-
Davide Anapha GoliyatiZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 40
Davide Anapha Goliyati
Yehova anauza Samueli kuti: ‘Pita kunyumba ya Jese. Mwana wake wina adzakhala mfumu ya Isiraeli.’ Samueli anapitadi ndipo ataona mwana woyamba wa Jese, anaganiza kuti: ‘Amene adzakhale mfumu uja ndi ameneyu.’ Koma Yehova anauza Samueli kuti si ameneyo. Kenako anamuuzanso kuti: ‘Ine ndimaona mtima wa munthu osati zimene anthu amaona.’
Jese anabweretsa ana ake ena 6 koma Samueli anati: ‘Apa palibe aliyense amene Yehova wamusankha. Kodi anyamata anu onse ndi omwewa basi?’ Jese anati: ‘Watsala mmodzi wamng’ono kwambiri, dzina lake Davide. Wapita koweta nkhosa.’ Davide atafika, Yehova anauza Samueli kuti: ‘Ndi ameneyu!’ Zitatero Samueli anathira mafuta pamutu pa Davide. Kusonyeza kuti anamudzoza kuti adzakhale mfumu ya Isiraeli.
Pa nthawi ina, Aisiraeli ankamenyana ndi Afilisiti. Ndiyeno kumbali ya Afilisitiwo kunali chimunthu chachikulu komanso champhamvu dzina lake Goliyati. Tsiku lililonse, Goliyati ankanyoza Aisiraeli. Ankanena kuti: ‘Ndipatseni munthu woti ndimenyane naye! Ngati angandigonjetse nʼkundipha, ndiye kuti tidzakhala antchito anu. Koma ngati ndingamugonjetse, inuyo mudzakhala antchito athu.’
Davide anafika pamalo pamene panali asilikali a Isiraeli n’cholinga choti apereke chakudya kwa azichimwene ake omwe anali asilikali. Davide anamva zimene Goliyati ankanena ndipo anati: ‘Ine ndikamenyana naye ameneyu.’ Mfumu Sauli atamva anati: ‘Iwe ndiwe mwana.’ Davide anayankha kuti: ‘Yehova andithandiza.’
Sauli anaveka Davide zovala zake zomenyera nkhondo koma iye anati: ‘Sindingathe kumenya nkhondo ndi zovala zimenezi.’ Choncho anangotenga chinthu choponyera miyala chotchedwa gulaye n’kutsetserekera kukamtsinje. Ndiyeno anatola miyala yosalala bwino 5 n’kuika m’kachikwama kake. Kenako Davide anayamba kuthamangira kumene kunali Goliyati. Goliyatiyo atamuona anati: ‘Mwana iwe! Bwera ndikuphe ndipo ukhala chakudya cha mbalame ndi zilombo zakutchire.’ Davide sanachite mantha. M’malomwake anamuyankha kuti: ‘Iwe ukubwera kudzamenyana ndi ine ndi lupanga komanso mkondo, koma ine ndikubwera kudzamenyana nawe mʼdzina la Yehova. Sukumenyana ndi ine ayi koma ndi Mulungu. Ndipo onse amene ali panowa adziwa kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga kapena mkondo. Nonsenu akuperekani mʼmanja mwathu.’
Kenako Davide anaika mwala pagulaye uja n’kuuponya mwamphamvu kwambiri. Yehova anamuthandiza moti mwalawo unathamanga n’kukaboola Goliyati pachipumi. Nthawi yomweyo Goliyati anagwa n’kufa. Afilisiti ataona zimenezi anayamba kuthawa. Kodi iweyo umadalira Yehova ngati mmene Davide ankachitira?
“Kwa anthu zimenezi nʼzosatheka, koma sizili choncho kwa Mulungu chifukwa zinthu zonse nʼzotheka kwa Mulungu.”—Maliko 10:27
-
-
Davide ndi SauliZimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
-
-
MUTU 41
Davide ndi Sauli
Davide atangopha Goliyati, Mfumu Sauli inamusankha kuti akhale mkulu wa asilikali. Davide anapambana nkhondo zambiri ndipo anatchuka kwambiri. Akamabwera kunkhondo, akazi ankavina komanso kuimba kuti: ‘Sauli wapha adani masauzande koma Davide wapha masauzande ambirimbiri.’ Sauli anapsa mtima kwambiri moti anayamba kufuna kupha Davide.
Davide ankadziwa kuimba zeze. Tsiku lina akuimbira Sauli nyimbo, Sauliyo anaponya mkondo wake kuti amuphe. Davide anazinda ndipo mkondowo unafikira pakhoma. Kungoyambira pamenepo, Sauli ankayesetsa kuti aphe Davide. Kenako Davide anathawira kuchipululu.
Sauli anatenga asilikali 3,000 n’kumakasakasaka Davide. Ndiyeno tsiku lina analowa kuphanga limene kunali Davide ndi anzake. Anzake a Davidewo anati: ‘Uwutu ndi mwayi wako kuti uphe Sauli.’ Davide anangoyenda chokwawa n’kukadula kansalu pa chovala cha Sauli koma Sauliyo sanadziwe chilichonse. Zitatero, Davide anadandaula kwambiri kuti sanalemekeze mfumu yodzozedwa ndi Mulungu. Iye sanalole kuti anzakewo aphe Sauli. Kenako Sauli atatuluka m’phangamo, Davide anafuula n’kumuuza kuti anali ndi mwayi woti amuphe koma anangomusiya. Kodi Sauli anasintha maganizo?
Ayi ndithu. Anapitirizabe kusakasaka Davide. Tsiku lina usiku, Davide ndi m’bale wake dzina lake Abisai anapita pamalo amene Sauli anagona ndi asilikali ake. Anapeza kuti Abineri, amene anali msilikali wolondera mfumu, nayenso anali atagona. Ndiyeno Abisai anati: ‘Mwayitu suposa apa. Bwanji ndimuphe?’ Koma Davide anati: ‘Ayi, ameneyutu adzalangidwa ndi Yehova. Tiye tingotenga mkondo wake ndi jagi yakeyo tizipita.’
Kenako Davide anakakwera paphiri lina lapafupi n’kufuula kuti: ‘Iwe Abineri! Ukungogona osateteza mfumuyo? Kodi mkondo wa Sauli ndi madzi ake zili kuti?’ Sauli atazindikira mawu a Davide anati: ‘Mpata woti undiphe unaupeza koma wandikomera mtima. Ndazindikira tsopano kuti iwe udzakhaladi mfumu ya Isiraeli.’ Apa tsopano Sauli anabwerera kunyumba kwake. Koma sikuti anthu onse a m’banja la Sauli ankadana ndi Davide.
“Ngati nʼkotheka, yesetsani mmene mungathere kuti muzikhala mwamtendere ndi anthu onse. Okondedwa, musamabwezere zoipa, koma siyirani malo mkwiyo wa Mulungu.”—Aroma 12:18, 19
-