene anali kudikirira akuba ndi nyama. Ndiponso, wamanga linga la miyala m’malire mwa munda wamphesawo. (Yesaya 5:5) Kawirikawiri anali kuchita zimenezi pofuna kuti nthaka isakokoloke.

Pokhala kuti anagwira ntchito zolimba kuti ateteze munda wake wamphesawo, mwiniyo moyenerera akuyembekezera kuti udzabereka bwino. Poyembekezera zimenezi, akusema moponderamo mphesa. Koma kodi akolola zinthu zimene akuyembekezerazo? Ayi, munda wamphesawo ukubereka mphesa zosadya.

ip-1 76 ¶8-9

Tsoka Munda Wamphesa Wosakhulupirika!

Yesaya akutchula Yehova, mwini wake wa munda wamphesawo, kuti “wokondedwa wanga.” (Yesaya 5:1) Yesaya atha kulankhula za Mulungu mwachikondi moteromo kokha chifukwa chakuti ali ndi unansi wolimba ndi Mulunguyo. Komabe, chikondi cha mneneriyu pa Mulungu ndi chochepa poyerekeza ndi chikondi chimene Mulungu wasonyeza pa “munda [wake] wamphesa”​—mtundu umene ‘anauwoka.’​—Yerekezani ndi Ekisodo 15:17; Salmo 80:8, 9.

Yehova “anawoka” mtundu wake m’dziko la Kanani naupatsa malamulo ndi malangizo ake, amene anali ngati khoma lowateteza kuti asaipitsidwe ndi mitundu ina. (Ekisodo 19:5, 6; Salmo 147:19, 20; Aefeso 2:14) Ndiponso, Yehova anawapatsa oweruza, ansembe, ndi aneneri kuti aziwalangiza. (2 Mafumu 17:13; Malaki 2:7; Machitidwe 13:20) Pamene Israyeli anali kuopsezedwa ndi magulu ankhondo, Yehova anali kupereka anthu oti awapulumutse. (Aheberi 11:32, 33) Pachifukwa chomveka, Yehova akufunsa kuti: “Ndikanachitanso chiyani ndi munda wanga wamphesa, chimene sindinachite mmenemo?”

w06 6/15 18 ¶1

Samalirani “Mpesa Uwu”!

Yesaya anayerekezera “banja la Israyeli” ndi munda wa mphesa umene pang’ono ndi pang’ono unabereka “mphesa zosadya,” kapena kuti, mphesa zowola. (Yesaya 5:2, 7) Mphesa zosadya zimakhala zazing’ono poyerekezera ndi mphesa zakudya ndipo zimakhala ndi mnofu wochepa kwambiri, popeza nthanga zake zimadzaza pafupifupi mphesa yonseyo. Mphesa zosadya sangapangire vinyo kapena kuzidya. Ichi n’chizindikiro chabwino cha mtundu wopandukawo, umene chipatso chake chinali kuphwanya malamulo m’malo mwa kuchita chilungamo. Kubereka chipatso chopanda ntchitoku silinali vuto la Mlimi wa mpesawo. Yehova anachita zonse zomwe akanatha kuti apangitse mtunduwo kukhala wobala zipatso. Iye anafunsa kuti: “Ndikanachitanso chiyani ndi munda wanga wamphesa, chimene sindinachite mmenemo”?​—Yesaya 5:4.

w06 6/15 18 ¶2

Samalirani “Mpesa Uwu”!

Popeza mpesa wa Israyeli unakhala wosabereka, Yehova anawachenjeza kuti adzagwetsa mpanda umene anamanga mozungulira anthu ake kuti uwateteze. Sadzaduliranso mpesa wake wophiphiritsira kapena kulimira dothi lake. Mvula ya m’nyengo ya masika yomwe zipatsozo zinkadalira sidzabwera, ndipo minga ndi udzu zidzamera m’munda wa mphesawo.​—Yesaya 5:5, 6.

Mfundo Zothandiza

ip-1 80 ¶18-19

Tsoka Munda Wamphesa Wosakhulupirika!

Mu Israyeli wakale dziko lonse kwenikweni linali la Yehova. Banja lililonse linali ndi cholowa chopatsidwa ndi Mulungu, chimene anali kutha kubwereka wina kapena kumupatsa pa ngongole koma osati kugulitsa “chigulitsire.” (Levitiko 25:23) Lamulo limeneli linali kuteteza kugwiritsa ntchito molakwa zinthu, monga ngati kuphangira malo. Linalinso kuteteza mabanja kuti asasauke kwambiri. Komabe, anthu ena mu Yuda anali kuswa mwadyera malamulo a Mulungu onena za malo. Mika analemba kuti: “Akhumbira minda, nailanda; ngakhale nyumba, nazichotsa; asautsa mwamuna ndi nyumba yake, inde munthu ndi cholowa chake.” (Mika 2:2) Koma Miyambo 20:21 imachenjeza kuti: “Cholowa chingalandiridwe msangamsanga poyamba pake; koma chitsiriziro chake sichidzadala.”

Yehova akulonjeza kuti anthu adyera amenewa adzawalanda zinthu zimene anapeza m’njira zolakwika. Nyumba zimene akulanda ena zidzakhala “zopanda wokhalamo.” Minda imene akuisirira idzabereka pang’ono kwambiri kusiyana ndi mmene ikuberekera. Sizikutchulidwa kuti temberero limeneli lidzachitika motani kwenikweni ngakhalenso nthawi yake yeniyeni imene lidzakwaniritsidwa. Pang’ono chabe, mwina likunena za mikhalidwe imene idzakhalapo pamene adzakhala akapolo ku Babulo.​—Yesaya 27:10.

DECEMBER 8-14

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 6-8

“Ine Ndilipo! Nditumizeni”

ip-1 93-94 ¶13-14

Yehova Mulungu Ali M’kachisi Wake Wopatulika

Tiyeni timvetsere zimene Yesaya akumva. “Ndinamva mawu a Ambuye akuti, Ndidzatumiza yani, ndipo ndani adzatimukira ife? Ndipo ine ndinati, Ndine pano; munditumize ine.” (Yesaya 6:8) Funso limene Yehova akufunsa mwachionekere lalinganizidwa kuti Yesaya ayankhe, popeza kuti palibe mneneri winanso waumunthu m’masomphenyawo. Popanda kukayika Yesaya akuitanidwa kuti akhale mthenga wa Yehova. Koma kodi ndi chifukwa chiyani Yehova akufunsa kuti, “Ndani adzatimukira ife?” Mwa kusintha kanenedweko kuchoka pa kunena za munthu m’modzi kuti “ndidzatumiza” n’kunena za anthu ambiri kuti “adzatimukira,” tsopano Yehova akuphatikizapo munthu winanso m’modzi pa iye mwini. Ndaniyo? Kodi ameneyu sanali Mwana wake wobadwa yekha, amene kenako anadzakhala munthu wotchedwa Yesu Khristu? Indedi, anali Mwana mmodzimodziyu amene Mulungu anamuuza kuti, “tipange munthu m’chifanizo chathu.” (Genesis 1:26; Miyambo 8:30, 31) Inde, Mwana wake wobadwa yekha ali pambali pake Yehova m’mabwalo akumwamba.​—Yohane 1:14.

Yesaya sakuchedwa kuyankha! Mosasamala kanthu kuti uthengawo ndi wotani, iye mofulumira akuyankha kuti: “Ndine pano; munditumize ine.” Iye sakufunsa chimene adzapindulapo ngati atavomera ntchitoyo. Mzimu wake wofunitsitsa uli chitsanzo chabwino kwambiri kwa atumiki onse a Mulungu lerolino, amene apatsidwa ntchito yolalikira ‘uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse lapansi.’ (Mateyu 24:14) Mofanana ndi Yesaya, mokhulupirika amagwirabe ntchito yawoyo ndipo amakwanitsa kuchita ‘umboni kwa anthu a mitundu yonse,’ mosasamala kanthu kuti anthu ambiri salabadira. Ndipo mwachidaliro amapitirizabe kugwira ntchitoyi, monga mmene Yesaya anachitira, podziwa kuti ntchito yawoyo inalamulidwa ndi munthu wamkulu kwambiri.

ip-1 95 ¶15-16

Yehova Mulungu Ali M’kachisi Wake Wopatulika

Tsopano Yehova akulongosola zimene Yesaya adzanene ndiponso mmene anthu adzalabadirire: “Kauze anthu awa, Imvani inu ndithu [“mobwerezabwereza,” NW], koma osazindikira; yang’anani inu ndithu [“mobwerezabwereza,” NW], koma osadziwitsa. Nenepetsa mtima wa anthu awa, lemeretsa makutu awo, nutseke maso awo; angaone ndi maso awo, angamve ndi makutu awo, angazindikire ndi mtima wawo, nakabwerenso, nachiritsidwe.” (Yesaya 6:9, 10) Kodi izi zikutanthauza kuti Yesaya azilankhula mosazindikira bwino ndi mopanda luso akumatsutsa Ayuda, kuwapangitsa kuti asamvane ndi Yehova? Ayi ndithu! Awa ndi anthu a mtundu wake Yesaya amene akuwaona kuti ndi abale ake. Koma mawu a Yehova akusonyeza mmene anthu adzachitira ndi uthenga wake, mosasamala kanthu za mmene Yesaya akagwirira ntchito yake mokhulupirika.

Anthu ndiwo ali ndi vuto. Yesaya adzalankhula “mobwerezabwereza,” koma uthengawo sadzaulandira ngakhalenso kuumvetsa. Ochuluka adzakhala ouma khosi ndi osalabadira, ngati kuti ndi akhungu ndi ogontha kotheratu. Mwa kuwayendera mobwerezabwereza, Yesaya adzalola “anthu awa” kuti asonyeze kuti safuna kumvetsetsa. Adzaonetsa kuti safuna kuti uthenga wa Yesaya​—uthenga wa Mulungu​—umene adzauzidwa ulowe m’maganizo mwawo ndi m’mitima yawo. Anthu a m’masiku ano akuchitanso mofananamo! Ambiri amakana kumvetsera Mboni za Yehova pamene zikulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu umene ukubwerawo.

ip-1 99 ¶23

Yehova Mulungu Ali M’kachisi Wake Wopatulika

Pogwira mawu a Yesaya, Yesu anasonyeza kuti ulosiwo unalinso ndi kukwaniritsidwa m’masiku ake. Anthuwo monga gulu anali ndi mtima wonga wa Ayuda a m’masiku a Yesaya. Iwo anadzipangitsa kukhala akhungu ndi ogontha ku uthenga wake ndipo moteronso anawonongedwa. (Mateyu 23:35-38; 24:1, 2) Zimenezi zinachitika pamene ankhondo a Aroma motsogoleredwa ndi Kazembe Tito anaukira Yerusalemu mu 70 C.E. ndi kuphwasula mzindawo ndi kachisi wake. Komabe, ena anamvetsera Yesu ndipo anakhala ophunzira ake. Yesu anawatcha kuti “odala.” (Mateyu 13:16-23, 51) Anawauza kuti pamene adzaona “Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo,” iwo ‘akathawire kumapiri.’ (Luka 21:20-22) Motero “mbewu yopatulika” imene inasonyeza chikhulupiriro ndi imene inapangidwa kukhala mtundu wauzimu, “Israyeli wa Mulungu,” inapulumuka.​—Agalatiya 6:16.

Mfundo Zothandiza

w06 12/1 9 ¶4

Mfundo Zazikulu za M’buku la Yesaya​—Gawo 1

7:3, 4​—N’chifukwa chiyani Yehova anapulumutsa Ahazi mfumu yoipa? Mafumu a Aramu ndi Isiraeli anakonza zochotsa Mfumu Ahazi ya Yuda pampando wachifumu n’kuikapo wolamulira woti azingowamvera iwowo. Wolamulira wake anali mwana wamwamuna wa Tabeeli, yemwe sanali mbadwa ya Davide. Nzeru zochokera kwa Satana zimenezi zikanasokoneza pangano la Ufumu la pakati pa Yehova ndi Davide. Yehova anapulumutsa Ahazi n’cholinga choteteza mzere umene “Kalonga Wamtendere” adzabadwiremo.​—Yesaya 9:6.

DECEMBER 15-21

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 9-10

Analosera za “Kuwala Kwakukulu”

ip-1 125-126 ¶16-17

Lonjezo la Kalonga wa Mtendere

Inde, “nthawi ina m’tsogolo” imene Yesaya analosera ndi nthawi ya utumiki wapadziko lapansi wa Khristu. Yesu ali padziko lapansi anakhalitsa kwambiri ku Galileya. Munali m’dera la Galileya mmene anayambira utumiki wake ndi kuyamba kulengeza kuti: “Ufumu wa Kumwamba wayandikira.” (Mateyu 4:17) Ku Galileya, anapereka Ulaliki wake wotchuka wa pa Phiri, anasankha atumwi ake, anachita chozizwitsa chake choyamba, ndipo ataukitsidwa anaonekera kwa otsatira ake pafupifupi 500. (Mateyu 5:1–7:27; 28:16-20; Marko 3:13, 14; Yohane 2:8-11; 1 Akorinto 15:6) Mwa njirayi Yesu anakwaniritsa ulosi wa Yesaya mwa kuchitira ulemu “dziko la Zebuloni, ndi dziko la Naftali.” Zoona, Yesu sanangochita utumiki wake kwa anthu a ku Galileya okha. Mwa kulalikira uthenga wabwino m’dziko lonselo, Yesu ‘anachitira ulemu’ mtundu wonse wa Israyeli, kuphatikizapo Yuda.

Nanga bwanji za “kuwala kwakukulu” mu Galileya kumene Mateyu akutchula? Mawu amenewanso anawatenga mu ulosi wa Yesaya. Yesaya analemba kuti: “Anthu amene anayenda mumdima, aona kuwala kwakukulu; iwo amene anakhala m’dziko la mthunzi wa imfa, kuwala kwatulukira kwa iwo.” (Yesaya 9:2) Pofika zaka za zana loyamba C.E., kuwala kwa choonadi kunali kutabisika ndi mabodza achikunja. Atsogoleri achipembedzo achiyuda anawonjezera vutolo mwa kumamatira ku miyambo yawo yachipembedzo imene ‘anapeputsa [nayo] mawu a Mulungu.’ (Mateyu 15:6) Anthu odzichepetsa anali kuponderezedwa ndi kusokonezedwa maganizo, anali kutsatira “atsogoleri akhungu.” (Mateyu 23:2-4, 16) Pamene Yesu Mesiyayo anaoneka, maso a anthu ambiri odzichepetsa anatsegulidwa modabwitsa zedi. (Yohane 1:9, 12) Ntchito ya Yesu pamene anali padziko lapansi ndiponso madalitso obwera chifukwa cha nsembe yake analongosoledwa bwino mu ulosi wa Yesaya kuti ndi “kuwala kwakukulu.”​—Yohane 8:12.

ip-1 126-128 ¶18-19

Lonjezo la Kalonga wa Mtendere

Amene analabadira kuwalako anali ndi chifukwa chokwanira chokhalira okondwa. Yesaya anapitiriza kuti: “Inu mwachulukitsa mtundu, inu mwaenjezera kukondwa kwawo; iwo akondwa pamaso panu monga akondwera m’masika, monga anthu akondwa pogawana zofunkha.” (Yesaya 9:3) Chifukwa cha kulalikira kwa Yesu ndi otsatira ake, anthu oona mtima anaoneka, anadzionetsa kuti anali kukhumba kulambira Yehova mu mzimu ndi m’choonadi. (Yohane 4:24) Pa zaka zosakwana zinayi, anthu ambiri zedi anakhala Akhristu. Anthu 3,000 anabatizidwa pa tsiku la Pentekoste mu 33 C.E. Patapita nthawi yochepa, “chiwerengero cha amuna chinali ngati zikwi zisanu.” (Machitidwe 2:41; 4:4) Pamene ophunzirawo anali kusonyeza kuwalako mwachangu, “chiwerengero cha akuphunzira chidachulukatu ku Yerusalemu; ndipo khamu lalikulu la ansembe linamvera chikhulupirirocho.”​—Machitidwe 6:7.

Mofanana ndi amene amakondwera ndi zotuta zochuluka kapena amene amasangalala pogawana zofunkha zamtengo wapatali atapambana nkhondo, otsatira a Yesu anakondwera kuti anali kuwonjezeka. (Machitidwe 2:46, 47) M’kupita kwa nthawi, Yehova anapangitsa kuwalako kuwalira amitundu. (Machitidwe 14:27) Motero anthu a mafuko onse anakondwera kuti njira yofikira kwa Yehova inatsegulidwa kwa iwo.​—Machitidwe 13:48.

ip-1 128-129 ¶20-21

Lonjezo la Kalonga wa Mtendere

Zotsatira za ntchito ya Mesiya sizidzatha, monga momwe tikuonera m’mawu otsatira a Yesaya akuti: “Goli la katundu wake, mkunkhu wa paphewa pake, ndodo ya womusautsa, inu mwazithyola monga tsiku la Midyani.” (Yesaya 9:4) Zaka mazana angapo Yesaya asanabadwe, Amidyani limodzi ndi Amoabu anakonza chiwembu kuti achimwitse Israyeli. (Numeri 25:1-9, 14-18; 31:15, 16) Kenako, Amidyani anakhaulitsa Aisrayeli mwa kukantha ndi kufunkha midzi yawo ndi minda yawo kwa zaka zisanu ndi ziwiri. (Oweruza 6:1-6) Komano Yehova, kupyolera mwa mtumiki wake Gideoni, anakantha gulu lankhondo la Midyani. Kuchokera pa “tsiku la Midyani” limenelo, palibe umboni uliwonse wosonyeza kuti anthu a Yehova anavutitsidwanso ndi Amidyani. (Oweruza 6:7-16; 8:28) Posachedwa m’tsogolo, Yesu Khristu, Gideoni wamkulu, adzakantha adani amakono a anthu a Yehova. (Chivumbulutso 17:14; 19:11-21) Ndiyeno, “monga tsiku la Midyani,” padzakhala chipambano chotheratu ndi chokhalitsa, osati mwa maluso aumunthu, koma mwa mphamvu ya Yehova. (Oweruza 7:2-22) Anthu a Mulungu sadzavutikanso m’goli lopondereza!

Kusonyeza mphamvu yaumulungu si kutamanda nkhondo. Yesu woukitsidwayo ali Kalonga wa Mtendere, ndipo mwa kufafaniziratu adani ake, adzabweretsa mtendere wosatha. Tsopano Yesaya akunena za zida zankhondo kuti zikuwonongedwa kotheratu ndi moto: “Zida zonse za mwamuna wovala zida za nkhondo m’phokosomo, ndi zovala zovimvinika m’mwazi, zidakhala zonyeka ngati nkhuni.” (Yesaya 9:5) Phokoso la mgugu wa nsapato za asilikali oguba silidzamvekanso. Mayunifolomu amagazi a asilikali okonda nkhondo sadzaonekanso. Sikudzakhalanso nkhondo!​—Salmo 46:9.

Mfundo Zothandiza

ip-1 130 ¶23-24

Lonjezo la Kalonga wa Mtendere

Phungu ndi munthu amene amapereka uphungu, kapena malangizo. Pamene anali padziko lapansi Yesu Khristu anapereka uphungu wodabwitsa. M’Baibulo timawerenga kuti “makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake.” (Mateyu 7:28) Iye ndi Phungu wanzeru ndi wachifundo, amene amamvetsetsa chibadwa cha anthu mwapadera kwambiri. Uphungu wake sukhala kudzudzula kapena kupereka chilango kokhakokha. Kawirikawiri, umakhala kuphunzitsa ndi kulangiza mwachikondi. Uphungu wa Yesu ndi wodabwitsa chifukwa nthawi zonse uli wanzeru, wangwiro, ndi wosalakwika. Pamene watsatiridwa, umapezetsa moyo wosatha.​—Yohane 6:68.

Uphungu wa Yesu suli wotero chabe chifukwa chakuti amaganiza kwambiri. M’malo mwake, iye akuti: “Chiphunzitso changa sichili changa, koma cha Iye amene anandituma Ine.” (Yohane 7:16) Monga mmene zinalili ndi Solomo, Yehova Mulungu ndiye Gwero la nzeru za Yesu. (1 Mafumu 3:7-14; Mateyu 12:42) Chitsanzo cha Yesu chiyenera kusonkhezera aphunzitsi ndi aphungu mu mpingo wachikristu kuti nthawi zonse zophunzitsa zawo zizichokera m’Mawu a Mulungu.​—Miyambo 21:30.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

ijwfq nkhani Na. 35

Kodi a Mboni za Yehova Anasintha Zina N’zina M’Baibulo Kuti Zigwirizane ndi Zimene Amakhulupirira?

Ayi sitinasinthe. M’malomwake, tikazindikira kuti zina n’zina zimene timakhulupirira sizikugwirizana ndi Baibulo, timasintha zimene tinkakhulupirirazo.

Tisanayambe kufalitsa Baibulo lachingelezi la Baibulo la Dziko Latsopano mu 1950, tinkafufuza mosamala zimene Baibulo limanena. Tinkagwiritsira ntchito Mabaibulo osiyanasiyana pofuna kuonetsetsa kuti zimene timakhulupirira n’zogwirizana ndi Baibulo. Taonani zitsanzo zochepa za zinthu zimene takhala tikuzikhulupirira kwa nthawi yaitali ndipo muone ngati n’zogwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa.

1. Zimene timakhulupirira: Palibe milungu itatu mwa Mulungu mmodzi. Nsanja ya Olonda ya mu July 1882, yomwe pa nthawiyo inkatchedwa Zion’s Watch Tower, inanena kuti: “Anthu amene amawerenga magazini athu amadziwa bwino kuti timakhulupirira Yehova, Yesu komanso Mzimu woyera. Amadziwanso kuti sitikhulupirira zoti pali milungu itatu mwa Mulungu mmodzi, chifukwa Baibulo siliphunzitsa zimenezi.”

● Zimene Baibulo limanena: “Yehova Mulungu wathu, Yehova ndiye mmodzi.” (Deuteronomo 6:4, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) “Koma kwa ife pali Mulungu m’modzi yekha, Atate, kwa amene zinthu zonse zidachokera ndi kwa amene ife tikhalira: ndipo pali Ambuye m’modzi, Yesu Khristu, amene zinthu zonse zinachokera ndi mwa Iye ife tili ndi moyo.” (1 Akorinto 8:6, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Ndipo Yesu ananena yekha kuti: “Atate ndi wamkulu kuposa Ine.”​—Yohane 14:28, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.

2. Zimene timakhulupirira: Kulibe malo amene anthu oipa amawotchedwako kwamuyaya. Magazini ya Nsanja ya Olonda ya mu June 1882 inali ndi mutu wochokera pa mawu a pa Aroma 6:23 mu Baibulo lachingelezi la King James Version. Magaziniyi inali ndi mutu wakuti, “Mphotho Yake ya Uchimo ndi Imfa,” ndipo inati: “Zimenezitu n’zosavuta kumva. Koma zodabwitsa n’zakuti, anthu ambiri amene amaona kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu, amatsutsanabe ndi lemba losavuta kumvetsali. Iwo amakhulupirirabe kuti Baibulo limaphunzitsa zakuti mphotho yake ya uchimo ndi moyo wozunzika kwamuyaya ku Gehena.”

● Zimene Baibulo limanena: “Moyo wochimwawo ndiwo udzafa.” (Ezekieli 18:4, 20, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Chilango chomaliza chimene chidzaperekedwe kwa anthu amene amatsutsa Mulungu chidzakhala “chiwonongeko chosatha,” osati kuzunzidwa kwamuyaya ku Gehena.​—2 Atesalonika 1:9, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

3. Zimene timakhulupirira: Ufumu wa Mulungu ndi boma lenileni, osati uli mumtima mwa munthu. Pofotokoza nkhani yokhudza Ufumu wa Mulungu, magazini ya Nsanja ya Olonda ya mu December 1881 inanena kuti: “Ufumuwu ukadzakhazikitsidwa udzachotsa maufumu onse a padziko lapansi.”

● Zimene Baibulo limanena: “Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire.”​—Danieli 2:44, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Kodi a Mboni za Yehova amadalira Baibulo la Dziko Latsopano pofuna kusonyeza kuti zimene amakhulupirira n’zochokeradi m’Baibulo?

Ayi sichoncho, chifukwa tikupitirizabe kugwiritsira ntchito Mabaibulo osiyanasiyana pa ntchito yathu yolalikira. Ngakhale kuti timaphunzira ndi anthu kwa ulele ndipo timawapatsa Baibulo la Dziko Latsopano popanda kuwauza mtengo, timaphunziranso ndi amene amafuna kuti tizigwiritsira ntchito Mabaibulo ena.

DECEMBER 22-28

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 11-13

Kodi Baibulo Linanena Zotani Zokhudza Mesiya?

ip-1 159 ¶4-5

Chipulumutso ndi Kusangalala mu Ulamuliro wa Mesiya

4 Zaka mazana ambiri Yesaya asanabadwe, olemba Baibulo achihebri ena anatchula za kubwera kwa Mesiya, Mtsogoleri woona, amene Yehova adzatumiza ku Israyeli. (Genesis 49:10; Deuteronomo 18:18; Salmo 118:22, 26) Tsopano kupyolera mwa Yesaya, Yehova akuwonjeza mbali zina. Yesaya akulemba kuti: “Padzatuluka mphukira pa tsinde la Jese, ndi nthambi yotuluka m’mizu yake idzabala zipatso.” (Yesaya 11:1; yerekezani ndi Salmo 132:11.) Mawu akuti “mphukira” komanso akuti “nthambi” akusonyeza kuti Mesiya adzakhala mbadwa ya Jese kupyolera mwa mwana wake Davide, amene anadzozedwa ndi mafuta kukhala mfumu ya Israyeli. (1 Samueli 16:13; Yeremiya 23:5; Chivumbulutso 22:16) Pamene Mesiya woona wafika, “nthambi” imeneyi, ya m’nyumba ya Davide, idzabala chipatso chabwino

Mesiya wolonjezedwayo ndi Yesu. Wolemba uthenga wabwino Mateyu ananena za mawu a pa Yesaya 11:1 pamene anati kunali kukwaniritsa mawu a aneneri kutchula Yesu kuti ‘Mnazara.’ Chifukwa chakuti anakulira m’tauni ya Nazarete, Yesu anatchedwa kuti Mnazara, dzina limene likuoneka kuti n’lofanana ndi liwu lachihebri logwiritsidwa ntchito pa Yesaya 11:1 kuti “nthambi.”​—Mateyu 2:23, NW, mawu am’munsi; Luka 2:39, 40.

ip-1 159 ¶6

Chipulumutso ndi Kusangalala mu Ulamuliro wa Mesiya

Kodi Mesiya adzakhala wolamulira wotani? Kodi adzakhala ngati Asuri wankhanza, amene akuwononga ufumu wakumpoto wa mafuko khumi wa Israyeli? Ndithudi ayi. Ponena za Mesiya, Yesaya akuti: “Mzimu wa Yehova udzamubalira [“uyenera kukhala pa,” NW] iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziwa ndi wakuopa Yehova; ndipo adzakondwera nako kumuopa Yehova.” (Yesaya 11:2, 3a) Mesiyayo akudzozedwa, osati ndi mafuta, koma ndi mzimu woyera wa Mulungu. Izi zikuchitika pa ubatizo wa Yesu, pamene Yohane Mbatizi akuona mzimu woyera wa Mulungu ukutsikira pa Yesu mooneka ngati nkhunda. (Luka 3:22) Mzimu wa Yehova ‘ukukhala pa’ Yesu, ndipo akupereka umboni wa zimenezi pamene akuchita zinthu mwanzeru, mozindikira, mwauphungu, mwamphamvu, ndi mwachidziwitso. Mikhalidwe yabwinotu kwambiri ya mtsogoleri!

ip-1 160 ¶8

Chipulumutso ndi Kusangalala mu Ulamuliro wa Mesiya

Kodi kuopa Yehova kumene Mesiya akusonyeza n’chiyani? Ndithudi Yesu sakuchita mantha oopa mkwiyo wa Mulungu, kuopa chiweruzo chake ayi. M’malo mwake, Mesiya amaopa Mulungu mwa kum’patsa ulemu, ali ndi mantha achikondi pa iye. Munthu amene amaopa Mulungu amalakalaka kuti nthawi zonse ‘azichita zimene zimamukondweretsa Iye,’ monga amachitira Yesu. (Yohane 8:29) Mwa mawu komanso chitsanzo chake, Yesu amaphunzitsa kuti palibe amene angakhale n’chimwemwe chachikulu kuposa amene tsiku lililonse akuyenda mu kuopa koyenerera kwa Yehova.

ip-1 160 ¶9

Chipulumutso ndi Kusangalala mu Ulamuliro wa Mesiya

Yesaya akulosera mikhalidwe inanso ya Mesiya kuti: “Sadzaweruza monga apenya maso, sadzadzudzula mwamphekesera.” (Yesaya 11:3b) Ngati munali kuweruzidwa m’khothi, kodi simungayamikire kukhala ndi woweruza wonga ameneyu? Pa udindo wake monga Woweruza wa anthu onse, Mesiya satengeka ndi mfundo zabodza, luso la kalankhulidwe kamachenjera pamilandu, mphekesera, kapena zinthu zimene munthu ali nazo, monga chuma. Amazindikira chinyengo ndipo amayang’ana kupyola pa maonekedwe akunja oshashalika, nazindikira “munthu wobisika wamtima,” “munthu wosaoneka.” (1 Petro 3:4, NW, mawu am’munsi) Chitsanzo chapamwamba cha Yesu chimenechi n’choyenera kuti onse amene afunika kuweruza milandu mumpingo wachikristu azichitsatira.​—1 Akorinto 6:1-4.

ip-1 161 ¶11

Chipulumutso ndi Kusangalala mu Ulamuliro wa Mesiya

Pamene otsatira ake akufunika kuwawongolera, Yesu amatero m’njira imene imawapindulitsa kwambiri​—chitsanzo chabwino kwambiri kwa akulu achikristu. Komabe, amene amachita zoipa angayembekezere chiweruzo chowawa kwambiri. Pamene Mulungu adzafuna kuti dongosolo la zinthu lino liyankhe pa zochita zake, Mesiya “adzamenya dziko” ndi mawu ake aulamuliro, kupereka chiweruzo cha chiwonongeko kwa onse oipa. (Salmo 2:9; yerekezani ndi Chivumbulutso 19:15.) Pomaliza pake, sipadzakhala anthu oipa osokoneza mtendere wa anthu. (Salmo 37:10, 11) Yesu, m’chiuno ndi mu impso zake atamangamo chilungamo ndi kukhulupirika, ali ndi mphamvu yochita zimenezi.​—Salmo 45:3-7.

Mfundo Zothandiza

ip-1 165-166 ¶16-18

Chipulumutso ndi Kusangalala mu Ulamuliro wa Mesiya

Kulambira koyera kunayamba kuukiridwa mu Edene pamene Satana anapambana posonkhezera Adamu ndi Hava kuti asamvere Yehova. Kufikira lerolino, Satana sanasiye cholinga chake cha kupatutsa kwa Mulungu anthu ochuluka monga mmene angathere. Koma Yehova sadzalola kuti kulambira koyera kuthe padziko lapansi. Dzina lake likuphatikizidwapo, ndipo amasamalira amene amamutumikira. Motero kupyolera mwa Yesaya akupereka lonjezo lochititsa chidwi ili: “Padzakhala tsiku lomwelo, kuti muzu wa Jese umene uima ngati mbendera ya mitundu ya anthu, amitundu adzafunafuna uwu; ndipo popuma pake padzakhala ulemerero.” (Yesaya 11:10) M’mbuyomo mu 537 B.C.E., Yerusalemu, mzinda umene Davide anaupanga kukhala likulu la dzikolo, unali ngati mbendera, unaitana Ayuda otsalira okhulupirika amene anali atamwazikana kuti abwere ndi kudzamanga kachisi..

Komabe, ulosiwu ukusonya zoposa pamenepo. Monga taonera kale, ukunena za ulamuliro wa Mesiya, Mtsogoleri yekha woona wa anthu a mitundu yonse. Mtumwi Paulo anagwira mawu Yesaya 11:10 posonyeza kuti m’masiku ake anthu a mitundu anali ndi malo mu mpingo wachikristu. Pogwira mawu matembenuzidwe a mu Septuagint a vesili, iye analemba kuti: “Yesaya ati, Padzali muzu wa Jese, ndi iye amene aukira kuchita ufumu pa anthu amitundu; Iyeyo anthu amitundu adzamuyembekezera.” (Aroma 15:12) Ndiponso, ulosiwu ukufika patali​—ukufika m’masiku athu ano pamene anthu amitundu akusonyeza chikondi kwa Yehova mwa kuchirikiza abale ake odzozedwa a Mesiya.​—Yesaya 61:5-9; Mateyu 25:31-40.

M’kukwaniritsidwa kwamakono, “tsiku lomwelo” lotchulidwa ndi Yesaya linayamba pamene Mesiya anaikidwa pa mpando wachifumu monga Mfumu ya Ufumu wa kumwamba wa Mulungu mu 1914. (Luka 21:10; 2 Timoteo 3:1-5; Chivumbulutso 12:10) Kuchokera nthawiyo, Yesu Khristu wakhala mbendera yooneka bwino, malo osonkhanako anthu, kwa Israyeli wauzimu ndi kwa anthu amitundu amene amakhumba kukhala ndi boma lachilungamo. Motsogoleredwa ndi Mesiya, uthenga wabwino wa Ufumu waperekedwa ku mitundu yonse, monga momwe Yesu analoserera. (Mateyu 24:14; Marko 13:10) Uthenga wabwino umenewu umakhudza anthu mwamphamvu. “Khamu lalikulu, loti palibe munthu [akhoza] kuliwerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse” likugonjera kwa Mesiya mwa kugwirizana ndi otsalira odzozedwa m’kulambira koyera. (Chivumbulutso 7:9) Pamene atsopano ambiri akupitiriza kuyanjana ndi otsalira mu “nyumba yopemphereramo” yauzimu ya Yehova, amawonjezera ulemerero wa “popuma” pa Mesiya, kachisi wauzimu waukulu wa Mulungu.​—Yesaya 56:7; Hagai 2:7.

DECEMBER 29–JANUARY 4

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU YESAYA 14-16

Adani a Anthu a Mulungu Adzalangidwa

ip-1 180 ¶16

Yehova Anyazitsa Mzinda Wodzikuza

Izi sizinachitike panthawi yomweyo mu 539 B.C.E. Komabe, lerolino n’zodziwika kwambiri kuti chilichonse chimene Yesaya analosera ponena za Babulo chakwaniritsidwa. Babulo “tsopano ndi malo ophwasulidwa aakulu, komanso ali mabwinja okhaokha, ndipo wakhala choncho kwa zaka mazana ambiri,” anatero munthu wina wothirira ndemanga pa Baibulo. Ndiyeno anatinso: “N’kosatheka kuona malo amenewa n’kusakumbukira mmene maulosi a Yesaya ndi Yeremiya akwaniritsidwira ndendende.” Mwachionekere, m’masiku a Yesaya palibe munthu amene akanalosera kugwa kwa Babulo ndi kudzafafanizidwa kwake. Ndiponsotu, Babulo anagwa kwa Amedi ndi Aperisi pafupifupi zaka 200 Yesaya atalemba buku lake! Ndipo kufafanizidwa kwake kunachitika zaka mazana angapo pambuyo pa zimenezi. Kodi zimenezi sizikulimbitsa chikhulupiriro chathu mu Baibulo monga Mawu ouziridwa a Mulungu? (2 Timoteo 3:16) Ndiponso, popeza kuti Yehova anakwaniritsa maulosi m’nthawi za m’mbuyomu, tingakhale ndi chidaliro chonse kuti maulosi a Baibulo amene sanakwaniritsidwebe adzakwaniritsidwa m’nthawi yoikika ya Mulungu.

ip-1 184 ¶24

Yehova Anyazitsa Mzinda Wodzikuza

M’Baibulo mafumu a banja lachifumu la Davide amafanizidwa ndi nyenyezi. (Numeri 24:17) Kuyambira ndi Davide, “nyenyezi” zimenezo zinali kulamulira zili pa Phiri la Ziyoni. Solomo atamanga kachisi mu Yerusalemu, dzina lakuti Ziyoni linali kugwiritsidwa ntchito pa mzinda wonsewo. Mu pangano la Chilamulo, amuna onse achiisrayeli anali kulamulidwa kupita ku Ziyoni katatu pachaka. Motero linakhala “phiri losonkhanako.” Mwa kutsimikiza mtima kukagonjetsa mafumu achiyuda ndiyeno n’kuwachotsa pa phiri limenelo, Nebukadinezara akulengeza cholinga chake cha kukhala pamwamba pa “nyenyezi” zimenezo. Sakuthokoza Yehova kuti ndiye wamutheketsa kuwagonjetsa. M’malo mwake, iye kwenikweni modzikuza akudziika pamalo a Yehova..

ip-1 189 ¶1

Uphungu wa Yehova Wotsutsa Amitundu

YEHOVA angagwiritse ntchito amitundu kulanga anthu ake chifukwa cha kuipa kwawo. Ngakhale n’choncho, mitunduyo saikhululukira chifukwa cha nkhanza zawo, kunyada kwawo, ndi kudana kwawo ndi kulambira koona. Motero kudakali nthawi yaitali kuti zichitike, akuuzira Yesaya kulemba za “katundu wa Babulo.” (Yesaya 13:1) Komabe, Babulo adzaopsa m’tsogolo. M’masiku a Yesaya, Asuri ndiye akupondereza anthu apangano a Mulungu. Asuri wawononga ufumu wakumpoto wa Israyeli ndi kusakaza Yuda kwambiri. Koma chipambano cha Asuri n’chochepa. Yesaya akulemba kuti: “Yehova wa makamu walumbira, nati, Ndithu monga ndaganiza, chotero chidzachitidwa . . . kuti Ine ndidzathyola Asuri m’dziko langa, ndi pamwamba pa mapiri anga ndidzawapondereza; pomwepo goli lidzachoka pa iwo, ndi katundu wake adzachoka paphuzi pawo.” (Yesaya 14:24, 25) Mosakhalitsa Yesaya atanena ulosi umenewu, kuopsa kwa Asuri mu Yuda kukuthetsedwa.

ip-1 194 ¶12

Uphungu wa Yehova Wotsutsa Amitundu

Kodi ulosiwu udzakwaniritsidwa liti? Posachedwapa. “Awa ndi mawu amene Yehova adanena za Moabu nthawi zapitazo. Koma tsopano Yehova wanena, nati, Zisanapite zaka zitatu monga zaka za wolembedwa ntchito, ulemerero wa Moabu udzakhala wonyozeka, ndi khamu lalikulu lake, ndi otsala adzakhala ang’onong’ono ndi achabe.” (Yesaya 16:13, 14) Mogwirizana ndi zimenezi, pali umboni wa ofukula za m’mabwinja kuti mu zaka za zana la chisanu ndi chitatu B.C.E., Moabu anavutika kwambiri ndipo m’midzi yake yambiri munatsala anthu ochepa. Tigilati Pilesere 3 anatchula Salamanu wa ku Moabu kuti anali m’modzi wa olamulira amene anali kumupatsa msonkho. Sanakeribu analandira msonkho kuchokera kwa Kamusunabi, mfumu ya Moabu. Mafumu a Asuri Esarihadoni ndi Ashabanipalu anati anali kulamulira Mfumu Musuri ndi Mfumu Kamashalitu, mafumu a Moabu. Zaka mazana angapo zapitazo, Amoabu sanakhalekonso monga mtundu wa anthu. Mabwinja a midzi yomwe ikulingaliridwa kuti inali ya Amoabu apezeka, koma kufikira lerolino pafukulidwa chabe umboni wochepa wa mdani wa Israyeli ameneyu amene panthawi ina anali wamphamvu.

Mfundo Zothandiza

w06 12/1 10 ¶11

Mfundo Zazikulu za M’buku la Yesaya​—Gawo 1

14:1, 2​— Kodi zinachitika motani kuti anthu a Yehova atengere m’ndende amitundu omwe poyamba anawatengera m’ndende iwowo ndiponso kuti ‘alamulire owavuta’? Zimenezi zinachitika kwa anthu ngati Danieli, amene anali ndi udindo waukulu ku Babulo pansi pa ulamuliro wa Amedi ndi Aperisi; Estere, amene anakhala mfumukazi ya Aperisi; Moredekai amene anakhala nduna yaikulu mu ufumu wa Aperisi.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Nkhani

ijwbq nkhani Na. 108

Kodi Ulosi Umatanthauza Chiyani?

Yankho la m’Baibulo

Ulosi ndi uthenga wochokera kwa Mulungu wopita kwa anthu. Baibulo limanena kuti aneneri “analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.” (2 Petulo 1:20, 21) Apa zikusonyeza kuti mneneri ndi munthu amene amalandira uthenga kuchokera kwa Mulungu n’kumauza anthu ena.​—Machitidwe 3:18.

Kodi aneneri ankalandira bwanji mauthenga ochokera kwa Mulungu?

Mulungu anagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana popereka mauthenga kwa aneneri ake:

● Kulemba. Mulungu anagwiritsa ntchito njira imeneyi pamene analemba Malamulo Khumi ndi kuwapereka kwa Mose.​—Ekisodo 31:18.

● Kulankhula kudzera mwa angelo. Mwachitsanzo, Mulungu anagwiritsa ntchito mngelo pouza Mose uthenga woti akapereke kwa Farao ku Iguputo. (Ekisodo 3:2-4, 10) Mulungu akafuna kuti uthenga wake ukhale ndi mawu ena apadera, ankauza angelo kuti akafotokozere anthu uthengawu ndendende mmene iyeyo waunenera. Mwachitsanzo anachita zimenezi pa nthawi imene anauza Mose kuti: “Dzilembere mawuwa chifukwa ine ndikuchita pangano ndi iwe ndi Isiraeli mogwirizana ndi mawu amenewa.”​—Ekisodo 34:27.

● Masomphenya. Nthawi zina mneneri ankaona masomphenya ali m’maso komanso akudziwa zimene zikuchitika. (Yesaya 1:1; Habakuku 1:1) Masomphenya ena ankaoneka ngati ndi zenizeni moti anthu amene anaonetsedwa masomphenyawo ankachita zinthu ngati kuti zikuchitikadi. (Luka 9:28-36; Chivumbulutso 1:10-17) Koma nthawi zina aneneri ankaona masomphenya atachita ngati akomoka. (Machitidwe 10:10, 11; 22:17-21; Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Mulungu ankatumizanso uthenga wake kwa aneneri pogwiritsa ntchito maloto aneneriwo ali m’tulo.​—Danieli 7:1; Machitidwe 16:9, 10.

● Kutsogolera maganizo awo. Mulungu ankatsogolera maganizo a aneneri ake kuti iwo azindikire uthenga wake. Izi n’zogwirizana ndi mawu a m’Baibulo akuti: “Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu.” Mawu amene anamasuliridwa kuti ‘kuuzira’ akhoza kumasuliridwanso kuti ‘kupumira.’ (2 Timoteyo 3:16; The Emphasised Bible) Choncho zinali ngati Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu wake woyera, kapena kuti mphamvu imene amagwiritsa ntchito, kuti apumire uthenga wake m’maganizo mwa atumiki ake. Ndiyeno aneneriwo akalandira uthenga wochokera kwa Mulungu, ankasankha mawu abwino oti agwiritse ntchito poulemba.​—2 Samueli 23:1, 2.

Kodi nthawi zonse ulosi umaneneratuzam’tsogolo?

Ayi, sikuti maulosi onse a m’Baibulo amangonena zam’tsogolo zokha. Koma n’zoona kuti mauthenga ambiri ochokera kwa Mulungu amanena zinazake zokhudza m’tsogolo. Mwachitsanzo, kawirikawiri aneneri a Mulungu ankachenjeza Aisiraeli chifukwa cha makhalidwe awo oipa. Aneneriwo ankafotokoza madalitso amene Aisiraeliwo angalandire akamvera chenjezolo komanso tsoka limene angakumane nalo akapanda kumvera. (Yeremiya 25:4-6) Zotsatirapo zake zinkadalira zimene Aisiraeliwo angasankhe kuchita.​—Deuteronomo 30:19, 20.

Zitsanzo za maulosi a m’Baibulo omwe sananeneretu zam’tsogolo

● Nthawi ina Aisiraeli atapempha kuti Mulungu awathandize, iye anatuma mneneri kuti akawauze zoti Mulungu sanawathandize chifukwa choti sanamvere malamulo ake.​—Oweruza 6:6-10.

● Pamene Yesu ankalankhula ndi mayi wachisamariya, ananena zinthu zokhudza mbiri ya mayiyo zomwe Yesuyo sakanazidziwa popanda kuuzidwa ndi Mulungu. Mayiyo anazindikira kuti Yesu anali mneneri ngakhale kuti sananeneretu chilichonse cham’tsogolo.​—Yohane 4:17-19.

● Pa nthawi imene anthu ankaimba Yesu mlandu, adani ake anamuphimba kumaso, kumumenya ndi kumuuza kuti: “Losera. Wakumenya ndani”? Apa sikuti adaniwo ankafuna kuti Yesu anene zam’tsogolo koma kuti, mothandizidwa ndi Mulungu, anene amene wamumenya.​—Luka 22:63, 64.

[Mawu a M’munsi]

a Anthu a zikhalidwe zina sakhala pa chibwenzi asanakwatirane. Baibulo silinena kuti anthu ayenera kukhala kaye pa chibwenzi kuti akwatirane.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena