Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Mwana wa Mayi Wamasiye Anaukitsidwa
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
    • Eliya akuitana mayi wamasiye amene akutola nkhuni

      MUTU 48

      Mwana wa Mayi Wamasiye Anaukitsidwa

      Mtsuko wa ufa ndi wa mafuta

      Pamene ku Isiraeli kunali chilala, Yehova anauza Eliya kuti: ‘Pita ku Zarefati. Kumeneko mayi wina wamasiye azikakupatsa chakudya.’ Eliya atafika mumzindawo, anaona mayi wosauka komanso wamasiye akutola nkhuni. Iye anam’pempha kuti amupatseko madzi. Pamene mayiyo ankapita kukatenga madziwo, Eliya anamuuzanso kuti: ‘Mundibweretserekonso chakudya pang’ono.’ Koma mayiyo anati: ‘Ndilibe chakudya choti ndingakupatseni. Ndangotsala ndi kaufa kochepa ndi timafuta toti ndiphikire chakudya chokwanira ineyo ndi mwana wanga basi.’ Koma Eliya anamuuza kuti: ‘Yehova wanena kuti mukandipatsa, ndiye kuti ufa ndi mafuta anu sizitha mpaka mvula idzagwe.’

      Ndiyeno mayiyo anapita kukakonza chakudya n’kupatsa mneneri wa Yehovayo. Mogwirizana ndi zimene Yehova ananena, mayiyo ndi mwana wake anali ndi chakudya pa nthawi yonse yachilalayo. Mtsuko wake wa ufa komanso wa mafuta unkangokhalabe wodzadza.

      Kenako panachitika zinthu zomvetsa chisoni. Mwana uja anadwala kwambiri mpaka kumwalira. Ndiyeno mayiyo anapempha Eliya kuti amuthandize. Eliya anatenga mwana wakufayo n’kupita naye kuchipinda cham’mwamba. Anamugoneka pabedi ndipo anapemphera kuti: ‘Chonde Yehova, ukitsani mwanayu.’ Kodi ukuganiza kuti n’chifukwa chiyani zimene Eliya anapemphazi zinali zodabwitsa? Chifukwa kuyambira kalekale, zimenezi zinali zisanachitikepo. Komanso mayiyu ndi mwana wakeyo sanali Aisiraeli.

      Koma mwana uja anakhalanso ndi moyo ndipo anayamba kupuma. Eliya anauza mayiyo kuti: ‘Mwana wanu uja tsopano ali moyo.’ Mayiyo anasangalala kwambiri ndipo anauza Eliya kuti: ‘Ndinudi munthu wa Mulungu. Ndikutero chifukwa mumalankhula zimene Yehova wakuuzani.’

      Eliya waukitsa mwana ndipo akumupereka kwa mayi ake

      “Ganizirani za akhwangwala: Iwo safesa mbewu kapena kukolola. Alibe nkhokwe kapena nyumba yosungiramo zinthu, koma Mulungu amawadyetsa. Kodi inu si amtengo wapatali kuposa mbalame?”​—Luka 12:24

      Mafunso: Kodi mayi wamasiye wa ku Zarefati anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira Yehova? Kodi tikudziwa bwanji kuti Eliya analidi mneneri wa Mulungu?

      1 Mafumu 17:8-24; Luka 4:25, 26

  • Yehova Anapereka Chilango kwa Mfumukazi Yoipa
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
    • Antchito a Yezebeli akumuponyera pansi kudzera pawindo

      MUTU 49

      Mfumukazi Yoipa Inalangidwa

      Mfumu Ahabu akayang’ana pawindo ali m’nyumba yake ku Yezereeli, ankaona munda wa mpesa wa Naboti. Ahabu ankaufuna kwambiri mundawo ndipo anauza Naboti kuti amugulitse. Koma Naboti anakana chifukwa Chilamulo cha Yehova chinkaletsa anthu kugulitsa cholowa kapena kuti malo amene anapatsidwa ndi makolo awo. Kodi Ahabu anasangalala kuti Naboti wachita zoyenera? Ayi. M’malomwake iye anakwiya kwambiri ndipo anakana kudya komanso sanatuluke kuchipinda kwake.

      Ndiyeno mkazi wake Yezebeli yemwe anali woipa kwambiri anamuuza kuti: ‘Ndinu mfumu ya Isiraeli. Choncho mungathe kupeza chilichonse chimene mukufuna. Ndipanga zotheka kuti mundawu ukhale wanu.’ Yezebeli analemba makalata kwa akuluakulu a mzinda n’kuwauza kuti amunamizire Naboti kuti wanyoza Mulungu ndipo amuphe pomugenda ndi miyala. Akuluakuluwo anachitadi zimenezi. Kenako Yezebeli anauza Ahabu kuti: ‘Naboti wafa. Tsopano munda uja ndi wanu.’

      Koma sikuti Yezebeli anapha Naboti yekha. Iye anaphanso anthu ambiri osalakwa amene ankakonda Yehova. Komanso Yezebeli ankalambira mafano ndiponso ankachita zinthu zambiri zoipa. Yehova ankaona zonsezi. Ndiye kodi anatani?

      Ahabu atamwalira, mwana wake Yehoramu, anakhala mfumu. Yehova anatumiza munthu wina dzina lake Yehu kuti akapereke chilango kwa Yezebeli ndi banja lake.

      Yehu anakwera galeta n’kuuyamba ulendo wopita ku Yezereeli kumene Yezebeli ankakhala. Atatsala pang’ono kufika, Yehoramu anamuchingamira pa galeta lake. Ndiyeno anamufunsa kuti: ‘Kodi ukubwerera zamtendere Yehu?’ Koma Yehu anayankha kuti: ‘Mtendere ungakhalepo bwanji, mayi ako a Yezebeli akuchita zoipa zambirimbiri?’ Yehoramu atamva zimenezi anatembenuza galeta lake n’kuyamba kuthawa. Koma Yehu anamubaya ndi muvi ndipo anafera pompo.

      Yehu akulamula kuti Yezebeli aponyedwe pansi

      Kenako Yehu anapita kunyumba kwa Yezebeli. Yezebeli atamva kuti Yehu akubwera, anadzikongoletsa n’kukonzanso tsitsi lake ndipo anapita pawindo n’kumakamudikira. Yehu atafika, Yezebeli anamulonjera mwachipongwe. Ndiyeno Yehu anauza antchito a Yezebeli kuti: “M’ponyeni pansi.” Iwo anaponyadi Yezebeli kudzera pawindo ndipo anagwera pansi n’kufa.

      Zitatero Yehu anapha ana aamuna 70 a Ahabu n’kuthetsa kulambira Baala m’dziko lonselo. Kodi waona kuti Yehova amadziwa zonse ndipo pa nthawi yoyenera amapereka chilango kwa anthu amene akuchita zoipa?

      “Munthu akapeza cholowa mwadyera, pamapeto pake Mulungu sadzamudalitsa.”​—Miyambo 20:21

      Mafunso: Kodi Yezebeli anatani kuti Mfumu Ahabu atenge munda wa Naboti? N’chifukwa chiyani Yehova anapereka chilango kwa Yezebeli?

      1 Mafumu 21:1-29; 2 Mafumu 9:1-37; 10:1-30

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena