Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Zimene Zinachitika Paphiri la Karimeli
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
    • Moto wochokera kwa Yehova ukupsereza nsembe ya Eliya

      MUTU 46

      Zimene Zinachitika Paphiri la Karimeli

      Ufumu wa mafuko 10 wa Isiraeli unali ndi mafumu ambiri oipa. Koma Mfumu Ahabu ndi amene anali woipa kuposa onsewo. Iye anakwatira mkazi woipa amene ankalambira Baala ndipo dzina lake anali Yezebeli. Ahabu ndi Yezebeli ankapha aneneri a Yehova komanso anapangitsa kuti anthu ambiri a ku Isiraeli azilambira Baala. Ndiye kodi Yehova anatani? Anatumiza mneneri Eliya kuti akapereke uthenga kwa Ahabu.

      Eliya anauza mfumuyi kuti popeza inkachita zoipa, m’dziko la Isiraeli simugwa mvula. Kwa zaka zoposa zitatu anthu sanathe kulima chakudya chifukwa kunali chilala. Choncho m’dzikolo munagwa njala. Kenako Yehova anatumizanso Eliya kwa Ahabu. Ndiyeno mfumuyo inati: ‘Iwe ndi amene wabweretsa mavuto onsewa.’ Koma Eliya anayankha kuti: ‘Ayi si ine. Mwabweretsa chilalachi ndi inuyo chifukwa mukulambira Baala. Sonkhanitsani anthu ndi aneneri a Baala pamwamba pa phiri la Karimeli kuti tikaone umboni wa zimenezi.’

      Anthu anasonkhanadi paphirilo. Ndiyeno Eliya anawauza kuti: ‘Sankhani Mulungu woti muzimulambira. Ngati Yehova ali Mulungu woona mʼtsatireni, koma ngati Mulungu woona ndi Baala tsatirani ameneyo. Atumiki 450 a Baala akonze nsembe ndipo apemphere kwa mulungu wawo kuti apsereze nsembeyo. Inenso ndikonza nsembe yanga ndipo ndipemphera kwa Yehova kuti aipsereze. Mulungu amene angathe kupserezadi nsembezi ndiye woona.’ Anthuwo anavomera.

      Aneneri a Baala anakonzadi nsembe yawo. Iwo anapemphera kwa mulungu wawo tsiku lonse kuti: ‘Inu a Baala, tiyankheni!’ Koma Baala sanawayankhe. Kenako Eliya anayamba kuwaseka. Anawauza kuti: ‘Muitaneni mokweza. Mwina wagona ndipo pakufunika wina amudzutse.’ Aneneri a Baala anapitirizabe kupemphera mpaka madzulo koma Baalayo sanawayankhe.

      Kenako Eliya anaika nsembe yake paguwa ndipo anathirapo madzi. Ndiyeno anapemphera kuti: ‘Inu Yehova, chititsani kuti anthu awa adziwe kuti inu ndinu Mulungu woona.’ Nthawi yomweyo Yehova anatumiza moto kuchokera kumwamba ndipo unapsereza nsembeyo. Anthu ataona zimenezi anayamba kufuula kuti: “Mulungu woona ndi Yehova!” Eliya anati: “Gwirani aneneri a Baala! Muonetsetse kuti pasapezeke wothawa!” Pa tsikuli aneneri onse a Baala okwana 450 anawapha.

      Kenako kunyanja kunaoneka kamtambo kakang’ono ndipo Eliya anauza Ahabu kuti: ‘Kugwa chimvula champhamvu. Kwerani galeta muzipita kwanu.’ Mwadzidzidzi kunja kunachita mdima wa mitambo, kunayamba kuwomba chimphepo ndipo kenako chimvula chinayamba kugwa. Apa ndiye kuti chilala chija chinatha. Ahabu anayamba kuthamangitsa galeta lake n’cholinga choti chimvulacho chisamutsekereze. Koma mothandizidwa ndi Yehova, Eliya anathamanga mpaka kupitirira galeta la Ahabu lija. Ndiye kodi mavuto a Eliya anathera pamenepa? Tiona m’nkhani yotsatira.

      “Anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, inu nokha ndinu Wamʼmwambamwamba, woyenera kulamulira dziko lonse lapansi.”​—Salimo 83:18

      Mafunso: Kodi paphiri la Karimeli panachitika zotani? Kodi Yehova anayankha bwanji pemphero la Eliya?

      1 Mafumu 16:29-33; 17:1; 18:1, 2, 17-46; Yakobo 5:16-18

  • Yehova Analimbikitsa Eliya
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
    • Eliya waima pakhomo la phanga paphiri la Horebe ndipo akumvetsera zimene mngelo wa Yehova akunena

      MUTU 47

      Yehova Analimbikitsa Eliya

      Yezebeli atamva zimene zinachitikira aneneri a Baala, anakwiya kwambiri. Ndiyeno anatumiza uthenga kwa Eliya wakuti: ‘Mawa nawenso ufa ngati mmene afera aneneri a Baala.’ Eliya atamva zimenezi anachita mantha kwambiri ndipo anathawira kuchipululu. Kumeneko anapemphera kuti: ‘Yehova, zimene zikuchitikazi ndatopa nazo. Ndiloleni kuti ndingofa.’ Chifukwa chotopa, Eliya anagona tulo pansi pa mtengo.

      Kenako kunabwera mngelo n’kumugwedeza ndipo anamuuza kuti: ‘Dzuka udye.’ Eliya atayang’ana, anaona chikho cha madzi komanso mkate wozungulira uli pamiyala yotentha. Anadya mkatewo n’kumwa madziwo ndipo kenako anagonanso. Patapita nthawi, mngelo uja anabweranso kudzamudzutsa n’kumuuza kuti: ‘Idyanso kuti upeze mphamvu chifukwa uyenda ulendo wautali.’ Choncho Eliya anadzuka n’kudyanso. Kenako anayenda kwa masiku 40, masana ndi usiku mpaka kukafika paphiri la Horebe. Kumeneko Eliya analowa kuphanga n’kugona. Koma Yehova anamufunsa kuti: ‘Ukudzatani kuno Eliya?’ Eliya anayankha kuti: ‘Aisiraeli aswa pangano lawo ndi inu. Agwetsa maguwa anu ansembe ndipo apha aneneri anu. Panopa akufunanso kupha ineyo.’

      Koma Yehova anamuuza kuti: ‘Pita ukaime paphiri.’ Ndiyeno panawomba chimphepo kudutsa pakhomo la phangalo. Kenako kunachita chivomerezi ndipo pambuyo pa chivomerezicho, kunabuka moto. Zitatere Eliya anamva mawu achifatse apansipansi. Atangomva mawuwo, anaphimba nkhope yake ndi chovala chake ndipo anatuluka n’kukaima pakhomo la phanga lija. Yehova anamufunsanso kuti: ‘Ukudzatani kuno Eliya?’ Eliya anayankha kuti: ‘Ndatsala ndekhandekha.’ Koma Yehova anamuuza kuti: ‘Suuli wekha. Mu Isiraeli mulinso anthu ena okwana 7,000 amene akundilambirabe. Pita ukadzoze Elisa kuti adzakhale mneneri mʼmalo mwako.’ Nthawi yomweyo Eliya anapita kukachita zimene Yehova anamuuzazo. Kodi ukuganiza kuti nawenso Yehova angakuthandize ukamachita zimene amafuna? Inde angakuthandize. Tsopano tiye tione zimene zinachitika pa nthawi yachilala.

      “Musamade nkhawa ndi chinthu chilichonse. Mʼmalomwake, nthawi zonse muzipemphera kwa Mulungu, muzimuchonderera kuti azikutsogolerani pa chilichonse ndipo nthawi zonse muzimuthokoza.”​—Afilipi 4:6

      Mafunso: Kodi n’chifukwa chiyani Eliya anathawa? Kodi Yehova anamuuza chiyani Eliya?

      1 Mafumu 19:1-18; Aroma 11:2-4

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena