Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yonatani Anali Wolimba Mtima Komanso Wokhulupirika
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
    • Yonatani ndi mtumiki wake amene ankamunyamulira zida

      MUTU 42

      Yonatani Anali Wolimba Mtima Komanso Wokhulupirika

      Mwana wamkulu wa Mfumu Sauli anali Yonatani ndipo anali msilikali wolimba mtima. Davide ananena kuti Yonatani ankathamanga kuposa chiwombankhanga ndipo anali wamphamvu kuposa mkango. Tsiku lina, Yonatani anaona asilikali 20 a Afilisiti ali paphiri. Iye anauza mtumiki wake amene ankamunyamulira zida kuti: ‘Awotu tikhoza kuwagonjetsa. Tiye tione ngati Yehova angatipatse chizindikiro. Akatiuza kuti tipite ndiye kuti ndi nthawi yabwino ndipo tikawagonjetsa.’ Nthawi yomweyo Afilisitiwo anafuula kuti: ‘Bwerani tikukhaulitseni!’ Yonatani ndi mtumiki wakeyo anakweradi phirilo ndipo anakawagonjetsa.

      Yonatani akupatsa Davide zinthu zake zina

      Popeza Yonatani anali mwana woyamba, anali woyenera kudzalowa ufumu wa Sauli. Koma iye ankadziwa kuti Yehova anasankha Davide ndipo sankamuchitira nsanje. Yonatani ndi Davide ankagwirizana kwambiri ndipo analonjezana kuti azitetezana. Yonatani anapatsa Davide zovala zake zankhondo, lupanga, uta ndi lamba posonyeza kuti ndi mnzake wapamtima.

      Pa nthawi ina, Davide akuthawa Sauli, mnzakeyu anapita kukamuuza kuti: ‘Limba mtima ndipo usaope chilichonse. Yehova wakusankha kuti ukhale mfumu. Ngakhale bambo anga akudziwa zimenezi.’ Kodi iweyo ungafune kukhala ndi mnzako wabwino ngati Yonatani?

      Yonatani ankaika moyo wake pangozi pofuna kuthandiza Davide. Iye ankadziwa zoti Mfumu Sauli akufuna kupha Davide ndiye anauza bambo akewo kuti: ‘Bambo mukudziwa kuti mukulakwa? Kodi Davide wakulakwirani chiyani kuti mumuphe?’ Koma Sauli anamukwiyira kwambiri Yonatani. Patapita zaka, Sauli ndi Yonatani anafera kunkhondo.

      Yonatani atafa, Davide anafufuza mwana wake dzina lake Mefiboseti. Atamupeza anamuuza kuti: ‘Bambo ako tinkagwirizana kwambiri choncho ndikusamalira kwa moyo wako wonse. Uzikhala m’nyumba mwanga ndipo tizidyera limodzi.’ Apatu Davide anasonyeza kuti sanaiwale Yonatani.

      “Muzikondana mofanana ndi mmene ine ndimakukonderani. Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa cha munthu amene wapereka moyo wake chifukwa cha anzake.”​—Yohane 15:12, 13

      Mafunso: Kodi Yonatani anasonyeza bwanji kuti anali wolimba mtima? Nanga anasonyezanso bwanji kuti anali wokhulupirika?

      1 Samueli 14:1-23; 18:1-4; 19:1-6; 20:32-42; 23:16-18; 31:1-7; 2 Samueli 1:23; 9:1-13

  • Tchimo la Mfumu Davide
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
    • Mneneri Natani akudzudzula Mfumu Davide

      MUTU 43

      Tchimo la Mfumu Davide

      Sauli atafa, Davide anakhala mfumu. Iye anayamba kulamulira ali ndi zaka 30. Tsiku lina ali padenga la nyumba yake anaona mkazi wokongola. Atafufuza anapeza kuti dzina lake anali Bati-seba ndipo anali mkazi wa Uriya,yemwe anali msilikali. Davide anaitanitsa mkaziyo kuti abwere kunyumba kwake. Iye anagona naye ndipo mkaziyo anakhala oyembekezera. Davide anayesa kupeza njira yoti tchimo lakelo lisadziwike. Iye anauza mkulu wa asilikali kuti aike Uriya kutsogolo n’kumusiya kuti aphedwe. Uriya ataphedwa ku nkhondo, Davide anakwatira Bati-seba.

      Mfumu Davide akupempha Mulungu kuti amukhululukire

      Koma Yehova ankaona zoipa zonsezi. Ndiye kodi anatani? Iye anatumiza Natani kuti akakambirane ndi Davide za nkhaniyi. Natani atafika kwa Davide anamuuza kuti: ‘Panali munthu wina wolemera amene anali ndi nkhosa zambiri ndiye panalinso wosauka yemwe anali ndi kankhosa kamodzi kokha. Wosaukayo ankakakonda kwambiri kankhosa kakeko. Ndiyeno munthu wolemera uja analanda kankhosa ka wosaukayo kuti kakhalenso kake.’ Davide atamva zimenezi, anakwiya kwambiri ndipo anati: ‘Munthu ameneyu ayenera kufa basi.’ Natani anauza Davide kuti: ‘Munthu wolemerayo ndi inuyo.’ Davide anazindikira zimene Natani ankatanthauza ndipo anamva chisoni. Ndiyeno anauza Natani kuti: ‘Ndachimwira Yehova.’ Tchimo limeneli linam’bweretsera mavuto Davide limodzi ndi banja lake. Yehova anapereka chilango kwa Davide koma sanamuphe chifukwa anadzichepetsa komanso analapa kuchokera pansi pa mtima.

      Davide ankafuna kumanga nyumba ya Yehova. Koma Yehova anasankha mwana wake Solomo kuti ndi amene adzamange nyumbayo. Davide anayamba kusonkhanitsa zinthu zoti Solomo adzagwiritse ntchito pomanga. Iye anati: ‘Nyumba ya Yehova ikufunika idzakhale yokongola kwambiri. Popeza Solomo adakali mwana, ndimuthandiza kupeza zipangizo zomangira nyumbayi.’ Choncho Davide anapereka ndalama zambiri zoti zidzathandize pa ntchito yomanga nyumbayo. Anapeza anthu aluso komanso anasonkhanitsa golide ndi siliva wambiri ndiponso anasonkhanitsa matabwa a mtengo wa mkungudza ochokera ku Turo ndi ku Sidoni. Davide atatsala pang’ono kumwalira, anapatsa Solomo pulani ya mmene adzamangire nyumbayo. Anati: ‘Yehova anandiuza kuti ndikulembere pulaniyi. Usachite mantha chifukwa iye akuthandiza. Limba mtima ndipo yamba kugwira ntchitoyi.’

      Davide akukambirana ndi Solomo zokhudza mapulani a kachisi

      “Wobisa machimo ake zinthu sizidzamuyendera bwino, koma amene amawaulula nʼkuwasiya adzachitiridwa chifundo.”​—Miyambo 28:13

      Mafunso: Kodi Davide anachita tchimo lotani? Kodi Davide anathandiza bwanji Solomo kuti amange nyumba ya Yehova?

      2 Samueli 5:3, 4, 10; 7:1-16; 8:1-14; 11:1-27; 12:1-14; 1 Mbiri 22:1-19; 28:11-21; Salimo 51:1-19

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena